Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukukumbukira?

Kodi Mukukumbukira?

 Kodi Mukukumbukira?

Kodi mwapindula powerenga magazini aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Tayesani kuyankha mafunso otsatirawa:

• Kodi tingatani kuti tizilankhula bwino “chinenero choyera,” chomwe ndi choonadi chonena za Mulungu komanso zolinga zake? (Zef. 3:9, NW)

Mofanana ndi kuphunzira chinenero china chilichonse, kuti tilankhule bwino “chinenero choyera” tiyenera kumvetsera anthu odziwa chinenerocho akamalankhula, kutsanzira amene amalankhula bwino, kuloweza maina a mabuku a m’Baibulo ndiponso mavesi ena, kuwerenga mobwereza zimene taphunzira, kuwerenga mokweza, kuphunzira malamulo kapena mfundo za choonadi, kupitiriza kuphunzira, kukhala ndi nthawi yeniyeni yophunzira komanso kulankhulalankhula chinenero choyeracho.​—8/15, masamba 21-25.

• Kodi ndi zinthu ziti zimene munthu ayenera kudziwa kuti afike pom’dziwadi Mulungu?

Ayenera kudziwa kuti ‘dzina lake ndi Yehova,’ ndipo amafuna kuti tidziwe dzina lakelo. (Eks. 15:3) Iye ndi “Mulungu wachikondi ndi wamtendere.” (2 Akor. 13:11) Ndiponso ndi “Mulungu wanzeru” ndi “chipulumutso.” (1 Sam. 2:3; Sal. 25:5) Mulungu amayandikira kwa anthu amene amadziwa zinthu zonsezi zokhudza iye.​—9/1, masamba 4-7.

• Kodi zingatheke bwanji kukhala ndi “chingwe cha nkhosi zitatu “ m’banja?

Mawu akuti “chingwe cha nkhosi zitatu “ ndi ophiphiritsa. (Mla. 4:12) Zingwe ziwiri zoyamba zimaimira mwamuna ndi mkazi wake, amene amapotedwa pamodzi ndi chingwe chachitatu, chimene chikuimira Mulungu. M’banja mukakhala Mulungu, banjalo limakhala lolimba mwauzimu ndipo limatha kupirira mavuto komanso limakhala losangalala​—9/15, tsamba 16.

• Pa Aheberi 6:2, kodi Paulo ankatanthauza chiyani pamene ananena za “kuika manja”?

Apa sanali kunena za kuika Akhristu kukhala akulu mumpingo. Iye ayenera kuti amanena zoika manja popereka mphatso zozizwitsa za mzimu. (Mac. 8:14-17; 19:6)​—9/15, tsamba 32.

• Kodi bambo wabwino amadziwa kuti ayenera kuchitira ana ake zinthu ziti?

Ayenera (1) kukonda ana ake, (2) kupereka chitsanzo chabwino, (3) kuonetsetsa kuti ana akusangalala pakhomo, (4) kuphunzitsa ana ake kukonda Mulungu, (5) kulanga ndi kulangiza ana ake, (6) kuteteza ana ake.​—10/1, masamba 18-21.

• Kodi abale amene amatsogolera mu mpingo angalemekeze bwanji anthu ena?

Njira imodzi imene mkulu angachitire zimenezi ndiyo kusauza ena kuti achite zinthu zimene iyeyo sangafune kuchita. Amasonyezanso kuti akulemekeza ena powauza chifukwa chimene akuwapemphera kuchita chinachake kapena chifukwa chimene akuwapatsira malangizo enaake.​—10/15, tsamba 22.

• Kodi ndi zinthu ziti zimene zingathandize kuti mupitirize kukhala wokhulupirika mu ukwati wanu?

(1) Muziona banja lanu kukhala lofunika kwambiri. (2) Muzipewa kuchita chilichonse chosonyeza kusakhulupirika. Kaya m’banja mwanu mumagwirizana kapena ayi, mkazi kapena mwamuna wanu ayenera kudziwa kuti inuyo mukuyesetsa kuti banja lanu liziyenda bwino. Mfundo ziwirizi zingakuthandizeni kuchita zimenezi.​—11/1, masamba 18-21.

• Kodi abusa achiisiraeli ankagwiritsira ntchito bwanji ndodo yokhota kumapeto, nanga akulu achikhristu angaphunzirepo chiyani?

Kalelo, ku Isiraeli m’busa ankakhala ndi ndodo yaitali yokhota kumapeto, yomwe ankakusira nkhosa zake. Nkhosazo zikamalowa kapena kutuluka m’khola, ‘zinkadutsa pansi pa ndodoyo’ ndipo m’busayo ankaziwerenga. (Lev. 27:32) Abusa achikhristu nawonso ayenera kudziwa bwino gulu la nkhosa za Mulungu n’kumaonetsetsa kuti nkhosa iliyonse ilipo ndipo ili bwino.​—11/15, tsamba 9.

• Kodi mayi angasonyeze bwanji kuti amaona kuti ukhondo ndi wofunika?

Mayi amadziwa kuti chakudya chimawonongeka m’njira zambiri, choncho amasamba m’manja asanagwire chakudya ndiponso amachivindikira. Amayesetsanso kukonza m’nyumba kuti musakhale makoswe, ntchentche ndi tizilombo tina. Komanso amachapa zovala ndi kusamba nthawi zonse. Zimenezi n’zimene Baibulo limafuna.​—12/1, masamba 9-11.