Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Ndakhala Wosangalala Chifukwa Chochita Chifuniro cha Mulungu

Ndakhala Wosangalala Chifukwa Chochita Chifuniro cha Mulungu

Ndakhala Wosangalala Chifukwa Chochita Chifuniro cha Mulungu

Yosimbidwa Ndi Bill Yaremchuk

Mu March 1947, nditangomaliza kumene maphunziro aumishonale, ndinapita kukatumikira ku Singapore. Maphunzirowa anali a kalasi ya nambala 8 a Sukulu ya Gileadi Yophunzitsa Baibulo, ndipo ankachitikira ku South Lansing, mumzinda wa New York, ku United States.

ANANDITUMIZA kuti ndikatumikire ku Singapore limodzi ndi mnzanga wa ku Canada, dzina lake Dave Farmer. Iyeyu anamaliza maphunziro a Gileadi a kalasi ya nambala 7. Pochoka ku San Francisco, mumzinda wa California, tinakwera sitima inayake imene kale inali yankhondo.

Doko loyamba kuima ku Asia linali la ku Hong Kong. Zimene tinaona kumeneko zinali zochititsa mantha. Kunali mavuto adzaoneni chifukwa cha nkhondo yachiwiri ya padziko lonse. Moti anthu anali atagonagona mu msewu, akufa ndi njala. Posakhalitsa tinakweranso sitima ija ulendo wa ku Manila, likulu la dziko la Philippines.

Kumenekunso nkhondo ija inasakaza zedi. Padoko panali zidutswa zokhazokha za sitima zimene zinawonongedwa pankhondoyo, ndipo kunali umphawi wadzaoneni. Tinakumana ndi abale athu a Mboni za Yehova angapo ndipo tinapita nawo limodzi ku Nyumba yawo ya Ufumu. Iwo anali osangalala ngakhale kuti anali pamavuto.

Kenako tinaimanso ku Batavia (komwe pano amati ku Jakarta) m’dziko la Indonesia. Kumeneku kunali nkhondo yapachiweniweni choncho sanatilole kuti titsike m’sitima yathu chifukwa nkhondo inkachitikira chapafupi. Titauyamba ulendo wopita ku Singapore, sitimadziwa kuti tikaona zotani kumeneko. Moti tinayamba kudzifunsa kuti, kodi mayiko okongola omwe amatchuka m’mabuku a za maulendo aja ndi amenewadi?

Koma patangopita masiku ochepa chabe nkhawa yanga inatha. Zimene tinaona, zinatitsimikizira kuti ine ndi Dave tinalidi pa ulendo wotumidwa ndi Mulungu.

Mmene Anatilolera Kukhala M’dzikolo

Patapita mwezi umodzi kuchokera pamene tinanyamuka ku San Francisco, sitima yathu inafika pachilumba cha St. John, pomwe sitima zimafikira kuti zipatsidwe chilolezo cholowa m’dziko la Singapore. Apolisi oona za anthu olowa m’dzikolo, anatidindira mapasipoti athu kuti tilowe m’dzikoli. M’mawa mwake sitima yathu inakaima padoko. Ndipo mkulu wina wogwira ntchito m’sitimayi ataona zikalata zathu, anatilola kutsika.

Tsiku lotsatira, tinapitanso ku doko kuja kukatsanzikana ndi amishonale anzathu amene tinali nawo paulendowu. Iwo amapita ku India ndi ku Ceylon (masiku ano amati Sri Lanka). Mkulu woyendetsa sitimayo atationa, anatsika kuti alankhule nafe. Iye anakwiya kwambiri ndipo anatikalipira chifukwa chotsika m’sitimayi. Mkuluyu anakwiya chifukwa choti wamkulu wa apolisi odinda mapasipoti dzina lake Haxworth, anamuuza kuti tikakafika ku doko kuja asakatilole kutsika. Koma ife zimenezi sitimazidziwa komanso mkulu amene anatilola kutsika uja samazidziwanso.

Atapita nafe kwa bambo Haxworth, iwonso anakwiya nazo. Anatikalipira kwambiri ndipo anatiuza kuti sitinali ololedwa kulowa m’dziko la Singapore. Koma popeza kuti sitimadziwa kuti taletsedwa kulowa m’dzikoli, tinamusonyeza mapasipoti athu omwe anali ndi zidindo zosonyeza kuti tinali ololedwa kulowa m’dziko la Singapore. Mokwiya, anatilanda mapasipotiwo ndi kukhwatcha zidindozo. Tsoka lake sitimayo inali itapita kale. Bambo Haxworth aja anasunga mapasipoti athu kwa chaka chonse. Koma kenako anatibwezera atawadindanso kuti taloledwa kulowa m’dzikolo.

Utumiki Unatiyendera Bwino ku Singapore

Titafika ku Singapore mu April 1947, kunali wa Mboni mmodzi yekha basi, dzina lake Joshua. Iye anali mtumiki wa nthawi zonse kapena kuti mpainiya mpaka pamene anamwalira, kumayambiriro kwa m’ma 1970. Patapita nthawi, anthu ena amene amaphunzira choonadi cha m’Baibulo, anayamba kuuza ena zimene amaphunzirazo. Mulungu anayamba kuyankha mapemphero athu akuti pakhale antchito ambiri.​—Mateyo 9:37, 38.

Mu 1949, a Haxworth ali ku tchuthi ku England, amishonale 6 omwe anamaliza maphunziro a Gileadi a kalasi ya nambala 11, anafika ku Singapore. Panthawiyi Dave, amene anali m’mishonale mnzanga kwanthawi yaitali, anachoka ku Singapore chifukwa chodwala. Anapita ku Australia, kumene anakatumikira mokhulupirika mpaka pamene anamwalira mu 1973. Pa amishonale 6 atsopano aja, panali Aileen Franks, yemwe ndinakwatirana naye mu 1956.

Pazaka zonsezi, tinaphunzira Baibulo ndi anthu ambiri, ndipo anthuwa anakhala a Mboni pamodzi ndi ana awo. Ngakhale panopa, ena mwa iwo ali mu utumiki wa nthawi zonse m’mayiko ena. Nkhani imodzi yolimbikitsa ndi ya Lester ndi Joanie Haynes, omwe anachokera ku United States. Tinayamba kuphunzira nawo Baibulo cha m’ma 1950. Anapita patsogolo kwambiri mwauzimu ndipo anakabatizidwa atabwerera kwawo ku United States. Patapita nthawi, iwo anayamba kuchita bwino kwambiri muutumiki moti anathandiza anthu ambiri kukhala Mboni, kuphatikizapo ana awo atatu.

Nthawi ina Joanie anatilembera kuti: “Ndikaganiza za chaka chimenechi ku Singapore, moyo wathu unasinthiratu. Mukanakhala kuti simunatitenge ngati ana anu, bwenzi tikungoyendayendabe m’dzikoli. Ndimasangalala kuti ndinu munam’phunzitsa Lester choonadi chifukwa mutangoyamba kum’phunzitsa, munam’thandiza kukonda Yehova ndi abale athu achikhristu. Mpaka pano amachitabe zimenezi.”

Tinatumikirabe ku Singapore Tili ndi Mwana

Mu 1962, moyo wathu unasintha mosayembekezereka. Dokotala wathu anauza mkazi wanga Aileen kuti ali ndi mimba. Tinkafunitsitsa kupitirizabe umishonale koma kodi zikanatheka bwanji tili ndi mwana? Nathan H. Knorr, amene panthawiyo amayang’anira ntchito ya Mboni za Yehova padziko lonse, anatilembera kalata yotilimbikitsa kuti tipeze ntchito konko kuti tisachoke ku Singapore. Zimenezi zinali zovuta kwambiri.

Anthu ambiri ochokera m’mayiko ena, amagwira ntchito zapamwamba m’makampani akunja amene anali m’dzikomo. Koma panthawiyi n’kuti ndilibe maphunziro antchito iliyonse popeza ndinayamba utumiki wanthawi zonse nditangomaliza sukulu ya sekondale zaka pafupifupi 23 zapitazo. Choncho, ndinakalipira ndalama ku bungwe lina la ku London limene limapezera anthu ntchito kuti lindipezere ntchito. Ndipo bungweli linatumiza makalata ondifunira ntchito yogwirizana ndi imene ndimadziwa ya umishonale ku makampani ambiri ochokera ku mayiko ena amene anali ku Singapore.

Nthawi zambiri amandiyankha kuti, “Pepani, palibe ntchito yokhudzana ndi maphunziro anu.” Amanditenga ngati wophunzira kwambiri. Patapita miyezi ingapo, mwana wathu, Judy, anabadwa. M’bale Knorr, atabwera ku Singapore panthawiyi, anapita ku chipatala kukaona Judy ndi mayi ake. Anatiuza kuti, “Mukhoza kumakhalabe ku nyumba ya amishonale mpaka Bill atapeza ntchito.”

Patapita miyezi ingapo, ndinapeza ntchito ku kampani ya ndege. Malipiro ake anali ochepa, ongokwanira kugula chakudya basi. Patatha zaka ziwiri, ndinayamba ntchito ku kampani inanso ya ndege ya ku America ndipo malipiro ake anali ambiriko, kuwirikiza kawiri oyamba aja. Patapita nthawi, ndinakhazikika pantchitoyi ndipo ndimapeza mpata wocheza ndi banja langa ndiponso wolalikira.

Tinkakonda kwambiri kutumikira Yehova ndipo nthawi zonse takhala tikuika zinthu zauzimu patsogolo. Zimenezi zathandiza kuti ndikhale ndi maudindo ambiri m’gulu la Yehova. Aileen anadzayambanso utumiki wa nthawi zonse. Panthawiyi ntchito yolalikira Ufumu ku Singapore inali ikupita patsogolo. Cha m’ma 1965, tinagula nyumba yosanjikizana m’tauni. Nyumbayi timaigwiritsa ntchito ngati Nyumba ya Ufumu ndipo munkasonkhana mipingo inayi.

Ntchito Yathu Inaletsedwa

Tinayamba kuona kuti ntchito yathu ikhoza kusokonezedwa nthawi ina iliyonse. Ndiyeno tsiku lina pa January 14, 1972, tinapita ku Nyumba ya Ufumu kuti tikasonkhane monga mwa chizolowezi chathu. Koma tinapeza pakhomo patatsekedwa ndi tcheni komanso loko. Ndipo panali chikwangwani chonena kuti Mboni za Yehova ku Singapore si zovomerezeka ndi boma. Apa ntchito yathu inaletsedwa. *

Kutsekedwa kwa Nyumba ya Ufumu sikunatiletse kulambira Yehova. Koma ndinkadzifunsa kuti, ‘Kodi banja langa Mulungu alinalo cholinga chotani?’ Ndinaganiza kuti ngati atatiuza kuti tichoke ku Singapore, sitidzakhalanso ndi mwayi wobweranso m’dzikoli kudzaona anzathu. Choncho, ndinapempha bwana wanga kuti ndizikagwirira ntchito ku Kuala Lumpur, m’dziko la Malaysia. Ndinaona kuti ngati zimenezi zingatheke, ndiye kuti banja langa lingamabwere m’dzikoli mosavuta. Zinandidabwitsa kwambiri kuona kuti bwana wanga anandilola ndipo anandiuza kuti ndikakhale bwana ku ofesi ya ku Kuala Lumpur. Analonjeza kuti awonjezera malipiro anga kawiri ndi kuti kampani izikandichitira zinthu zambiri.

Koma kenako ndinadzifunsa kuti, ‘Kodi ndi cholingadi cha Mulungu kuti banja lathu lichoke ku Singapore ndi kusiya abale athu?’ Tinapemphera kwa Yehova n’kumuuza za nkhaniyi. Kenako tinazindikira kuti Yehova ndiye anatibweretsa kuno. Choncho tinaganiza kuti tisasamuke. Bwana wanga anadabwa kwambiri nditakana ntchito yabwino ngati imeneyi.

Kukhala komanso kugwira ntchito ku Singapore panthawi imeneyi kunali kovuta chifukwa tinkaona kuti nthawi ina iliyonse akhoza kutimanga. Nthawi zingapo, tinaona kuti mawu a pa Salmo 34:7 ndi oona. Mawuwa amati: “Mngelo wa Yehova azinga kuwachinjiriza iwo akuopa Iye, nawalanditsa iwo.”

Tinayamba Utumiki Wina

Kenaka mu 1993, titatumikira ku Singapore zaka zoposa 46, tinapemphedwa kupita ku New Zealand, kuti tikachite utumiki wathu momasuka. Zinali zomvetsa chisoni kusiyana ndi abale athu amene tinali kuwakonda kwambiri. Komabe, tinalimbikitsidwa kudziwa kuti chikhulupiriro chawo chinali chomangidwa ndi zinthu zosagwira moto. Zimenezi zawathandiza kupirira mavuto zaka zonsezi mpaka pano.​—1 Akorinto 3:12-14.

Tikunena pano, tatha zaka zoposa 14 tili ku New Zealand. Ngakhale kuti takalamba, ine ndi mkazi wanga tikutumikirabe Yehova monga apainiya apadera. Akulu anga awiri, Mike wa zaka 94 ndi Peter wa zaka 90, akutumikirabe Yehova mokhulupirika kwathu ku Canada.

Mu 1998, mwana wathu Judy anapitanso kukatumikira ku dziko lina la ku Asia, komwe watumikirako zaka zambiri. Nthawi ina anatilembera kalata n’kutiuza kuti: “Ndimathokoza Yehova tsiku lililonse chifukwa cha mwayi wapadera wodzatumikira kuno. Ndikuthokozanso inu nonse awiri pondiphunzitsa mwachikondi komanso chifukwa chondithandiza kuti zonsezi zitheke.” Mu 2003, mwana wathu Judy anabwerera ku New Zealand kudzatisamalira. *

Tikuthokoza kwambiri Yehova chifukwa tinakwanitsa kuthandiza nawo pa ntchito yotuta, pomvera mawu a Ambuye. Takhala osangalala kwambiri chifukwa chochita ntchito imeneyi. Ndipo poti “dziko likupita,” monga mmene Baibulo limanenera, tidzasangalala kuona kukwaniritsidwa kwa lonjezo losangalatsa la Mulungu lakuti: “Wochita chifuniro cha Mulungu akhalabe kosatha.”​—1 Yohane 2:17.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 25 Onani Nsanja ya Olonda ya Chingelezi ya June 1, 1972, masamba 341-349.

^ ndime 32 Aileen anamwalira pa January 24, 2008, nkhaniyi ikulembedwa.

[Chithunzi patsamba 29]

Titafika ku Singapore mu 1947, kunali wa Mboni mmodzi yekha basi, dzina lake Joshua

[Chithunzi patsamba 29]

Ndili ndi Dave Farmer ku Hong Kong, tikupita ku Singapore mu 1947

[Chithunzi patsamba 29]

Ndili ndi Aileen mu 1958

[Chithunzi patsamba 31]

Tili ndi mwana wathu Judy

[Mawu a Chithunzi]

Kimroy Photography

[Mawu a Chithunzi patsamba 28]

Kimroy Photography