Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Dziko Loyenda Mkaka ndi Uchi”

“Dziko Loyenda Mkaka ndi Uchi”

“Dziko Loyenda Mkaka ndi Uchi”

YEHOVA MULUNGU atapulumutsa Aisiraeli ku Igupto, anawalonjeza kuti awalowetsa “m’dziko labwino komanso lalikulu, dziko loyenda mkaka ndi uchi.”​—Ekisodo 3:8.

Aisiraeli atalowa m’Dziko Lolonjezedwa anayamba kuweta ng’ombe, nkhosa ndiponso mbuzi. Zimenezi zinachititsa kuti asamasowe mkaka. Nanga bwanji uchi umene watchulidwa palembali? Ena amakhulupirira kuti uchi umenewu unali madzi otsekemera opangidwa kuchokera ku zipatso monga kanjedza, nkhuyu kapena mphesa. Koma nthawi zambiri pamene Baibulo latchula uchi wa njuchi, limanena za njuchi za kutchire, osati uchi opangidwa kuchokera ku zipatso. (Oweruza 14:8, 9; 1 Samueli 14:27; Mateyu 3:1, 4) Ndiyeno kodi Dziko Lolonjezedwa linalidi “loyenda” mkaka ndi uchi?

Zimene akatswiri ofukula zinthu zakale apeza posachedwapa ku Israel zingatithandize kuyankha funso limeneli. Ponena za zimene anapezazo, chikalata chimene yunivesite ina ku Israel inatulutsa chinanena kuti: “Pulofesa (Amihai) Mazar ananena kuti, ming’oma ya njuchi imeneyi ndi yakale kwambiri ndipo aka n’koyamba kupeza zimenezi pa madera onse ozungulira nyanja ya Mediterranean. Ming’oma imeneyi ndi ya m’zaka za m’ma 900 B.C.E. mpaka cha kumayambiriro kwa m’ma 800 B.C.E.”

Ofukula zinthu zakale amenewa anapeza ming’oma yoposa 30 yondandalikidwa m’mizere itatu, ndipo akuganiza kuti pamalo onsewo payenera kuti panali ming’oma yoposa 100. Ataunika bwinobwino ming’oma imeneyi anapeza kuti inali ndi tizidutswa ndiponso phula la njuchi. Akatswiri ena akuganiza kuti mwina “pa chaka ankafula uchi wokwana makilogalamu pafupifupi 500 m’ming’oma imeneyi.”

Kale uchi unali chakudya chokoma kwambiri komanso phula la njuchi ankaligwiritsa ntchito popanga zinthu zachitsulo ndi zachikopa. Pa nthawi imeneyo, anthu ankapanganso mabolodi olembapo pogwiritsa ntchito zisa za njuchi zimene ankatha kuzisungunula kuti azigwiritsenso ntchito pa zinthu zina. Ndiyeno kodi anthu ofukula zinthu zakalewa akukhulupirira chiyani pa zimene apezazi?

Chikalata chija chinapitiriza kufotokoza kuti: “Ngakhale kuti Baibulo silinena kuti kale Aisiraeli ankachita ulimi wa njuchi, kupezeka kwa ming’oma imeneyi ku Tel Rehov ndi umboni wakuti nthawi imeneyo ankachita ulimi wa njuchi. Ulimiwu unali wotchuka kwambiri kuyambira kale moti mmene Kachisi Woyamba [wa Solomo] ankamangidwa n’kuti anthu atayamba kale kuchita ulimi umenewu. Choncho n’kutheka kuti mawu akuti ‘uchi,’ amene amapezeka m’Baibulo akunenadi za uchi weniweni wa njuchi.”

[Mawu a Chithunzi patsamba 15]

Institute of Archaeology/​Hebrew University © Tel Rehov Excavations