Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Kamtsikana Kachiisiraeli” Kamakono

“Kamtsikana Kachiisiraeli” Kamakono

 “Kamtsikana Kachiisiraeli” Kamakono

M’CHAKA cha 2006, kutatsala milungu iwiri kuti mwambo wokumbukira imfa ya Yesu uchitike, munthu aliyense wa m’banja la a Sales limene limakhala mu mzinda wa Praia Grande, m’dziko la Brazil, analemba mayina a anthu amene ankafuna kuwaitana ku mwambowu. Mwana wamkazi wa m’banjali wa zaka 6 dzina lake Abigayl anapatsidwa kapepala kamodzi koitanira anthu ku mwambowu ndipo makolo ake anamufunsa kuti aitana ndani.

Iye anati: “Ndiitana bambo amene amandisekerera nthawi zonse aja.”

Makolo ake anamufunsa kuti: “Bambo ake ati?”

Iye anayankha kuti: “Amene amayenda pa njinga aja.”

Patapita masiku anayi, Abigayl anawaonetsa makolo ake bambowo. Iwo ndi a Walter ndipo amakhala pafupi kwambiri ndi Nyumba ya Ufumu. Zaka zoposa 15 zapitazo, bambowa anachita ngozi ya galimoto ali ndi zaka 28 ndipo analumala miyendo. Popeza kuti anali wolemera anali ndi antchito awiri omulondera. Abigayl ataloledwa kukalankhula ndi bambowa, makolo ake anauza bamboyu kuti mwana wawoyo akufuna kuwaitanira ku mwambo wokumbukira imfa ya Yesu.

Atawauza zimene anabwererazo, Abigayl anati: “Anthu ena onse ku Nyumba ya Ufumu yathu ali ndi timapepala tambiri toitanira anthu ku mwambowu, koma ine ndili ndi kapepala kamodzi kokha. Ndiye ndaitana inu nokha basi. Ngati simudzabwera ndiye kuti palibe amene abwere woitanidwa ndi ineyo. Koma mukadzabwera ndidzasangalala ndipo Yehova adzasangalalanso kwambiri.”

Patsiku la mwambowu, Mboni za Yehova za m’derali ndi Abigayl yemwe, zimayeretsa Nyumba ya Ufumu pokonzekera mwambowu madzulo ake. Masana a tsikuli, a Walter amadutsa pafupi ndi Nyumba ya Ufumuyi ndipo ataona Abigayl anamuuza dalaivala wawo kuti aime. Iwo anatsegula windo la galimoto yawo ndi kumufunsa Abigayl zimene amachita. Iye anawauza kuti amakonza nyumbayo kuti iwowo akabwera idzakhale ikuoneka bwino.

Patsiku limeneli madzulo, Abigayl anali ndi nkhawa zedi. Mpaka nkhani inayamba, iye amangoyang’ana uku ndi uku kuti aone ngati a Walter abwera. Kenako, anangoona a Walter atulukira ndi antchito awo aja. Iye anasangalala kwambiri. Nkhani itatha, a Walter anati amapita kwina kwake koma anasintha maganizo n’kubwera ku mwambowu chifukwa cha iyeyo. Ndipo anatinso: “Nkhaniyi ndi yofunikira kwambiri kwa ine.” Anapempha Baibulo ndipo anayamba kuphunzira ndi kupita ku misonkhano.

Achemwali a a Walter ankafunitsitsa atamuona Abigayl, amene achimwene awo amakonda kumutchula. Atakumana naye, anasangalala kwambiri kuona kuti Abigayl ndi mwana wabwino kwambiri. Iwo anati: “Tsopano ndadziwa chifukwa chake achimwene anga ali osangalala kwabasi.”

A Walter akuphunzirabe Baibulo ndiponso amapita ku misonkhano. Iwo amayankhanso pa misonkhanoyi ndiponso amalalikira. Ndithudi, Abigayl akutikumbutsa za kamtsikana kachiisiraeli kamene kanathandiza Namani kudziwa Mulungu woona, Yehova.​—2 Mafumu 5:2-14.