Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Abulahamu Anali Munthu Wolimba Mtima

Abulahamu Anali Munthu Wolimba Mtima

 Abulahamu Anali Munthu Wolimba Mtima

Abulahamu ndi banja lake komanso antchito ake anali akukonzekera ulendo wopita kudziko la Kanani. (Genesis 12:1-5) Abulahamu ankati akaona anthuwo ankadziwa kuti ali ndi udindo waukulu chifukwa gulu lonselo linkadalira iyeyo pa zosowa zawo za tsiku ndi tsiku. Koma kodi Abulahamu akasamukira kudziko lachilendolo, akakwanitsa bwanji kusamalira anthuwa? N’kutheka kuti ali ku Uri sankavutika kusamalira anthuwa chifukwa dzikoli linali lotukuka, linali ndi malo ambiri odyetsera ziweto, linali lachonde komanso linali losasowa madzi. Nanga kodi Abulahamu akakadwala kapena kumwalira kudziko lachilendolo, ndani akasamalire banja lake? N’kutheka kuti Abulahamu ankadera nkhawa zinthu zimenezi, komabe sizinamulepheretse kusamuka. Iye anatsimikiza kumvera lamulo la Mulungu zivute zitani ndipo zimenezi zikusonyeza kuti anali wolimba mtima.

 KODI KULIMBA MTIMA N’KUTANI? Kulimba mtima kumatanthauza kuchita zinthu mopanda mantha. Komabe sikuti munthu wolimba mtima samaopa chilichonse. M’malomwake, munthu amene Mulungu amamuthandiza kukhala wolimba mtima, amachitabe zinthu ngakhale atakhala ndi mantha.

KODI ABULAHAMU ANASONYEZA BWANJI KULIMBA MTIMA? Abulahamu anali wokonzeka kuchita zinthu zosiyana ndi zimene anthu ena onse ankachita. Abulahamu anakulira m’dera limene anthu ake ankalambira milungu yambiri komanso mafano. Komabe, sanalephere kuchita zinthu zimene ankadziwa kuti n’zolondola chifukwa choopa mmene anthu ena azimuonera. M’malomwake, molimba mtima anasankha kulambira Mulungu mmodzi yekha, Yehova, yemwe ndi “Mulungu Wam’mwambamwamba.”​—Genesis 14:21, 22.

Abulahamu ankaona kuti kulambira Mulungu woona kunali kofunika kwambiri kuposa zinthu zakuthupi. Iye anali wokonzeka kusiya moyo wabwino kudziko la Uri n’kupita kuchipululu ndipo anali ndi chidaliro choti Yehova adzamusamalira. N’kutheka kuti patadutsa zaka zingapo, Abulahamu anayamba kukumbukira moyo wabwino umene anali nawo ali ku Uri. Komabe ankakhulupirira ndi mtima wonse kuti Yehova adzapitirizabe kumusamalira limodzi ndi banja lake. Iye analimba mtima kumvera malamulo a Mulungu chifukwa chakuti ankaona kuti Yehova ndi Munthu wofunika kwambiri pa moyo wake.

ZIMENE TIKUPHUNZIRAPO: Tingatsanzire Abulahamu mwa kuyesetsa kukhala olimba mtima kumvera Yehova ngakhale zitakhala kuti anthu ena amene timakhala nawo samvera Mulungu. Mwachitsanzo, Baibulo limatiphunzitsa kuti nthawi zina anthu amene amatumikira Yehova Mulungu mokhulupirika angatsutsidwe ndi anthu ena, kuphatikizapo anzawo kapena abale awo. (Yohane 15:20) Komabe, tikamakhulupirira kwambiri zimene taphunzira ponena za Yehova, timakhala okonzeka kuteteza chikhulupiriro chathu ndipo timachita zimenezi mwaulemu.​—1 Petulo 3:15.

Tiyeneranso kukhulupirira lonjezo la Mulungu loti anthu amene amamukhulupirira, adzawapatsa zosowa za pa moyo wawo. Tikakhala ndi chikhulupiriro chimenecho, tidzalimba mtima kuika zinthu zauzimu pamalo oyamba pa moyo wathu m’malo modalira zinthu zakuthupi. (Mateyu 6:33) Tiyeni tione mmene banja lina linachitira zimenezi.

Doug ndi mkazi wake Becky ankafuna kusamukira kudziko lina komwe kunkafunika anthu okathandiza kulalikira uthenga wabwino wa m’Baibulo, ngakhale kuti iwo anali ndi ana awiri aang’onoang’ono. Atafufuza mokwanira komanso kupemphera mochokera pansi pa mtima, iwo anaganiza zosamukabe. Doug anati: “Tinafunika kulimba mtima kuti tithe kusamuka ndi ana n’kupita kudziko lina chifukwa sitinkadziwa kuti zinthu kumeneko zikatiyendera bwanji. Koma masiku oyambirira pamene tinkakambirana za ulendowu, tinali titakambirana kale za chitsanzo cha Abulahamu ndi Sara. Kuganizira mmene anasonyezera kudalira Yehova komanso kuona kuti Yehova sanawagwiritse mwala, kunatithandiza kwambiri.”

Ponena za mmene moyo wawo ulili m’dziko limene anasamukiralo, Doug anati: “Kuchita zimenezi kwatibweretsera madalitso osaneneka. Chifukwa choti tikukhala moyo wosalira zambiri, timakhala ndi nthawi yambiri yocheza monga banja, yolalikira limodzi komanso yosewera ndi ana athu. Panopo tili pa mtendere weniweni moti n’zovuta kulongosola mmene tikusangalalira.”

N’zoona kuti si aliyense amene angathe kuchita zimene banjali linachita. Komabe, tonse tingathe kutsatira chitsanzo cha Abulahamu mwa kuonetsetsa kuti kulambira Mulungu kuzikhala chinthu chofunika kwambiri pa moyo wathu. Pochita zimenezi tizikhulupirira kuti Mulungu adzatisamalira. Tikamachita zimenezi ndiye kuti tikutsatira malangizo a m’Baibulo akuti “tikhale olimba mtima ndithu ndipo tinene kuti: ‘Yehova ndiye mthandizi wanga. Sindidzaopa.’”​—Aheberi 13:5, 6.

[Mawu Otsindika patsamba 7]

Munthu amene Mulungu amamuthandiza kukhala wolimba mtima, amachitabe zinthu ngakhale atakhala ndi mantha

 [Bokosi/​Chithunzi patsamba 8]

Sara Anali Mayi Woopa Mulungu Komanso Mkazi Wabwino

Sara anakwatiwa ndi mwamuna wachikhulupiriro cholimba kwambiri. Komabe nayenso payekha anasonyeza chitsanzo chabwino chimene tiyenera kutengera. Ndipotu Baibulo limatchula katatu konse kuti Sara ndi chitsanzo chabwino kwa akazi onse oopa Mulungu. (Yesaya 51:1, 2; Aheberi 11:11; 1 Petulo 3:3-6) Ngakhale kuti Malemba sanena zambiri zokhudza mayi ameneyu, tingathe kuphunzira zambiri pa makhalidwe ake abwino.

Mwachitsanzo, taganizirani zimene Sara anachita Abulahamu atamuuza kuti Mulungu wawauza kuti asamuke ku Uri. Kodi anayamba kuda nkhawa kuti akupita kuti komanso n’chifukwa chiyani akuyenera kusamuka? Kodi ananyinyirika chifukwa choganiza kuti azikapeza bwanji zosowa zawo za tsiku ndi tsiku? Kodi anadandaula poganizira kuti asiyana ndi anzake komanso abale ake ndipo mwina sadzaonana nawonso? N’kutheka kuti Sara anaganizirapo za zinthu zimenezi komabe anamvera ndipo ananyamuka pokhulupirira kuti Yehova adzamudalitsa chifukwa cha kumvera kwakeko.​—Machitidwe 7:2, 3.

Kuwonjezera pa kumvera Mulungu, Sara analinso mkazi wabwino kwambiri. Iye sankapikisana ndi mwamuna wake pa nkhani zokhudza banja lawo. M’malomwake, iye ankalemekeza kwambiri mwamuna wake ndipo ankamuthandiza mwachikondi mwamunayo akamatsogolera banja lawo. Makhalidwe abwino amenewa, anawonjezera kukongola kwake.​—1 Petulo 3:1-6.

Kodi makhalidwe amenewa angathandizenso akazi okwatiwa masiku ano? Mkazi wina dzina lake Jill, yemwe wakhala m’banja mosangalala kwa zaka zoposa 30, ananena kuti: “Chitsanzo cha Sara chinandiphunzitsa kuti ndiyenera kumasuka kunena maganizo anga kwa mwamuna wanga. Komabe ndimakumbukira kuti monga mutu wabanja, mwamuna wanga ndi amene ayenera kusankha zoyenera kuchita. Akatero, ineyo ndimayesetsa kumuthandiza kuti zimene wasankhazo zitheke.”

Chinthu china chofunika kwambiri chimene tingaphunzire kwa Sara n’choti: Iye sanali wonyada ngakhale kuti anali wokongola kwambiri. (Genesis 12:10-13) Sara ankathandiza Abulahamu pa mavuto ndi pa mtendere pomwe ndipo ankachita zimenezi modzichepetsa. N’zoonekeratu kuti banja la Abulahamu ndi Sara linali lokhulupirika kwa Mulungu, lodzichepetsa ndiponso lokondana. Zimenezi zinachititsa kuti onse adalitsidwe.