Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Akhristu Ayenera Kumenya Nawo Nkhondo?

Kodi Akhristu Ayenera Kumenya Nawo Nkhondo?

 Kodi Akhristu Ayenera Kumenya Nawo Nkhondo?

“Kodi pali lamulo lililonse la makhalidwe abwino limene limaphwanyidwa chifukwa chomenya nkhondo? N’zovuta kupeza yankho la funso limeneli.”​—Anatero, Oliver O’Donovan, pulofesa wa zikhulupiriro zachikhristu

KU Canada kuli chithunzi chimene dzina lake ndi Nsembe. Chithunzichi, n’chokhudza nkhondo yoyamba ya padziko lonse ndipo chili m’nyumba yosungira zinthu zakale zokhudza nkhondo. Pachithunzipo pali asilikali ataphedwa, asilikali ena ofooka opulumuka pankhondo, ndiponso mabanja abale a asilikaliwo ali kunyumba zawo. Chapamwamba pa chithunzichi pali Yesu Khristu atakhomedwa pamtanda. Koma anthu ena amadabwa kwambiri kuona kuti Yesu, yemwe ndi “Kalonga wa mtendere,” anajambulidwa pamodzi ndi zithunzi za nkhondo. (Yesaya 9:6) Ena chifukwa choyamikira zimene anthu a dziko lawo anachita, amaona kuti Mulungu ndi Mwana wake amafuna kuti Akhristu azimenya nkhondo n’cholinga choteteza dziko lawo kapena ufulu wawo.

Kwa zaka zambiri, atsogoleri azipembedzo akhala akulalikira zinthu zolimbikitsa nkhondo. Mwachitsanzo, m’chaka cha 417 C.E., bishopu wina wachikatolika, dzina lake Augustine, analemba kuti: “Musamaganize kuti Mulungu sasangalala ndi munthu aliyense amene ndi msilikali. . . . Anthu ena akukupemphererani pokumenyerani nkhondo yolimbana ndi Satana ndi ziwanda zake, pamene inu mukuwamenyera nkhondo yolimbana ndi adani a dziko lathu.” Ndipo m’zaka za m’ma 1200, Thomas Aquinas anafotokoza kuti “nkhondo ndi yabwino ngati cholinga chake ndi kuteteza anthu osauka ndiponso dziko lanu kwa adani.”

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi Mulungu amadalitsa anthu akamamenya nkhondo pazifukwa zooneka ngati zomveka, monga kuteteza dziko kapena anthu amene akuponderezedwa? Kodi ndi “mfundo za makhalidwe abwino” ziti zimene Akhristu angadalire pofuna kudziwa maganizo a Mulungu pankhaniyi?

Chitsanzo cha Yesu Khristu

Kodi maganizo a Mulungu ndi otani pankhani zovuta kumvetsa, monga nkhondo zamasiku ano? Mtumwi Paulo ankadziwa kuti anthu angafunikire kudziwa maganizo a Mulungu pankhani ngati zimenezi. Iye anafunsa kuti: “‘Ndani akudziwa maganizo a Yehova kuti am’langize?’ Koma ifeyo tili ndi maganizo a Khristu.” (1 Akorinto 2:16) Pofuna kutithandiza, Yehova Mulungu anatumiza Yesu padziko lino lapansi kuti atipatse chitsanzo. Zimene Yesu ankanena ndiponso kuchita zinasonyeza maganizo a Yehova. Choncho, kodi Yesu ananena chiyani pankhani ya nkhondo?

Anthu ena angaganize kuti ngati panali chifukwa chomveka kwambiri chomenyera nkhondo, chinali kuteteza Yesu Khristu. Petulo, yemwe anali mtumwi wa Yesu, ankaganizanso choncho. Yesu ataperekedwa ndiponso  kumangidwa ndi gulu la asilikali omwe anabwera pakati pausiku, Petulo “anasolola lupanga lake ndi kukantha nalo kapolo wa mkulu wa ansembe ndi kuduliratu khutu lake.” Koma kodi Petulo anali ndi chifukwa chomveka chogwiritsira ntchito chida pofuna kuteteza Yesu? Yesu anamuuza kuti: “Bwezera lupanga lako m’chimake, pakuti onse ogwira lupanga adzafa ndi lupanga.”​—Mateyo 26:47-52.

Zimene Yesu ananenazi sizodabwitsa. Zaka ziwiri m’mbuyomo zimenezi zisanachitike, iye ananena kuti: “Koma ine ndikukuuzani: Pitirizani kukonda adani anu ndi kupempherera amene akukuzunzani; kuti musonyeze kuti ndinudi ana a Atate wanu wa kumwamba, popeza kuti amawalitsira dzuwa lake pa anthu oipa ndi abwino, ndi kuvumbitsira mvula anthu olungama ndi osalungama omwe.” (Mateyo 5:43-45) Zingakhale zosamveka ngati Akhristu atamanena kuti amakonda ndiponso kupempherera adani awo koma n’kumamenyana nawonso.

Pali maumboni ambirimbiri osonyeza kuti anthu ambiri ankadana ndi Akhristu. Mwachitsanzo, Yesu Khristu anaweruzidwa ndiponso kuphedwa ndi Aroma. Patapita nthawi pang’ono, munthu ankatha kuphedwa chifukwa chongodziwika kuti ndi Mkhristu. Yesu ankadziwa kuti monga anachitira Ayuda ena, Akhristu akanatha kuukira boma lankhanza la Aroma lomwe linkawapondereza. Choncho, ponena za otsatira ake, iye anati: “Iwo sali mbali ya dziko, monganso ine sindili mbali ya dziko.” (Yohane 17:16) Akhristu anasankha kusalowerera ndale. Motero, panalibe chifukwa chomveka chakuti Akhristu amenye nkhondo ngakhale atachitiridwa zinthu zopanda chilungamo, atawopsezedwa kapena dziko lawo litaukiridwa.

Akhristu Ali Kumbali ya Ufumu wa Mulungu

Akhristu oona sankalowerera ndale monga Yesu anachitira. Taganizirani zimene zinachitika ku Ikoniyo, mzinda wa ku Asia Minor. “Amitundu ndi Ayuda pamodzi ndi olamulira awo, anakonza chiwembu kuti achitire chipongwe [Paulo ndi Baranaba] ndi kuwaponya miyala. Koma iwo atadziwitsidwa zimenezi, anathawira m’mizinda ya Lukaoniya, Lusitara, Debe, ndi m’madera ozungulira. Kumeneko anapitiriza kulengeza uthenga wabwino.” (Machitidwe 14:5-7) Onani kuti ataukiridwa, Akhristu sanamenye nkhondo podziteteza komanso sanabwezere. Koma anapitirizabe kulalikira “uthenga wabwino.” Kodi ankalalikira uthenga wabwino wa chiyani?

 Akhristu ankalalikira uthenga wofanana ndi umene Yesu ankalalikira. Iye anati: “Ndiyenera kukalengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu.” (Luka 4:43) Yesu ndi otsatira ake anali kumbali ya Ufumu wa Mulungu. Koma iye sanateteze Ufumu umenewu pogwiritsa ntchito asilikali a dziko. Iye anati: “Ufumu wanga suli mbali ya dziko lino. Ufumu wanga ukanakhala mbali ya dziko lino, atumiki anga akanamenya nkhondo kuti ndisaperekedwe kwa Ayuda. Koma tsopano ufumu wanga si wochokera pansi pano ayi.”​—Yohane 18:36.

‘Muzikondana Wina ndi Mnzake’

Panthawi ya nkhondo, olambira oona amadziwika chifukwa salowerera m’nkhondo. Yesu anati: “Mwa ichi onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukondana wina ndi mnzake.” (Yohane 13:35) Anthu ambiri amasangalala akalowa m’gulu la Akhristu amene amasonyeza chikondi chimenechi, ngakhale kuti amanyozedwa, kumangidwa ngakhalenso kuphedwa kumene chifukwa chokana kumenya nawo nkhondo.

Mu ulamuliro wa Anazi ku Ulaya, akuluakulu a boma anamanga Mboni za Yehova pafupifupi 10,000 chifukwa chokana kumenya nawo nkhondo. Mwa anthu amenewa, 3,000 anapititsidwa kundende zozunzirako anthu. Ndipo panthawi yomweyi ku America, anthu oposa 4,300 a Mboni za Yehova anamangidwa chifukwa chokana kulowa usilikali. Mboni za Yehova za ku Germany ndi ku America sizinatenge zida kukamenyana ndi Akhristu anzawo kapenanso anthu ena. Zikanakhala zosamveka kunena kuti amakonda Akhristu anzawo komanso anthu ena ngati akanamenya nawo nkhondo.

Koma anthu ambiri amaona kuti ndi bwino kumenya nkhondo podziteteza. Taganizirani mfundo iyi: Akhristu a m’nthawi ya atumwi anapulumuka ngakhale kuti sanabwezere panthawi imene ankazunzidwa mwankhanza. Ufumu wamphamvu wa Roma unalephera kuthetsa Chikhristu. Ndipo masiku ano, Akhristu oona akupitirizabe kuchuluka ndiponso kusalowerera nkhondo. M’malo mobwezera, amadalira kwambiri Mulungu kuti awathandiza. Mawu ake, Baibulo, amati: “Okondedwa, musabwezere choipa, koma siyirani malo mkwiyo wa Mulungu; pakuti Malemba amati: ‘Kubwezera ndi kwanga; ndidzawabwezera ndine, atero Yehova.’”​—Aroma 12:19.

[Bokosi patsamba 30]

NKHONDO ZIMENE MULUNGU ANADALITSA

Aisiraeli akale, mtundu umene Mulungu anausankha, nthawi zina ankaloledwa kumenya nkhondo. Asanalowe m’dziko la Kanani, lomwe Mulungu analonjeza Abulahamu, Aisiraeli anauzidwa kuti: ‘Yehova Mulungu wanu adzapereka mitundu isanu ndi iwiri pamaso panu, ndipo mukawakanthe; pamenepo muwawononge konse; musapangane nawo pangano, kapena kuwachitira chifundo.’ (Deuteronomo 7:1, 2) Choncho, Yoswa, yemwe anali mtsogoleri wa nkhondo wa Aisiraeli, anagonjetsa mitundu ya adani “monga Yehova Mulungu wa Isiraeli adalamulira.”​—Yoswa 10:40.

Kodi Aisiraeli anamenya nkhondo imeneyi chifukwa cha nkhanza ndiponso dyera? Ayi, ndithu. Mitundu imeneyi inali yoipa chifukwa inkalambira mafano, inkapha anthu ndiponso anthu ake anali achiwerewere. Komanso iwo anafika pomapereka ana awo nsembe powaotcha pamoto. (Numeri 33:52; Yeremiya 7:31) Mulungu anawononga anthu onse oipawo chifukwa chakuti iye ndi woyera, wachilungamo ndiponso amakonda anthu ake. Komabe, Yehova anasanthula mtima wa munthu wina aliyense, zimene msilikali sangachite masiku ano, ndipo anapulumutsa anthu okhawo amene anali ofunitsitsa kusiya njira zawo zoipa ndi kuyamba kumutumikira.

[Chithunzi patsamba 31]

Kodi Yesu amafuna kuti otsatira ake azimenya nkhondo pomuteteza kapena poteteza Akhristu anzawo?

[Chithunzi patsamba 31]

Mboni za Yehova zitamasulidwa ku ndende yozunzirako anthu ku Buchenwald mu 1945