Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi N’zosathekadi?

Kodi N’zosathekadi?

Kodi N’zosathekadi?

SITIMA ya Titanic imene inayamba kugwira ntchito m’chaka cha 1912, inali yaikulu komanso yapamwamba kuposa sitima zonse zapamadzi za nthawi imeneyo. Chifukwa choti sitimayi inapangidwa mwaukatswiri kwambiri anthu ankaona ngati n’zosatheka kuti imire. Koma sitimayi inamira pa ulendo wake woyamba itawomba madzi oundana kumpoto kwa Nyanja ya Atlantic, ndipo anthu okwana 1,500 anamira nayo limodzi. Sitima imene inkaoneka ngati singamire, inapezeka kuti yamira m’nyanja patangotha maola owerengeka chabe.

Pali zinthu zosiyanasiyana zimene zingatipangitse kuganiza kuti zinthu zinazake n’zosatheka. Nthawi zina timanena kuti chinthu china n’chosatheka chifukwa choti ifeyo tikuona kuti sitingakwanitse kuchichita, sitingachipilire kapenanso sitingachimvetse. Zinthu zamakono zambiri zimene zilipo masiku ano, m’mbuyomu zinkaoneka ngati zosatheka chifukwa pa nthawiyo anthu analibe luso lopangira zinthuzo komanso sankadziwa kuti kudzabwera zinthu zimenezi. Masiku ano anthu amachita zinthu monga kupita kumwezi, kutumiza galimoto ku Mars n’kumaiwongolera ali padziko lapansi pano, kudziwa mmene chibadwa cha anthu chilili, komanso kutha kuona zinthu zimene zikuchitika m’madera osiyanasiyana padziko lonse lapansi. Zinthu zimenezi zinkaoneka ngati zosatheka zaka 50 zapitazo. Zimene zikuchitikazi zinafotokozedwa bwino kwambiri ndi pulezidenti wakale wa ku America, dzina lake Ronald Reagan, pamene ankalankhula kwa akatswiri osiyanasiyana a sayansi. Iye anati: “Inuyo ndi amene mwathandiza kuti zinthu zimene kale zinkaoneka ngati zosatheka, zikhale zotheka.”

Poona zinthu zambiri zogometsa zimene zikuchitika masiku ano, pulofesa wina dzina lake John Brobeck ananena kuti: “Katswiri wa sayansi sanganene motsimikiza kuti chinthu chinachake n’chosatheka. Akhoza kungonena kuti n’zokayikitsa kuti chinthucho chingatheke. Kapena anganene kuti chinthucho n’chovuta kuchilongosola malinga ndi zomwe tikudziwa panopa.” Iye ananenanso kuti ngati chinthu chinachake chikuoneka chosatheka kwa ifeyo, “tiyenera kugwiritsa ntchito mphamvu yapadera imene sifotokozedwa m’mabuku athu a sayansi. M’Malemba, mphamvu imeneyi imafotokozedwa kuti ndi mphamvu ya Mulungu.”

Zinthu Zonse N’zotheka ndi Mulungu

Kale kwambiri, Pulofesa Brobeck asanalankhule zimenezi, Yesu wa ku Nazareti amene amadziwika kuti anali munthu wamkulu woposa onse amene anakhalako, ananena kuti: “Zinthu zosatheka ndi anthu n’zotheka ndi Mulungu.” (Luka 18:27) Mzimu woyera wa Mulungu ndi mphamvu yoposa china chilichonse m’chilengedwechi. Palibe njira iliyonse ya sayansi imene ingathe kutithandiza kudziwa kukula kwa mphamvu imeneyi. Mzimu woyera ungatithandize kuchita zinthu zimene patokha sitikanatha kuchita.

Nthawi zambiri anthufe timakumana ndi zinthu zimene timaona kuti n’zosatheka kuzipirira. Mwachitsanzo, munthu amene timam’konda akhoza kumwalira kapena m’banja mwathu mukhoza kukhala mavuto aakulu moti tingamaone kuti silipitirira. Mwinanso zinthu zina pa moyo wathu zikhoza kusokonekera moti n’kusoweratu pogwira. Zimenezi zikachitika, tingathedwe nzeru komanso tingasowe mtengo wogwira. Kodi zikatero tingatani?

Baibulo limatiuza kuti ngati munthu amakhulupilira Mulungu Wamphamvuyonse, ndipo amam’pempha kuti amupatse mzimu wake komanso amachita zinthu zimene iye amakondwera nazo, angathe kupilira mavuto ooneka ngati osatheka kuwagonjetsa. Taonani mawu olimbikitsa amene Yesu ananena. Iye anati: “Ndithu ndikukuuzani kuti aliyense wouza phiri ili kuti, ‘Nyamuka pano udziponye m’nyanja,’ ndipo sakukayika mumtima mwake, koma ali ndi chikhulupiriro kuti zimene wanena zichitikadi, zidzaterodi.” (Maliko 11:23) Palibe vuto limene sitingathe kulipirira ngati timalola Mawu a Mulungu komanso mzimu wake kutitsogolera pa moyo wathu.

Taganizirani chitsanzo cha mwamuna wina amene anakhala m’banja kwa zaka 38, koma kenako mkazi wake anamwalira ndi matenda a khansa. Iye anakhumudwa kwambiri ndipo zimenezi zinam’chititsa kuona kuti sangathenso kukhala moyo. Moti nthawi zina ankangofuna atafa kusiyana n’kuti akhale ndi moyo popanda mkazi wake. Iye ananena kuti anavutika maganizo kwambiri moti ankangoona ngati akuyenda m’chigwa cha mdima wandiweyani. Akamakumbukira mmene zinthu zinalili pa nthawiyo, iye amakhulupilira kuti mapemphero amene ankapereka kwinaku akulira, kuwerenga Baibulo tsiku ndi tsiku komanso kupempha thandizo la mzimu woyera, ndi zimene zinamuthandiza kupirira zinthu zimene ankaona ngati n’zosatheka kuzipirira.

Banja lina silinkayenda bwino ndipo linangotsala pang’ono kutha. Mwamuna wa m’banjamo anali wachiwawa komanso anali ndi makhalidwe ambiri oipa moti mkazi wake ankaona kuti palibenso chifukwa chokhalira ndi moyo. Pa nthawi ina mkaziyo ankafuna kudzipha. Koma kenako mwamuna uja anayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova. Zimene ankaphunzira zinamuthandiza kuti asiye makhalidwe ake oipa komanso kupsa mtima msanga. Mkazi wake anadabwa kwambiri ataona mmene mwamuna wake anasinthira chifukwa poyamba ankaganiza kuti n’zosatheka kuti mwamuna wake angasinthe.

Mwamuna wina amene ankagwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo komanso kuchita chiwerewere ananena kuti ankakhala moyo wosasangalala. Iye ananena kuti: “Khalidwe langa linkandichotsera ulemu.” Choncho anapemphera kwa Mulungu mochokera pansi pa mtima kuti: “Ambuye ndikudziwa kuti mulipo, chonde ndithandizeni.” Zotsatira zake zinali zoti iye anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova ndipo zimenezi zinachititsa kuti asinthe makhalidwe ake oipa. Iye anati: “Nthawi zambiri ndinkadziimba mlandu komanso ndinkadziona ngati ndine munthu wosafunikira. Nthawi zina ndinkavutika maganizo. Komabe Mawu a Mulungu anandithandiza kuthetsa maganizo olakwika. Nthawi zina usiku ndikamalephera kugona, ndinkalakatula mavesi a m’Baibulo amene ndinaphunzira. Kuchita zimenezi kunandithandiza kwambiri kuchotsa maganizo olakwika mumtima mwanga.” Panopa munthu ameneyu anakwatira ndipo banja lake likuyenda bwino. Iye ndi mkazi wake amadzipereka kwambiri pothandiza ena kuti azidalira Mawu a Mulungu. Munthuyu ali mnyamata sankaganiza n’komwe kuti angathe kudzakhala ndi moyo umene ali nawo panopa.

Zitsanzo zimenezi zikusonyeza kuti Mawu a Mulungu ndi amphamvu ndipo mzimu wake woyera ungathe kutithandiza kuchita zinthu zimene poyamba zinkaoneka ngati zosatheka. Koma mwina munganene kuti, “Kuti zimenezo zitheke m’pofunika chikhulupiriro.” Chikhulupiriro n’chofunikadi, ndipotu Baibulo limanena kuti: “Popanda chikhulupiriro n’zosatheka kukondweretsa Mulungu.” (Aheberi 11:6) Koma tayerekezerani kuti mnzanu wapamtima, yemwe ndi manijala wa banki inayake kapena munthu wina waudindo, wakuuzani kuti: “Musadandaule, mukafuna kanthu kalikonse, muzindiuza.” Mosakayikira mungasangalale kwambiri ndi lonjezo limeneli. Komabe n’zomvetsa chisoni kuti nthawi zambiri anthu amalephera kukwaniritsa zimene alonjeza. Mwina mnzanuyo angakumane ndi mavuto ena amene angachititse kuti zikhale zosatheka kuti akwaniritse lonjezo lakelo. Komanso ngati mnzanuyo atamwalira, ndiye kuti zabwino zonse zimene amafuna kukuchitirani zingatherenso pompo. Koma Mulungu sangakumane ndi zinthu zimene zingamulepheretse kukwaniritsa zofuna zake. Baibulo limatitsimikizira kuti: “Palibe chinthu chosatheka ndi Mulungu.”​Luka 1:37, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero.

“Kodi Ukukhulupirira Zimenezi?”

M’Baibulo muli nkhani zambiri zimene zimasonyeza kuti mawu a palemba la Luka 1:37 limene lili pamwambali ndi oona. Taganizirani zitsanzo izi:

Mayi wina wazaka 90, dzina lake Sara, anaseka pamene anauzidwa kuti adzakhala ndi mwana wamwamuna. Koma mtundu wa Isiraeli ndi umboni wakuti zimenezi zinachitikadi. Mwamuna wina anamezedwa ndi chinsomba ndipo anakhala m’mimba mwa chinsombacho masiku atatu kenako chinamulavula ndipo analemba yekha zimene zinamuchitikirazi. Munthu ameneyu ndi Yona. Luka, yemwe anali dokotala ndipo ankadziwa kusiyana pakati pa munthu amene wakomoka ndi amene wafa, analemba nkhani ya mnyamata wina dzina lake Utiko. Iye analemba kuti mnyamatayu anagwa kuchokera pawindo la chipinda chapamwamba cha nyumba yosanja ndipo anafa koma anaukitsidwa. Zimenezi si nthano chabe. Kuwerenga nkhani zimenezi bwinobwino kungakuthandizeni kutsimikizira kuti zimenezi zinachitikadi.​—Genesis 18:10-14; 21:1, 2; Yona 1:17; 2:1, 10; Machitidwe 20:9-12.

Yesu anauza Malita, yemwe ankacheza naye kwambiri, kuti: “Aliyense amene ali moyo ndi kukhulupirira mwa ine sadzafa ayi.” Kuwonjezera pa lonjezo looneka ngati losathekali, Yesu anafunsanso Malita funso lofunika ili: “Kodi ukukhulupirira zimenezi?” Masiku anonso, funso limeneli ndi lofunika kuliganizira.​—Yohane 11:26.

Kodi Mumaona Kuti N’zosatheka Kukhala ndi Moyo Wosatha Padziko Lapansi?

Pofotokoza zimene zingachitike munthu akakhala ndi moyo wautali, anthu ena analemba kuti: “Posachedwapa anthufe tizidzakhala ndi moyo wautali kuposa panopa. Mwinanso tizidzakhala ndi moyo mpaka kalekale.” Buku lina linanena kuti zikuoneka kuti timati munthu wamwalira thupi lake likasiyiratu kugwira ntchito ngakhale kuti chimene chimachititsa zimenezi sichidziwika bwinobwino. Komabe, sikuti imfa imangochitika chifukwa cha kutha ntchito kwa maselo a m’thupi. * Bukuli linati: “Sikuti chimene chimachititsa kuti anthufe tizikalamba ndi kutha kwa maselo a m’thupi basi. Koma palinso chinthu china chimene sitikuchidziwa chimene chimachititsa ukalamba.”​—The New Encyclopædia Britannica.

Aliyense amafuna atadziwa zimene zimachititsa kuti anthufe tizikalamba ndi kufa. Komabe Baibulo, osati sayansi, ndi limene limatipatsa chifukwa chomveka chokhulupirira kuti tingakhale ndi moyo wosatha. Mlengi wathu Yehova Mulungu, yemwe ndi amene analenga zamoyo zonse, akulonjeza kuti “adzameza imfa kwamuyaya.” (Salimo 36:9; Yesaya 25:8) Kodi mukukhulupirira zimenezi? Lonjezo limeneli likuchokera kwa Yehova amene sanganame.​—Tito 1:2.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 18 Kuti mudziwe zambiri pa nkhani ya ukalamba ndi kutalika kwa moyo wa munthu, werengani nkhani zoyambirira mu Galamukani! ya May 2006, yakuti “Kodi Mukhoza Kukhala ndi Moyo Wautali Bwanji?” Magazini imeneyi ndi yofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Mawu Otsindika patsamba 27]

‘Zinthu zimene kale zinkaoneka ngati zosatheka, masiku ano zikutheka.’​—RONALD REAGAN

[Mawu Otsindika patsamba 28]

Zinthu zikakhala kuti sizikuyenda bwino pa moyo wanu, kodi mumadalira ndani?

[Mawu a Chithunzi patsamba 27]

NASA photo