Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi mawu achigiriki akuti eu·nouʹkhos amatanthauza chiyani?

Chithunzi cha munthu wofulidwa wa ku Siriya

Nthawi zina m’Baibulo mawuwa anamasuliridwa kuti munthu wofulidwa. Amuna ena omwe alakwa ankawapatsa chilango chowafula. Ena ankafulidwa chifukwa choti ndi akapolo ogwidwa pa nkhondo. Amuna ena ofulidwawo, omwe anali okhulupirika, ankawasankha kuti aziyang’anira nyumba za akazi, akazi a mfumu komanso nyumba zachifumu. Mwachitsanzo, Baibulo limanena kuti Hegai ndi Sasigazi ankayang’anira akazi ndi atsikana a Mfumu Ahasiwero. Ahasiwero anali mfumu ya Perisiya ndipo ena amati anali Sasita Woyamba.—Esitere 2:3, 14.

Komabe m’Baibulo mawuwa anamasuliridwanso kuti nduna kutanthauza munthu amene anali ndi udindo waukulu m’nyumba ya mfumu. Zitsanzo za anthu amenewa ndi Ebedi-meleki, yemwe anali mnzake wa Yeremiya komanso munthu yemwe sanatchulidwe dzina wa ku Itiyopiya, amene analalikiridwa ndi Filipo. Zikuoneka kuti Ebedi-meleki anali ndi udindo waukulu chifukwa ankatha kulankhula ndi Mfumu Zedekiya pamasom’pamaso. (Yeremiya 38:7, 8) Pomwe munthu wa ku Itiyopiya anali woyang’anira chuma chonse ndipo pa nthawi imene anakumana ndi Filipo ankachokera ku “Yerusalemu kukapembedza Mulungu.”—Machitidwe 8:27.

N’chifukwa chiyani abusa akale ankalekanitsa nkhosa ndi mbuzi?

Yesu ananena zimene zidzachitike pa nthawi ya chiweruzo. Anati: “Mwana wa munthu akadzafika mu ulemerero wake, . . . adzalekanitsa anthu, mmene m’busa amalekanitsira nkhosa ndi mbuzi.” (Mateyu 25:31, 32) N’chifukwa chiyani abusa ankalekanitsa nkhosa ndi mbuzi?

Nthawi zambiri ziwetozi zinkadyera limodzi masana. Kukada ankazitsekera m’khola pofuna kuziteteza ku nyama zolusa, akuba komanso kuti zisazizidwe. (Genesis 30:32, 33; 31:38-40) Koma ankazitsekera m’makola osiyana pofuna kuteteza nkhosa zoyamwitsa komanso ana a nkhosazo kuti asavulazidwe ndi mbuzi zolusa. Buku lina linafotokoza chifukwa chinanso chomwe abusa ankalekanitsira nkhosa ndi mbuzi. Linati ankachita zimenezi “akafuna kuzikwatitsa, kuzikama mkaka komanso kuzimeta ubweya.” (All Things in the Bible) Choncho, Yesu anagwiritsa ntchito fanizo lonena za zinthu zodziwika bwino kwa anthu a ku Isiraeli omwe ambiri anali abusa.