Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Mulungu wa Chitonthozo Chonse”

“Mulungu wa Chitonthozo Chonse”

Yandikirani Mulungu

“Mulungu wa Chitonthozo Chonse”

2 Akorinto 1:3, 4

ANTHUFE timakumana ndi mavuto ambiri m’moyo monga kuzunzika, kukhumudwa ndiponso kusungulumwa. Tikakumana ndi zimenezi timada nkhawa komanso kutaya mtima. Ndiye zikatero timadzifunsa kuti, ‘Kodi ndigwire mtengo wanji?’ Mawu a Mtumwi Paulo opezeka pa 2 Akorinto 1:3, 4 amatiuza kuti Yehova Mulungu yekha ndi amene angathe kutitonthoza.

Pa vesi 3 Mulungu akutchedwa kuti “Tate wa chifundo chachikulu.” Kodi mawu amenewa amatanthauza chiyani? Mawu a Chigiriki amene anamasuliridwa kuti “chifundo chachikulu” angatanthauze kukhudzidwa mtima anthu ena akamavutika. * Buku lina lofotokoza mawu a m’Baibulo limati mawuwa tingawalembenso kuti “amamva chisoni” kapena kuti “amakonda kwambiri anthu.” Chifukwa chakuti Mulungu ndi wa chifundo chachikulu, amathandiza anthu pamavuto. Kudziwa khalidwe la Mulungu limeneli kumachititsa kuti timukonde kwambiri.

Paulo ananenanso kuti Yehova ndi “Mulungu wa chitonthozo chonse.” Buku lina linati mawu a Paulo palembali amatanthauzanso “kulimbikitsa, kutonthoza, kapena kupereka thandizo kwa munthu amene ali pa mavuto kapena pa chisoni.” Bukulo linapitiriza kuti “Munthu akamavutika timamutonthoza pomulimbitsa mtima kuti apirire mavuto akewo.”​—The Interpreter’s Bible.

Koma mwina mungafunse kuti, ‘Kodi Mulungu amatitonthoza ndi kutilimbikitsa motani?’ Amatero makamaka pogwiritsa ntchito Mawu ake Baibulo komanso pemphero, lomwe ndi mphatso yomwe iye anatipatsa. Paulo ananena kuti Mulungu anatipatsa Mawu ake mwachikondi pofuna kuti “mwa chitonthozo cha m’Malemba tikhale ndi chiyembekezo.” Kuwonjezera pamenepo tikamapemphera mochokera pansi pamtima tingathe kupeza “mtendere wa Mulungu wopambana luntha lonse la kulingalira.”​—Aroma 15:4; Afilipi 4:7.

Kodi Yehova amatonthoza anthu ake pa zinthu zotani? Paulo ananena kuti Mulungu “amatitonthoza m’masautso athu onse.” (2 Akorinto 1:4) Kaya tikhale pa mavuto kapena masautso otani Mulungu angathe kutilimbitsa mtima ndi kutipatsa mphamvu kuti tithe kupirira. Kodi zimenezi si zolimbikitsa?

Munthu akalimbikitsidwa ndi Mulungu nayenso amalimbikitsa ena. Paulo anapitiriza kunena kuti Mulungu amatitonthoza n’cholinga choti “tikathe kutonthoza amene ali m’masautso a mtundu uliwonse mwa chitonthozo chimene nafenso Mulungu akutitonthoza nacho.” Tikatonthozedwa pa nthawi imene tili pa masautso timaphunzira kumvera ena chifundo motero timayamba kuwathandiza pa mavuto awo.

N’zoona kuti Yehova ndi “Mulungu wa chitonthozo chonse” koma si kuti amatichotsera mavuto athu onse. Komabe tisakayike ngakhale pang’ono kuti tikamupempha kuti atitonthoze, iye angatithandize kuti tithe kupirira mavuto ndiponso masautso onse pamoyo wathu. Mulungu wa chifundo chotere ndi woyeneradi kuti tizimulambira ndi kumutamanda.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Mulungu amatchedwa “Tate [kapena kuti magwero] a chifundo chachikulu,” chifukwa choti iye ndi amene anayambitsa khalidwe la chifundo ndipo ndi mbali ya umunthu wake.