Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Matenda a Dzikoli Ndi Ochiritsika?

Kodi Matenda a Dzikoli Ndi Ochiritsika?

 Kodi Matenda a Dzikoli Ndi Ochiritsika?

KUTENTHA kwa dzikoli ndi chizindikiro chakuti likudwala. Chitsanzo cha zimenezi ndi tawuni ya mphepete mwa nyanja ya Newtok ku Alaska, yomwe ili kudera lozizira kwambiri. Tawuniyi inamangidwa pa madzi oundana koma panopo madziwo ayamba kusungunuka. Munthu wina dzina lake Frank yemwe amakhala m’tawuniyi anati: “Sindikufunanso kukhala kuno. Chifukwa panopo kumangokhala matope okhaokha.” Ofufuza akuti tawuni imeneyi ingathe kukokoloka pasanathe zaka 10.

Bungwe lina la zanyengo linati: “N’zosachita kufunsa kuti padziko pano payamba kutentha kwambiri.” Asayansi akuti kusintha kwa nyengo kumeneku n’kumene kukubweretsa padziko lonse mavuto monga zilala, mvula yamphamvu, mpweya wotentha kwambiri, ndi mphepo ya mkuntho. Kodi n’chiyani chidzachitikire dzikoli? Kodi pali njira yochizira matenda a dzikoli?​—Intergovernmental Panel on Climate Change (IPCC).

Kupeza Vuto Lake

Dzikoli likudwala matenda akayakaya ndipo asayansi ya zanyengo ali ngati madokotala amene akupima matendawo. Asayansiwa amagwiritsira ntchito zinthu monga makina a mlengalenga pounika madzi oundana amene akusungunuka, malo a zanyengo poona mmene mvula ikugwera, zipangizo za panyanja poyeza kutentha kwa madzi m’nyanja, ndiponso amagwiritsira ntchito ndege poyeza mpweya wa mlengalenga. Akapeza zinthu zokhudza nyengo zonsezi amazilemba m’makopyuta awo apamwamba. Akatero makompyutawo amawasonyeza mmene zinthu zidzakhalire m’zaka 10 kapena 100 zikubwerazo.

Kodi apeza kuti vuto la dzikoli n’chiyani? Akatswiri ena akuti m’mlengalenga mwadzaza mpweya woipa. Magazini ina inati m’chaka cha 2006 chokha, m’mlengalenga munali mpweya wochuluka woterewu “wokwana matani 32 biliyoni.” (Time) Mpweya umenewu ukuchititsa kuti dziko lizingotukutira. Kodi nanga tsogolo  la dzikoli ndi lotani? Bungwe la IPCC linati, zinthu zikapanda kusintha, mpweya woipawu udzachititsa kuti “nyengo isinthe kwambiri padziko lonse” kuposa kale lonse. Anthu ambiri tsopano akuona kuti njira yothetsera vutoli ndiyo kuchepetsa utsi umene umapita m’mlengalenga. Komabe, ngakhale mpweya umenewu utachepetsedwa, makompyuta a akatswiri a zanyengo akusonyeza kuti “kutentha kwa dziko ndi kusungunuka kwa madzi oundana kudzapitirizabe kwa zaka zambiri.”

Kodi Tingapeze Kuti Thandizo?

Sayansi ya zanyengo si yophweka. Mwachitsanzo magazini ina inafunsa kuti, “Kodi n’chiyani chimachitikira mitambo kukatentha? Kodi mitambo imene imatenthetsa dzikoli imachuluka kuposa imene imaliziziritsa?” Magaziniyo inanena kuti “Pakalipano a sayansi sangathe kuyankha mafunsowa.”​—Earth Observatory.

Koma Baibulo limatiuza kuti Yehova Mulungu ndiye “mwini kumwamba ndi dziko lapansi” komanso “thambo la kumwamba.” (Genesis 14:19; Miyambo 8:28) Iye anafotokoza mwandakatulo kuti “analonga nzeru m’mitambo.” Inde, zimene asayansi sangamvetse Yehova amazimvetsa bwinobwino.​—Yobu 38:36

Taonani zimene Mulungu ananena zokhudza mlengalenga, zomwe zinalembedwa m’Baibulo zaka 2,700 zapitazo. “Mvula imagwa pansi . . . kuchokera kumwamba yosabwerera komweko, koma ikhamiza nthaka.” (Yesaya 55:10) Awatu ndi mawu achidule kwambiri ofotokoza kayendedwe ka madzi. Madzi amapita m’mlengalenga monga nthunzi ndipo amakaundana n’kupanga mitambo kenako n’kugwa monga mvula imene ‘imakhamiza nthaka.’ Kutentha kwa dzuwa kumachititsa kuti madzi asanduke nthunzi n’kubwereranso kumwamba “komweko,” kuti akaundane n’kugwanso ngati mvula. Mabuku a zanyengo asanalembedwe n’komwe, Mawu a Yehova anali atafotokoza kale za mmene madzi amayendera padziko lapansi pano. Kodi zimenezi sizikukuchititsani kuti muyambe kumukhulupirira kwambiri Mlengiyo? Ndiyeno pankhani ya matenda a dzikoli n’zoonekeratu kuti tiyenera kudalira ‘amene analenga mphepo,’ yemwenso ‘anabala mvula.’ Iyeyo ndi amene amadziwa mmene dzikoli limayendera.​—Amosi 4:13; Yobu 38:28.

Dziko Linalengedwa N’cholinga

Inde anthu sagwirizana chimodzi pankhani ya tsogolo la dzikoli, koma mfundo yosatsutsika ndi yakuti: Dzikoli linapangidwa modabwitsa. Mosiyana ndi mapulaneti ena, dziko lapansi lili ndi zamoyo zosiyanasiyana. Kodi n’chiyani chimachititsa kuti padzikoli pakhale zamoyo? Asayansi amapereka zifukwa zosiyanasiyana. Mwa zina iwo amati, dzikoli lili ndi madzi ambiri, linatalikirana bwino ndi dzuwa, komanso lili ndi mlingo woyenerera wa mpweya wosiyanasiyana womwe zamoyo zimapuma.

Mwina mungadabwe kudziwa kuti Baibulo  limatchula zinthu zimenezi m’nkhani ya kulengedwa kwa zinthu. Mwachitsanzo, pofotokoza za kuchuluka kwa madzi padzikoli, lemba la Genesis 1:10 limati, Mulungu anasonkhanitsa pamodzi “madzi n’kuwatcha kuti nyanja.” Ndipo lemba la Genesis 1:3 limati: “Ndipo anati Mulungu, Kuyere.” Dzikoli linatalikirana bwino ndi dzuwa kuti madzi ambiri asamaundane, komanso kuti asamasanduke nthunzi.

Lemba la Genesis 1:6 limati Mulungu anapanga “thambo,” kapena kuti mlengalenga. Kenako pavesi 11 ndi 12 pamati Mulungu anameretsa udzu, mbewu ndi mitengo. Zonsezi zikusonyeza kuti panali mpweya umene anthu ndi nyama zimapuma.

Choncho, kodi zimenezi zikutisonyeza chiyani? Zikutisonyeza kuti Mulungu anali ndi cholinga polenga dziko lapansi kuti likhale ndi madzi ambiri osaundana, litalikirane bwino ndi dzuwa komanso likhale ndi mlingo woyenerera wa mitundu yosiyanasiyana ya mpweya. Baibulo limati: ‘Mulungu sanalilenga mwachabe; Iye analiumba akhalemo anthu.’ (Yesaya 45:18) Lemba la Salmo 115:16 limati: “Kunena za kumwamba, kumwamba ndiko kwa Yehova; koma dziko lapansi analipereka kwa ana a anthu.” Inde, dziko linalengedwa kuti anthu azikhalamo.

Malemba amasonyeza kuti Mulungu analenga anthu awiri oyambirira n’kuwaika m’paradaiso wokongola, wotchedwa munda wa Edene. Iye anawauza kuti “aulime nauyang’anire.” (Genesis 2:15) Mulungu anawauzanso kuti: “Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse.” (Genesis 1:28) Tangoganizirani mmene tsogolo lawo likanakhalira. Iwo akanafutukula mundawo moti dziko lonse likanadzakhala Paradaiso ndipo akanakhala mmenemo kosatha. Ilitu linali tsogolo labwino kwambiri.

Koma n’zomvetsa chisoni kuti iwo sanamvere Mulungu, m’malo mwake anam’pandukira, monga achitiranso anthu ambiri masiku ano. (Genesis 3:1-6) Kodi zimenezi zabweretsa mavuto otani? M’malo molima ndi kusamalira dziko, anthu “akuwononga dziko” kwambiri kuposa kale lonse. (Chivumbulutso 11:18) Komabe n’zolimbikitsa kudziwa kuti cholinga cha Mulungu chokhudza dziko lapansi sichinasinthe. Baibulo limatiuza kuti: “[Mulungu] anakhazika dziko lapansi pa maziko ake, silidzagwedezeka ku nthawi yonse.” (Salmo 104:5) Ndipo paulaliki wa paphiri, Yesu analonjeza kuti: “Osangalala ali iwo amene ali ofatsa, popeza adzalandira dziko lapansi.” (Mateyo 5:5) Kodi zimenezi zidzatheka bwanji?

Tikuyembekezera Tsogolo Labwino

Pulezidenti wina wakale wa dziko la United States anati “vuto la kusintha kwa zanyengo ndi lapadziko lonse.” Choncho mungaone kuti vutoli n’lofunika kulithetsa padziko lonse. Yesu Khristu ananena kuti Ufumu wa Mulungu ndi umene ungathetse vutoli. Iye analangiza anthu om’tsatira kuti azipemphera kuti: “Ufumu wanu ubwere.” (Mateyo 6:9,10) Malingana ndi ulosi wa m’Baibulo, Ufumu wa kumwamba umenewu ndi boma la padziko lonse  limene posachedwa ‘lidzaphwanye ndi kutha maufumu awo onse,’ kapena kuti maboma onse amene alipo masiku anowa. (Danieli 2:44) Chinanso n’chakuti ufumuwo ‘udzawononga iwo owononga dziko lapansi.’ (Chivumbulutso 11:18) Pamenepa n’zoonekeratu kuti anthu amene akuwononga dziko ndi chilengedwe chake adzaimbidwa mlandu n’kuwonongedwa.

Nanga poti dzikoli aliwononga kale, ndiye lidzakonzedwa bwanji? Kumbukirani kuti Yesu ali padziko lapansi anachita zozizwitsa pa zinthu zachilengedwe, monga mphepo ndi nyanja. Iye anatonthoza mafunde ndi mawu basi. (Maliko 4:35-41) Motero akamadzalamulira ali kumwamba monga “Mbuye wa ambuye ndi Mfumu ya mafumu,” Yesu adzakhala ndi mphamvu zochuluka zedi pa zochitika za dzikoli, ngakhalenso pa zanyengo. (Chivumbulutso 17:14) Kwenikweni, Yesu anati ulamuliro wakewu udzakhala “nthawi ya kukonzanso zinthu.” (Mateyo 19:28) Yesu adzakonzanso zinthu padziko pano kuti zikhale mmene zinalili m’munda wa Edene. Paradaiso adzabwezeretsedwa. (Luka 23:43) Ufumu wa Mulungu udzachiza matenda amene dziko likudwala.

Ngakhale panopo, mungathe kupindula ndi ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu. Kodi mungapindule motani? Yesu analosera kuti: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukakhale umboni ku mitundu yonse.” (Mateyo 24:14) Chifukwa cha zimenezi, anthu ambiri akumva uthenga wabwino n’kusintha moyo wawo. Akusiya zizolowezi zawo zoopsa. Mabanja awo akuyamba kuyenda bwino. Anthu a mafuko amene ankadana ayamba kukondana. Ndipotu Ufumu wa Mulungu ukuchita zinthu zimene palibe boma lililonse la anthu limene lingazikwanitse. Ufumuwu wagwirizanitsa pafupifupi anthu 7 miliyoni ochokera m’mayiko oposa 235 kuti akhale pa ubale weniweni wa padziko lonse. Inde, poti anthu onsewa akulamulidwa ndi Ufumu wa Mulungu, zimene akuchitazi zikuwathandiza kukonzekera moyo wosatha m’Paradaiso padziko lapansi pano.

Dzikoli lilidi ndi tsogolo labwino. Nanunso yesetsani kuti tsogolo lanu likhale labwino.

[Chithunzi patsamba 27]

Mabuku a zanyengo asanalembedwe n’komwe, Baibulo linali litafotokoza kale za mmene madzi amayendera padziko lapansi pano

[Chithunzi patsamba 28]

Yesu ‘anadzudzula mphepo ndi kuuza nyanja kuti: “Leka! Khala bata!” Ndipo mphepoyo inaleka, kenako panagwa bata lalikulu ndithu’

[Chithunzi patsamba 29]

Paradaiso akadzabwezeretsedwa dzikoli lidzachira

[Mawu a Chithunzi patsamba 26]

Godo-Foto