Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Nkhani za M’baibulo N’zogwirizana

Nkhani za M’baibulo N’zogwirizana

 Nkhani za M’baibulo N’zogwirizana

“Ulosi sunayambe wanenedwapo mwa kufuna kwa munthu, koma anthu analankhula mawu ochokera kwa Mulungu motsogoleredwa ndi mzimu woyera.”​—2 PETULO 1:21.

KODI BAIBULO NDI LOSIYANA BWANJI NDI MABUKU ENA? Nkhani zambiri zofotokoza zinthu zimene zinachitika kale zimatsutsana ngakhale zitakhala kuti zinalembedwa nthawi yofanana. Komanso nthawi zambiri mabuku oti analembedwa ndi anthu osiyana, pamalo osiyana komanso zaka zosiyana sakhala ogwirizana. Komabe, chifukwa choti mabuku onse 66 a m’Baibulo anauziridwa ndi Mulungu, nkhani zake ndi zogwirizana.​—2 Timoteyo 3:16.

CHITSANZO: Mose, yemwe anali m’busa wa nkhosa cha m’ma 1500 B.C.E., analemba zokhudza “mbewu” imene idzapulumutse anthu. Iye analemba zimenezi m’buku loyambirira la m’Baibulo. Kenako iye analembanso m’buku lomweli kuti mbewuyo idzakhala mbadwa ya Abulahamu, Isaki ndi Yakobo. (Genesis 3:15; 22:17, 18; 26:24; 28:14) Patadutsa zaka 500, mneneri Natani ananena kuti mbewuyo idzachokera mu mzera wachifumu wa Davide. (2 Samueli 7:12) Patatha zaka 1,000 mtumwi Paulo ananena kuti Yesu limodzi ndi otsatira ake osankhidwa, ndi amene amapanga mbewu imeneyi. (Aroma 1:1-4; Agalatiya 3:16, 29) Ndiyeno chakumapeto kwa nthawi ya atumwi, buku lomaliza la m’Baibulo linalosera kuti ena mwa anthu amene ali mbali ya mbewu ija azidzachitira umboni za Yesu ndipo kenako adzaukitsidwa kupita kumwamba kumene adzalamulire ndi Yesu zaka 1,000. Mbewu imeneyi idzawononga Mdyerekezi ndi kupulumutsa anthu.​—Chivumbulutso 12:17; 20:6-10.

ZIMENE AKATSWIRI A BAIBULO ANENA: Louis Gaussen atafufuza bwinobwino mabuku onse 66 a m’Baibulo, analemba zosonyeza kuti anachita chidwi kwambiri ndi “kugwirizana kwa nkhani za m’Baibulo, buku limene linalembedwa ndi anthu osiyanasiyana pa zaka 1,500.” Anachitanso chidwi poona kuti anthu amene analemba Baibulo “anali ndi cholinga chimodzi ndipo anayesetsa kuti chikwaniritsidwe ngakhale kuti sankadziwa zonse zokhudza cholingachi. Cholinga chimenechi ndi chokhudza kuwomboledwa kwa mtundu wonse wa anthu kudzera mwa Mwana wa Mulungu.”​—Theopneusty​—The Plenary Inspiration of the Holy Scriptures.

KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI? Kodi mungayembekezere kuti buku limene linalembedwa ndi anthu osiyanasiyana okwana 40 kwa zaka 1,500 lingakhale ndi nkhani zogwirizana? Komatu nkhani za m’Baibulo ndi zogwirizana ngakhale kuti linalembedwa ndi anthu 40 pa zaka 1,500. Kodi zimenezi sizikusonyeza kuti Baibulo ndi buku lapadera?

[Mawu Otsindika patsamba 7]

“Mabuku onse a m’Baibulo ukawaphatikiza amapanga buku limodzi. . . Padziko lonse lapansi palibenso buku lofanana ndi limeneli.”​—THE PROBLEM OF THE OLD TESTAMENT, LOLEMBEDWA NDI JAMES ORR