Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 Phunzitsani Ana Anu

Semu Anaona Kuipa kwa Anthu Chigumula Chisanachitike Ndiponso Chitachitika

Semu Anaona Kuipa kwa Anthu Chigumula Chisanachitike Ndiponso Chitachitika

MWANA wa Nowa, dzina lake Semu, anapulumuka pamene anthu oipa anawonongedwa ndi Chigumula. Kodi ukudziwa chifukwa chake anthuwo anawonongedwa?​— * Nanga iye ndi anthu a m’banja lake anatani kuti apulumuke pamene anthuwo anawonongedwa?​— Tiye tione nkhani imeneyi.

Semu ali mwana, Baibulo limanena kuti “kuipa kwa anthu” kunali kochuluka. Anthu ankangoganiza ‘zoipa zokhazokha.’ Kodi ukudziwa zimene Mulungu anachita?​— Iye anabweretsa Chigumula chimene chinawonongeratu anthu onse oipawo. Mtumwi Petulo analemba kuti: “Dziko la panthawiyo linawonongeka pamene linamizidwa ndi madzi.”​—Genesis 6:5; 2 Petulo 3:6.

Kodi ukuona chifukwa chake Mulungu anawononga anthuwo?​— Iwo anali oipa, ndipo zimene ankaganiza zinali ‘zoipa zokhazokha.’ Yesu anatchulanso za nkhani imeneyi. Iye anati: “Chigumula chisanafike, anthu anali kudya ndi kumwa” komanso anali ‘kukwatira ndi kukwatiwa.’ Yesu anawonjezera kuti: “Sanazindikire kanthu mpaka chigumula chinafika ndi kuwaseseratu onsewo.”​—Mateyo 24:37-39.

Kodi anthuwo analephera kuzindikira chiyani?​— Nowa, yemwe anali bambo a Semu, anali “mlaliki wa chilungamo,” koma anthu sankamumvera. Nowa anamvera Mulungu ndipo anamanga chingalawa, changati sitima ya panyanja, kuti iye ndi banja lake apulumukiremo panthawi ya Chigumula. Amene ankachita zimene Mulungu ankafuna anali Nowa yekha, mkazi wake ndi ana ake, omwe ndi Semu, Hamu, ndi Yafeti ndiponso akazi awo. Koma ena onse ankangochita zimene akufuna, choncho Chigumula chinawasesa.​—2 Petulo 2:5; 1 Petulo 3:20.

Patapita pafupifupi chaka chimodzi Chigumula chitachitika, Semu ndi abale ake anatuluka m’chingalawacho. Anthu onse oipa anali atatheratu, koma pasanapite nthawi zinthu zinaipanso. Kanani, mwana wa mchimwene wake wa Semu, dzina lake Hamu, anachita zoipa kwambiri moti Nowa anati: “Wotembereredwa ndi Kanani.” Nimrode, mdzukulu wake wa Hamu, analinso woipa. Iye anatsutsana ndi Mulungu woona, Yehova, ndipo anauza anthu kuti amange nsanja yaitali, yotchedwa  Babele, kuti atchuke. Kodi ukuganiza kuti Semu ndi bambo ake anamva bwanji ndi zimenezi?​—Genesis 9:25; 10:6-10; 11:4, 5.

Iwo anakwiya, ndipo Yehova anakwiyanso. Kodi ukudziwa chimene Yehova anachita?​— Iye anasokoneza chinenero cha anthuwo kuti asamamvane. Ndiyeno anthuwo anasiya kumanga nsanjayo ndipo anapita m’madera osiyanasiyana. Anthu amene ankalankhula chinenero chimodzi anapita m’dera limodzi. (Genesis 11:6-9) Koma Mulungu sanasinthe chilankhulo cha Semu ndi abale ake. Choncho, ankakhala limodzi ndipo anatumikira Mulungu limodzi. Kodi ukudziwa kuti Semu anatumikira Yehova kwa nthawi yaitali bwanji?​—

Semu anakhala ndi moyo zaka 600. Iye anakhala zaka 98 Chigumula chisanachitike ndiponso zaka 502 Chigumulacho chitachitika. N’zosakayikitsa kuti iye anathandiza Nowa kumanga chingalawa ndiponso kuchenjeza anthu za Chigumulacho. Kodi ukuganiza kuti Semu ankachita chiyani pa zaka zoposa 500 zimene anakhala ndi moyo Chigumula chitachitika?​— Nowa anatchula Yehova kuti ndi “Mulungu wa Semu.” Choncho, Semu ayenera kuti ankatumikira Yehova ndipo ankathandiza anthu a m’banja lake kuchita zomwezo. Patapita nthawi, Abulahamu, Sara ndi Isake anadzakhala mbadwa za Semu.​—Genesis 9:26; 11:10-31; 21:1-3.

Ndiyeno taganizira dziko la masiku ano, limene laipa kwambiri kuyambira m’masiku a Semu. Kodi chidzachitikire dzikoli n’chiyani?​— Baibulo limati ‘likupita.’ Koma onanso zimene limalonjeza: “Wochita chifuniro cha Mulungu akhalabe kosatha.” Choncho, tikamachita zimene Mulungu amafuna, tingakhale m’gulu la anthu amene adzapulumuke, kulowa m’dziko latsopano limene Mulungu walonjeza. Ndiyeno, mothandizidwa ndi Mulungu, tingathe kudzakhala mosangalala kwamuyaya padziko lino lapansi.​—1 Yohane 2:17; Salmo 37:29; Yesaya 65:17.

^ ndime 3 Ngati mukuwerenga nkhaniyi ndi mwana wanu, pamene pali mzere pakusonyeza kuti muime kaye kuti mwanayo anenepo maganizo ake.