Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Kodi Yehova Amatikondanso Amwenyefe?”

“Kodi Yehova Amatikondanso Amwenyefe?”

 Kalata Yochokera ku Mexico

“Kodi Yehova Amatikondanso Amwenyefe?”

MELESIO amakhala kudera lamapiri ndipo amalankhula Chiwodamu. Iye nthawi zina ankabwera m’tauni kudzafuna ntchito. Akafika, ankasonkhana ndi Mboni za Yehova ndipo pobwerera kwawo ankatenga mabuku ofotokoza Baibulo kuti akawerenge limodzi ndi anthu akwawo. Nthawi ina Melesio anapempha kuti wa Mboni adzafike kwawo kuti adzawaphunzitse Baibulo.

Anthu a mtundu wa Wodamu amakhala kudera lakumidzi kwa okhaokha, kumapiri a kumpoto chapakati pa Mexico ndipo ndi mtunda wamakilomita 240 kuchokera pamene pali mpingo wapafupi wa Mboni za Yehova. Tsiku lina anthu angapo tinagwirizana zopita kukawachezera anthuwa.

Tinayenda pa galimoto yaing’ono ya bokosibode ndipo tinatenga matenti ndi zogonera. Tinatenganso mafuta a galimoto ndi zakudya zokwanira masiku atatu. Ulendowu tinanyamukira mumzinda wa Durango. Tinanyamuka 4 koloko m’mawa ndipo tinayenda pa galimoto kwa maola 8 mumsewu wafumbi ndiponso wamapiri mpaka tinafika pamene msewuwu unathera. Pamene panathera msewupa ndi pamene panayambira dera limene kumakhala anthu olankhula Chiwodamu ndipo kutsogolo kwathu kunali chigwa ndiponso phiri lina.

Tinaimika galimoto lathu pa ranchito. Amenewa ndi mawu a Chisipanishi otanthauza mudzi. Tinayamba kuyenda wapansi kwa maola atatu, titanyamula katundu wathu, kutsetsereka mpaka kukafika m’munsi mwenimweni mwa chigwa chija. Tinafika pamenepa kunja kutada choncho tinaganiza zogona pompo. Tinatola nkhuni n’kukoleza moto n’cholinga choti nyama zakutchire zithawe. Tinkagona mosinthana ndipo aliyense ankakhala maso kwa maola atatu n’cholinga chakuti azionetsetsa kuti moto uja usazime.

Kutacha m’mawa tinayamba ulendo wathu wokwera phiri. M’phirimo munali tinjira tambirimbiri ndipo ifeyo tinasokera kangapo konse. Pagulu lathulo panali munthu mmodzi amene ankatha pang’ono kulankhula Chiwodamu. Choncho tinkayenda tikulalikira anthu a m’midzi imene tinkadutsa. Tinadabwa kwambiri anthuwa atatiuza kuti ku Los Arenales, komwe ife tinkapita, kunali anthu ena amene ankanena kuti ndi Mboni za Yehova. Anatiuzanso kuti anthuwa amachita misonkhano yophunzira Baibulo. Tinadabwa ndi zimenezi komabe zinali zolimbikitsa kwambiri.

Tinafika ku Los Arenales, koma pa nthawiyi n’kuti mapazi anthu atatuluka matuza. Tinapeza kuti kuderali kuli nyumba za zidina komanso zofolera ndi makatoni.  Nyumbazi ndi zotalikirana ndipo kulibe sukulu ndiponso magetsi. Anthuwa amakhala kwa okhaokha ndipo ndi osauka kwambiri. Chakudya chawo chachikulu ndi zitumbuwa. Kenako tinakumana ndi Melesio ndipo atationa anasangalala kwambiri. Anatiuza kuti tilowe m’nyumba yake, imene inali yaing’ono. Iye anatiuzanso kuti wakhala akupemphera kwa Yehova kuti atumize Mboni Zake kudzaphunzitsa Baibulo abale ake komanso anthu ena a mtundu wa Wodamu chifukwa ankaona kuti iyeyo sangathe kuyankha mafunso onse amene anthu kumeneko anali nawo.

Anthu a mtundu wa Wodamu amalambira mizimu ya makolo ndipo pochita zimenezi iwo amagwiritsa ntchito zinthu monga nthenga ndi mafupa a mbalame yotchedwa nkhwazi. Komanso amalambira mphamvu zachilengedwe ndipo nthawi zonse amakhala mwamantha kuopa asing’anga amizimu amenenso amawadyera masuku pamutu. Melesio anafotokoza kuti pa maulendo amene anapita kutauni anamva kuti Yehova ndi Mulungu woona. Chifukwa cha zimenezi, iye anataya zinthu zake zonse zimene ankagwiritsa ntchito polambira mafano. Atachita zimenezi anthu a m’mudziwo anayamba kunena kuti milungu yawo ilanga Melesio chifukwa cha zimene anachitazi. Koma ataona kuti palibe chimene chinamuchitikira, anazindikira kuti Yehova ndi wamphamvu koposa milunguyo. Zotsatira zake, anthuwa anayamba kubwera kudzamvetsera Melesio akamaphunzira Baibulo ndi banja lake pogwiritsa ntchito mabuku a Mboni.

Melesio anati: “Ndinawauza kuti choyamba ayenera kuwotcha zithumwa ndiponso mafano awo.” Ambiri mwa anthuwa anasiya kuopa mizimu ndipo chiwerengero cha anthu amene ankabwera kwa Melesio chinawonjezereka mpaka chinafika anthu oposa 80. Tinasangalala kwambiri kumva zimenezi moti tinaganiza zopangitsa msonkhano masana a tsiku lomwelo. Choncho tinatuma anthu pamahosi kuti akaitane anthu amene nthawi zonse ankabwera kunyumba kwa Melesio kudzaphunzira Baibulo. Anthu okwana 25 anafika ngakhale kuti munali mkati mwa mlungu ndiponso tinangowadzidzimutsa. Ena anayenda pansi ndipo ena anabwera pa abulu.

Tinayankha mafunso awo ambiri ndipo Melesio ndi amene ankamasulira. Iwo anatifunsa mafunso monga akuti: “Kodi Yehova amatikondanso Amwenyefe?” “Kodi amamva mapemphero athu tikamapemphera m’Chiwodamu?” “Popeza ife tikukhala kumudzi, kutali kwambiri ndi tauni, kodi Aramagedo ikadzafika Yehova adzatikumbukira?” Tinasangalala kwambiri kugwiritsa ntchito Baibulo kuthandiza anthu odzichepetsa amenewa. Tinawathandiza kuzindikira kuti Yehova amaganizira anthu onse amtima wabwino, mosaganizira za chinenero kapenanso kumene amakhala. Anatipempha kuti tikawatumizire munthu kuti adzawaphunzitse zambiri.

Msonkhanowu utatha, tinadya chakudya chathu chija limodzi ndi mabwenzi athu atsopanowa. Kunja kunada ndipo kunkazizira kwambiri chifukwa panali pamalo okwera. Koma tinasangalala atatiuza kuti tikagone m’nyumba ina imene anali asanamalize kumanga. M’mawa tsiku lotsatira, anatiperekeza kumene kunali galimoto yathu kuja potidutsitsa njira yachidule. Kenako tinafika ku Durango. Tinali osangalala kwambiri ngakhale kuti tinali titatopa ndi ulendowu.

Tikuona kuti ndi mwayi waukulu kukumana ndi anthu amitima yabwino amenewa, ofunitsitsa kuphunzira za Mulungu woona ndi kuyamba kumulambira, ngakhale kuti palibe mabuku ofotokoza Baibulo m’chilankhulo chimene ambiri mwa anthu amenewa angathe kuwerenga. Kuchokera pamene tinapita kuderali, anthu 6 a Mboni za Yehova akhala ali kumeneku kwa milungu itatu. Iwo athandiza anthu pafupifupi 45 kuyamba kutumikira Yehova. Anthu onsewa amapezeka pa misonkhano ya Mboni za Yehova mlungu uliwonse.

Palinso chinthu china chochititsa chidwi kwambiri ndi anthu akuderali. Ku Los Arenales kuli kagolosale kamodzi kokha koma eniake asiya kugulitsa fodya chifukwa anthu ambiri akuderali akuphunzira Baibulo ndipo asiya kusuta fodya. Komanso anthuwa analembetsa maukwati awo kuboma.

[Chithunzi patsamba 24]

Melesio, ali ndi mkazi wake, ana ake anayi komanso apongozi ake

[Zithunzi patsamba 25]

Kuphunzitsa anthu Baibulo komanso kuchita msonkhano ku Los Arenales

[Mawu a Chithunzi patsamba 25]

Servicio Postal Mexicano, Correos de Mexico