Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Munthu Wosadziwa Zinthu Amakhulupirira Mawu Alionse’

‘Munthu Wosadziwa Zinthu Amakhulupirira Mawu Alionse’

Wolemba mabuku wina wa ku Germany anati: “Munthu amene sawerenga nyuzipepala ndi wopusa koma wopusa kwambiri ndi amene amakhulupirira chilichonse chimene wawerenga m’nyuzipepalayo.”—August von Schlözer (anabadwa mu 1735 n’kumwalira mu 1809).

NGATI zaka 200 zapitazo munthu sankatha kukhulupirira zonse zimene zinalembedwa m’nyuzipepala, kuli bwanji zimene timawerenga masiku ano? Pa Intaneti timatha kupeza mosavuta nkhani zambirimbiri. Zina zimakhala zoona ndiponso zothandiza koma zina zimakhala zonama, zachabechabe komanso zoopsa. Choncho tiyenera kusankha mwanzeru zimene tikufuna kuwerenga. Anthu akangoyamba kumene kugwiritsa ntchito Intaneti, amakhulupirira nkhani iliyonse imene amapeza kapena imene mnzawo wawatumizira. Amachita zimenezi ngakhale kuti nkhaniyo ndi yokayikitsa kwambiri. Koma Baibulo limanena kuti: “Munthu amene sadziwa zinthu amakhulupirira mawu alionse, koma wochenjera amaganizira za mmene akuyendera.”—Miy. 14:15.

Kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife ochenjera? Sitiyenera kukhulupirira nkhani iliyonse imene ili pa Intaneti tisanafufuze bwinobwino. Tiyenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi nkhaniyi ili pawebusaiti yodalirika kapena ili pamalo oti aliyense akhoza kulembapo maganizo ake? Kodi webusaiti ina yodalirika yasonyeza kuti nkhaniyi ndi yabodza?’ * Ndiyeno tikapeza mayankho a mafunsowa, tizichita zinthu mwanzeru. (Miy. 7:7) Nthawi zambiri nkhani imene tikuikayikira imakhaladi yabodza. Komanso tikawerenga nkhani inayake yonena zoipa za munthu wina, tiyenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi cholinga cha nkhaniyi ndi chiyani? Nanga ndikaifalitsa ithandiza ndani?’

KODI TIMAFULUMIRA KUTUMIZIRA ENA MAUTHENGA?

Anthu ena amafulumira kutumizira anthu ambirimbiri uthenga asanafufuze ngati zili zoona komanso asanaganizire mavuto amene angabwere ngati ataufalitsa. Mwina amachita zimenezi chifukwa cha mtima wofuna kuti anthu azimvera kwa iwowo nkhani iliyonse imene yangochitika kumene. (2 Sam. 13:28-33) Koma munthu “wochenjera” amayamba waganizira  ngati nkhaniyo ingaipitse mbiri ya munthu kapena gulu.

Pamafunika khama ndithu kuti munthu atsimikizire ngati nkhani ili yoona kapena yabodza. N’chifukwa chake anthu ambiri amangofalitsa nkhani kuti wolandirayo azikafufuza yekha ngati ndi yoona kapena ayi. Koma funso ndi lakuti: Kodi enawo alidi ndi nthawi yofufuzira kuti atsimikizire? Tisaiwale kuti nawonso safuna kuwononga nthawi yawo pa zinthu zosafunika. (Aef. 5:15, 16) Choncho ngati nkhani inayake tikuikayikira, ndi bwino kungoisiya osati kuitumiza kwa ena.

Mafunso ena oyenera kudzifunsa ndi awa: ‘Kodi ineyo ndimafulumira kutumizira ena mauthenga? Kodi nthawi ina ndinapepesapo anthu ena chifukwa chowatumizira zinthu zolakwika kapena zabodza? Kodi pali munthu wina amene anandiuzapo kuti ndisamamutumizirenso mauthenga?’ Tizikumbukira kuti ngati anzathuwo ali ndi adiresi ya imelo, ndiye kuti akhoza kuona okha zinthu pa Intaneti. Sikuti angafunikire kuti ifeyo tiziwatumizira mauthenga, timavidiyo kapena zithunzi zambirimbiri. Si bwinonso kujambula nkhani za Baibulo zimene ena akamba n’kutumizira anzathu. * Ena amafufuza nkhani zosiyanasiyana za m’Baibulo kapena mayankho a mafunso a nkhani za pa misonkhano n’kutumizira anzawo. Koma zimenezi n’zosathandiza chifukwa munthu amalimbikitsidwa ngati wafufuza yekha osati kufufuziridwa.

Kodi uthenga umenewu nditumiziredi anthu ena?

Kodi tiyenera kuchita chiyani ngati taona nkhani inayake pa Intaneti yoipitsa mbiri ya gulu la Yehova? Ndi bwino kusiyiratu kuiwerenga ndipo sitiyenera kuikhulupirira. Ena amafuna kuuza anzawo n’cholinga choti amve maganizo awo. Koma zimenezi zimangochititsa kuti nkhani yoipayo ifalitsidwe kwambiri. Ngati nkhani ina imene mwaona pa Intaneti ikukudetsani nkhawa, chofunika n’kupempha Yehova kuti akupatseni nzeru ndiponso kupita nokha kukafotokozera abale odalirika. (Yak. 1:5, 6; Yuda 22, 23) Sitiyenera kudabwa anthu akamatinenera mabodza chifukwa n’zimene zinachitikiranso Yesu. Paja iye anauza ophunzira ake kuti: ‘Anthu adzawazunza komanso kuwanamizira zinthu zoipa  zilizonse.’ (Mat. 5:11; 11:19; Yoh. 10:19-21) Choncho tiyenera kukhala ‘oganiza bwino’ ndiponso ‘ozindikira’ n’cholinga choti tisapusitsidwe ndi anthu ‘onena zinthu zopotoka’ komanso “achinyengo m’zochita zawo zonse.”—Miy. 2:10-16.

TIZILEMEKEZA ANTHU ENA

Tiyeneranso kukhala osamala tikalandira uthenga wonena za abale ena kapena zimene akumana nazo potumikira Yehova. Ngakhale nkhaniyo itakhala yoona, si nthawi zonse pamene tiyenera kuifalitsa. (Mat. 7:12) Mwachitsanzo, si bwino kumangofalitsa nkhani zokhudza anthu ena. (2 Ates. 3:11; 1 Tim. 5:13) Kumbukirani kuti nkhani zina zimakhala zachinsinsi, ndipo eniake sangafune kuti anthu ena azidziwe pa nthawiyo komanso m’njira imeneyo. Choncho, tiyenera kulemekeza maganizo awo chifukwa pamakhala mavuto ambiri tikafulumira kuulula nkhani zina.

Masiku ano nkhani imatha kupita patali m’kanthawi kochepa kwambiri. Mwachitsanzo, ngati mwatumiza uthenga kwa munthu mmodzi, iyeyo akhoza kutumizira anthu ena padziko lonse pa masekondi ochepa. Choncho sitiyenera kufulumira kutumiza uthenga kwa wina aliyense amene timadziwana naye. N’zoona kuti chikondi “chimakhulupirira zinthu zonse,” koma zimenezi sizikutanthauza kuti tizingokhulupirira nkhani iliyonse imene tamva. (1 Akor. 13:7) Sitingakhulupirire ngakhale pang’ono zinthu zabodza zokhudza abale athu komanso gulu la Yehova. Ndipo anthu amene amafalitsa mabodza amenewa amakhala akutumikira Satana Mdyerekezi yemwe ndi “tate wake wa bodza.” (Yoh. 8:44) Choncho tiyenera kukhala osamala ndi nkhani zambiri zimene timawerenga. Paja Baibulo limati: “Anthu osadziwa zinthu, ndithu adzakhala opusa, koma kwa ochenjera, kudziwa zinthu kudzakhala ngati chovala cha kumutu.”—Miy. 14:18.

^ ndime 4 Nkhani zabodza zimene zinafalitsidwa kalekale zikhoza kulembedwanso n’kusinthidwa zina ndi zina n’cholinga choti zioneke ngati zoona.

^ ndime 8 Werengani “Bokosi la Mafunso” mu Utumiki Wathu wa Ufumu wachingelezi wa April 2010.