Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Iye Sali Kutali ndi Aliyense wa Ife”

“Iye Sali Kutali ndi Aliyense wa Ife”

Yandikirani Mulungu

“Iye Sali Kutali ndi Aliyense wa Ife”

Machitidwe 17:24-27

CHILENGEDWE chonsechi ndi chachikulu kwambiri moti sitingachiyerekezere n’komwe ndi anthufe. Mwina munadzifunsapo kuti, ‘Kodi n’zothekadi kuti munthu akhale paubwenzi ndi Mulungu yemwe Wamphamvuyonse?’ Zimenezi zingatheke pokhapokha ngati Mulungu, yemwe dzina lake ndi Yehova, wafuna kuti timuyandikire. Koma kodi iye amafunadi kuti titero? Yankho lolimbikitsa tingalipeze m’mawu a pa Machitidwe 17:24-27, amene mtumwi Paulo analankhula kwa anthu ophunzira kwambiri a ku Atene. Taonani zinthu zinayi zokhudza Yehova zimene Paulo anatchula.

Choyamba, Paulo ananena kuti Mulungu “anapanga dzikoli ndi zinthu zonse zili mmenemu.” (Vesi 24) Zinthu zokongola ndiponso zosiyanasiyana zimene zimapangitsa moyo kukhala wosangalatsa, zimapereka umboni wakuti Mlengi wathu amatiganizira ndiponso amatikonda. (Aroma 1:20) Kungakhale kupanda nzeru kuganiza kuti Mulungu wamakhalidwe oterewa angasankhe kuti anthu amene anawalenga chifukwa cha chikondi chake asam’dziwe.

Chachiwiri, Yehova “amapatsa anthu onse moyo, mpweya, ndi zinthu zonse.” (Vesi 25) Yehova ndi Wochirikiza moyo. (Salmo 36:9) Zinthu zofunika kwambiri pamoyo, monga mpweya, madzi ndi chakudya, ndi mphatso zochokera kwa Mlengi wathu. (Yakobe 1:17) Ndiye kodi zingakhale zomveka kukhulupirira kuti Mulungu, yemwe ndi wopatsa, angadzibise kuti tisam’dziwe ndiponso kuti tisakhale naye paubwenzi?

Chachitatu, “kuchokera mwa munthu mmodzi [Mulungu] anapanga mtundu wonse wa anthu.” (Vesi 26) Yehova ndi wopanda tsankho m’pang’ono pomwe. (Machitidwe 10:34) Ndiyeno kodi iye angachite bwanji zinthu zosemphana ndi khalidwe limeneli? Mulungu analenga “munthu mmodzi,” amene ndi Adamu, ndipo iye ndi kholo la anthu amitundu yonse. “Chifuniro [cha Mulungu] n’chakuti anthu, kaya akhale a mtundu wotani, apulumuke.” (1 Timoteyo 2:4) Motero tonsefe, mosaganizira za mtundu kapena fuko lathu, tili ndi mwayi wokhala naye paubwenzi.

Chachinayi, Paulo anafotokoza mfundo yolimbikitsa kwambiri yakuti: Yehova “sali kutali ndi aliyense wa ife.” (Vesi 27) Ngakhale kuti Yehova ndi wokwezeka kwambiri, munthu amene akufunitsitsa kukhala naye paubwenzi angathe kum’fikira nthawi iliyonse. Mawu ake amatitsimikizira kuti iye sali kutali, koma “ali pafupi ndi onse akuitanira kwa Iye.”​—Salmo 145:18.

Malinga ndi zimene Paulo ananenazi, n’zoonekeratu kuti Mulungu amafuna kuti timuyandikire. Komabe, iye amalola kuyandikirana ndi anthu okhawo omwe ‘akum’funafuna’ ndi ‘kum’papasa.’ (Vesi 27) Buku lina lothandiza anthu omasulira Baibulo limati, “mawu awiri onsewa akuoneka kuti akufotokoza za chinthu chomwe n’chotheka kuchipeza . . . kapena chinthu chomwe munthu angachifune n’kuchipezadi.” Tifanizire motere: M’chipinda chomwe munachizolowera koma muli mdima, mungapapasire chitseko kapena poyatsira magetsi koma mukudziwiratu kuti mupeza chitsekocho kapena poyatsira magetsipo. N’chimodzimodzinso ndi kufunafuna Mulungu ndiponso kum’papasa. Sitiyenera kukayikira kuti khama lathulo lipindula. Paulo anatitsimikizira kuti ‘tidzam’pezadi’ Mulunguyo.​—Vesi 27.

Kodi inuyo mumalakalaka kukhala paubwenzi ndi Mulungu? Ngati muli ndi chikhulupiriro n’kuyamba ‘kufunafuna Mulungu’ ndi ‘kum’papasa,’ simudzanong’oneza bondo. Yehova si wovuta kum’peza, chifukwa chakuti “iye sali kutali ndi aliyense wa ife.”