Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Baibulo Limasintha Anthu

Baibulo Limasintha Anthu

 Baibulo Limasintha Anthu

KODI zinatheka bwanji kuti mtsikana wina, amene ankagwira ntchito m’bala ndipo ankakonda kutukwana, kumwa mowa mwauchidakwa komanso kumwa mankhwala osokoneza bongo, asinthe moyo wake? Kodi n’chifukwa chiyani munthu wina wandale amene poyamba ankadana ndi chipembedzo, anasintha n’kukhala mtumiki wa Mulungu? Nanga kodi ndi zinthu ziti zimene munthu wina, amene poyamba ankaphunzitsa apolisi a ku Russia kumenyana ndi anthu ovuta, anafunika kusintha kuti akhale wa Mboni za Yehova? Werengani kuti mumve zimene anthu amenewa akunena.

“Ine ndi mayi anga tinayambiranso kugwirizana.”​—NATALIE HAM

CHAKA CHOBADWA: 1965

DZIKO: AUSTRALIA

POYAMBA: NDINKAMWA MANKHWALA OSOKONEZA BONGO

KALE LANGA: Ndinakulira m’tauni yaing’ono ya Robe ku South Australia. Anthu ambiri m’tauni imeneyi amagwira ntchito yopha nsomba, ndipo kumeneko anthu amakonda kukacheza ku hotelo. Nthawi zambiri makolo ndi ana awo amakhala ali kuhoteloko moti anawo amakhala nthawi yaitali ndi zidakwa, anthu okonda kutukwana ndi kusuta fodya.

Pamene ndinkakwanitsa zaka 12 n’kuti nditayamba kale kusuta, kutukwana kwambiri komanso ndinkakonda kukangana ndi mayi anga. Ndili ndi zaka 15, banja la makolo anga linavuta moti sankakhalanso nyumba imodzi. Kenako patatha miyezi 18 ineyo ndinachoka panyumba. Ndinayamba kumwa mowa mwauchidakwa, kumwa mankhwala osokoneza bongo ndiponso uhule. Nthawi zambiri ndinkakhala wokwiya ndipo ndinasokonezeka maganizo. Koma chifukwa chakuti kwa zaka zisanu ndinaphunzira karati komanso mmene munthu wamkazi angadzitetezere kwa anthu ofuna kumuchita chipongwe, ndinkaona kuti nditha kukhala ndekha bwinobwino. Komabe nthawi zambiri ndikakhala ndekha ndinkakhala wachisoni ndipo ndinkapemphera kwa Mulungu kuti andithandize. Popempherapo ndinkamuuza kuti: “Komabe ndikupempha kuti musandiuze kuti ndiyambe kupita kutchalitchi.”

Kenako mnzanga wina anandipatsa Baibulo. Iye ankakonda zopemphera koma sanali m’chipembedzo chilichonse. Komanso ankakonda kusuta chamba ngati anzanga ena onse. Komabe ankati amakhulupirira Mulungu ndi mtima wonse ndipo anandilimbikitsa kuti ndibatizidwe. Tsiku lina ananditenga n’kupita nane kunyanja ya m’dera lakwathuko ndipo anandibatiza. Kuyambira pamenepo ndinkaona kuti ndili pa ubwenzi ndi Mulungu. Komabe sindinkapeza nthawi yowerenga Baibulo.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA: Tsiku lina mu 1988 anthu awiri a Mboni za Yehova anagogoda pakhomo la nyumba imene ndinkakhala. Mmodzi wa anthuwa anandifunsa kuti: “Kodi dzina la Mulungu mukulidziwa?” Wa Mboniyo anandiwerengera m’Baibulo lake lemba la Salimo 83:18. Lembali limati: “Kuti anthu adziwe kuti inu, amene dzina lanu ndinu Yehova, Inu nokha ndinu Wam’mwambamwamba, wolamulira dziko lonse lapansi.” Ndinadabwa kwambiri ndi lembali.  Atachoka ndinapita pa galimoto yanga ku sitolo ina yogulitsa mabuku achikhristu. Ulendowu unali wamakilomita 56. Cholinga changa ndinkafuna kuti ndikaone zimene Mabaibulo ena amanena palembali. Ndinayang’ananso dzina la Mulungu mu dikishonale. Nditatsimikiza kuti dzina la Mulungu ndi Yehova, ndinayamba kuona kuti payenera kuti palinso zinthu zina zimene sindinkazidziwa.

Mayi ankandiuza kuti a Mboni za Yehova si anthu abwino. Komanso pa zochepa zimene ineyo ndinkadziwa zokhudza a Mboni ndinkaganiza kuti iwo amakhwimitsa zinthu kwambiri komanso sakonda kusangalala. Ndinali ndi maganizo akuti akadzabwera panyumba panga sindidzawalandira. Koma atabwera, ndinasintha maganizo ndipo ndinawalowetsa m’nyumba. Nthawi yomweyo tinayamba kuphunzira Baibulo.

Nthawi zonse ndikamaliza kuphunzira ndinkauza Craig, mnyamata yemwe ndinali naye pa chibwenzi, zimene ndaphunzirazo. Tsiku lina atatopa ndi zimene ndinkamuuzazo anandilanda buku limene tinkaphunzira n’kuyamba kuliwerenga ndipo pasanathe milungu itatu anazindikira kuti wapeza choonadi chonena za Mulungu. Patapita nthawi ineyo ndi Craig tinasiya kumwa mankhwala osokoneza bongo komanso kumwa mowa mwauchidakwa. Ndinasiyanso ntchito yanga ya m’bala. Ndipo potsatira mfundo za m’Baibulo, ine ndi Craig tinakwatirana.

PHINDU LIMENE NDAPEZA: Nthawi imene a Mboni za Yehova anayamba kutiphunzitsa Baibulo n’kuti ine ndi Craig titatsala pang’ono kuthetsa chibwenzi chathu. Masiku ano Craig ndi mwamuna wabwino kwambiri ndipo tili ndi ana aamuna awiri a mapasa. Tilinso ndi anzathu abwino amene nawonso ndi a Mboni za Yehova ndipo timawaona kuti ndi ofunika kwambiri.

Poyamba mayi anga atamva kuti ndayamba kuphunzira ndi Mboni za Yehova anakwiya kwambiri. Koma iwo ankachita zimenezi chifukwa chosamvetsa bwinobwino mmene Mboni za Yehova zilili. Panopo ine ndi mayi anga tinayambiranso kugwirizana. Masiku ano sindidzionanso kuti ndine wosafunika. M’malomwake moyo wanga uli ndi cholinga ndipo ndikuona kuti ndikupeza zosowa zanga zauzimu.​—Mateyu 5:3.

“Ndinaphunzira zinthu zambiri zochititsa chidwi m’Baibulo.”​—ISAKALA PAENIU

CHAKA CHOBADWA: 1939

DZIKO: TUVALU

POYAMBA: NDINALI WANDALE

KALE LANGA: Ndinabadwira pachilumba china chokongola cha Pacific chotchedwa Nukulaelae. Panopa chilumba chimenechi chili m’dziko la Tuvalu. Anthu otchuka pazilumbazi anali abusa a matchalitchi amene anaphunzira zaubusa pakoleji inayake ya ku Samoa. Unali udindo wa anthu apazilumbazi kuonetsetsa kuti abusa ndiponso mabanja awo tsiku lililonse ali ndi chakudya ndiponso malo ogona. Abusawo ankafuna kuti zonse zimene akuwapatsa zizikhala zabwino kwambiri. Ngakhale anthuwo atakhala kuti alibe chakudya chokwanira, ankayenerabe kupezera abusawa chakudya.

M’busa wapachilumba chakwathu anali ndi sukulu ndipo ankaphunzitsa zachipembedzo, masamu ndi jogalafe. Ndimakumbukira nthawi ina pamene m’busayu anamenya kwambiri ana asukulu moti anawo anali magazi okhaokha. Palibe amene analimba mtima kudzudzula zankhanzazi. Ngakhalenso makolo a anawo sananene chilichonse chifukwa nthawi imeneyo m’busa ankaopedwa kwambiri ngati Mulungu.

Ndili ndi zaka 10 ndinachoka panyumba kupita kusukulu ya boma ya m’derali yomwe inali  pachilumba china. Nditamaliza sukulu ndinayamba kugwira ntchito m’boma. Nthawi imeneyo zilumbazi zinali mbali ya zilumba zotchedwa Gilbert ndi Ellice ndipo zinkalamulidwa ndi dziko la Britain. Ndinagwira ntchito m’madipatimenti osiyanasiyana a boma ndipo pamapeto pake ndinadzakhala mkonzi wa nyuzipepala inayake ya boma imene inkatuluka kamodzi pamlungu. Zonse zinkayenda bwino mpaka pamene ndinafalitsa kalata yochokera kwa munthu wina yodandaula kuti boma likuwononga ndalama zambiri pokonzekera kubwera kwa mwana wa mfumu ya ku Britain. Amene analemba kalatayi sanatchule dzina lake lenileni choncho abwana anga anandiuza kuti ndiwauze dzina lenileni la munthuyo. Ndinakana kuwauza ndipo nkhaniyi inadziwika paliponse.

Patangopita nthawi yochepa zimenezi zitachitika ndinasiya ntchito n’kuyamba ndale. Ndinapambana zisankho zapachilumba cha Nukulaelae ndipo anandisankha kukhala Nduna ya Zamalonda ndi Zachilengedwe. Kenako, anthu akuchilumba cha Kiribati (kale chinkatchedwa kuti Gilbert) ndi chilumba cha Tuvalu (kale chinkatchedwa kuti Ellice) analandira ufulu wawo kuchokera ku dziko la Britain. Panthawi imeneyo gavanala anandipempha kuti ndikhale woyang’anira maofesi a boma ku Tuvalu. Koma sindinkafuna kuti ndioneke ngati ndinali kugwirizana ndi atsamunda. Choncho ndinapikisana nawo pa udindo wa nduna ya boma popanda kuthandizidwa ndi gavanalayo koma ndinaluza. Zitatero ine ndi mkazi wanga tinabwerera kuchilumba cha kwathu ndipo tinaganiza kuti ndibwino tizikakhala moyo wakumudzi.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA: Anthu a pachilumbachi ankakhulupirira kuti Lamlungu ndi tsiku la Sabata choncho anthu onse, kupatulapo ine ndekha, ankaliona kuti ndi tsiku lopatulika. Kwa ine, Lamlungu linali tsiku lokayendetsa boti langa panyanja komanso kupha nsomba. Sindinkafuna kuti anthu azindiona kuti ndine munthu wopemphera. Bambo anga anandiuza kuti iwo ndi anthu ena sankasangalala ndi khalidwe langa. Koma ndinali nditatsimikiza kuti sindikufuna kuti tchalitchi chizilamulira zochita zanga.

Tsiku lina ndinapita kuchilumba cha Funafuti komwe kuli likulu la dziko la Tuvalu. Ndili kumeneko, mng’ono wanga anandiitanira ku msonkhano wa Mboni za Yehova. Kenako mmishonale wina wa Mboni anandipatsa magazini ambiri a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! kuti ndiwerenge. Anandipatsanso buku lofotokoza mmene ziphunzitso zonyenga, zimene matchalitchi ambiri achikhristu amaphunzitsa zinayambira. Ndinawerenga bukulo kambirimbiri. Ndinaphunzira m’Baibulo zinthu zambiri zochititsa chidwi kuphatikizapo mfundo yakuti palibe lamulo lokakamiza Akhristu kusunga Sabata. * Ndinauza mkazi wanga zimene ndinaphunzirazi ndipo nthawi yomweyo anasiya kupita kutchalitchi.

Ngakhale zinali choncho, ineyo ndinali nditatemetsa kale nkhwangwa pamwala kuti sindidzalowa m’chipembedzo china chilichonse. Panapita zaka pafupifupi ziwiri koma ndinali ndisanaiwalebe zimene ndinaphunzira zija. Kenako ndinalembera kalata mmishonale uja amene ankakhala ku Funafuti, kumuuza kuti tsopano ndinali nditakonzeka kusintha zina ndi zina pa moyo wanga. Nthawi yomweyo iye anakwera boti ndipo anabwera kwathu kudzandiphunzitsa zambiri za m’Baibulo. Bambo anga anakwiya kwambiri atamva kuti ndikufuna kukhala wa Mboni za Yehova. Koma ndinawauza kuti a Mboniwo andiphunzitsa mfundo zambiri za m’Baibulo moti ndasankha kuti ndikhale wa Mboni za Yehova.

PHINDU LIMENE NDAPEZA: Mu 1986 ndinabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova ndipo mkazi wanga anabatizidwa chaka chotsatira. Ana athu awiri aakazi nawonso anaphunzira Baibulo ndipo anasankha kukhala a Mboni za Yehova.

Panopo ndikusangalala kwambiri kukhala m’gulu lachipembedzo limene anthu ake sasankhana ndipo alibe azibusa. Zimenezi ndi zofanana ndi mmene zinalili m’nthawi ya atumwi. (Mateyu 23:8-12) Anthu amenewa amatsatiranso chitsanzo cha Yesu modzichepetsa ndipo amaphunzitsa ena za boma la Ufumu wa Mulungu. (Mateyu 4:17) Ndikuthokoza kwambiri Yehova Mulungu chifukwa chondilola kuphunzira choonadi chonena za iye komanso anthu ake.

“A Mboni sanandikakamize kuti ndizikhulupirira zimene ankandiphunzitsa.”​—ALEXANDER SOSKOV

CHAKA CHOBADWA: 1971

DZIKO: RUSSIA

POYAMBA: NDINKAPHUNZITSA APOLISI KUMENYANA NDI ANTHU OVUTA

 KALE LANGA: Ndinabadwira ku Moscow ndipo nthawi imeneyo mzindawu unali likulu la dziko la Soviet Union. Banja lathu linkakhala m’nyumba yaikulu ndipo ambiri mwa anthu amene tinkakhala nawo pafupi ankagwira ntchito pafakitale imodzi. Ndikukumbukira kuti ndili mwana, anthuwo ankandinena kuti ndidzafa msanga kapena ndidzamangidwa chifukwa ndinali mwana wopulupudza kwambiri. Mogwirizana ndi mawu amenewa pamene ndinkakwanitsa zaka 10 n’kuti nditamangidwapo kale.

Ndili ndi zaka 18 ndinalowa usilikali ndipo anditumiza kuti ndizikalondela kumalire a dziko lathu. Patapita zaka ziwiri ndinabwerera kunyumba ndipo ndinayamba kugwira ntchito pafakitale ija koma ntchitoyo siinkandisangalatsa. Choncho ndinayamba ntchito yapolisi mumzinda wa Moscow ndipo ndinali mphunzitsi wa gulu lomenyana ndi anthu ochita zachiwawa. Ndinathandiza nawo kugwira anthu oswa malamulo mumzinda wa Moscow ndipo ndinkapita m’malo osiyanasiyana kumene kunkachitika ziwawa m’dziko la Russia. Nthawi zonse ndinkavutika maganizo kwambiri moti ndikafika panyumba nthawi zina ndinkagona pandekha poopa kuti ndikamalota ndingavulaze mkazi wanga.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA: Nditayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova ndinazindikira kuti zachiwawa zimene ndinkachita zinali zosagwirizana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa. Ndinaonanso kuti ndinafunika kusiya kusuta fodya komanso kumwa mowa mwauchidakwa. Komabe sindinkafuna kusiya ntchito chifukwa ndinkaona kuti panalibenso ntchito ina imene ndikanagwira kuti ndizipeza ndalama zosamalirira banja langa. Ndinkaonanso kuti sindingathe kumalalikira ngati mmene a Mboni ankachitira.

Pamapeto pake ndinazindikira kuti zimene Baibulo limanena ndi zolondola ndipo mfundo ya pa Ezekieli 18:21, 22 inandilimbikitsa kwambiri. Lembali limati: “Munthu woipa akabwerera, kusiya machimo ake onse amene anali kuchita . . . , zolakwa zonse zimene anachita sizidzakumbukiridwa ndipo sadzalangidwa nazo.”

Ndinasangalala kuti a Mboni sanandikakamize kuti ndizikhulupirira zimene ankandiphunzitsa koma anangondithandiza kuganizira mozama mfundo zimene ndinkaphunzirazo. Ndinatenga magazini awo okwana 40 kapena kuposa, ndipo ndinawawerenga pasanathe milungu itatu. Zimene ndinaphunzirazo zinandithandiza kuzindikira kuti ndapeza chipembedzo choona.

PHINDU LIMENE NDAPEZA: Ndisanayambe kuphunzira Baibulo banja lathu linali litangotsala pang’ono kutha, koma panopa likuyenda bwino. Nditangoyamba kuphunzira Baibulo, mkazi wanga nayenso anayamba kuphunzira ndipo tinagwirizana kuti tiyambe kutumikira Yehova. Panopa banja lathu ndi losangalala. Komanso ndinapeza ntchito yomwe siitsutsana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa.

Nditangoyamba kumene kulalikira nyumba ndi nyumba, mtima wanga unkagunda kwambiri ngati mmene ndinkamvera tikafuna kuyamba kumenyana ndi anthu ovuta. Koma panopa ndinasintha moti ndimadziletsa ngakhale munthu atandiputa. Ndaphunzira kukhala woleza mtima pochita zinthu ndi anthu. Ndimangodandaula kuti ndinawononga nthawi ndi zimene ndinkachita, komabe panopa ndimaona kuti moyo wanga ndi waphindu. Ndimasangalala kugwiritsa ntchito mphamvu zanga potumikira Yehova Mulungu ndiponso kuthandiza ena.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 24 Kuti mudziwe zambiri, werengani nkhani yakuti “Kodi Muyenera Kusunga Sabata?” mu Nsanja ya Olonda ya February 1, 2010, tsamba 11 mpaka 15.