Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Chigumula cha Nowa Chinachitikadi Kapena Ndi Nthano?

Chigumula cha Nowa Chinachitikadi Kapena Ndi Nthano?

Chigumula cha Nowa Chinachitikadi Kapena Ndi Nthano?

KODI mumalakalaka dzikoli litasintha, anthu akukhala mwamtendere ndi anzawo, nkhondo, chiwawa ndiponso kuponderezana zitatha? Ngati ndi choncho, nkhani ya Nowa ingakulimbikitseni. Nowa anali munthu wabwino amene anamanga chingalawa chimene chinapulumutsa iye ndi banja lake panthawi ya chigumula cha padziko lonse chimene chinawononga oipa.

Nkhani ya Nowa ndi yodziwika kwambiri padziko lonse. Nkhaniyi imapezeka m’Baibulo, pa Genesis chaputala 6 mpaka 9. Inalembedwanso m’Korani ndipo padziko lonse pali nthano zambiri zimene zimatchula za nkhani imeneyi. Kodi chigumulachi chinachitikadi kapena ndi nthano chabe yongolimbikitsa anthu kuchita zabwino? Akatswiri amaphunziro a zaumulungu ndiponso asayansi akhala akulimbana za nkhani imeneyi kwa zaka zambiri. Koma Mawu a Mulungu, Baibulo, amasonyezeratu kuti nkhaniyi si nthano koma kuti inachitikadi. Taganizirani izi:

Buku la Genesis limanena chaka, mwezi, ndi tsiku lenileni limene chigumula chinayamba. Limatiuzanso nthawi ndi malo amene chingalawa chinaima, ndiponso nthawi imene madzi anauma padziko. Limafotokozanso mwatsatanetsatane kamangidwe ka chingalawacho, kukula kwake ndiponso mtundu wa zomangira zake. Koma nthano sizilongosola zinthu motsimikizirika chonchi.

Nkhani ziwiri za m’Baibulo zotchula mzera wobadwira wa anthu, zimasonyeza kuti Nowa anali munthu weniweni. (1 Mbiri 1:4; Luka 3:36) Ezara ndi Luka, amene analemba nkhani zimenezi anali anthu odziwa kufufuza bwino nkhani. Luka anafufuza ndi kupeza kuti Nowa anali m’gulu la makolo a Yesu Khristu.

Mneneri Yesaya ndi Ezekiel komanso atumwi achikhristu monga Paulo ndi Petulo, analemba za Nowa ndiponso chigumula.​—Yesaya 54:9; Ezekieli 14:14, 20; Aheberi 11:7; 1 Petulo 3:19, 20; 2 Petulo 2:5.

Yesu Khristu ananenanso za chigumula, kuti: “Monga zinachitikira m’masiku a Nowa, zidzachitikanso chimodzimodzi m’masiku a Mwana wa munthu: anthu anali kudya, anali kumwa, amuna anali kukwatira, akazi anali kukwatiwa, kufikira tsikulo pamene Nowa analowa mu chombo, ndipo chigumula chinafika ndi kuwononga anthu onsewo.” (Luka 17:26, 27) Chigumula chikanakhala kuti sichinachitike, mawu a Yesu onena za “Mwana wa munthu” akanakhala opanda tanthauzo.

Mtumwi Petulo analosera kuti kudzakhala “onyodola,” onyoza zimene Baibulo limanena. Petulo analemba kuti: “Anthu amenewa mwakufuna kwawo, amalephera kuzindikira mfundo iyi yakuti, . . . dziko la panthawiyo [ya Nowa] linawonongeka pamene linamizidwa ndi madzi.” Kodi ndi bwino kuti ifeyo tilephere kuzindikira ‘mfundoyi’? Ayi, popeza Petulo akupitiriza kunena kuti: “Miyamba imene ilipo tsopano limodzi ndi dziko lapansi, azisungira moto m’tsiku la chiweruzo ndi chiwonongeko cha anthu osaopa Mulungu.”​—2 Petulo 3:3-7.

Mulungu adzawononganso oipa koma padzakhalanso opulumuka. Ngati titsatira chitsanzo cha Nowa, tidzakhala m’gulu la anthu olungama omwe adzapulumuke n’kukhala m’dziko labwino kwambiri.