Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Abulahamu Anali Munthu Wodzichepetsa

Abulahamu Anali Munthu Wodzichepetsa

 Abulahamu Anali Munthu Wodzichepetsa

Tsiku lina kunja kukutentha kwambiri, Abulahamu anakhala pakhomo la hema wake. Atakweza maso, anaona amuna atatu amene anabwera kudzacheza m’deralo ataima chapatali. * Nthawi yomweyo, iye anathamanga kukakumana nawo ndipo anawapempha kuti akapume pang’ono kunyumba kwake. Iye anawauza alendowo kuti akufuna kuwakonzera “kachakudya” koma kenako anawakonzera chakudya chapamwamba kwambiri. Anakonza makeke, mkaka, mafuta a mkaka ndiponso nyama yofewa bwino. Pamenepatu Abulahamu anasonyeza kuti anali wochereza alendo komanso, monga tionere, anasonyeza kuti anali wodzichepetsa kwambiri.​—Genesis 18:1-8.

KODI KUDZICHEPETSA N’KUTANI? Kudzichepetsa kumatanthauza kusakhala wonyada kapena wodzikuza. Munthu wodzichepetsa amazindikira kuti anthu ena amam’posa pa zinthu zina. (Afilipi 2:3) Iye amamva maganizo a anthu ena komanso amatha kugwira ntchito zooneka ngati zotsika potumikira anthu ena.

KODI ABULAHAMU ANASONYEZA BWANJI KUDZICHEPETSA? Abulahamu ankasangalala kutumikira anthu ena. Monga tafotokozera kale, Abulahamu ataona alendo atatu aja, nthawi yomweyo anaganiza zowachereza. Nayenso Sara, mkazi wake, anayamba kukonza chakudya mwamsangamsanga. Koma kodi ndani anagwira ntchito yambiri? Nkhaniyi imati: Abulahamu anathamanga kukakumana ndi alendowo n’kuwapempha kuti awakonzere chakudya. Iye anathamanganso kupita kumene kunali ziweto n’kusankha ng’ombe yabwino yoti aphe. Kenako Abulahamu anabweretsa zakudya zonsezo kumene kunali alendowo. M’malo mongotuma antchito ake kuti achite zonse, munthu wodzichepetsa ameneyu anagwira nawo ntchitoyo. Iye sanaganize kuti ntchito zimenezi ndi zonyozeka moti iye sangagwire nawo.

Abulahamu ankatha kutsatira maganizo a anthu  omwe ankawayang’anira. Mwachitsanzo, m’Baibulo muli nkhani zochepa zomwe zimanena za Abulahamu akulankhulana ndi Sara. Komabe pa nkhani zochepa zomwezo timamva kuti kawiri konse Abulahamu anamvera maganizo a Sara ndipo anachitapo kanthu. (Genesis 16:2; 21:8-14) Nthawi ina Sara anapereka maganizo amene poyamba ‘Abulahamu anaipidwa nawo kwambiri.’ Koma Yehova atam’fotokozera kuti maganizo a Sarawo anali abwino, iye anamvera ndipo modzichepetsa anatsatira zimene Sara ananena.

ZIMENE TIKUPHUNZIRAPO: Ngati ndife odzichepetsadi, tidzakhala ofunitsitsa kutumikira ena. Tidzayesetsa kuchita zilizonse zimene tingathe kuti tithandize ena kukhala ndi moyo wabwino.

Tingasonyezenso kudzichepetsa tikamamvera maganizo a anthu ena. Si bwino kukana kutsatira maganizo a anthu ena kokha chifukwa chakuti ifeyo sitinaganize mwa njira imeneyo. (Miyambo 15:22) Makamaka anthu amene ali ndi udindo ndi amene ayenera kukhala okonzeka kumvera maganizo a anthu ena. Munthu wina, dzina lake John, yemwe wakhala ndi udindo kwa nthawi yaitali ananena kuti: “Ndaona kuti munthu amene amayang’anira anthu ayenera kuonetsetsa kuti khalidwe lake lisamalepheretse anthu kufotokoza maganizo awo momasuka.” Iye ananenanso kuti: “Munthu amafunika kukhala wodzichepetsa kuti azitha kuzindikira kuti anthu ena omwe amawayang’anira, amadziwa njira yabwino yochitira zinthu zina kuposa iyeyo. Ndipotu maganizo abwino akhoza kuchokera kwa munthu aliyense, ngakhale yemwe si woyang’anira.”

Tikamatsanzira Abulahamu pomvera maganizo a anthu ena komanso kugwira ntchito zooneka ngati zotsika pofuna kutumikira ena, Yehova adzatikonda. Ndipotu, “Mulungu amatsutsa odzikweza, koma odzichepetsa amawasonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu.”​—1 Petulo 5:5.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 N’kutheka kuti poyamba Abulahamu sanazindikire alendowo, koma iwo anali angelo otumidwa ndi Mulungu.​—Aheberi 13:2.