Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mfumu Ahasiwero ya ku Perisiya yotchulidwa m’Baibulo m’buku la Esitere anali ndani?

Buku la m’Baibulo la Esitere limanena kuti Ahasiwero anasankha mtsikana wachiyuda dzina lake Esitere kuti akhale mkazi wake ndipo Esitere anapulumutsa anthu a mtundu wake pamene ankafuna kuphedwa. Kwa nthawi yaitali anthu akhala akusiyana maganizo pa nkhani yakuti, kodi Ahasiwero ameneyu anali ndani? Komabe, zoona zinadziwika anthu atatulukira mawu olembedwa m’zinenero zitatu amene amapezeka pazipilala za ku Perisiya. Zimene anapezazo zikusonyezeratu kuti Ahasiwero anali Sasita Woyamba, mwana wa Dariyo Wamkulu (Hystaspis). Mmene dzina la Sasita analilembera pazipilalazi, akalimasulira m’Chiheberi, limafanana ndi mmene linalembedwera m’Chiheberi m’buku la Esitere.

Zonse zimene zili m’buku la Esitere zokhudza Ahasiwero zikugwirizana ndi Sasita Woyamba. Mfumu ya ku Perisiya imeneyi inali ndi likulu lake ku Susa (Susani), ku Elamu, ndipo inkalamuliranso ku Mediya. Ulamuliro wake unkayambira ku India mpaka ku zilumba za m’nyanja ya Mediterranean. (Esitere 1:2, 3; 8:9; 10:1) Katswiri wina wamaphunziro, dzina lake Lewis Bayles Paton, ananena kuti: “Pa mafumu onse a ku Perisiya, mbiri imeneyi imagwirizana ndi Sasita basi. Khalidwe la Ahasiwero lofotokozedwa m’Buku la Esitere, limagwirizananso kwambiri ndi zimene Herodotus komanso akatswiri ena a mbiri yakale a ku Girisi analemba zokhudza Sasita.”

Kodi pali umboni wosonyeza kuti anthu ankaumba njerwa ku Iguputo wakale?

Buku la m’Baibulo la Ekisodo limanena kuti Aiguputo ankagwiritsa akapolo awo achiheberi ntchito youmba njerwa. Akapolowo ankapatsidwa nambala ya njerwa zoti aumbe tsiku lililonse ndipo ankagwiritsa ntchito matope ndi udzu.​—Ekisodo 1:14; 5:10-14.

Kale, anthu ambiri okhala m’mbali mwa mtsinje wa Nailo ankakonda kugwira ntchito youmba njerwa. Zipilala zomangidwa ndi njerwa za m’nthawi ya Iguputo wakale zidakalipo mpaka pano. Chithunzi cha m’ma 1400 B.C.E. chomwe chinajambulidwa pamanda a Rekhmire, omwe ali mumzinda wakale wa Thebes, chimasonyeza mmene ntchito youmba njerwa inkachitikira. Chithunzi chimenechi chinajambulidwa pa nthawi imene zinthu zolembedwa m’buku la Ekisodo zinkachitika.

Buku lina limafotokoza zochitika zimene zili pachithunzichi motere: “Ankatunga madzi pachitsime, ankasakaniza matope ndi khasu ndipo kenako ankawatenga kupita nawo pamalo abwino oumbira njerwa. Matopewo ankawatsendera m’chikombole chathabwa chimene ankachiika pansi. Kenako ankachotsa chikombolecho n’kusiya njerwayo kuti iume ndi dzuwa. Ankaumba njerwa zambirimbiri ndipo zikauma ankazisanja podikira kuti adzazigwiritse ntchito. Mpaka pano anthu a m’madera onse ozungulira nyanja ya Mediterranean amaumbabe njerwa mwa njira imeneyi.”​—The International Standard Bible Encyclopedia.

Mapepala a gumbwa osiyanasiyana a m’zaka za m’ma 1900 B.C.E. amanenanso za akapolo amene ankaumba njerwa. Amafotokoza kuti akapolowo ankagwiritsa ntchito matope ndi udzu komanso ankapatsidwa nambala ya njerwa zoti aumbe pa tsiku.

[Chithunzi patsamba 22]

Chithunzi cha pamwala cha Sasita (waimirirayo) ndi Dariyo Wamkulu (wakhalayo)

[Mawu a Chithunzi]

Werner Forman/​Art Resource, NY

[Chithunzi patsamba 22]

Mbali imodzi ya chithunzi chimene chili m’manda a Rekhmire

[Mawu a Chithunzi]

Erich Lessing/​Art Resource, NY