Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 Zoti Achinyamata Achite

Pewani Chilichonse Chokhudza Mizimu Yoipa

Pewani Chilichonse Chokhudza Mizimu Yoipa

Malangizo: Chitani zotsatirazi muli pamalo opanda phokoso. Pamene mukuwerenga mavesiwo, yerekezerani kuti nkhanizo zikuchitika inuyo muli pomwepo. Yesani kuona m’maganizo mwanu zimene zikuchitika. Mukhale ngati mukumva zimene anthuwo akulankhula. Yesani kumva mmene anthu a mu nkhanizi akumvera mumtima mwawo.

1 ONANI NKHANIZI BWINOBWINO.​—WERENGANI GENESIS 6:1-6 NDI MACHITIDWE 19:11-20.

Kodi mukuganiza kuti Anefili ankaoneka bwanji? Fotokozani.

․․․․․

Kodi mukuganiza kuti amuna amenewa anamva bwanji pambuyo polimbana ndi mzimu woipa, mogwirizana ndi lemba la Machitidwe 19:13-16?

․․․․․

2 FUFUZANI MOZAMA.

Gwiritsani ntchito zinthu zofufuzira zimene muli nazo kuti mudziwe zambiri zokhudza Anefili. Kodi mukuganiza kuti n’chifukwa chiyani ankakonda chiwawa?

․․․․․

Kodi n’chifukwa chiyani tinganene kuti mizimu yoipa ‘inasiya malo awo okhala’? (Werengani Yuda 6.) Kodi mukuganiza kuti n’chifukwa chiyani sizinali zachibadwa komanso zinali zolakwika kuti mizimu yoipa ikwatire akazi a padziko lapansi?

․․․․․

Kodi nkhani ziwiri zomwe mwawerengazi zikukuuzani chiyani pa nkhani ya mmene mizimu yoipa imakondera zachiwerewere komanso zachiwawa?

․․․․․

  3 GWIRITSANI NTCHITO ZIMENE MWAPHUNZIRA. LEMBANI ZIMENE MWAPHUNZIRA ZOKHUDZA . . .

Kuopsa komanso kudzikonda kwa mizimu yoipa.

․․․․․

MMENE MUNGAGWIRITSIRE NTCHITO MFUNDOZI.

Popeza mizimu yoipa singathenso kuvala matupi a anthu, kodi ndi njira ziti zosadziwika zimene ingagwiritse ntchito kuti ikusocheretseni?

․․․․․

Masiku ano, kodi ndi zosangalatsa ziti zimene zimasonyeza makhalidwe amene mizimu yoipa imakonda?

․․․․․

Kodi mungasonyeze bwanji kuti ndinu wotsimikiza mtima kupewa chilichonse chokhudza mizimu yoipa? (Werenganinso Machitidwe 19:18, 19.)

․․․․․

4 M’NKHANIZI, KODI NDI MFUNDO ZITI ZIMENE ZAKUKHUDZANI MTIMA KWAMBIRI, NDIPO N’CHIFUKWA CHIYANI?

․․․․․

Ngati Mulibe Baibulo, uzani a Mboni za Yehova, kapena kawerengeni Baibulo pa adiresi ya pa intaneti iyi: www.jw.org/ny.