Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

N’chifukwa chiyani Pontiyo Pilato anachita mantha atamva kuti Yesu “akudziyesa yekha mwana wa Mulungu”?​—Yohane 19:7.

Juliasi Kaisara atafa, boma la Roma linamutcha kuti iye ndi mulungu. Ndiyeno mwana wake wom’peza, yemwe analowa m’malo mwake dzina lake Okutavia, anatchedwa divi filius, kutanthauza kuti “Mwana wa Mulungu.” Kenako, mafumu a Roma anayamba kupatsidwa dzina lachilatini lopatulika limeneli. Umboni wa zimenezi ndi wakuti dzinali limapezeka pa maguwa ansembe, pa makachisi, pa zosema, ndiponso pa ndalama zachiroma. Choncho, Ayuda atamva kuti Yesu akudzitcha “Mwana wa Mulungu,” iwo anamuimba mlandu woukira boma chifukwa dzinali linali la mfumu basi.

Panthawi imene Yesu amaimbidwa mlandu, Tiberiyo ndi amene anapatsidwa dzina limeneli lakuti divi filius [Mwana wa Mulungu]. Mfumu imeneyi inali ndi mbiri yopha aliyense amene imamuona kuti ndi mdani wake. Choncho, Ayuda anaopseza Pilato kuti akapanda kum’peza Yesu ndi mlandu, adzadana ndi Kaisara. N’chifukwa chake bwanamkubwa wachiromayu “anachita mantha kwambiri.” Mapeto ake, iye anawagonjera anthuwo ndipo analamula kuti Yesu aphedwe.​—Yohane 19:8, 12-16.

N’chifukwa chiyani Zekariya analosera za kuwonongedwa kwa Turo, mzindawu utawonongedwa kale ndi Ababulo?

Mzinda wa Turo unali pafupi ndi nyanja ya Mediterranean, ndipo unali ndi madera awiri. Dera lina linali kumtunda ndipo lina linali pachilumba.

Panthawi ina anthu a ku Turo anali paubale ndi Aisiraeli. Koma kenako, mzinda wa Turo unalemera ndipo anthu ake anayamba kunyoza Yehova Mulungu mpaka kufika pomaba golide ndi siliva m’kachisi ndi kugulitsa Aisiraeli ku ukapolo. (Yoweli 3:4-6) Zimenezi zinachititsa kuti Yehova awononge mzinda wa Turo. Kudzera mwa aneneri ake, Yehova analosera kuti mzinda wa Turo udzawonongedwa ndi mfumu ya Ababulo Nebukadinezara, amene anabwera ndi asilikali ake ku mzindawu atawononga Yerusalemu mu 607 B.C.E.​—Yesaya 23:13, 14; Yeremiya 27:2-7; Ezekieli 28:1-19.

Ababulo anawononga dera la kumtundali n’kutsala mabwinja okhaokha. Kenako anthu a ku Turo anathawira ku dera la pachilumba ndi katundu wawo. Patapita zaka pafupifupi 100, Yehova anauzira mneneri wake Zekariya kulengeza za kuwonongedwa kwa Turo. Iye anati: “Taonani, Yehova adzam’landa zake, nadzakantha mphamvu yake igwe m’manja; ndipo adzatha ndi moto.”​—Zekariya 9:3, 4.

Pokwaniritsa ulosi wa Zekariya umenewu, mzinda wa pachilumbawu, unawonongedwa mu 332 B.C.E ndi Alesandro Wamkulu. Kuti athe kuwononga mzindawu, Alesandro anamanga mlatho kuchokera kumtunda kufika ku chilumbachi, pogwiritsa ntchito mitengo ndi miyala yotengedwa ku mzinda wa Turo umene unawonongedwa uja. Nayenso Ezekieli anali atalosera zimenezi.​—Ezekieli 26:4, 12.

[Chithunzi patsamba 27]

“Kugonjetsedwa Kwa Turo”

[Mawu a Chithunzi]

Drawing by Andre Castaigne (1898-1899)