Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Tizilemekeza Kwambiri Abale Ngati Amenewa

Tizilemekeza Kwambiri Abale Ngati Amenewa

KUYAMBIRA mu 1992, abale a m’Bungwe Lolamulira amasankha abale okhulupirika omwe ndi akulu kuti aziwathandiza. * Abalewa ndi a “nkhosa zina” ndipo amachita zambiri pothandiza m’makomiti a Bungwe Lolamulira. (Yoh. 10:16) Iwo amapezeka pa misonkhano ya komiti imene amathandizayo. Abalewa amapereka mfundo ndiponso maganizo awo pa misonkhanoyi, koma a m’Bungwe Lolamulira ndi amene amasankha zochita. Abale amenewa amaonetsetsa kuti zimene komiti yasankha zizichitika ndipo amagwira bwino ntchito iliyonse imene apatsidwa. Amapitanso ku misonkhano yapadera ndiponso ya mayiko limodzi ndi abale a m’Bungwe Lolamulira. Nthawi zina amapemphedwa kuti akhale oimira likulu la Mboni za Yehova n’kumayendera maofesi a nthambi.

M’bale wina amene wagwira ntchito yothandiza Bungwe Lolamulira kuyambira mu 1992 ananena kuti: “Ntchito imene ndimagwira imathandiza kuti abale a m’Bungwe Lolamulira azigwira ntchito zina zofunika kwambiri.” M’bale winanso amene wagwira ntchitoyi kwa zaka 20 anati: “Ndimaona kuti ndi mwayi waukulu kwambiri kuthandiza abalewa ndipo sindinkayembekezera kuti ndingachite zimenezi.”

Bungwe Lolamulira lapatsa abale okhulupirikawa udindo waukulu ndipo limayamikira zimene amachita. Tiyeni tonse tizilemekeza kwambiri abale ngati amenewa.—Afil. 2:29.

^ ndime 2 Kuti mudziwe ntchito za makomiti 6 a Bungwe Lolamulira, werengani bokosi lakuti “Mmene Bungwe Lolamulila Limayendetsera Zinthu za Ufumu” m’mutu 12 wa buku lakuti, Ufumu wa Mulungu Ukulamulira.