Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Anathetsa Mantha Ndiponso Mtima Wokayikira

Anathetsa Mantha Ndiponso Mtima Wokayikira

 Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo

Anathetsa Mantha Ndiponso Mtima Wokayikira

KUNJA kunali mdima, komabe Petulo anapalasa ngalawa mwamphamvu. Atayang’ana chakum’mawa, anaona kuwala koti mbuu ndipo ankaganiza kuti kunja kwayamba kucha. Apa n’kuti msana ndiponso mapewa ake zikumupweteka chifukwa chopalasa ngalawayo kwanthawi yaitali. Tsitsi lake linali lili petupetu chifukwa cha chimphepo chomwenso chinachititsa mafunde pa nyanja ya Galileya. Iye ananyowa chifukwa cha mafunde amene ankawomba kutsogolo kwa ngalawayo, komabe anapitiriza kupalasa.

Panthawiyi n’kuti Petulo ndi anzake atasiya Yesu kumtunda. Patsikuli, iwo anaona Yesu akudyetsa chikhamu cha anthu ndi mikate ingapo ndiponso tinsomba tochepa. Yesu atachita zimenezi, anthuwo anafuna kumugwira kuti amulonge ufumu, koma iye anakana. Komanso iye anayesetsa kuthandiza otsatira ake kuti asamalowerere ndale. Pothawa gulu la anthulo, Yesu anauza ophunzira ake kuti akwere ngalawa kuti apite kudera lina la nyanjayo. Ndipo iye anakwera m’phiri yekhayekha kukapemphera.​—Maliko 6:35-45; Yohane 6:14, 15.

Panthawi imene ophunzirawa ankanyamuka, mwezi unali uli pamwamba; koma tsopano unali utayamba kulowa. Ngakhale zinali choncho, iwo anali atangoyenda kamtunda kochepa chifukwa cha mafunde. Zinali zovuta kuti ophunzirawa azimvana chifukwa cha mphepo, mafunde ndiponso chifukwa chotanganidwa ndi kupalasa. N’kutheka kuti panthawiyi maganizo a Petulo anali ali kwina.

Panali zinthu zambiri zoti aganizire. Petulo anali atakhala wotsatira wa Yesu wa ku Nazarete kwa zaka zoposa ziwiri. Iye anali ataphunzira zambiri ndipo panalinso zambiri zoti aphunzire. Mtima wake wofunitsitsa kuthana ndi mantha ndiponso kukayikira, ndi chitsanzo chabwino kwambiri kwa ife. Tiyeni tione zimene tingaphunzire kwa iye.

“Ifetu Tapeza Mesiya”

Petulo ankakumbukira bwino tsiku limene anakumana koyamba ndi Yesu wa ku Nazarete. Andireya, yemwe anali mchimwene wake, ndi amene anayamba kumuuza za uthenga wochititsa chidwi kuti: “Ifetu tapeza Mesiya.” Mawu amenewa anathandiza kwambiri kuti Petulo asinthe moyo wake.​—Yohane 1:41.

Petulo ankakhala ku Kaperenao, mzinda womwe unali mphepete mwa nyanja ya Galileya. Iye ndi mchimwene wake Andireya ankagwira ntchito yosodza pamodzi ndi Yakobe ndi Yohane, omwe anali ana a Zebedayo. Petulo sankangokhala ndi mkazi wake yekha, koma ankakhalanso ndi apongozi ake ndiponso Andireya. Kuti azitha kusamalira banja lake, iye anafunika kuchita khama kwambiri pogwira ntchito yosodzayi. Tingathe kuona m’maganizo athu kuti nthawi zambiri, iye ndi anzake ankagwira ntchito mwakhama usiku wonse. Iwo ankaponya ndi kukoka khoka pogwiritsa ntchito m’ngalawa ziwiri. Kukacha, ankakhala ndi chintchito chachikulu. Ankasankha nsombazo n’kuziika m’magulu, kenako n’kuzigulitsa. Akatero ankachapa ndiponso kusoka makoka amene ang’ambika.

Baibulo limanena kuti poyamba, Andireya anali wophunzira wa Yohane Mbatizi. N’zosakayikitsa kuti Petulo anamvetsera mwachidwi pomwe mchimwene wake ankamuuza zimene Yohane ankalalikira. Tsiku lina Andireya anaona Yohane akuloza Yesu wa ku Nazarete n’kunena kuti: “Onani, Mwanawankhosa wa Mulungu!” Nthawi yomweyo Andireya anakhala wotsatira wa Yesu ndipo anakauza Petulo mosangalala za nkhani yabwinoyi kuti kwabwera Mesiya. (Yohane 1:35-40)  Patapita zaka 4,000, anthu atagalukira Mulungu m’munda wa Edene, Yehova Mulungu analonjeza kuti padzabwera munthu wapadera, amene adzathandize anthu kukhala ndi chiyembekezo chenicheni. (Genesis 3:15) Andireya anali atakumana ndi Mpulumutsi ameneyu, yemwe anali Mesiya. Choncho, Petulo nayenso anathamanga kukakumana ndi Yesu.

Kuyambira kale, Petulo ankadziwika ndi dzina lakuti Simoni kapena kuti Simeoni. Koma patsikuli, Yesu anamuyang’ana n’kumuuza kuti: “‘Iwe ndiwe Simoni mwana wa Yohane; udzatchedwa Kefa’ (dzina limene kumasulira kwake ndi Petulo).” (Yohane 1:42) Dzina lakuti “Kefa” limatanthauza “mwala” kapena “thanthwe.” Zikuoneka kuti mawu a Yesu amenewa anali ulosi. Iye anaona kuti mtsogolo Petulo angathe kudzakhala thanthwe, kutanthauza kuti angadzakhale munthu wodalirika komanso wolimbikitsa otsatira a Khristu. Komano kodi Petulo ankaona kuti angathedi kuchita zimenezi? N’zokayikitsa. Ndiponso anthu ena masiku ano amene amawerenga Mauthenga Abwino, saona kuti Petulo anali munthu wodalirika kwenikweni. Ena amati iye anali wosadalirika, wosinthasintha maganizo ndiponso wokayikakayika.

N’zoona kuti Petulo anali ndi zofooka zake ndipo Yesu ankadziwa zimenezo. Koma nthawi zonse Yesu, mofanana ndi Atate wake, Yehova, amaona zabwino mwa anthu. Ndipo Yesu anaona kuti Petulo anali ndi makhalidwe abwino, choncho anayesetsa kumuthandiza kuti akulitse makhalidwewo. Masiku anonso, Yehova ndi Mwana wake amaona zabwino mwa ife. Mwina tingakayikire kuti Yehova ndi Yesu sangapeze zabwino mwa ife. Koma tiyenera kukhulupirira zimenezi ndipo tiyenera kudzipereka kuti atiphunzitse ndiponso atiumbe ngati mmene anachitira ndi Petulo.​—1 Yohane 3:19, 20.

“Usachite Mantha”

Zikuoneka kuti Petulo anapita nawo pamaulendo ena a Yesu olalikira. Choncho, n’kutheka kuti iye anaona chozizwitsa choyamba chimene Yesu anachita, chosandutsa madzi kukhala vinyo, paphwando la ukwati umene unachitika ku Kana. Koma chofunika kwambiri n’choti Petulo anamva ulaliki wa Yesu umene unkathandiza anthu kukhala ndi chiyembekezo. Ulalikiwu unali wonena za Ufumu wa Mulungu. Komabe, iye anasiya kuyenda ndi Yesu n’kukapitiriza ntchito yake yosodza. Koma patatha miyezi ingapo, Petulo anakumananso ndi Yesu ndipo nthawi imeneyi Yesu anamupempha kuti akhale wotsatira wake nthawi zonse.

Petulo anali atagwira ntchito usiku wonse. Iye ndi anzake anali ataponya maukonde awo mobwerezabwereza koma osapha nsomba ngakhale imodzi. N’zosakayikitsa kuti Petulo anayesetsa mwaluso kwambiri kuti aphe nsomba. Anayesa kuponya maukonde m’malo osiyanasiyana panyanjayo, omwe ankaganiza kuti mungakhale nsomba zambiri. Zikatere, asodzi ankalakalaka atangolowa m’madzimo kuti akakusire nsomba mu ukonde. Mwinanso Petulo panthawiyi ankaganiza zimenezi. Koma maganizo amenewa ankangowonjezera nkhawa zimene anali nazo. Petulo sankagwira ntchitoyi pongofuna kusangalala, koma ankasodza chifukwa anthu ena ankadalira iyeyo. Komabe, pamapeto pake iye anabwerera chimanjamanja. Ngakhale zinali choncho, iye anafunika kuchapa makokawo. N’chifukwa chake Yesu anam’peza akuchapa makoka.

Yesu anazunguliridwa ndi chikhamu cha anthu omwe ankamvetsera mwachidwi zimene ankaphunzitsa. Chifukwa cha gulu la anthulo, Yesu analowa m’ngalawa ya Petulo, n’kumuuza kuti aisunthire m’madzi pang’ono. Kenako Yesu anayamba kuphunzitsa anthuwo ndipo gulu lonselo linkamumva bwinobwino. Mofanana ndi anthu ena onse, Petulo ankamvetsera mwachidwi kwambiri. Iye sanatope kumvetsera ulaliki wa Yesu, womwe mfundo yake yaikulu inali Ufumu wa Mulungu.  Choncho, unali mwayi waukulu kwambiri kugwira ntchito yolalikira uthenga umenewu limodzi ndi Khristu. Koma kodi iye akanakwanitsa kugwira nawo ntchito imeneyi? Kodi akanatani kuti athe kusamalira banja lake? Mwina Petulo anaganiziranso za usikuwo popeza anangogwira ntchito koma osapha kanthu.​—Luka 5:1-3.

Yesu atamaliza kulankhula, anauza Petulo kuti: “Palasira kwakuya, muponye maukonde anu kuti muphe nsomba.” Koma Petulo anakayikira kwambiri, choncho iye anauza Yesu kuti: “Mlangizi, ife tagwira ntchito usiku wonse koma osapha kalikonse, koma popeza inu mwanena, ndiponya maukondewa.” N’zosakayikitsa kuti Petulo sankafuna n’komwe kuponyeranso maukondewo m’madzi, makamaka panthawiyi chifukwa nsomba sizinkadyera. Komabe iye anamvera mawu a Yesu, n’kuitana anzake omwe anali m’ngalawa ina kuti amutsatire.​—Luka 5:4, 5.

Pokoka maukondewo, Petulo anadabwa kumva kuti akulemera. Iye anakoka kwambiri ndipo posakhalitsa anangoona nsomba zambirimbiri zikuphiriphitha mu ukondemo. Mwamsanga iye anakodola anzake omwe anali m’ngalawa ina aja kuti adzamuthandize. Atabwera, anaika nsomba m’ngalawa zonsezo koma sizinakwane. Ndipo chifukwa cha kulemera kwa nsombazo, ngalawazo zinayamba kumira. Petulo anadabwa kwambiri ndi zimenezi. Iye anali ataona Khristu akuchita zozizwitsa kwa anthu ena, koma chozizwitsa chimenechi chinali chapadera, chifukwa chinakhudza kwambiri iyeyo. Ndithudi, Yesu ankatha ngakhale kulamula nsomba kulowa mu ukonde. Zimenezi zinamuchititsa mantha kwambiri Petulo. Ndipo anagwada n’kuuza Yesu kuti: “Mundichokere pano Ambuye, chifukwa ine ndine munthu wochimwa.” Iye ankaona kuti sangathe kuyandikana ndi munthu amene ankasonyeza mphamvu za Mulungu m’njira imeneyo.​—Luka 5:6-9.

Mokoma mtima, Yesu anamuuza kuti: “Usachite mantha. Kuyambira lero uzisodza anthu amoyo.” (Luka 5:10, 11) Choncho, imeneyi sinali nthawi yoti azikayika kapena kuchita mantha. Petulo sanafunike kuda nkhawa kuti ndani azisamalira banja lake ngati iye atasiya ntchito yake yosodza. Ndipo sanafunikenso kuopa kuti anali ndi zofooka ndiponso kuti panali zinthu zimene sangathe kuchita. Iye ankatumikira Mulungu amene ‘amakhululukira koposa.’ (Yesaya 55:7) Yesu anali ndi ntchito yaikulu yoti achite, ndipo ntchito imeneyi inali yokhudza kwambiri tsogolo la anthu. Choncho, Yehova akanatha kuwapatsa zinthu zimene amafunika pamoyo wawo watsiku ndi tsiku ndiponso pamoyo wawo wauzimu.​—Mateyo 6:33.

Nthawi yomweyo, Petulo anamvera mawu a Yesu monga anachitiranso Yakobe ndi Yohane. Baibulo limanena kuti: “Anabwerako nakochezanso ngalawazo, ndipo iwo anasiya chilichonse ndi  kumutsatira.” (Luka 5:11) Petulo anakhulupirira Yesu komanso Mulungu. Apatu Petulo anasankha bwino kwambiri. Masiku ano, Akhristu amasonyezanso chikhulupiriro akamathana ndi mantha ndiponso mtima wokayika n’cholinga choti atumikire Mulungu. Ndipo iwo salakwitsa kuchita zimenezi.​—Salmo 22:4, 5.

“N’chifukwa Chiyani Wakayikira?”

Patatha zaka ziwiri atakumana ndi Yesu, usiku wina kunja kuli chimphepo, Petulo anapalasa ngalawa panyanja ya Galileya monga mmene tafotokozera kumayambiriro kwa nkhani ino. N’zoona kuti sitingadziwe kuti panthawiyi iye ankaganiza chiyani. Koma panali zambiri zoti aziganizire. Yesu anali atangochiritsa apongozi ake a Petulo ndiponso anali atalalikira pa ulaliki wake wapaphiri. Komanso, Yesu anasonyeza kambirimbiri kuti anali wosankhidwa wa Yehova ndiponso Mesiya, polalikira ndiponso pochita zozizwitsa. Patapita miyezi, zofooka za Petulo, monga mantha komanso mtima wokonda kukayika, zinali zitachepa. Ndipotu Yesu anasankha Petuloyo kuti akhale mmodzi wa ophunzira ake 12. Komabe, Petulo anali asanasiyiretu kukayikira ndiponso kuchita mantha.

Usiku umenewu, paulonda wachinayi kapena kuti chapakati pa 3:00 koloko m’mawa ndi nthawi yotuluka dzuwa, mwadzidzidzi Petulo anasiya kupalasa ngalawayo n’kukhala tsonga. Anaona chinthu chikuyenda chakumene kumachokera mafunde. Popeza kunja kunali mwezi, kodi chimayendacho chinali mafunde omwe amawala? Ayi, popeza chinthucho chinali choimirira. Anali munthu amene ankayenda pamwamba pa madzipo. Munthuyo atayandikira pafupi, anaoneka ngati akubwera kutsogolo kwenikweni kwa ngalawayo. Choncho, ophunzirawo anachita mantha ndipo anaganiza kuti ndi mzukwa. Ndipo munthuyo anati: “Limbani mtima, ndine; musachite mantha.” Munthuyo anali Yesu.​—Mateyo 14:25-28.

Petulo anayankha kuti: “Ambuye, ngati ndinudi, ndiuzeni ndiyende pamadzipa ndibwere kuli inuko.” Poyamba iye anasonyeza kulimba mtima. Pochita chidwi kuti Yesu akuyenda pamadzi, Petulo anafuna kulimbitsa chikhulupiriro chake. Choncho iye anafuna kuti nayenso ayende pamadzi ndipo mokoma mtima Yesu anamuitana. Petulo anatsika m’ngalawayo n’kuyamba kuyenda pamadzi. Tangoganizirani mmene Petulo anamvera ataona kuti waima bwinobwino pamadzipo. Akupita chakumene kunali Yesu, Petulo ayenera kuti anadabwa kwambiri kuona kuti akuyendadi pamadzipo. Koma posapita nthawi, iye anayamba kukayika ndiponso kuchita mantha.​—Mateyo 14:29.

Petulo anafunika kupitiriza kuyang’anitsitsa ndiponso kudalira Yesu chifukwa mwa mphamvu ya Yehova, anam’thandiza kuyenda panyanjapo. Ndipo Yesu anachita zimenezi chifukwa choti Petulo  anasonyeza chikhulupiriro. Komabe, Petulo anasokonezeka ndi zinthu zina. Timawerenga kuti: “Poona mphepo yamkuntho, anachita mantha.” Iye ataona mafunde akuomba ngalawayo, anachita mantha kwambiri. Ayenera kuti ankaganiza kuti amira n’kufera m’nyanjayo. Mantha akewo atakula, chikhulupiriro chake chinachepa. Munthu amene anatchedwa Thanthwe chifukwa cha kulimba mtima uja, anayamba kumira chifukwa chosowa chikhulupiriro. Petulo ankadziwa kusambira, koma panthawiyi sanadalirenso luso limeneli. Iye anakuwa kuti: “Ambuye, ndipulumutseni!” Yesu anam’gwira dzanja n’kumuvuula. Kenako, ali pamadzi pomwepo, Yesu anaphunzitsa Petulo phunziro lofunika kwambiri. Iye anati: “Wachikhulupiriro chochepa iwe, n’chifukwa chiyani wakayikira?”​—Mateyo 14:30, 31.

Mawu akuti “wakayikira” ndi oyeneradi kwambiri. Mtima wokayikira ndi woipa kwambiri chifukwa tikaulekerera umayamba kuwononga chikhulupiriro chathu. Choncho, tiyenera kuyesetsa kuti tithetse mtima umenewu. Koma kodi tingauthetse bwanji? Tiyenera kuganizira zinthu zoyenera chifukwa tingapitirizebe kukayikira ngati timangoganizira zinthu zimene zimatidetsa nkhawa, zimatikhumudwitsa ndiponso zimene zimatidodometsa potumikira Yehova ndi Mwana wake. Koma chikhulupiriro chathu chidzalimba ngati timaganizira za Yehova ndi Mwana wake, zimene iwo achita, zimene akuchita panopo, komanso zimene adzachitire anthu amene amakonda Mulungu.

Petulo akupita ndi Yesu kukakwera ngalawayo, anaona kuti chimphepo chija chatha ndipo panyanja ponsepo pali bata. Petulo ndi ophunzira anzakewo ananena kuti, “Ndinudi Mwana wa Mulungu.” (Mateyo 14:33) Kunja kutayamba kucha, Petulo ayenera kuti anasangalala kwambiri. Iye anaphunzira kuti sayenera kulola mtima wokayikira ndiponso mantha kumulepheretsa kukhulupirira Yehova ndi Yesu. N’zoona kuti iye anafunika kusintha zinthu zambiri kuti akhale Mkhristu wolimba ngati thanthwe, amene Yesu analosera. Komabe, iye anatsimikiza mtima kuyesetsa komanso kupitirizabe kulimbitsa chikhulupiriro chake. Kodi inunso mwatsimikiza mtima kuchita zimenezi? Ndithudi, tiyenera kutsanzira chikhulupiriro cha Petulo.

[Chithunzi pamasamba 22, 23]

Yesu anaona kuti m’tsogolo, msodzi wodzichepetsa uyu angadzakhale munthu wabwino kwambiri

[Chithunzi patsamba 23]

“Ambuye. . . ine ndine munthu wochimwa”

[Chithunzi pamasamba  24, 25]

“Poona mphepo yamkuntho, anachita mantha”