Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kupirira Panthawi Yachisoni

Kupirira Panthawi Yachisoni

Kupirira Panthawi Yachisoni

‘Ana [a Yakobo] onse aamuna ndi aakazi anauka kuti am’tonthoze: Koma anakana kutonthozedwa; ndipo anati, Pakuti ndidzatsikira kumanda kwa mwana wanga, ndikulirabe. Atate wake ndipo anam’lirira.’​—Genesis 37:35.

YAKOBO anamva chisoni kwambiri atauzidwa kuti mwana wake wamwalira. Iye anaona kuti chisoni chakecho sichidzatha mpaka imfa yake. Mofanana ndi Yakobo, mwina nanunso mungaganize kuti chisoni chachikulu chimene muli nacho chifukwa cha imfa ya munthu amene mumam’konda sichidzatha. Kodi munthu akakhala ndi chisoni chachikulu ndiye kuti alibe chikhulupiriro mwa Mulungu? Ayi, si choncho.

Baibulo limasonyeza kuti Yakobo anali ndi chikhulupiriro cholimba kwambiri. Iye anatchulidwa pamodzi ndi anthu amene anali ndi chikhulupiriro cholimba zedi, monga Abulahamu, yemwe anali agogo ake, komanso Isaki, yemwe anali abambo ake. (Aheberi 11:8, 9, 13) Ndipo panthawi ina, iye analimbana ndi mngelo usiku wonse kuti am’patse madalitso ochokera kwa Mulungu. (Genesis 32:24-30) N’zoonekeratu kuti Yakobo anali paubwenzi wolimba ndi Mulungu. Ndiyeno, kodi tingaphunzirepo chiyani pa chisoni chimene Yakobo anali nacho? Kukhala ndi chisoni chachikulu sikutanthauza kuti munthu alibe chikhulupiriro cholimba mwa Mulungu. N’kwachibadwa ndiponso sikulakwa kumva chisoni munthu amene timam’konda akamwalira.

Kumva Chisoni

Timakhudzidwa ndi chisoni m’njira zosiyanasiyana, koma kwa ambirife, timamva ululu mumtima. Mwachitsanzo, taonani zimene zinachitikira mnyamata wina dzina lake Leonardo. Bambo ake anamwalira ndi matenda a mtima ndi mapapo, iye ali ndi zaka 14. Leonardo amakumbukirabe tsiku limene amayi ake aang’ono anamuuza za imfayo ndipo atangomuuza, iye sanakhulupirire. Ngakhale kuti anaona mtembo wa bambo akewo pamwambo wamaliro, iye sanakhulupirirebe. Panadutsa miyezi 6 Leonardo asanayambebe kukhulupirira zimenezi, ndipo nthawi zambiri ankadikirira bambo akewo poganiza kuti abwera kuchokera kuntchito. Panatha chaka chathunthu kuti iye avomereze zoti bambo akewo anamwaliradi. Ndipo zitatero, anayamba kumva kuti ali yekhayekha. Iye ankaganizira kwambiri za bambo akewo akafika kunyumba n’kupeza kuti kulibe wina aliyense. Kawirikawiri panthawi ngati zimenezi Leonardo ankangolira basi.

Nkhani ya mnyamata ameneyu ikusonyeza bwino kuti nthawi zina tingakhale ndi chisoni kwambiri. Komabe, chosangalatsa n’choti ndi zotheka kupirira panthawi yachisoni ngakhale kuti zingatenge nthawi yaitali. Mofanana ndi mmene bala lalikulu lingatengere nthawi yaitali kuti lipole, chisoni chimatenganso nthawi yaitali kuti chithe. Pangapite miyezi kapena zaka zingapo, mwinanso zochuluka ndithu kuti chisoni chithe. Koma ululu waukulu womwe mungamve masiku oyambirira amene muli pachisoni ungachepe, mwina kutha kumene m’kupita kwa nthawi.

Anthu amati chisoni ndi njira yabwino yothandiza kuti munthu aphunzire ndiponso azolowere zinthu zikasintha chifukwa cha imfa ya munthu amene anali kum’konda. Ndipo kukhala ndi chisoni ndi njira yabwino yosonyezera mmene mukumvera. N’zoona kuti anthufe sitisonyeza chisoni m’njira yofanana. Komabe palibe amene angatsutse mfundo iyi: Kudzilimbitsa kuti musasonyeze chisoni kungakusokonezeni maganizo kwambiri ndiponso kungakudwalitseni. Ndiyeno, kodi mungatani kuti musonyeze chisoni m’njira yoyenera? Baibulo lili ndi malangizo odalirika pankhani imeneyi. *

Kodi Mungatani Kuti Mupirire Panthawi Yachisoni?

Anthu ambiri amene anali ndi chisoni aona kuti kuuzako ena mmene munthu ukumvera n’kothandiza zedi. Mwachitsanzo, taonani zimene Yobu ananena ana ake onse 10 atafa ndiponso iye atakumana ndi mavuto ena ambiri. Iye anati: “Mtima wanga ulema nawo moyo wanga, ndidzadzilolera kudandaula kwanga, ndidzalankhula pakuwawa mtima wanga.” (Yobu 1:2, 18, 19; 10:1) Onani kuti palembali, Yobu ananena kuti “ndidzalankhula pakuwawa mtima wanga.” Zimenezi zikusonyeza kuti iye ankauza ena mmene anali kumvera.

Paulo, yemwe mayi ake anamwalira, ananena kuti: “Chimodzi mwa zinthu zimene zandithandiza ndicho kuuzako anthu ena za mayi anga.” Motero, kuuza mnzanu wapamtima mmene mukumvera kungachepetse chisoni chanu. (Miyambo 17:17) Mayi a Yone atamwalira, iye anapempha kuti abale ake achikhristu azimuyendera pafupipafupi. Iye anati: “Kulankhula ndi ena kunathandiza kuti chisoni changa chichepe.” Mwina nanunso mungapirire mosavuta ngati mungafotokozere munthu wina wodalirika mmene mukumvera.

Njira ina imene ingakuthandizeni ndiyo kulemba. Anthu ena amene amalephera kunena mmene akumvera, mwina sangavutike kulemba zimene zili mu mtima mwawo. Mwachitsanzo, Sauli ndi Jonatani atamwalira, Davide yemwe anali munthu wokhulupirika analemba nyimbo imene anafotokozamo za chisoni chake. Nyimbo imeneyi inadzakhala mbali ya buku la m’Baibulo la Samueli Wachiwiri.​—2 Samueli 1:17-27.

Kulira ndi njira inanso yothandiza. Baibulo limati: “Kanthu kalikonse kali ndi nthawi yake . . . [ngakhalenso] mphindi ya kulira.” (Mlaliki 3:1, 4) Kunena zoona, munthu amene mumam’konda akamwalira, imakhaladi “mphindi ya kulira.” Motero palibe chilichonse chochititsa manyazi ndi kulira. M’Baibulo muli zitsanzo zambiri za amuna ndi akazi okhulupirika amene analira chifukwa cha chisoni. (Genesis 23:2; 2 Samueli 1:11, 12) Yesu Khristu “anagwetsa misozi” atayandikira pa manda a Lazaro, yemwe anali mnzake.​—Yohane 11:33, 35.

Pamafunika kudekha kuti mupirire panthawi yachisoni chifukwa chakuti pangatenge nthawi yaitali kuti maganizo anu akhazikike. Ndipo kumbukirani kuti kulira si chinthu chochititsa manyazi. Anthu ambiri okhulupirika aona kuti kulira akakhala pa chisoni sikulakwa ndipo kumawathandiza kwambiri kuti apirire.

Yandikirani Mulungu

Baibulo limatiuza kuti: “Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.” (Yakobe 4:8) Njira imodzi imene ingakuthandizeni kuti muyandikire Mulungu ndiyo pemphero. Baibulo limatilonjeza kuti: “Yehova ali pafupi ndi iwo a mtima wosweka, apulumutsa iwo a mzimu wolapadi.” (Salmo 34:18) Ndiponso limatitsimikizira kuti: “Um’senze Yehova nkhawa zako, ndipo Iye adzakugwiriziza.” (Salmo 55:22) Ndiyeno taganizirani izi: Monga mmene taonera, anthu ambiri aona kuti n’zothandiza kuuzako munthu wina wodalirika mmene iwo akumvera. Mulungu akulonjeza kuti adzatilimbikitsa. Motero, kodi sizingakhale zothandiza kwambiri kumuuza mmene tikumvera?​—2 Atesalonika 2:16, 17.

Paulo, amene tam’tchula kale uja anati: “Ndikaona kuti zandivuta kupirira, ndinkangogwada pansi n’kupemphera kwa Mulungu kuti andithandize.” Paulo akukhulupirira kuti mapempherowo anam’thandiza. Inunso mudzaona kuti chifukwa cha kupemphera kwanu mwakhama, “Mulungu wa chitonthozo chonse” adzakulimbikitsani ndi kukupatsani mphamvu kuti mupirire.​—2 Akorinto 1:3, 4; Aroma 12:12.

Chiyembekezo cha Kuuka kwa Akufa

Yesu anati: “Ine ndine kuuka ndi moyo. Aliyense wokhulupirira mwa ine, ngakhale amwalire, adzakhalanso ndi moyo.” (Yohane 11:25) Baibulo limaphunzitsa kuti anthu akufa adzauka. * Pamene Yesu anali padziko lapansi, anasonyeza kuti angathe kuukitsa akufa. Panthawi ina, iye anaukitsa mtsikana wa zaka 12. Kodi makolo a mtsikanayo anamva bwanji ndi zimenezi? Iwo “anasangalala kwadzaoneni.” (Maliko 5:42) Mu ulamuliro wa Ufumu wake, Yesu Khristu yemwe ndi Mfumu yakumwamba, adzaukitsa anthu osawerengeka kuti akhale ndi moyo padziko lapansi lamtendere ndi chilungamo. (Machitidwe 24:15; 2 Petulo 3:13) Tangoganizani chisangalalo chimene chidzakhalapo pamene anthu adzauka n’kukumananso ndi abale ndiponso anansi awo.

Claudete, yemwe mwana wake Renato anafa pangozi ya ndege uja, anaika chithunzi cha mwana wakeyo pafiriji. Iye amaona chithunzicho kawirikawiri, ndipo mumtima mwake amati, ‘Tidzaonananso akadzaukitsidwa.’ Nayenso Leonardo amayerekezera akuona bambo ake ataukitsidwa m’dziko latsopano limene Mulungu walonjeza. N’zoona, anthu ambiri amene abale ndi anansi awo anamwalira amalimbikitsidwa kwambiri podziwa kuti akufa adzauka. Zimenezi zingakuthandizeninso inuyo.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 8 Kuti mumve zimene mungachite pothandiza ana omwe ali ndi chisoni chifukwa cha imfa ya munthu amene anali kum’konda, onani nkhani yakuti “Kuthandiza Mwana Wanu Panthawi Yachisoni,” patsamba 18 mpaka 20 m’magazini ino.

^ ndime 19 Kuti mumve zambiri pa zimene Baibulo limanena pankhani ya kuuka kwa akufa, onani mutu 7 wa buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 7]

“Mulungu wa Chitonthozo Chonse”

“Adalitsike Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Tate wa chifundo chachikulu ndi Mulungu wa chitonthozo chonse.”​—2 Akorinto 1:3.

Vesi limeneli likusonyeza kuti Mulungu akhoza kuthandiza atumiki ake okhulupirika kuti apirire mavuto alionse amene angakumane nawo. Njira imodzi imene Yehova angatitonthozere kapena kuti kutilimbikitsa ndiyo kudzera mwa anzathu amene tili nawo m’chipembedzo chimodzi.

Leonardo, yemwe bambo ake anamwalira uja, amakumbukira zimene zinam’thandiza ndiponso kumulimbikitsa. Tsiku lina atangofika kunyumba, n’kukumbukira kuti kulibe aliyense, anayamba kulira kwambiri. Ndiyeno anapita ku paki ina yapafupi ndi kumene ankakhala. Iye anakhala pa benchi n’kumapitiriza kulira. Ali mkati molira, anapemphera kwa Mulungu kuti am’thandize. Mwadzidzidzi, galimoto ina inaima chapafupi, ndipo Leonardo anazindikira kuti amene amayendetsa galimotoyo ndi m’bale wake wachikhristu. M’baleyo anali pa ntchito yake yosiya katundu kwa makasitomala ake m’malo osiyanasiyana ndipo panthawiyi anali atasochera. Leonardo analimbikitsidwa kwambiri kulankhula ndi m’baleyo panthawiyi.

Panthawi ina, bambo wina amene mkazi wake anamwalira ankaona kuti ali yekhayekha ndiponso anasokonezeka maganizo kwambiri. Iye ankaona kuti pamoyo wake palibe chilichonse chimene chingakhalenso bwino, moti ankangolira. Bamboyu anapemphera kwa Mulungu ndi mtima wonse ndipo ali mkati mopemphera, foni yake inalira. Yemwe anaimba foniyo anali mdzukulu wake. Bamboyu anati: “Zimene tinakambirana panthawi imeneyi zinandilimbikitsa kwambiri ngakhale kuti tinacheza kwa nthawi yochepa. Ndinaona kuti pemphero langa layankhidwa.”

[Bokosi patsamba 9]

Kulimbikitsa Anthu Ena

“[Mulungu] amatitonthoza m’masautso athu onse, kuti tikathe kutonthoza amene ali m’masautso a mtundu uliwonse mwa chitonthozo chimene nafenso Mulungu akutitonthoza nacho.”​—2 Akorinto 1:4.

Akhristu oona ambiri angavomereze kuti mawu amenewa amakwaniritsidwa. Popeza iwo anatonthozedwapo kapena kuti kulimbikitsidwa mnzawo kapena wachibale wawo atamwalira, nawonso amatha kulimbikitsa ena.

Taonani chitsanzo cha Claudete uja, yemwe amakonda kuyendera anthu ndi kuwafotokozera mfundo za m’Baibulo zimene iye amakhulupirira. Mwana wake uja asanamwalire, Claudete ankakonda kuchezera mayi wina yemwe mwana wake anamwalira ndi matenda a khansa ya m’magazi. Mayiyo ankasangalala kucheza naye, koma ankaganiza kuti Claudete sakumvetsa mmene imfa ya mwana wakeyo inam’khudzira. Koma patangopita nthawi yochepa mwana wa Claudete atamwalira, mayi uja anapita ku nyumba kwa Claudete n’kumuuza kuti akufuna kudzaona ngati iye akukhulupirirabe Mulungu ngakhale kuti mwana wake wamwalira. Atachita chidwi ndi chikhulupiriro cholimba cha Claudete, mayiyo anayamba kuphunzira Baibulo nthawi zonse ndi Claudete ndipo akulimbikitsidwa kwambiri ndi Mawu a Mulungu.

Bambo ake atamwalira, Leonardo anaganiza zophunzira chinenero chamanja n’cholinga choti azilalikira uthenga wolimbikitsa wa m’Baibulo kwa anthu ogontha. Ndipo iye waona kuti zimene akuchita polimbikitsa anthu ogontha zam’thandiza kwambiri. Iye anati: “Chimodzi mwa zinthu zimene zandithandiza kupirira panthawi yachisoni ndi mtima wanga wofuna kuthandiza anthu ogontha kuti aphunzire za Mulungu. Ndimadzipereka kwambiri pothandiza anthu amenewa. Chisoni changa chonse chinatheratu pamene ndinaona munthu woyamba yemwe ndinkaphunzira naye Baibulo akubatizidwa. Kunena zoona, iyi inali nthawi yoyamba imene ndinasangalala kwambiri kuchokera pamene bambo anga anamwalira.”​—Machitidwe 20:35.

[Chithunzi patsamba 5]

Kuuzako ena mmene mukumvera kungakuthandizeni kuti chisoni chanu chichepe

[Chithunzi patsamba 6]

Kulemba mmene mukumvera kungakuthandizeni kufotokoza mosavuta maganizo anu

[Chithunzi patsamba 6]

Kuwerenga nkhani zokhudza chiyembekezo cha kuuka kwa akufa kungakulimbikitseni kwambiri

[Chithunzi pamasamba 8, 9]

Yesu analonjeza kuti anthu amene amam’khulupirira adzauka