Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi lamulo lokhudza khunkha linali lotani, ndipo ndani ankapindula ndi lamuloli?

Chilamulo cha Mose chinkaletsa alimi kukolola mbewu zonse m’minda yawo. Chilamulochi chinkanena kuti anthu akamakolola, asamachotse zokolola zonse m’mphepete mwa munda wawo. Mwachitsanzo chinkanena kuti akamakolola mphesa, asamatole zimene zamwazika m’munda komanso asamabwerere kukakolola zimene zinali zisanakhwime pa nthawi imene ankakolola. Chilamulo chinkanenanso kuti, akamakwapula nthambi za mitengo ya maolivi, zipatso zimene sizinagwe azizisiya. (Levitiko 19:9, 10; Deuteronomo 24:19-21) Amene ankayenera kukunkha zotsalazo anali anthu osauka, ana amasiye, akazi amasiye komanso alendo.

Lamulo lokhudza khunkha linkapindulitsa anthu onse amene ankakhala ku Isiraeli. Kwa eni minda, lamulo limeneli linkawalimbikitsa kukhala owolowa manja, oganizira ena ndiponso linkawachititsa kukhulupirira kuti Mulungu awadalitsa. Kwa anthu amene ankakunkhawo, lamuloli linkawaphunzitsa kugwira ntchito mwakhama chifukwa ntchito yokunkha inali yotopetsa. (Rute 2:2-17) Dongosolo loti anthu azikunkha linkathandiza kuti osauka asamakhale ndi njala komanso kuti asamavutitse ena. Dongosolo limeneli linkathandizanso kuti anthu osaukawo asachite kufika pomadalira chakudya chochita kupemphetsa, chifukwa zinali zochititsa manyazi kwambiri.

Kodi n’chifukwa chiyani Solomo anaitanitsa mitengo kuchokera ku Lebanoni, komwe kunali kutali kwambiri, kuti amangire kachisi ku Yerusalemu?

Nkhani imene ili palemba la 1 Mafumu 5:1-10 imanena za pangano limene Solomo anachita ndi Hiramu mfumu ya ku Turo. Malinga ndi zimene anagwirizana, Hiramu anatumiza mitengo ya mkungudza ndiponso mitengo ina yofanana ndi mkungudza, kuchokera ku Lebanoni kupita ku Isiraeli kudzera panyanja kuti Solomo akamangire kachisi.

Nthawi imeneyo matabwa a mkungudza ankayenda malonda kwambiri ku Middle East. Ku Iguputo ndi ku Mesopotamiya matabwawa ankagwiritsidwa ntchito pomangira akachisi ndi nyumba za mafumu. M’malaibulale akale achifumu komanso m’mabuku ndi m’zolembalemba zina zakale muli nkhani zosonyeza kuti mafumu akum’mwera kwa Mesopotamiya ankaitanitsa mitengo imeneyi kuchokera ku Lebanoni. Nthawi zina ankatenga mitengoyi kwa adani awo amene awagonjetsa pa nkhondo kapenanso mfumu inkapereka mitengoyi kwa mfumu ina yaikulu ngati msonkho. Ku Iguputo matabwa amenewa ankawagwiritsa ntchito kupangira maboti achifumu, mabokosi a maliro ndi zinthu zina zogwiritsa ntchito pa maliro.

Matabwa a ku Lebanoni anali odziwika kwambiri chifukwa anali olimba, okongola, akafungo kabwino ndiponso sankafumbwa. Choncho Solomo anagwiritsa ntchito matabwa apamwamba kwambiri pomanga kachisi. Masiku ano dera lamapiri ku Lebanoni kumene kalelo kunali nkhalango yaikulu ya mikungudza, kunangotsala nkhalango zing’onozing’ono za apo ndi apo.

[Chithunzi patsamba 15]

Zithunzi za Asuri Zimene Zinapezeka Kunyumba ya Mfumu Sarigoni Zosonyeza Ngalawa Zonyamula Mitengo ya Mkungudza Kuchokera ku Lebanoni

[Mawu a Chithunzi]

Erich Lessing/​Art Resource, NY