Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Anthu Ogwirizana Ngakhale Kuti Ali M’mayiko Osiyana

Anthu Ogwirizana Ngakhale Kuti Ali M’mayiko Osiyana

Anthu Ogwirizana Ngakhale Kuti Ali M’mayiko Osiyana

A Mboni za Yehova amayesetsa kuti chilichonse chisawalepheretse kukhala ogwirizana ndiponso okondana. Iwo amatsatira mfundo ya m’mawu amene Yesu anauza ophunzira ake, akuti: “Nonsenu ndinu abale.” (Mateyu 23:8) Zimene a Mboni amachita kumalo awo awiri olambirira, ku Portugal komanso ku Spain, zikusonyeza kuti zimenezi ndi zoona.

MZINDA wa Valença do Minho, womwe uli kumpoto kwa dziko la Portugal, unamangidwa m’nthawi ya nkhondo. Mzindawu uli ndi mpanda wokhala ndi nsanja ndipo munthu akaima pansanjapo amatha kuona mtsinje wa Minho, womwe ndi malire a dziko la Spain ndi la Portugal. Kutsidya lina la mtsinjewu kuli mzinda wa Tui, womwe uli m’dziko la Spain, ndipo mumzinda umenewu muli tchalitchi chachikulu chimene chimaoneka kuti ndi chotetezeka kwambiri. Nyumba zambiri komanso mipanda yotetezera mzinda wa Tui komanso wa Valença zinamangidwa zaka za m’ma 1600 pa nthawi imene dziko la Spain linkamenyana ndi dziko la Portugal. Mayiko awiriwa ali m’bungwe la Mgwirizano wa Mayiko a ku Ulaya.

Mu 1995, zinthu zimene anamanga pamalire a mayiko awiriwa komanso malamulo oona za katundu wolowa ndi kutuluka m’mayikowa zinachotsedwa. Koma kuchita zimenezi pakokha sikungathandize kuti anthu ayambe kugwirizana. Kuti anthu ayambe kugwirizana amafunikira kusintha maganizo olakwika amene ali nawo okhudza anthu enawo. Mumzinda wa Valença muli Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova yaing’ono koma yokongola ndipo m’Nyumba ya Ufumuyi mumasonkhana a Mboni ochokera ku Spain komanso ochokera ku Portugal. Zimene anthu amenewa amachita zimasonyeza kuti anthu amitundu yosiyana akhoza kukhala limodzi mogwirizana.

Anthu amenewa anayamba kugwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumu imodzi m’chaka cha 2001 chifukwa pa nthawi imeneyi a Mboni a mumzinda wa Tui ankafunika malo ena olambirira. Iwo anafunika kuchoka pamalo amene ankachita lendi ndipo analibe ndalama zoti n’kumangira Nyumba ya Ufumu yawoyawo. Popeza mpingowo unali waung’ono, iwo sakanakwanitsa kumapeza ndalama zolipirira lendi. Choncho a Mboni amenewa anapempha a Mboni a ku Valença ku Portugal ngati angawalole kuti azigwiritsa nawo ntchito Nyumba ya Ufumu yawo, chifukwa ili pafupi ndi mzinda wa Tui.

Munthu wina yemwe ali mumpingo wa ku Tui ku Spain, dzina lake Eduardo Vila, anati: “Tinakambirana nkhaniyi mu December 2001. Titamaliza zokambiranazo, ndinaona kuti Yehova anathandiza abale a ku Portugal kuti atikomere mtima. Iwo anali atagwira ntchito modzipereka kuti amange Nyumba ya Ufumu yokongolayi ndipo zinali zolimbikitsa kwambiri kuona kuti alola kuti tizigwiritsa nawo ntchito nyumba yawoyi.”

Wa Mboni wina wa ku Portugal yemwe anali nawo pa zokambiranazo, dzina lake Américo Almeida, ananena kuti: “Tinalandira ndi manja awiri abale athu a ku Spain kuti azigwiritsa nawo ntchito Nyumba ya Ufumuyi. Tonse tinavomereza zimenezi ndipo tinali ndi chikhulupiriro choti Yehova adalitsa zimene tasankhazo.” A Mboni a m’mayiko awiri onsewa amachita zinthu mogwirizana. Paolo, yemwe amakhala ku Valença, anati: “Ngakhale kuti kwa ena zimenezi zingaoneke zachilendo, ifeyo sitimaganiza za komwe wina wachokera. Timangoona kuti tonse ndife abale auzimu.”

Alendo akalowa m’Nyumba ya Ufumuyi, chinthu choyamba chimene amachita nacho chidwi ndi mawotchi awiri ofanana omwe ali pakhoma lakumbuyo kwa nyumbayi. Mawotchi amenewa amasonyeza nthawi zosiyana chifukwa nthawi ya ku Spain imatsogola ndi ola limodzi kusiyana ndi ya ku Portugal. Anthu amene amasonkhana m’Nyumba ya Ufumu imeneyi amangosiyana pa nkhani ya nthawi yokhayi basi. Pamene nyumbayi inkafunika kukonzedwanso, Komiti Yomanga Yachigawo ya ku Spain inkayang’anira ntchito imene anthu odzipereka ochokera m’mipingo iwiri yonseyi ankagwira. Paolo anati: “Abale ndi alongo ambiri a ku Spain, omwe ndi akatswiri pa ntchitoyi, anabwera kudzatithandiza. Ena anachokera kutali kwambiri moti anayenda mtunda woposa makilomita 160. Ntchito imeneyi inachititsa kuti anthu a m’mipingo iwiriyi azikondana kwambiri.”

Tsopano tiyeni tikambirane chitsanzo chachiwiri cha anthu amene amakondana ngakhale kuti ndi ochokera m’mayiko osiyana.

Anthu Ogwirizana Ngakhale kuti Ali M’chigwa Chogawanika

Mzinda wa Puigcerdá uli m’dziko la Spain koma uli m’malire a dzikolo ndi la France. Mzindawu uli pakatikati pa chigwa chachonde ndipo wazunguliridwa ndi mapiri aatali otchedwa Pyrenees. Poyamba chigwa chonsechi, chomwe chimatchedwa Cerdaña, chinali m’dziko la Spain. Koma pa zokambirana zofuna kuthetsa kusamvana kumene kunalipo pakati pa mayikowa, zomwe zinachitika mu 1659 (Treaty of the Pyrenees), dziko la Spain linalola kupereka hafu ya chigwachi ku dziko la France.

Masiku ano anthu a ku France amapita kukagula zinthu zosiyanasiyana ku Puigcerdá, womwe ndi mzinda waukulu pachigwachi. Ndipo kuyambira mu 1997, a Mboni za Yehova a ku Puigcerdá analolanso kuti abale awo a ku France azigwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumu yawo. Pa nthawi imeneyi a Mboni a ku France anafunika kuchoka m’nyumba imene ankachita lendi. Nyumba ya Ufumu ya m’dziko la France imene anali nayo pafupi inali kutali mtunda woyenda ola limodzi pa galimoto ndipo njira zake, zomwe zimadutsa m’mapiri, n’zosatheka kudutsa m’miyezi yozizira chifukwa cha madzi oundana.

A Mboni a ku France atafotokoza zoti akufuna malo oti azisonkhana, nthawi yomweyo a Mboni a ku Spain anawauza kuti akhoza kumagwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumu yawo. Munthu wina dzina lake Prem, yemwe amasonkhana m’Nyumba ya Ufumu yomweyi, anati: “Abale onse a ku Spain anagwirizana ndi mfundo yoti nyumbayi izigwiritsidwanso ntchito ndi abale a ku France. Abalewa anasonyeza mtima wofuna kugawana zinthu umenewu chifukwa cha zimene tinaphunzira m’Baibulo. Patadutsa milungu ingapo, abale a ku France anayambadi kusonkhana m’Nyumba ya Ufumu yathu ndipo takhala tikusonkhana limodzi kwa zaka 13 tsopano.”

Eric, yemwe ndi woyang’anira mumpingo wa ku France, anati: “Tikuona kuti kusonkhana mu Nyumba ya Ufumu ya ku Puigcerdá kuli bwino kwambiri. Ndimakumbukirabe mmene abale a ku Spain anatilandirira ndi manja awiri. Iwo anakongoletsa nyumbayo ndi chimpukutu chachikulu cha maluwa ndipo analembamo mawu akuti, ‘Takulandirani ndi manja awiri, abale ndi alongo athu okondedwa.’”

Eric anawonjezera kuti: “Titasiya kugwiritsa ntchito nyumba imene tinkachita lendi ku France, anthu ankaganiza kuti basi mpingowo wathera pomwepo. Koma ataona kuti tikupitirizabe kulalikira komanso kugawira anthu timapepala towaitanira ku misonkhano yathu ku Spain, anadziwa kuti mpingowo udakalipobe. Anthu achidwi amasangalala kubwera ku Nyumba ya Ufumu ya ku Spain. Kuwonjezera pamenepo, kusonkhana nyumba imodzi ndi abale athu a ku Spain kwachititsa kuti tizigwirizana kwambiri ndi abalewa. Poyamba tinkadziwa zoti m’dziko linalo muli mpingo wina wa Mboni koma sitinkadziwana kwambiri ndi abale athu a kumeneko. Koma panopa, popeza timaonana nawo pafupipafupi, sitimaonanso ngati tilipo tokha m’chigwachi, chomwe chili kutali ndi kumene anthu ena amakhala.”

Kodi anthuwa amakhala momangika chifukwa chosiyana mitundu? Mayi wina wa ku France yemwe ali ndi zaka za m’ma 80, anati: “Poyamba ndinali ndi nkhawa nditamva zoti tsopano tizikasonkhana ku Spain. Koma nditaona mmene abale athu a ku Puigcerdá anatilandirira komanso nditaona kuti ndi anthu ochezeka, kusamukaku sindinakuonenso ngati vuto. M’malomwake, kusamukaku kwatithandiza kutsimikizira kuti anthu a Yehova ndi ogwirizanadi padziko lonse lapansi.”

Chimene Chachititsa Kuti Anthuwa Akhale Ogwirizana

Anthu amene anayambitsa bungwe la mgwirizano wa mayiko a ku Ulaya ananena kuti mayiko amene ali m’bungweli “ankafunitsitsa kukhazikitsa njira imene ingathandize kuti anthu onse a ku Ulaya akhale ogwirizana.” Zimene anachita m’zaka za m’ma 1980 ndi 1990 pogumula zinthu zimene anamanga m’malire a mayikowa, inali njira imodzi yothandizira kuti mgwirizanowu utheke. Koma kuti anthu ayambedi kugwirizana, anafunikanso kuchotsa chidani m’mitima yawo.

A Mboni za Yehova amayesetsa kuti asamasankhane mitundu komanso kuti asamakayikirane. Iwo amadziwa kuti kukhala limodzi ndi anthu azikhalidwe zosiyanasiyana kuli ndi ubwino wake. Amadziwanso kuti “Mulungu alibe tsankho.” (Machitidwe 10:34) Akakhala pa misonkhano yawo ya mayiko komanso pa Nyumba za Ufumu, iwo amazindikira kuti “ndi zabwino komanso zosangalatsa kwambiri abale akakhala pamodzi mogwirizana!” (Salimo 133:1) Umboni wa zimenezi ndi mgwirizano umene a Mboni a ku Valença ndi ku Puigcerdá ali nawo ndi abale awo a m’mayiko ena.

[Mawu Otsindika patsamba 13]

“Ngakhale kuti kwa ena zimenezi zingaoneke zachilendo, ifeyo sitimaganiza za komwe wina wachokera. Timangoona kuti tonse ndife abale auzimu”

[Mawu Otsindika patsamba 14]

“Ntchito imeneyi inachititsa kuti anthu a m’mipingo iwiriyi azikondana kwambiri”

[Mawu Otsindika patsamba 15]

“Ndi zabwino komanso zosangalatsa kwambiri abale akakhala pamodzi mogwirizana!” SALIMO 133:1

[Chithunzi pamasamba 12, 13]

Mmene mzinda wa Tui komanso mtsinje wa Minho umaonekera munthu akakhala mumzinda wa Valença do Minho

[Chithunzi patsamba 14]

Ntchito yokonzanso Nyumba ya Ufumu

[Chithunzi patsamba 15]

Mapiri a Pyrenees komanso chigwa cha Cerdaña

[Chithunzi patsamba 15]

Mkulu wa mpingo wa ku France komanso wa ku Spain amene amasonkhana mu Nyumba ya Ufumu ya ku Puigcerdá