Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Mboni za Yehova Sizimenya Nawo Nkhondo?

N’chifukwa Chiyani Mboni za Yehova Sizimenya Nawo Nkhondo?

 Zimene Owerenga Amafunsa

N’chifukwa Chiyani Mboni za Yehova Sizimenya Nawo Nkhondo?

Kuyambira kale kwambiri Mboni za Yehova padziko lonse zimadziwika kuti sizimenya nawo nkhondo, kaya ikhale ya pakati pa mayiko kapena ya pachiweniweni. Zaka 50 zapitazo buku lina linati: “Mboni za Yehova sizimenya nawo nkhondo ngakhale pang’ono.”​—Australian Encyclopædia.

Chifukwa chachikulu chimene Mboni za Yehova sizimenyera nawo nkhondo n’chakuti sizifuna kuchita zinthu zosemphana ndi chikumbumtima chawo. Mboni za Yehova zili ndi chikumbumtima chimene chimatsatira malamulo ndiponso chitsanzo cha Ambuye Yesu Khristu. Yesu analamula otsatira ake kuti azikonda anansi awo. Iye anawalamulanso kuti: “Pitirizani kukonda adani anu, kuchita zabwino kwa amene akudana nanu.” (Luka 6:27; Mateyo 22:39) Pamene wophunzira wina anayesa kuteteza Yesu ndi lupanga, iye anamuuza kuti: “Bwezera lupanga lako m’chimake, pakuti onse ogwira lupanga adzafa ndi lupanga.” (Mateyo 26:52) Motero mwa zolankhula ndiponso zochita zake, Yesu anasonyeza otsatira ake kuti sayenera kumenya nkhondo.

Chifukwa china chimene Mboni za Yehova sizimenyera nawo nkhondo n’chakuti chipembedzo chawo chili pa dziko lonse lapansi. Kumenya nkhondo kungawachititse kumenyana ndi abale awo ndipo zimenezi zingasemphane ndi lamulo la Yesu lakuti ‘mukondane wina ndi mnzake.’​—Yohane 13:35.

Mboni za Yehova sikuti zimangolankhula za mfundo za m’Baibulo zimene tatchulazi, zomwe ndi zolimbikitsa chikondi, koma zimazitsatira pamoyo wawo. Mwachitsanzo, taonani zomwe zinachita panthawi ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse mu 1939 mpaka 1945. Ku United States, Mboni za Yehova zoposa 4,300 zinaikidwa m’ndende chifukwa chokana kulowerera m’nkhondo. Nakonso ku Britain, Mboni zoposa 1,500, kuphatikizapo azimayi oposa 300, zinaikidwa m’ndende. Ndipo ku Germany, panthawi ya ulamuliro wa Nazi, Mboni zoposa 270 zinaphedwa chifukwa chokana kupita ku nkhondo ndipo Mboni zoposa 10,000 zinaikidwa m’ndende. Nazonso Mboni za ku Japan zinazunzidwa kwambiri. Choncho wina aliyense amene m’bale wake kapena mnansi wake anaphedwa pankhondoyi, ngakhalenso pankhondo zina zotsatira, sanganene kuti munthuyo anaphedwa ndi Mkhristu wa Mboni za Yehova.

M’mawu ake omaliza, Wolfgang Kusserow analongosola bwino mmene Mboni za Yehova zimaonera nkhondo. Chifukwa chokana kupita ku nkhondo, a chipani cha Nazi ku Germany anam’nyonga mu 1942 ali ndi zaka 20. (Yesaya 2:4) Iye anauza khoti la asilikali kuti: “Ndinaleredwa monga wa Mboni za Yehova, motsatira mawu a Mulungu opezeka m’Malemba Opatulika. Lamulo lalikulu ndiponso lopatulika kwambiri limene iye anapatsa anthu n’lakuti: ‘Uzikonda Mulungu wako kuposa wina aliyense ndiponso uzikonda mnansi wako ngati mmene umadzikondera wekha.’ Ndipo lamulo lina limati: ‘Usaphe.’ Kodi Mlengi wathu anapereka malamulo amenewa kwa mitengo?”​—Maliko 12:29-31; Eksodo 20:13.

Mboni za Yehova zimakhulupirira kuti ndi Yehova yekha, yemwe ndi Mulungu wamphamvuyonse, amene adzabweretse mtendere wosatha padziko lapansili. Mbonizo zimayembekezera mwachidwi kuti iye adzakwaniritse lonjezo lake ‘loletsa nkhondo ku malekezero adziko lapansi.’​—Salmo 46:9.