Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Mukakafika pa Mtsinje wa Coco, Mukakhotere Kumanja”

“Mukakafika pa Mtsinje wa Coco, Mukakhotere Kumanja”

 Kalata Yochokera ku Nicaragua

“Mukakafika pa Mtsinje wa Coco, Mukakhotere Kumanja”

“MUTENGE galimoto yamphamvu yoti ingayende m’matope, chingwe choikokera ngati itatitimira m’matope, komanso musaiwale kutenga zigubu za mafuta. Mudziwe kuti mukadutsa m’matope ambiri. Mukakafika pa mtsinje wa Coco, mukakhotere kumanja.”

Mawu a m’mishonale mnzangawa sanandithandize kuchepetsa mantha amene ndinali nawo. Komabe, Lachiwiri m’mawa ndinauyamba ulendo wopita ku msonkhano waukulu wachikhristu womwe unachitikira ku tawuni yaing’ono yotchedwa Wamblán kumpoto kwa Nicaragua.

Dzuwa lisanatuluke ndinayamba ulendowu pa galimoto yanga yomwe inali yakale koma yamphamvu ndipo ndinadzera mu msewu waukulu bwino wa ku America wotchedwa Pan-American Highway. Nditafika pa tawuni yotchedwa Jinotega ndinatenga msewu wafumbi umene anthu a kumeneko amautcha kuti msewu wa feo, kutanthauza kuti msewu woipa kwambiri. M’tawuni imeneyi ndinaona masitolo awiri. Yoyamba inalembedwa kuti “Chozizwitsa cha Mulungu” ndipo yachiwiri inalembedwa kuti “Kuuka kwa Akufa.”

Msewu wake unali wokhotakhota komanso wa zitunda ndi mitsetse. M’maphedi ndinkangoyendetsa pang’onopang’ono. Ndinadutsa mphepete mwa nyanja ina yaitali yomwe inali m’chigwa cha phiri lina. Phirilo linakutidwa ndi mitambo pamwamba pake. Ngakhale kuti kunachita nkhungu, ndinkatha kuona mitengo ina yoyangidwa ndi ndere komanso maluwa.

Pamalo ena, msewu unangokhota mwadzidzidzi moti ndinatsala pang’ono kuwombana ndi basi ina imene inkayenda pakati pa msewu. Basiyo inkatulutsa utsi wambiri ndipo matayala ake ankaponya miyala podutsana nayo. M’dziko la Nicaragua si zachilendo kuona madalaivala olusa atalemba mayina ongodzipatsa m’mawindo a mabasi awo. Ena ankalemba kuti “Amunamuna,” “Chinkhanira,” “Nsato,” kapena “Cham’tchire.”

Mmene nthawi imakwana 12 koloko masana ndinali ndikudutsa m’chigwa cha Pantasma. M’dera limeneli ndinadutsa nyumba ina yamatabwa ndipo panja pake panali posesa bwino kwambiri ndipo inkangooneka ngati chithunzi chokongola. Panyumbapo panali bambo wachikulire atakhala pa benchi. Pambali pake panali galu atagona pansi pa mtengo ndipo cha poteropo panali ng’ombe ziwiri zomwe anazimangirira ku ngolo ya matayala a matabwa. Nditafika m’tawuni ina ndinaona gulu la ana akuweruka ku sukulu. Anavala mayunifolomu a buluu ndipo anangoti mbwee mumsewu.

Dzuwa linayamba kutentha kwambiri pamene ndinafika ku tawuni yotchedwa Wiwilí. Apa m’pamene ndinayamba kuona mtsinje waukulu wa Coco. Madzi a mtsinjewu ankaonekera patali kwambiri. Pokumbukira malangizo amene anandipatsa aja ndinakhotera kumanja ndipo ndinatenga msewu woopsa kwambiri wopita ku tawuni ya Wamblán. Ulendo wotsalawo unali wautali makilomita 37.

Msewuwo unali wa mabampu komanso mayenje ndipo tinawoloka mitsinje 8 kapena 9. Ndinayesetsa kuzemba mabampuwo koma fumbi lokha ndiye linali losapeweka. Malinga ndi mmene anthu a kuno amanenera,  fumbi ndinalibwiradi. Kenako ndinafika ku Wamblán, dera lomwe dzuwa silioneka chifukwa cha kuchuluka kwa mitengo. Ulendo wanga unathera pamenepa.

M’tawuni imeneyi, zikuoneka kuti aliyense anali atadzuka kale mmene nthawi imakwana 4:30 m’mawa. Ineyo tulo tinandithera msanga chifukwa cha kulira kwa atambala moti ndinangodzuka n’kukawongola miyendo mumsewu waukulu wa kumeneko. Kafungo ka mikate imene inali kuphikidwa m’mauvuni kanangoti ngandee m’dera lonselo.

Makoma a nyumba zambiri anali ndi zithunzi zokongola zosonyeza paradaiso zojambulidwa ndi akatswiri a kumeneko. M’masitolo ambiri munali mawu ndi zithunzi zochemerera zakumwa zosiyanasiyana zoziziritsa kukhosi. M’malo ambiri munalinso zikwangwani zakale zosonyeza zinthu zimene zipani zitatu zomwe zinalamulirapo dzikoli zinali kulonjeza panthawiyo. Kunalinso zimbuzi za malata zokhala ndi masilabu pansi pake.

Nditakumana ndi anthu ndinayamba kuwapatsa moni m’chilankhulo cha ku Nicaragua ponena kuti “Adiyosi.” Ndikatero anthu ankamwetulira n’kuyamba kundilankhula mosangalala. Tinkalankhula mokweza kwambiri chifukwa cha phokoso la mahatchi ndi abulu amene ankadutsa chapafupi.

Pofika Lachisanu madzulo, pa malo amsonkhano wa masiku awiriwo, panali patafika mabanja ambirimbiri. Ena anabwera wapansi, ena pa hatchi ndipo ena anayenda pa galimoto. Panali anyamata ndi atsikana ena amene anayenda maola 6 atavala masandasi a pulasitiki. M’malo owolokera mitsinje yambiri munakwiriridwa mabomba komanso munali misundu yambiri, yomwe ndi nyongolotsi zoyamwa magazi. Komabe iwo analimba mtima n’kudutsa. Anthu ambiri ochokera kutali sanatenge chakudya chambiri, koma anangotenga mpunga wothira mafuta a nkhumba. Kodi n’chifukwa chiyani anayenda ulendowu?

Iwo anabwera kudzalimbikitsidwa kuti apitirize kuyembekezera tsogolo labwino, kudzamva mfundo za m’Baibulo zikufotokozedwa momveka bwino, komanso anafuna kudzasangalatsa Mulungu.

Tsiku Loweruka litafika tinasonkhana pa malo ena amene anafoleredwa ndi malata. Anthu oposa 300 anakhala m’mabenchi a matabwa ndipo ena anakhala pa mipando ya pulasitiki. Azimayi ena ankayamwitsa ana awo. Chapafupi panali famu ina ndipo kunkamveka kulira kwa nkhumba ndi tiatambala.

Kenako kunayamba kutentha kwambiri. Komabe anthu ankamvetsera mwachidwi nkhani za malangizo osiyanasiyana zimene zinkakambidwa. Wokamba nkhani akatchula lemba iwo ankatsegula Mabaibulo awo n’kumawerenga. Ankaimba nyimbo zokhala ndi mfundo zochokera m’Baibulo ndipo ankamvetsera mwatcheru mapemphero amene ankaperekedwa.

Chigawo cha msonkhano chikatha ndinkasewera chipako ndi ana. Kenako ndinayamba kukambirana nawo mfundo zimene analemba pamsonkhanopo. Pambuyo pake, ndinayamba kuwasonyeza zithunzi za nyenyezi ndi milalang’amba pa kompyuta. Anawa ndiponso makolo awo anasangalala kwambiri.

Msonkhanowo tinauona kufulumira kwambiri. Komabe utatha aliyense anabwerera kwawo. Tsiku lotsatira ndinauyamba ulendo wobwerera kwathu. Ndinali wosangalala kwambiri pokumbukira zinthu zosangalatsa zimene zinachitika komanso ndinkangoganizira za anthu amene ndinadziwana nawo kumeneku. Anthu amenewa ndinachita nawo chidwi kwambiri moti ndikufuna kutsanzira mtima wawo wosalira zinthu zambiri pamoyo komanso womadalira kwambiri Mulungu.

[Zithunzi patsamba 17]

Mabanja ambiri anayenda ulendo wautali kuti akapezeke pa msonkhano wa ku Wamblán