Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MBIRI YA MOYO WAWO

Sananong’oneze Bondo ndi Zimene Anasankha Ali Mnyamata

Sananong’oneze Bondo ndi Zimene Anasankha Ali Mnyamata

AGOGO anga dzina lawo a Nikolai Dubovinsky anabadwa mu 1926, m’mudzi winawake ku Ukraine ndipo makolo awo anali osauka. Agogowo analemba zinthu zosangalatsa komanso zovuta zimene anakumana nazo pa nthawi imene boma la Soviet Union linaletsa ntchito yolalikira. Ngakhale kuti ankakumana ndi mavuto ambiri, anakhalabe okhulupirika kwa Yehova ndipo ankakhala mosangalala. Iwo ankafuna kuti achinyamata adziwe zimene anakumana nazo pa moyo wawo. Choncho ndikufuna kuti ndifotokoze zinthu zina zimene ananena.

KODI ANAYAMBA BWANJI KUPHUNZIRA BAIBULO?

Agogowo anafotokoza kuti: “Tsiku lina mu 1941, mchimwene wanga wamkulu dzina lake Ivan anapatsidwa buku lakuti, Zeze wa Mulungu ndiponso lakuti, The Divine Plan of the Ages. Anapatsidwanso magazini ena a Nsanja ya Olonda komanso timabuku tina. Atabwera kunyumba, ndinawerenga mabuku ndi magazini onsewo. Ndinadabwa nditamva kuti amene amachititsa mavuto a m’dzikoli ndi Mdyerekezi osati Mulungu. Ndinawerenganso mabuku a m’Baibulo a Uthenga Wabwino ndipo ndinazindikira kuti mfundo zimene ndikuphunzira ndi zoona. Choncho ndinayamba kuuza ena zimene ndinkawerengazo. Ndinkaphunzira kwambiri mabukuwo ndipo ndinayamba kumvetsa bwino mfundo za m’Baibulo komanso kufunitsitsa kutumikira Yehova.

“Nthawiyi inali ya nkhondo ndipo ine sindikanalola kulowa usilikali n’kumapha anthu. Choncho ndinkadziwa kuti ndidzazunzidwa chifukwa cha zimene ndinkakhulupirira. Ndiyeno ndinayamba kukonzekera mavutowo poloweza malemba monga Mateyu 10:28 ndi 26:52. Ndinatsimikiza mumtima mwanga kuti ndidzakhala wokhulupirika kwa Yehova zivute zitani.

“Mu 1944, ndinakwanitsa zaka 18 ndipo ndinaitanidwa kuti ndikalowe usilikali. Kumeneko kunali Akhristu anzanga ndipo aka kanali koyamba kukumana nawo. Panali abale achinyamata ambiri amene anaitanidwa. Tinauza akuluakulu a asilikali amene anatiitanawo kuti sitingamenye nawo nkhondo. Iwo anakwiya kwambiri n’kunena kuti akhoza kutimana chakudya, kutigwiritsa ntchito yokumba mayenje apo ayi atiwombera. Atatero, tinawayankha kuti: ‘Chitani chilichonse chimene mukufuna. Koma ife tidzamverabe lamulo la Mulungu lakuti, “Usaphe munthu.”’—Eks. 20:13.

“Ine ndi abale ena awiri tinatumizidwa kudziko la Belarus kukagwira ntchito yolima komanso yokonza nyumba zowonongeka. Nditafika kumeneko ndinaona zinthu zoopsa zimene zinachitika chifukwa cha nkhondo. Kunali mitengo yambiri imene inapsa ndipo  mitembo ya anthu ndi mahatchi akufa zinali paliponse. Ndinaona zida zankhondo zimene zinasiyidwa komanso ndege yophwasuka. Onsewa anali mavuto obwera chifukwa chosamvera malamulo a Mulungu.

“Nkhondoyi inatha mu 1945 koma ife anatiuza kuti tikhalabe m’ndende zaka 10 chifukwa chokana usilikali. Pa zaka zitatu zoyambirira, tinalibe mwayi wolankhulana ndi Akhristu anzathu kapena kuwerenga buku lililonse. Tinalembera kalata alongo ena koma nawonso anamangidwa n’kuweruzidwa kuti akhale m’ndende zaka 25.

“Tinamasulidwa mu 1950 zaka 10 zija zisanathe. Nditafika kunyumba ndinapeza kuti mayi anga ndiponso mchemwali wanga dzina lake Mariya analinso a Mboni. Achimwene anga awiri anali asanabatizidwe koma ankaphunziranso Baibulo. Apolisi ataona kuti ndinkalalikirabe mwakhama ankafuna kundimanganso. Ndiyeno abale amene ankatsogolera ntchito yathu anandipempha kuti ndizithandiza nawo kusindikiza mabuku mobisa. Apa n’kuti ndili ndi zaka 24.”

ANKASINDIKIZA MABUKU

“A Mbonife tinkakonda kunena kuti: ‘Ngakhale boma laletsa ntchito yolalikira tipitirizabe mobisa.’ (Miy. 28:28) Pa nthawiyi, tinkasindikiza mabuku athu m’zipinda zapansi. Poyamba ndinkagwira ntchitoyi m’chipinda chinachake chapansi pamalo amene mkulu wanga dzina lake Dmitry ankakhala. Nthawi zina sindinkachoka m’chipindachi kwa milungu iwiri. Mpweya wabwino ukachepa, nyali yanga inkazima ndipo ndinkangogona n’kumadikira kuti mpweya wina ubwere.

Zithunzi za chipinda chapansi chimene Nikolai ankasindikizira mabuku

“Tsiku lina m’bale wina amene ndinkagwira naye ntchito anandifunsa kuti, ‘Nikolai,  kodi unabatizidwa?’ Apa n’kuti nditatumikira Yehova kwa zaka 11, koma ndinali ndisanabatizidwe. Iye anandifotokozera kufunika kobatizidwa ndipo usiku wa tsikulo ndinakabatizidwa m’nyanja inayake ndili ndi zaka 26. Patapita zaka zitatu, ndinapemphedwa kuti ndikhale mu komiti yoyang’anira ntchito yolalikira m’dzikolo. Pa nthawiyi, abale amene anali mu komitiyi anali atamangidwa. Choncho abale enafe tinapemphedwa kulowa m’malo mwawo n’cholinga choti ntchito yolalikira iziyendabe.”

MAVUTO AMENE ANKAKUMANA NAWO

“Ntchito yosindikiza mabuku mobisa inali yovuta kwambiri kuposa kukhala kundende. Sindinasonkhane ndi mpingo kwa zaka 7 n’cholinga choti apolisi asandigwire choncho ndinkafunika kuchita khama kwambiri kuphunzira Baibulo pandekha. Ndinkangoonana ndi anthu am’banja langa mwa apa ndi apo. Iwo ankandimvetsa ndipo ankandilimbikitsa kwambiri. Ndinkatopa kwambiri chifukwa chogwira ntchitoyi kwa nthawi yaitali. Pankafunika kukhala tcheru nthawi zonse. Mwachitsanzo, tsiku lina madzulo kunyumba kunabwera apolisi awiri. Ndiyeno ndinatulukira pawindo lakuseri n’kuthawira m’nkhalango. Ndikutuluka m’nkhalangoyo kulowa m’munda winawake, ndinamva phokoso lachilendo. Kenako ndinazindikira kuti akundiwombera. Mmodzi anakwera hatchi n’kupitiriza kundithamangitsa uku akuomba mfuti mpaka zipolopolo zinamuthera. Chipolopolo chimodzi chokha n’chimene chinandivulaza pamkono. Atandithamangitsa makilomita okwana 5, ndinazemba n’kukabisala m’nkhalango. Pa nthawi ina tili kukhoti, ndinamva kuti apolisiwo anawomba zipolopolo 32.

“Ndinkaoneka woyezuka chifukwa cha malo amene ndinkagwira ntchito. Komanso ndinayamba kudwala moti nthawi ina ndinalephera kupita ku msonkhano wina wofunika chifukwa choti ndinkatuluka magazi m’kamwa ndi m’mphuno. Choncho ndinkayesetsa kupeza nthawi yowothera dzuwa kuti apolisi asadabwe ndi maonekedwe anga.”

ANAMANGIDWA

Kundende ya ku Mordvinia mu 1963

“Pa January 26, 1957, ndinamangidwa. Ndiyeno patapita miyezi 6, khoti lalikulu la ku Ukraine linapereka chigamulo choti ndiphedwe  mochita kuwomberedwa. Koma popeza dzikoli linali litasiya kupereka chilango chopha anthu, ndinauzidwa kuti ndikakhale kundende zaka 25. Tikaphatikiza zaka zimene ine ndi anzanga 7 tinagamulidwa, zinakwana 130. Tinatumizidwa kundende ya ku Mordvinia kumene tinakapezana ndi anzathu a Mboni okwana 500. Tinkakumana mobisa m’timagulu kuti tiphunzire Nsanja ya Olonda. Msilikali wina atawerenga magazini amene anatilanda ananena kuti: ‘Mukapitiriza kuwerenga zimenezi, palibe angakugonjetseni.’ Tinkagwira ntchito iliyonse imene tapatsidwa ndipo nthawi zambiri tinkachita zoposa zimene tauzidwa. Komabe mkulu wa asilikali ananena kuti: ‘Ntchito imene mukugwirayi si yofunika kwa ife. Chimene tikufuna n’choti muzimvera boma.’”

“Tinkagwira ntchito iliyonse imene tapatsidwa ndipo nthawi zambiri tinkachita zoposa zimene tauzidwa”

ANAKHALABE OKHULUPIRIKA

Nyumba ya Ufumu ya ku Velikiye Luki

Agogo anga atamasulidwa mu 1967, anathandiza kwambiri kukhazikitsa mipingo ku Estonia ndi mumzinda wa St. Petersburg, ku Russia. Chakumayambiriro kwa 1991, khoti lina linaonanso zimene zinagamulidwa mu 1957 ndipo linapeza kuti panalibe umboni wakuti abale ndi alongo amene ankazunzidwa anali olakwa. Mu 1996, agogo anga anasamukira mumzinda wa Velikiye Luki womwe uli pa mtunda wa makilomita 500 kuchokera ku St. Petersburg. Atafika anagula nyumba ndipo mu 2003, Nyumba ya Ufumu inamangidwa pamalo awowo. Panopa mipingo iwiri imasonkhana pa Nyumba ya Ufumu imeneyi.

Ine ndi mwamuna wanga tikutumikira ku ofesi ya nthambi ku Russia ndipo agogo anga aja anabwera kudzationa mu March 2011. Uku kunali kuonana komaliza chifukwa anamwalira patangopita miyezi yochepa. Anatilimbikitsa kwambiri ndipo anatiuza mosangalala kuti: “Pamene zinthu zafikapa, zili ngati tayamba kuzungulira mzinda wa Yeriko pa tsiku la nambala 7.” (Yos. 6:15) Pa nthawiyi, anali ndi zaka 85. Ngakhale kuti anakumana ndi mavuto ambiri pa moyo wawo, iwo anati: “Ndikusangalala kwambiri kuti ndinasankha kutumikira Yehova ndili mnyamata. Sindinong’oneza bondo ngakhale pang’ono.”