“Lero Ndi Tsiku Limene Mwakhala Mukuliyembekezera”

“Lero Ndi Tsiku Limene Mwakhala Mukuliyembekezera”

Mwambo Womaliza Maphunziro a Giliyadi​—Gulu la Nambala 129

“Lero Ndi Tsiku Limene Mwakhala Mukuliyembekezera”

PA SEPTEMBER 11, 2010, anthu pafupifupi 8,000 anasonkhana kuti achite mwambo wapadera kwambiri wa omaliza maphunziro. Ophunzirawo anali m’gulu la nambala 129 la Sukulu ya Giliyadi Yophunzitsa Baibulo. M’bale Samuel Herd wa m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova anauza omaliza maphunzirowo kuti: “Lero ndi tsiku limene mwakhala mukuliyembekezera ndipo ife tili pano kuti tisangalale nanu limodzi.”

“Khutu Lakumva”

M’bale Herd anatsegulira mwambowu ndi nkhani yonena za kufunika koti Akhristu azigwiritsa bwino ntchito “khutu lakumva” mwa kumvetsera Mawu a Mulungu mosamala. (Miyambo 20:12) Iye anauza ophunzirawo kuti: “Kwa miyezi ingapo mwakhala mukumvetsera Yehova ndipo mupitiriza kuchita zimenezi kwamuyaya.”

Kodi amishonale amene angoyamba kumene ntchito yawo angagwiritse bwanji ntchito makutu awo mwanzeru? M’bale Herd anayankha kuti: “Mwa kumvetsera zimene Mawu a Mulungu amanena.” Iye anawonjezeranso kuti: “Pa mwambo uno mumva mfundo zambiri zimene zingakuthandizeni pa ntchito yanu ya umishonale pa zaka zikubwerazi.”

“Khulupirirani Yehova Ndi Mtima Wanu Wonse”

Kenako M’bale Gerrit Lösch, amenenso ali m’Bungwe Lolamulira, anakambira ophunzirawo nkhani ya mutu wochititsa chidwi wakuti, “Khulupirirani Yehova Ndi Mtima Wanu Wonse.” Iye anatchula zochitika zosiyanasiyana, zakale ndiponso za m’nthawi yathu ino, pamene anthu a Mulungu anasonyeza kukhulupirira Yehova.

M’bale Lösch ananena kuti mofanana ndi zimenezi, “amishonale ayenera kusonyeza kuti amakhulupirira Mulungu pochita utumiki wawo. Mwachitsanzo, mwina mungadzifunse kuti, ‘Kodi ndikatha kuphunzira chilankhulo chatsopano? Kodi ndikatha kuzolowera chikhalidwe chatsopano? Kodi ndikatha kulimbana ndi maganizo olakalaka kumudzi kwathu?’” Mbale Lösch anauza ophunzirawo kuti yankho la mafunso onsewa ndi lakuti ayenera “kukhulupirira Yehova.”

Kenako M’bale Lösch anawerenga lemba la Miyambo 14:26 limene limati: “Munthu woopa Yehova amakhulupirira Mulungu pa chilichonse.” Kuganizira njira zambiri zimene Yehova watidalitsira, kungatithandize kuti tizimukhulupirira kwambiri.

Baibulo limanena kuti munthu amene amakhulupirira Yehova “adzakhala ngati mtengo wobzalidwa m’mphepete mwa madzi, umene mizu yake imakafika m’ngalande za madzi. Kutentha kukadzafika iye sadzadziwa, koma masamba ake adzachuluka ndi kukhala obiriwira.”​—Yeremiya 17:7, 8.

Apa phunziro ndi loonekeratu. M’bale Lösch anati: “Kaya kutsogoloku mukumana ndi zotani, muyenera kukhulupirira Yehova.”

“Tsanzirani Angelo Okhulupirika”

Umenewu unali mutu wa nkhani imene M’bale Stephen Lett, wa m’Bungwe Lolamulira anakamba. Angelo amatipatsa chitsanzo chabwino kwambiri. M’bale Lett ananena kuti: “Zonse zimene Baibulo limanena zokhudza angelo okhulupirika ndi zoyenera kuzitsanzira.” Kenako iye anatchula makhalidwe anayi amene angelo okhulupirika ali nawo amene tiyenera kutsanzira. Makhalidwe amenewa ndi kupirira, kudzichepetsa, mtima wofunitsitsa kuthandiza ena ndiponso kukhulupirika.

Baibulo limanena kuti kwa masiku 21, mngelo wina analimbana ndi chiwanda chinachake champhamvu kwambiri chotchedwa ‘kalonga wa Perisiya.’ (Danieli 10:13) Mngelo ameneyo anasonyeza kupirira. Ndiyeno M’bale Lett anafotokoza kuti nafenso Akhristu ‘tikulimbana ndi . . . makamu a mizimu yoipa m’malo akumwamba.’ (Aefeso 6:12) Kenako anauza omaliza maphunzirowo kuti, “Yesetsani kuti musasiye utumiki wanu.”

Manowa, yemwe anali bambo ake a Samisoni, atafunsa mngelo wina kuti amuuze dzina lake, mngeloyo anakana. Mngelo ameneyu anasonyeza kudzichepetsa. (Oweruza 13:17, 18) M’bale Lett anauza omaliza maphunzirowo kuti: “Munthu wina akakutamandani chifukwa cha zinthu zimene mwakwanitsa kuchita, modzichepetsa muuzeni kuti Yehova ndi gulu lake ndi amene ayenera kutamandidwa.”​—1 Akorinto 4:7.

Pamene Yesu anali m’munda wa Getsemani, patatsala kanthawi kochepa kuti afe, “mngelo wochokera kumwamba anaonekera kwa iye ndi kumulimbikitsa.” (Luka 22:43) Mngelo ameneyu anasonyeza mtima wofuna kuthandiza ena. M’bale Lett ananena kuti: “Muzikapemphera mochokera pansi pa mtima kuti muzindikire zosowa zenizeni za anthu a kudera limene mwatumizidwa. Ndiyeno mothandizidwa ndi Yehova, muzikayesetsa kuwathandiza pa zosowa zimenezo.”

Popeza kuti ndi angelo ochepa chabe amene anagwirizana ndi Satana pa kupandukira Mulungu, tinganene kuti angelo ambiri ndi zitsanzo zabwino pa nkhani ya kukhulupirika.​Chivumbulutso 12:4.

Kenako M’bale Lett analimbikitsa ophunzirawo kuti: “Monga amachitira angelo okhulupirika, onetsetsani kuti simukumupatsa mpata Mdyerekezi. Tsutsani Mdyerekezi ndipo adzakuthawani.”​—Yakobo 4:7.

Nkhani Zina Zapamwambowu

“Yehova Akhale Thanthwe la Mtima Wanu.” M’bale Gary Breaux, wa mu Komiti ya Nthambi ku United States anakamba nkhani ya mutu wokopa chidwi umenewu, yomwe inali yochokera pa Salimo 73:26. Nkhani imeneyi inathandiza ophunzirawo kuona kufunika kodalira Yehova. Koma kodi n’chifukwa chiyani Baibulo limayerekezera Yehova ndi thanthwe? M’bale Breaux anati: “Thanthwe kapena kuti mwala waukulu ungathandize kuti pepala lisauluke ndi mphepo yamphamvu. Mofanana ndi zimenezi, Yehova angakuthandizeni kuteteza mtima wanu ndiponso kuukhazika pansi.” Komabe mtima ungatisocheretse tikakumana ndi mayesero. (Yeremiya 17:9) Zina mwa zimene zingachititse munthu kuganiza zongobwerera kwawo ndi zinthu monga nyengo yatsopano yosiyana ndi kumene anakulira, zakudya zatsopano ndiponso kukhala ndi anthu ena m’nyumba ya amishonale. M’bale Breaux ananenanso kuti: “Kumene mukupitako, mukakumana ndi nkhani zimene mukafunika kuziganizira komanso kusankha zochita. Kodi mukasankha zinthu zimene zingasangalatse Yehova? Ngati mungakatero, Yehova akakhala thanthwe la mtima wanu ndipo azikakutsogolerani.”

“Kodi Muli Ndi Chikhulupiriro Champhamvu Moti Simungaope Kuponda M’madzi?” M’bale Sam Roberson, amene ndi mlangizi wa Sukulu ya Giliyadi, anakamba nkhani ya mutu umenewu ndipo inali yochokera pa Yoswa chaputala 3. Kodi Aisiraeli mamiliyoni ambiri anatha bwanji kuwoloka mtsinje wa Yorodano pa nthawi imene madzi anali osefukira? Yehova anauza Yoswa kuti auze ansembe kuti ‘akalowe mumtsinje wa Yorodano ndi kuima m’mphepete mwa mtsinjewo.’ Mulungu anawalonjeza kuti: “Mapazi a ansembe . . . akangoponda m’madzi, madzi a mtsinje wa Yorodanowo aduka . . . n’kukhala damu limodzi.” (Yoswa 3:8, 13) M’bale Roberson anauza ophunzirawo kuti: “Pamoyo wanu mukumana ndi ‘mitsinje ya Yorodano’ imene ngati simusamala ingakulepheretseni kulandira madalitso a Mulungu.” Mwachitsanzo, zingakhale zovuta kugwirizana ndi amishonale ena. Kodi ophunzirawo angakathane nalo bwanji vuto limeneli? M’bale Roberson anawalangiza kuti: “Muzikaganizira kwambiri za ntchito yanu osati anthu amene mukugwira nawo ntchitowo. Mukamasonyeza chikhulupiriro cholimba n’kuponda m’madzi mosaopa, Yehova adzakuthandizani kuwoloka ‘mitsinje ya Yorodano,’ imene mudzakumana nayo m’moyo wanu monga amishonale.”

“Muzikhazikitsa Zolinga Zanu.” Umenewu ndi mutu wankhani imene mlangizi wa Sukulu ya Giliyadi, dzina lake William Samuelson anakamba. Nkhaniyi inali yochokera pa lemba la Miyambo 16:3 limene limati: “Pereka ntchito zako kwa Yehova, ndipo zolinga zako ndithu zidzakhazikika.” M’bale Samuelson anafunsa ophunzirawo kuti: “Kodi lembali likutanthauza kuti palibe chimene mungachite pofuna kukhazikitsa zolinga zanu, kusiyapo ‘kupereka ntchito yanu’ kwa Yehova basi?” Iye anafotokoza kuti lembali silikutanthauza zimenezo chifukwa lemba la Miyambo 16:1 limati: “Munthu ndiye amakonza maganizo mumtima mwake.” M’bale Samuelson anafotokozanso kuti: “Yehova sakonza maganizo a mtima wanu mozizwitsa. M’malomwake inuyo muyenera kuonetsetsa kuti mukuchita zinthu zoyenera. Mwa kuphunzira Mawu a Mulungu, kupemphera ndiponso kugwirizana kwambiri ndi ofesi ya nthambi, mudzapitiriza kukhala ndi mtima wothandiza, ndipo Yehova adzakhazikitsa zolinga zanu.”

Zokumana Nazo Komanso Kucheza Ndi Ophunzira

Ophunzira a Sukulu ya Giliyadi amapita kukasonkhana ndiponso kukalalikira limodzi ndi mipingo yapafupi ya Mboni za Yehova. Kuchita zimenezi ndi mbali ya maphunziro awo. Choncho, mlangizi wina wa Sukulu ya Giliyadi, dzina lake Mark Noumair, anacheza ndi ophunzira angapo kuti afotokoze zimene anakumana nazo polalikira. Ophunzira amene anafunsidwawa anafotokoza kuti pemphero linawathandiza kwambiri kupeza anthu achidwi.

Mwachitsanzo banja lina linapita kukadya kulesitilanti. Mnyamata wina wogwira ntchito mulesitilantimo anaona kuti anthuwa asanayambe kudya anapemphera chamumtima. Atamaliza kupemphera, mnyamatayu anawafunsa ngati anali a Mboni za Yehova. Atavomera, iye ananena kuti nayenso poyamba anali Mboni koma anasiya. Anafotokozanso kuti nthawi ina anapalamula mlandu ndipo anamangidwa moti anakhalapo kundende. Tsopano mnyamatayu anali akufuna kubwereranso kwa Yehova. Ananenanso kuti a Mboniwo asanalowe mulesitilantimo, iye anali atapemphera kwa Mulungu, kumupempha kuti amuthandize kusintha moyo wake. Apatu Mulungu anayankha pemphero la mnyamatayu.

M’bale Rudi Hartl, yemwe amagwira ntchito m’Dipatimenti Yoyankha Makalata, anakamba nkhani ya mutu wakuti: “Talawani Ndipo Muone Kuti Yehova Ndi Wabwino.” M’nkhaniyi, iye anafunsa Wayne Wridgway wochokera ku Mozambique, Jason Reed wochokera ku Chile ndi Kenji Chichii wochokera ku Nepal. Abale atatu onsewa ndi amishonale oti analowapo Sukulu ya Giliyadi. Abale amenewa ananena mosabisa mawu mavuto amene anakumana nawo atangoyamba kumene umishonale. Mavuto amenewa anali monga kuphunzira chinenero chatsopano, kuzolowera chikhalidwe chatsopano komanso kulimbana ndi maganizo olakalaka kumudzi kwawo. M’bale Chichii anati: “Chimene chinatithandiza kwambiri ndi kupeza mabwenzi mofulumira mumpingo watsopano. Pamene tinalimbitsa ubwenzi wathu ndi anthu amenewa, tinaona kuti zinali zosavuta kwenikweni kupirira maganizo olakalaka kumudzi kwathu.”

Ophunzira onse okwana 56 atalandira zikalata zosonyeza kuti amaliza maphunziro awo, mmodzi mwa ophunzirawo anawerenga kalata yothokoza imene kalasili linalemba. Kalatayo inali yokhudza mtima kwambiri. Mwa zina, inali ndi mawu awa, opita kwa abale a m’Bungwe Lolamulira: “Tonsefe m’kalasi lathu, taona tokha kudzipereka kwanu mwachikondi ndiponso mosatopa potikonzera maphunziro amenewa, kutiyendera komanso kutipatsa malangizo abwino kwambiri auzimu. Popeza mwatisonyeza chikondi chimenechi, nafenso kumene tikupitako tikayesetsa kutsanzira chikondi chanu, kuleza mtima, kudzichepetsa ndiponso kuchita chidwi ndi anthu.”

[Mawu Otsindika patsamba 28]

“Munthu wina akakutamandani . . . , muuzeni kuti Yehova ndi gulu lake ndi amene ayenera kutamandidwa”

[Mawu Otsindika patsamba 29]

“Pamoyo wanu mukumana ndi ‘mitsinje ya Yorodano’”

[Tchati/​Mapu patsamba 31]

ZA OPHUNZIRAWO

Mayiko amene ophunzira achokera: 9

Ophunzira: 56

Mabanja: 28

Avereji ya zaka zobadwa: 33.0

Avereji ya zaka zimene akhala Mboni kuchokera pamene anabatizidwa: 17.9

Avereji ya zaka zimene akhala akuchita utumiki wa nthawi zonse: 13.3

[Mapu]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Ophunzirawa anatumizidwa kumayiko 25 amene ali pansipa

KUMENE AMISHONALE ANATUMIZIDWA

BOLIVIA

BOTSWANA

BULGARIA

CONGO (KINSHASA)

CÔTE D’IVOIRE

GAMBIA

GERMANY

INDIA

INDONESIA

KENYA

LIBERIA

MACEDONIA

MADAGASCAR

MALAYSIA

MOZAMBIQUE

PANAMA

PERU

POLAND

ROMANIA

SERBIA

SIERRA LEONE

SWAZILAND

TANZANIA

UGANDA

ZIMBABWE

[Chithunzi patsamba 30]

Ophunzira akusonyeza zina mwa zimene anakumana nazo mu utumiki

[Chithunzi patsamba 31]

Gulu la Nambala 129 la Omaliza Maphunziro a Sukulu ya Giliyadi ya Watchtower Yophunzitsa Baibulo

Pamndandanda umene uli pansipa, mizera yayambira kutsogolo kupita kumbuyo, ndipo mumzera uliwonse mayina tawandandalika kuyambira dzina la munthu amene ali kumanzere kupita kumanja.

(1) Munaretto, R.; Olofsson, Y.; Budden, K.; Najdzion, L.; Moya, G.; Treviño, G.; Dion, A.; Fleegle, A.

(2) Smith, J.; Michael Raj, J.; Smith, S.; Paramo, A.; McDonald, J.; Deans, M.; Joyal, S.; Watson, L.

(3) Joyal, C.; Crawley, T.; Hacker, D.; Shynkarenko, J.; Knapp, T.; Ayling, J.; Highley, C.; Olofsson, B.

(4) Fitzpatrick, M.; Najdzion, B.; Skallerud, L.; Harris, A.; Harris, S.; Budden, R.; Paramo, Y.; Skallerud, K.

(5) Crawley, B.; Michael Raj, J.; Lodge, A.; Lodge, R.; Herms, N.; Fitzpatrick, J.; Moya, R.; Munaretto, P.

(6) Watson, S.; Deans, M.; Hacker, J.; McDonald, J.; Treviño, J.; Harris, S.; Herms, C.; Harris, P.

(7) Shynkarenko, V.; Highley, T.; Smith, A.; Dion, J.; Ayling, R.; Smith, B.; Knapp, T.; Fleegle, B.