NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) October 2015

Magaziniyi ili ndi nkhani zophunzira kuyambira pa November 30 mpaka December 27, 2015.

Tizilemekeza Kwambiri Abale Ngati Amenewa

Kodi ndi abale ati amene amathandiza m’makomiti a Bungwe Lolamulira? Kodi abalewa amachita chiyani?

Kodi Mumaona Dzanja la Mulungu Likukuthandizani?

Kodi Baibulo limatanthauza chiyani likamanena za “dzanja” la Mulungu?

“Tiwonjezereni Chikhulupiriro”

Kodi n’zotheka kukhala ndi chikhulupiriro patokha?

MBIRI YA MOYO WANGA

Sananong’oneze Bondo ndi Zimene Anasankha Ali Mnyamata

Nikolai Dubovinsky anatumikira Yehova mokhulupirika pa nthawi imene ntchito ya Mboni za Yehova inali yoletsedwa ku Soviet Union ndipo ankagwira ntchito yovuta kuposa kukhala kundende.

Tisalole Chilichonse Kutisokoneza Potumikira Yehova

Pafupifupi zaka 60 zapitazo, Nsanja ya Olonda inafotokoza mfundo inayake imene ikukwaniritsidwa masiku ano.

Tiziganizira Kwambiri za Yehova

Kodi mungaganizirebe Mawu a Mulungu ngati mwaletsedwa kukhala ndi Baibulo?

MBIRI YA MOYO WANGA

Kuyandikira kwa Mulungu Ndi Kwabwino

Sarah Maiga anasiya kukula ali ndi zaka 9 koma akutumikira Yehova mwakhama.

‘Munthu Wosadziwa Zinthu Amakhulupirira Mawu Alionse’

Kodi tingadziwe bwanji ngati uthenga umene talandira ndi woona kapena ayi?