Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Pali Kusiyana Maganizo Pankhani ya Mzimu Woyera

Pali Kusiyana Maganizo Pankhani ya Mzimu Woyera

Pali Kusiyana Maganizo Pankhani ya Mzimu Woyera

KODI mzimu woyera n’chiyani? Funsoli lingaoneke ngati lophweka, koma n’lovuta. Pankhani imeneyi, Papa Benedikito wa chi 16 anauza khamu la anthu ku Australia kuti: “Zikuoneka kuti n’zosatheka kudziwa kuti mzimu woyera n’chiyani.”

Anthu amayankha zosiyanasiyana akafunsidwa funso lakuti, Kodi mzimu woyera n’chiyani? Onani ena mwa mayankhowo:

• Mzimu woyera ndi munthu weniweni amene amakhala m’mitima mwa ophunzira a Khristu.

• Mzimu woyera ndi njira imene Mulungu amakhalira pansi pano.

• Mzimu woyera ndi munthu wachitatu pa Mulungu wa Utatu.

N’chifukwa chiyani anthu ali ndi maganizo osiyanasiyana chonchi? Kusiyana maganizo kumeneku kunayamba m’zaka za m’ma 300 C.E., akatswiri ena a zaumulungu atayamba kunena kuti mzimu woyera ndi munthu amene ali ofananako ndi Mulungu. Komabe, zimenezi n’zosiyana ndi zimene zili m’Malemba komanso zimene otsatira a Khristu oyambirira ankaphunzitsa. Buku lina linati: “Chipangano Chakale chimanena momveka bwino kuti mzimu wa Mulungu si munthu . . . Mzimu wa Mulungu ndi mphamvu ya Mulungu basi.” Buku lomweli limanenanso kuti: “Malemba ambiri m’Chipangano Chatsopano amasonyeza kuti mzimu woyera ndi chinthu chinachake, osati munthu; ndipo timaona zimenezi pa kufanana kumene kulipo pakati pa mzimu ndi mphamvu ya Mulungu.”​—New Catholic Encyclopedia.

Mpake kuti anthu amaona kuti mphamvu singakhale munthu. N’chifukwa chake kafukufuku wina waposachedwapa amene anachitika ku United States anasonyeza kuti anthu ambiri amakana mfundo yakuti mzimu woyera ndi munthu. Kodi maganizo amenewa ndi oona? Kapena kodi tiyenera kukhulupirira akatswiri a zaumulungu amene amalimbikira kunena kuti, “mzimu woyera ndi munthu payekha, wosiyana ndi Atate ndiponso Mwana”?

Kuti tipeze yankho lolondola, tiyenera kufufuza m’Mawu a Mulungu, amene amafotokoza bwino za mzimu woyera. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Mulungu adauzira Malembo onse, ndipo ndi wothandiza pophunzitsa, podzudzula, pakukonza cholakwa.”​—2 Timoteyo 3:16, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero.

N’chifukwa chiyani muyenera kuchita khama kuti mudziwe zolondola pankhani ya mzimu woyera? N’chifukwa chakuti kudziwa zolondola pankhani imeneyi kungachititse kuti Mulungu azikudalitsani. Kodi nthawi zina mumaona kuti simungathe kupirira mavuto enaake podalira mphamvu zanu zokha? Yesu analonjeza ophunzira ake kuti: “Pemphanibe, ndipo adzakupatsani; . . . Ngati inu . . . mumadziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, kuli bwanji Atate wakumwamba! Iye adzapereka mowolowa manja mzimu woyera kwa amene akum’pempha.”​—Luka 11:9, 13.

M’nkhani zotsatirazi, tiona zimene Malemba amanena zokhudza tanthauzo la mzimu woyera. Ndiponso tiona mmene mzimuwo ungatithandizire pamoyo wathu.

[Mawu Otsindika patsamba 3]

Malemba amatiuza tanthauzo la mzimu woyera