Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Ganizirani Mapeto Ake

Ganizirani Mapeto Ake

 Ganizirani Mapeto Ake

MOYO uli ngati ulendo. Pamoyo wathu wonse timayenera kusankha njira zambirimbiri. Ndipotu ndi chinthu chanzeru kudziwa mapeto a njira iliyonse imene tikufuna kusankha. Anthu ena anong’onezapo bondo chifukwa cha zimene anasankha. N’kutheka kuti inunso munadandaulapo kuti, ‘Ndikanadziwa sindikanayerekeza n’komwe kuchita zimenezi.’

Munthu wanzeru amafuna kudziwa kumene njira imene akuyenda ikulowera. Angathe kuona pa mapu kapenanso kufunsa anthu amene akudziwa deralo. Komanso sangalephere kuyang’ana zikwangwani za mumsewuwo. Komano kodi tingadziwe bwanji njira yabwino pa moyo wathu? Ponena za Aisiraeli, panthawi ina Mulungu ananena mawu otsatirawa kudzera mwa Mose: “Akadakhala nazo nzeru, akadazindikira ichi, akadasamalira chitsirizo chawo!”​—Deuteronomo 32:29.

Malangizo Abwino Kwambiri

Palibe chifukwa chokayikira kuti “chitsiriziro” cha ulendo wa moyo wathu chidzakhala chotani. Poti Mulungu amatha kuona patali, iye yekha ndi amene angathe kulangiza anthu za njira yabwino kwambiri imene angayende pa moyo wawo. Iye waona njira zambiri zimene anthu akhala akuyendamo ndipo wakhala akuonanso mapeto a njirazo. Baibulo limati: “Njira za munthu zili pamaso pa Yehova, asinkhasinkha za mayendedwe ake onse.”​—Miyambo 5:21.

Yehova amaganizira kwambiri anthu amene amamukonda. Kudzera m’Mawu ake, Baibulo, iye amawasonyeza njira yabwino kwambiri. Baibulo limati: “Ine ndidzakulangiza ndi kuphunzitsa  iwe za njira ukayendayo; ndidzakupangira ndi diso langa lakuyang’ana iwe.” Motero musanayambe n’komwe kuyenda pa njira iliyonse, n’kwanzeru kufunsira malangizo a Yehova, monga anachitira Davide, yemwe anali Mfumu ya Isiraeli. Iye anapemphera kuti: “Mundidziwitse njira ndiyendemo.”​—Salmo 32:8; 143:8.

Munthu akamayenda m’njira imene wauzidwa ndi munthu wina wodalirika amene akuidziwa bwino, amayenda mosakayika ndipo sachita mantha. Sada nkhawa kuti njirayo ikathera kuti. Davide anapempha Yehova kuti amulangize za njira yotereyi ndipo anaitsatira. Motero anali wokhazikika maganizo kwambiri monga mmene anasonyezera m’Salmo lotchuka zedi la nambala 23. Davide analemba kuti: “Yehova ndiye m’busa wanga; sindidzasowa. Andigonetsa ku busa lamsipu: Anditsogolera ku madzi odikha. Atsitsimutsa moyo wanga; anditsogolera m’mabande a chilungamo, chifukwa cha dzina lake. Inde, ndingakhale ndiyenda m’chigwa cha mthunzi wa imfa, sindidzaopa choipa.”​—Salmo 23:1-4.

Kodi Tsogolo Lawo N’lotani?

Munthu wina yemwe anayenera kusankha njira pa moyo wake anali wamasalmo. N’kutheka kuti wamasalmo ameneyu anali Asafu kapena mmodzi wa ana ake, iye anati “akadaterereka” n’kuchoka m’njira yoyenera. N’chiyani chinachititsa zimenezi? Iye anaona kuti anthu osaona mtima ndiponso achiwawa, zinthu zikuwayendera kwambiri ndipo anayamba kuchita nsanje poona “mtendere wa oipa.” Ankaona kuti moyo wa anthuwa ndi ‘wokhazikika.’ Ndiyeno wamasalmoyu anafika pokayikira kuti mwina sichinthu chanzeru kutsatira njira yachilungamo.​—Salmo 73:2, 3, 6, 12, 13.

Kenaka wamasalmoyo analowa m’kachisi wa Yehova n’kuyamba kupemphera ndi kuganizira za mapeto a anthu oipa. Iye anafuna “kulingalira chitsiriziro chawo.” Anasinkhasinkha za tsogolo la anthu amene ankawachitira nsanjewo. Ndiye kodi anazindikira kuti tsogolo lawo linali lotani? Anazindikira kuti anthu otere anali “poterera” ndipo ‘adzathedwa ndi zoopsa.’ Nanga anazindikira kuti njira imene iye anasankha mapeto ake anali otani? Iye anati: “Mutatero, mudzandilandira mu ulemerero.”​—Salmo 73:17-19, 24.

Kuganizira mapeto a zochita za anthu amene amayenda njira zachidule kapena zosayenera pofuna kuti zinthu ziziwayendera bwino, kunam’thandiza wamasalmoyu kuona kuti iye anali pa njira yoyenera. Motero anafika ponena kuti: “Koma ine, kundikomera kuyandikiza kwa Mulungu.” Inde, nthawi zonse kuyandikira kwa Yehova Mulungu kumatipatsa madalitso osatha.​—Salmo 73:28.

Dziwani Kumene Mukulowera

Nafenso tingakumane ndi zoterezi. Mwina mungapatsidwe mwayi wa ntchito inayake ya ndalama zambiri, mwayi wokwezedwa pantchito, kapena mwayi woti muchite nawo bizinesi inayake yopindulitsa kwambiri. Tikudziwa kuti nthawi zonse zinthu zikamayamba kumene  sizidziwika kuti ziyenda bwanji. Komabe ndi bwino kuganizira “chitsiriziro,” kapena kuti mapeto a zinthuzo. Dzifunseni kuti, ‘Kodi mapeto a zonsezi angakhale otani? Kodi ndidzafunika kumachoka panyumba kwa nthawi yaitali, n’kumasiya mkazi kapena mwamuna wanga ali yekhayekha? Kodi nthawi zambiri ndizikhala ku hotela kapena malo ena n’kumagwira ntchito ndi anthu osaopa Mulungu?’ Mukamayang’ana m’tsogolo mwa njira imene mukufuna kutsatira, mungathe kusankha mwanzeru. Tsatirani malangizo a Solomo akuti: “Dziwani kumene mukulowera.”​—Miyambo 4:26, Baibulo la Contemporary English Version.

Tonsefe, makamaka achinyamata, tiyenera kuganizira bwino malangizo amenewa. Mnyamata wina anabwereka filimu imene ankadziwa kuti muli zinthu zina zopatsa munthu chilakolako chofuna kugonana. Ataonera filimuyo akuti chilakolako chake chinakula kwambiri moti anakatenga hule linalake limene linkakhala chapafupi. Iye akuti mapeto ake anakhumudwa kwambiri, chikumbumtima chinkam’pweteka, ndipo anali ndi nkhawa kuti mwina watenga matenda. Zimene zinam’chitikirazi n’zogwirizana ndendende ndi zimene zinafotokozedwa m’Baibulo, zakuti: “Mnyamatayo am’tsata posachedwa, monga ng’ombe ipita kukaphedwa.” Akanaganizira kaye “chitsiriziro chake” sakanayerekeza n’komwe kuchita zimenezi.​—Miyambo 7:22, 23.

 Tsatirani Zikwangwani

Anthu ambiri amavomereza kuti sichinthu chanzeru kunyalanyaza zikwangwani. Koma n’zomvetsa chisoni kuti zimenezi n’zimene anthu ambiri amachita akaona kuti chikwangwani cha pa njira ya ku moyo chikutsutsana ndi zofuna zawo. Taganizirani chitsanzo cha Aisiraeli ena a m’nthawi ya Yeremiya. Panthawiyi Aisiraeli anayenera kusankha chochita, ndipo Yehova Mulungu anawalangiza kuti: “Funsani za mayendedwe akale, mmenemo muli njira yabwino, muyende mmenemo.” Koma anthuwo anachita makani ponena kuti “sitidzayendamo.” (Yeremiya 6:16) Kodi mapeto a kupanduka kumeneku anali otani? Mu 607 B.C.E., Ababulo anabwera n’kuwonongeratu mzinda wa Yerusalemu ndipo anagwira anthuwo kuti akakhale akapolo ku Babulo.

Kunyalanyaza zikwangwani zimene Mulungu waika kumapweteketsa nthawi zonse. Malemba amatilimbikitsa kuti: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; um’lemekeze m’njira zako zonse, ndipo Iye adzawongola mayendedwe ako.”​—Miyambo 3:5, 6.

Zikwangwani zina zimene Mulungu waika zili ndi machenjezo monga akuti “Musalowe.” Mwachitsanzo, Baibulo limati: ‘Usalowe m’mayendedwe ochimwa, usayende m’njira ya oipa.’ (Miyambo 4:14) Njira imodzi yoipa ndi imene imafotokozedwa pa Miyambo 5:3, 4, kuti: “Pakuti milomo ya mkazi wachiwerewere ikukha uchi; m’kamwa mwake muti see koposa mafuta. Chimaliziro chake n’chowawa ngati chivumulo, ndi chakuthwa ngati lupanga lakuthwa konsekonse.” Anthu ena angaone kuti kuchita chiwerewere ndi hule kapena munthu wina aliyense n’kosangalatsa. Komatu nthawi zonse kunyalanyaza chikwangwani chakuti “Musalowe” m’makhalidwe oipa kumalowetsa munthu m’mavuto.

Musanalowe m’njira imeneyi, dzifunseni kuti, ‘Kodi njira iyi ikupita kuti?’ Kuyamba mwaganizira kaye pang’ono za “chitsiriziro chake” kungakuthandizeni kupewa kuchita zinthu zimene zingakulowetseni m’mavuto. Njira yonse ya anthu amene amanyalanyaza zikwangwani zoterezi ndi yodzaza ndi mavuto monga Edzi, matenda osiyanasiyana opatsirana pogonana, kutenga mimba zapathengo, kutaya mimba, kutha kwa mabanja, kapena kudana ndi anthu ena ndiponso kuvutika ndi chikumbumtima. Mtumwi Paulo anafotokoza momveka bwino za mapeto a njira ya anthu amene amachita zachiwerewere. Iye anati “sadzalowa mu ufumu wa Mulungu.”​—1 Akorinto 6:9, 10.

“Njira Ndi Iyi”

Nthawi zina zimavuta kuona kumene njira inayake imene tatenga ikukathera. N’chifukwa chake timathokoza Mulungu akamatipatsa malangizo omveka bwino. Yehova anati: “Njira ndi iyi, yendani inu mmenemo.” (Yesaya 30:21) Kodi njira imene Yehova akutilozera imakathera kuti? Ngakhale kuti njira yake ndi yopapatiza ndiponso yovuta kuyendamo, Yesu anati imakafika ku moyo wosatha.​—Mateyo 7:14.

Taganizirani pang’ono za njira imene mukuyenda panopo. Kodi ndi njira yoyenera? Kodi ikulowera kuti? Pempherani kwa Yehova kuti akutsogolereni. Onani malangizo a m’Baibulo, omwe ali ngati mapu a ulendowu. Mwinanso mungaone kuti ndi bwino kufunsa munthu wina wodziwa bwino za ulendo woterewu, yemwe akuyesetsa kuyenda m’njira ya Mulungu. Ndiye mukaona kuti m’pofunika kusintha njira yanuyo, teroni mwamsanga.

Nthawi zambiri munthu amene akuyenda ulendo amalimba mtima akaona chikwangwani chosonyeza kuti ali mumsewu woyenera. Ngati mwaona kuti njira imene mukuyendamo panopo ndi yoyenera, musabwerere m’mbuyo chifukwa mwatsala pang’ono kupeza madalitso osaneneka omwe ali pamapeto pa ulendowu.​—2 Petulo 3:13.

Njira iliyonse imene munthu akuyendamo imakhala ndi kothera. Ndiye kodi njira imene mukuyendamo panopo ikakufikitsani kuti? Dziwani kuti mukakafika pamene njirayo imathera n’zosatheka kubwerera koma muzikangodandaula kuti, ‘N’kanadziwa n’kanasankha njira ina.’ Choncho musanasapitirize kuyenda m’njira imene mukuyendamo panopo, dzifunseni kuti, ‘Kodi “chitsiriziro,” kapena kuti mapeto a njira imeneyi ndi otani?’

[Bokosi/​Zithunzi patsamba 10]

Kodi Mapeto Ake Ndi Otani?

Nthawi zambiri achinyamata amayesedwa ndiponso amakakamizidwa kuchita nawo zinazake zimene anzawo ambiri akuchita. Zina mwa zinthuzo ndi izi.

Mnzanu angakuuzeni kuti musute fodya kuti musaoneke ngati wopusa.

Mphunzitsi amene amakukondani angakulimbikitseni kuti mukachite maphunziro apamwamba kuyunivesite.

Mungaitanidwe ku phwando kumene anthu akaledzere ndiponso mwina kugwiritsira ntchito mankhwala osokoneza bongo.

Munthu wina angakuuzeni kuti muike zinthu zonse zokhudza moyo wathu pa Intaneti kuti anthu akudziweni.

Mnzanu angakuitaneni kuti mukaonere filimu yosonyeza zachiwawa kapena zachiwerewere.

Kodi mungatani ngati zoterezi zitakuchitikirani? Kodi mungangololera, kapena mungaganizire mosamala za “chitsiriziro chake”? Mungachite bwino kudzifunsa kuti: “Kodi mwamuna angatenge moto pa chifuwa chake, osatentha zovala zake? Pena kodi mwamuna angayende pa makala oyaka, osapsa mapazi ake?”​—Miyambo 6:27, 28.