Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndani Akulalikira Uthenga Wabwino?

Kodi Ndani Akulalikira Uthenga Wabwino?

 Kodi Ndani Akulalikira Uthenga Wabwino?

“ . . . udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu.”​—MATEYU 24:14.

AMBONI ZA YEHOVA ndi amene akulalikira uthenga wabwino padziko lonse. Iwo akuchita zimenezi m’njira zosiyanasiyana. Tiyeni tione njira zimenezi.

1. Kulankhula ndi Anthu. Mofanana ndi Yesu komanso ophunzira ake, a Mboni za Yehova amapita kukauza anthu uthenga wabwino. (Luka 8:1; 10:1) Iwo sangokhala, n’kumadikira kuti anthu awapeze. A Mboni onse, omwe panopa alipo opitirira 7 miliyoni padziko lonse, akugwira ntchito yolalikira za Ufumu wa Mulungu imeneyi. Iwo amalalikira kunyumba ndi nyumba, m’misewu, pafoni ndi njira zina. Chaka chathachi a Mboni anatha maola oposa 1.5 biliyoni akugwira ntchito yolalikira.

Iwo amaphunzitsa anthu za Ufumu wa Mulungu komanso ‘zinthu zonse zimene [Yesu] anawalamulira.’ (Mateyu 28:20) Akuchititsa maphunziro a Baibulo apanyumba oposa 8 miliyoni ndipo maphunziro amenewa ndi aulere.

A Mboni za Yehova akulalikira padziko lonse m’mayiko okwana 236. Iwo amalalikira kwa anthu amitundu yonse komanso azikhalidwe zosiyanasiyana. Amalalikira kumidzi, m’mizinda ndi mu nkhalango zothinana za m’mphepete mwa mtsinje wa Amazon ndiponso mu m’nkhalango za kudera lozizira kwambiri lotchedwa Siberia. Amalalikiranso m’zipululu za ku Africa kuno ndiponso m’mapiri aatali kwambiri padziko lapansi otchedwa Himalaya. Iwo salipidwa pa ntchito imeneyi. M’malomwake, akamagwira ntchitoyi amagwiritsa ntchito ndalama zawo ndiponso nthawi yawo. Iwo amachita zimenezi chifukwa chokonda Mulungu ndiponso anthu anzawo.

2. Mabuku. Magazini ino dzina lake lonse ndi Nsanja ya Olonda, Yolengeza Ufumu wa Yehova ndipo ikufalitsidwa m’zinenero 185. Magazini oposa 42 miliyoni amafalitsidwa mwezi uliwonse. Magazini inanso imene imalengeza Ufumu wa Mulungu ndi Galamukani! Magazini imeneyi imafalitsidwa m’zinenero 83 ndipo mwezi ulionse magazini pafupifupi 40 miliyoni amafalitsidwa.

Palinso zinthu monga mabuku, timabuku, timapepala ma CD, ma MP3 ndiponso ma DVD zimene zimafotokoza zimene Baibulo limaphunzitsa ndipo zinthu zimenezi zikupezeka m’zinenero 540. A Mboni za Yehova atulutsa ndiponso kugawira anthu zinthu zimenezi zoposa 20 biliyoni pa zaka 10 zokha zapitazi. Pamenepa tingati pa avereji agawira zinthu zitatu kwa munthu aliyense padziko lonse.

Komanso a Mboni za Yehova asindikiza ndi kufalitsa Mabaibulo m’zinenero zosiyanasiyana. Panopa Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika lomwe linamasuliridwa, kusindikizidwa ndiponso kufalitsidwa ndi Mboni za Yehova likupezeka lonse lathunthu kapena mbali yake m’zinenero 96. Padakali pano Mabaibulo oposa 166 miliyoni afalitsidwa.

3. Misonkhano Yachikhristu. Mlungu uliwonse, a  Mboni za Yehova amachita misonkhano m’Nyumba za Ufumu zimene zili m’madera osiyanasiyana. Misonkhano imeneyi simapemphero wamba koma imakonzedwa n’cholinga chofuna kuphunzitsa anthu. Pa misonkhanoyi pamakambidwa nkhani zogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo komanso anthu amaphunzira Baibulo pogwiritsa ntchito magazini a Nsanja ya Olonda ndi mabuku ena. Pa misonkhanoyi a Mboni za Yehova amaphunziranso zimene angachite kuti azilalikira uthenga wabwino mogwira mtima.

Padziko lonse lapansi pali mipingo ya Mboni za Yehova yoposa 107,000 ndipo onse amaphunzira zofanana. Zimenezi zimathandiza kuti azikhala ogwirizana. Aliyense ndi wolandiridwa ndi manja awiri pa misonkhano imeneyi. Pa misonkhanoyi sipayendetsedwa mbale ya zopereka. A Mboni za Yehova amadziwa kuti zonse zimene amachitazi zingakhale zopanda phindu ngati sachita zimene amaphunzitsa. Choncho iwo amayesetsa kukhala ndi khalidwe labwino.

4. Khalidwe Labwino. A Mboni amayesetsa kukhala ndi khalidwe labwino monga Akhristu ndipo amayesetsa kuchitira ena zimene iwo amafuna kuti ena aziwachitira. (Mateyu 7:12) Ngakhale kuti nawonso ndi anthu, ndipo nthawi zina amalakwitsa, iwo amafunitsitsa kusonyeza anthu onse chikondi mwa kuwalalikira uthenga wabwino komanso kuwathandiza m’njira zina.

A Mboni za Yehova akamalalikira, cholinga chawo si kukopa anthu onse kuti akhale a Mboni. Koma iwo amadziwa kuti Yehova akadzaona kuti uthenga walalikidwa mokwanira, mapeto adzafika monga Yesu ananenera. Kodi zimenezi zidzakhudza bwanji dziko lapansi ndiponso anthu okhala padzikoli?

[Chithunzi patsamba 7]

A Mboni za Yehova akulalikira uthenga wabwino padziko lonse