Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mudzasungabe Umphumphu?

Kodi Mudzasungabe Umphumphu?

 Kodi Mudzasungabe Umphumphu?

“Mpaka kufa ine sinditaya ungwiro [“umphumphu,” NW] wanga.”​—YOBU 27:5.

1, 2. Kodi kumanga nyumba ndi kofanana ndi kutani, nanga tikambirana mafunso ati?

TIYEREKEZERE kuti mwasankha pulani ya nyumba imene mukufuna kumanga. Ndiyeno mukusangalala kwambiri ndi pulaniyo. Mukusangalalanso poganiza kuti nyumbayo idzakhala yabwino kwa inuyo ndi banja lanu. Komatu kungoganizira pulani ndi ubwino wa nyumbayo si kokwanira. Nyumba ya pulani yoteroyo ingaoneke ubwino wake ngati mutaimangadi, kulowamo komanso kupitiriza kuisamalira.

2 N’chimodzimodzinso ndi umphumphu. Khalidwe limeneli ndi lofunika kwambiri kwa ife ndiponso kwa anthu amene timawakonda. Komatu kungoganizira za kufunika kwa umphumphu si kokwanira. Chofunika ndi kukhala anthu osunga umphumphu nthawi zonse. Masiku ano, kumanga nyumba kumafuna ndalama zambiri. (Luka 14:28, 29) Mofananamo, kuti munthu asunge umphumphu zimatenga nthawi ndipo pamafunika khama. Ndipo ndi mmenedi ziyenera kukhalira. Tiyeni tikambirane mafunso atatu awa: Kodi tingatani kuti tikhale anthu osunga umphumphu? Nanga tingatani kuti tisasiye kusunga umphumphu? Kodi munthu angatani ngati panthawi ina walephera kusunga umphumphu?

Kodi Tingatani Kuti Tikhale Anthu Osunga Umphumphu?

3, 4. (a) Kodi Yehova amatiphunzitsa bwanji kusunga umphumphu? (b) Kodi chitsanzo cha Yesu chimatithandiza motani kuti tisunge umphumphu?

3 M’nkhani yoyamba ija taona kuti pankhani yosunga umphumphu Yehova watipatsa ufulu wosankha. Koma ubwino wake ndi wakuti, sanatisiye opanda thandizo pankhani imeneyi. Iye amatiphunzitsa mmene tingakhalire anthu osunga umphumphu. Amatipatsanso mzimu woyera umene ungatithandize kuchita zimene amatiphunzitsazo. (Luka 11:13) Kuwonjezera pamenepo Yehova amateteza mwauzimu anthu amene amasunga umphumphu.​—Miy. 2:7.

4 Kodi Yehova amatiphunzitsa bwanji kusunga umphumphu? Chinthu chofunika kwambiri chimene anachita ndi kutumiza Mwana wake Yesu. Iye anamvera Mulungu kwa moyo wake wonse. ‘Anakhala womvera mpaka imfa.’ (Afil. 2:8) Yesu anamvera Atate wake wakumwamba pa chilichonse ngakhale panthawi imene kuchita zimenezi kunali kovuta. Panthawi ina iye anapemphera kwa Yehova kuti: “Chifuniro chanu chichitike, osati changa.” (Luka 22:42) Motero tonsefe tingachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ineyo ndili ndi mtima  womvera ngati umene Yesu anali nawo?’ Tikakhala omvera, tili ndi zolinga zabwino tidzakhala anthu osunga umphumphu. Taganizirani mbali zina pamoyo wathu zimene kumvera kumakhala kofunika kwambiri.

5, 6. (a) Kodi Davide anatsindika motani kufunika kwa kusunga umphumphu ngakhale pamene anthu ena sakutiona? (b) Kodi ndi zinthu ziti masiku ano zimene zingayese umphumphu wa Akhristu akakhala okha?

5 Tiyenera kumvera Yehova ngakhale pamene tili tokha. Wamasalmo Davide ankadziwa kufunika kwa kusunga umphumphu ngakhale panthawi imene anali yekha. (Werengani Salmo 101:2.) Popeza Davide anali mfumu, nthawi zambiri ankakhala ndi anthu ena. N’zosachita kufunsa kuti pena ankakhala pakati pa anthu mahandiredi kapenanso masauzande ambiri. (Yerekezerani ndi Salmo 26:12.) Monga mfumu, panthawi imeneyi anafunika kusunga umphumphu kuti apereke chitsanzo chabwino kwa anthu ake. (Deut. 17:18, 19) Komabe, Davide anadziwa kuti anafunika kusungabe umphumphu ngakhale panthawi imene ali yekha, ‘m’nyumba mwake.’ Nanga bwanji ifeyo?

6 Pa Salmo 101:3 Davide anati: “Sindidzaika chinthu choipa pamaso panga.” Masiku ano, palinso zinthu zambirimbiri zimene zingatichititse kuona zinthu zoipa makamaka tikakhala tokha. Intaneti yabweretsanso mavuto pankhani imeneyi. N’zosavuta kuti munthu akopeke n’kumaona zinthu zokayikitsa kapena zolaula pa Intaneti. Koma kodi tinganene kuti munthu wochita zimenezi amamvera Mulungu amene anauzira Davide kulemba mawu ali pamwambawa? Kuonera zolaula n’koopsa kwambiri, chifukwa munthu aliyense amene amaonera zolaula amayamba kulakalaka zinthu zoipa ndipo amakhala ndi mtima wadyera. Ndipo zimenezi zingawononge chikumbumtima chake, banja lake komanso kuipitsa khalidwe lake.​—Miy. 4:23; 2 Akor. 7:1; 1 Ates. 4:3-5.

7. Kodi ndi mfundo iti imene ingatithandize kusunga umphumphu tikakhala tokha?

7 N’zoona kuti palibe mtumiki wa Yehova aliyense amene amakhaladi yekhayekha. Nthawi zonse Atate wathu amatiyang’anira chifukwa chotikonda. (Werengani Salmo 11:4.) Yehova amasangalala kwambiri akaona inuyo mukukana zoipa mukamayesedwa. Mukamatero mumakhala mukumvera chenjezo limene Yesu anapereka pa Mateyo 5:28. Choncho zivute zitani musalole kuona zithunzi zimene zingakukopeni kuti muchite zoipa. Musayerekeze kugulitsa umphumphu wanu ndi zinthu zochititsa manyazi monga ngati kuonera kapena kuwerenga zolaula.

8, 9. (a) Kodi Danieli ndi anzake anayesedwa motani pankhani yosunga umphumphu? (b) Kodi masiku ano Akhristu achinyamata amasangalatsa motani Yehova ndi Akhristu anzawo?

8 Tingasonyezenso kuti timasunga umphumphu mwa kumvera Yehova panthawi imene tili ndi anthu osakhulupirira. Taganizirani za Danieli ndi anzake atatu aja. Iwo ali anyamata anagwidwa n’kukakhala akapolo ku Babulo. Kumeneko, iwo anali kukhala ndi anthu osakhulupirira amene ankangomudziwa pang’ono Yehova, mwinanso sankamudziwa  n’komwe. Aheberi anayiwa anayesedwa kuti adye zakudya zimene Chilamulo cha Mulungu chinkaletsa. Anyamata amenewa akanatha kupeza zifukwa zodzikhululukira. Panthawiyo makolo awo, akuluakulu achiyuda kapena ansembe anali kutali moti sakanaona zimene akuchita. Koma kodi ndani akanawaona? Yehova ndi amene akanawaona. Motero ngakhale kuti anakakamizidwa, iwo analimba mtima n’kumvera Yehova mosasamala kanthu kuti zimenezo zikanaika moyo wawo pachiswe.​—Dan. 1:3-9.

9 Padziko lonse achinyamata a Mboni za Yehova amayesedwa ndi anzawo kuti akhale osakhulupirika kwa Mulungu. Koma mofanana ndi Aheberi aja, iwo salolera zimenezo. Achinyamata mukamakana kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, ziwawa, kutukwana, chiwerewere ndi zoipa zina mumasonyeza kuti mumamvera Yehova. Mukachita zimenezo mumasunga umphumphu wanu, mumapindula komanso mumasangalatsa Yehova ndi Akhristu anzanu.​—Sal. 110:3.

10. (a) Tchulani maganizo oipa amene achinyamata ambiri ali nawo pankhani ya dama omwe amawalepheretsa kusunga umphumphu. (b) Kodi kusunga umphumphu kumatithandiza bwanji kuti tithawe dama?

10 Tiyenera kukhalanso omvera tikakhala ndi anthu omwe si amuna kapena akazi anzathu. Tonse tikudziwa kuti Mawu a Mulungu amaletsa dama. Koma ngati sitingasamale tikhoza kusiya kumvera ndi kuyamba moyo wotayirira. Mwachitsanzo achinyamata ena achitapo makhalidwe oipa monga kugonana mkamwa, kugonana kumatako ndi kuseweretsana maliseche. Iwo amati zimenezi si zoipa kwenikweni poganiza kuti si dama. Achinyamata amene amakhala ndi maganizo amenewa, amaiwala kapena kunyalanyaza dala mfundo yakuti, mawu a m’Baibulo akuti dama amaphatikizapo makhalidwe oipa onsewa. Ndipo munthu wochita zimenezi angachotsedwe mumpingo. * Chomvetsa chisoni kwambiri ndi chakuti iwo amanyalanyaza kufunika kosunga umphumphu. Popeza cholinga chathu ndi kusunga umphumphu, sitiyenera kupeza zifukwa zodzikhululukira kuti tichite zoipa. Sitingayerekeze dala kuchita zinthu zoipa poganiza kuti sizinafike poti tingachotsedwe nazo. Tisamangoganizira chilango chimene tingalandire ngati titachita zoipa. Koma tiyenera kuchita zinthu zimene zingasangalatse Yehova, n’kumapewa zimene zingamupweteketse mtima. M’malo modzikhululukira poganiza kuti kungochita izi si tchimo lalikulu, timapeweratu zoipa ndipo ‘timathawa dama.’ (1 Akor. 6:18) Tikatero timasonyeza kuti ndife anthu osungadi umphumphu.

Kodi Tingatani Kuti Tisasiye Kusunga Umphumphu?

11. N’chifukwa chiyani tinganene kuti kumvera kulikonse ngakhale pa zinthu zazing’ono n’kofunika? Perekani chitsanzo.

11 Tiyenera kupitirizabe kumvera kuti tisasiye kusunga umphumphu. Kumvera pa zinthu zing’onozing’ono kumaoneka ngati si nkhani yaikulu. Koma kuchita zimenezi kwanthawi yaitali n’kumene kumachititsa kuti munthu akhale ndi mbiri ya kumvera. Mwachitsanzo, njerwa imodzi ingaoneke ngati yopanda ntchito koma tikatolera  zambiri tikhoza kumangira nyumba yabwino. Motero tikamamvera nthawi zonse sitidzasiya kusunga umphumphu.​—Luka 16:10.

12. Kodi Davide anapereka chitsanzo chotani pankhani yosungabe umphumphu ngakhale panthawi imene ankachitiridwa zinthu zopanda chilungamo?

12 Umphumphu wathu umaonekeranso tikamapirira mavuto kapena tikamachitiridwa zinthu zopanda chilungamo. Taganizirani chitsanzo cha m’Baibulo cha Davide. Iye ali mnyamata anazunzidwa ndi mfumu imene inayenera kuchita zinthu zoimira ulamuliro wa Yehova. Panthawiyi, Yehova anali atasiya kuyanja mfumu Sauli ndipo Sauli anayamba kuchitira nsanje Davide chifukwa choti Mulungu ankamukonda. Komatu Sauli anakhalabe mfumu kwa kanthawi ndipo ankagwiritsa ntchito asilikali a Isiraeli posakasaka Davide. Yehova analola zimenezi kuchitika kwa zaka zingapo. Kodi Davide anaimba mlandu Mulungu chifukwa cha zimenezi? Kodi anayamba kuganiza kuti palibenso chifukwa chopitirizira kupirira? Ayi ndithu. Iye anapitiriza kulemekeza kwambiri udindo umene Mulungu anapatsa Sauli moti ngakhale pamene mpata unapezeka, iye anakana kubwezera Sauli.​—1 Sam. 24:2-7.

13. Kodi tingatani kuti tisasiye kusunga umphumphu munthu wina akachita zotipsetsa mtima kapena akatilakwira?

13 Chitsanzo cha Davide n’chothandiza kwambiri masiku ano. Mpingo wapadziko lonse umene ife tilimo ndi wa anthu opanda ungwiro ndipo wina angatilakwire kapena kuchita zinthu zosakhulupirika. Komabe chosangalatsa n’chakuti, nthawi imene tikukhala ino ndi yoti palibe amene angasokonezeretu anthu onse a Yehova. (Yes. 54:17) Komabe kodi tingatani munthu wina akatilakwira kapena kutipsetsa mtima. Mkhristu mnzathu akatilakwira tisalole kuti mkwiyo ukhalebe mu mtima mwathu chifukwa kuchita zimenezi kungatilepheretse kusunga umphumphu. Tisalole kuti khalidwe loipa la anthu ena litichititse kuimba mlandu Mulungu kapena kusiya kukhala okhulupirika. (Sal. 119:165) Kupirira panthawi ya mavuto kumatithandiza kuti tisasiye kusunga umphumphu.

14. Kodi anthu osunga umphumphu amatani gulu likasintha kayendetsedwe ka zinthu kapena mafotokozedwe a Malemba ena?

14 Kupewa mtima wopezera ena zifukwa kungatithandizenso kuti tisungebe umphumphu. Ndipo kuchita zimenezi, kumasonyeza kuti ndife okhulupirika kwa Yehova. Masiku ano iye akudalitsa anthu ake kuposa kalelonse ndipo kulambira koona kwakwezedwa kwambiri padziko lapansi moti sizinaonekenso. (Yes. 2:2-4) Gulu likasintha mafotokozedwe a Malemba ena kapena kachitidwe ka zinthu zina tiyenera kumvera. Timasangalala kuona umboni wakuti kuunika kukunkabe kuuwala. (Miy. 4:18) Ngati zikutivuta kumvetsa chifukwa chimene gulu lasinthira zinthu zina tiyenera kupempha Yehova kuti atithandize. Panopo timayesetsa kupirira, kumvera ndiponso kusunga umphumphu.

Kodi Munthu Angatani Ngati Panthawi Ina Walephera Kusunga Umphumphu?

15. Tchulani munthu mmodzi amene angaswe umphumphu wanu.

15 Mwina mungaone kuti funso limeneli ndi lovutitsa maganizo. Monga taona kale m’nkhani yoyamba ija, kusunga umphumphu n’kofunika kwambiri. Kupanda kutero sitingakhale paubwenzi  ndi Yehova komanso sitingakhale ndi chiyembekezo chenicheni. Koma dziwani kuti m’chilengedwe chonse pali munthu mmodzi yekha amene angaswe umphumphu wanu. Ndipo munthu wake ndi inuyo. Yobu ankaidziwa bwino mfundo imeneyi. Iye anati: “Mpaka kufa ine sinditaya ungwiro [“umphumphu,” NW] wanga.” (Yobu 27:5) Ngati mwatsimikiza mtima ngati Yobu komanso ngati mukuyandikirabe Yehova simudzataya umphumphu wanu.​—Yak. 4:8.

16, 17. (a) Kodi munthu amene wachita tchimo lalikulu sayenera kuchita chiyani? (b) Nanga ayenera kuchita chiyani?

16 Komabe pali anthu ena amene amasiya kusunga umphumphu. Nthawi ya atumwi, Akhristu ena ankachita machimo aakulu ndipo zimenezi zikuchitikanso masiku ano. Kodi zimenezi zikachitika kwa inu ndiye kuti basi chanu palibe? Ayi si choncho. Ndiyeno kodi mungatani? Choyamba tiyeni tikambirane zimene simuyenera kuchita. Mwachibadwa anthu amakonda kubisa machimo awo kuti makolo, Akhristu anzawo komanso akulu asadziwe. Komatu Baibulo limanena kuti: “Wobisa machimo ake sadzaona mwayi; koma wakuwavomereza, nawasiya adzachitidwa chifundo.” (Miy. 28:13) Anthu amene amayesa kubisa machimo awo amalakwitsa kwambiri chifukwa palibe chobisika pamaso pa Mulungu. (Werengani Aheberi 4:13.) Palinso anthu ena amene amakhala ndi moyo wachiphamaso. Iwo amatumikira Yehova, uku akuchita machimo ena. Moyo umenewu ndi wosemphana kwambiri ndi kusunga umphumphu, chifukwa kuchita zimenezi ndi kuswa umphumphuwo. Yehova sakondwera ndi anthu amene amam’tumikira, kwinaku akubisa machimo akuluakulu. Ndipo chinyengo choterechi chimam’kwiyitsa kwambiri.​—Miy. 21:27; Yes. 1:11-16.

17 Baibulo limanena njira yoyenera kutsatira Mkhristu akachita tchimo lalikulu. Zimenezi zikachitika ayenera kupempha thandizo kwa akulu achikhristu. Yehova anakonza njira yothandiza Mkhristu amene wadwala kwambiri mwauzimu. (Werengani Yakobe 5:14.) Musaope kufuna thandizo kuti muchire mwauzimu poganiza kuti mulangidwa kapena kudzudzulidwa. Ndipotu munthu wanzeru amene akudwala matenda oopsa, sangakane kubayidwa jakisoni kapena kuchitidwa opaleshoni chifukwa choopa ululu.​—Aheb. 12:11.

18, 19. (a) Kodi chitsanzo cha Davide chikusonyeza bwanji kuti munthu angayambirenso kusunga umphumphu? (b) Pankhani ya kusunga umphumphu, kodi mwatsimikiza kuchita chiyani?

18 Kodi munthu amene wachita tchimo lalikulu angachire mwauzimu? Kodi munthu ataswa umphumphu wake angayambirenso kuusunga? Taganiziraninso za Davide uja. Iye anachita tchimo lalikulu. Iye anasirira mkazi wamwini, anachita naye chigololo, ndipo kenako anakonza zoti mwamuna wake wosalakwa aphedwe. Kungoganizira nkhani imeneyi munthu akhoza kukayikira ngati Davide panthawiyi analidi kusunga umphumphu. Koma kodi iye analibenso chiyembekezo chilichonse? Davide anafunika chilango champhamvu ndipo iye anavomereza chilangocho. Kenako Yehova anamuchitira chifundo chifukwa chakuti analapa moona mtima. Davide anaphunzirapo kanthu pa chilangocho ndipo anayambiranso kusunga umphumphu mwa kumvera Mulungu nthawi zonse. Zimene zinamuchitikira Davide ndi chitsanzo cha mawu a pa Miyambo 24:16. Lembali limati: “Wolungama amagwa kasanu ndi kawiri, nanyamukanso.” Kodi zotsatira zake zinali zotani? Taganizirani zimene Yehova anauza Solomo, Davideyo atamwalira. (Werengani 1 Mafumu 9:4.) Izi zikusonyeza kuti Mulungu ankakumbukira Davide monga munthu wosunga umphumphu. Yehova amatha kuyeretsa munthu wolapa ngakhale atathimbirira motani ndi machimo aakulu.​—Yes. 1:18.

19 Mungathe kusunga umphumphu ngati mumvera Mulungu chifukwa chomukonda. Pitirizani kukhala okhulupirika komanso opirira. Ndipo mukachita tchimo lalikulu muyenera kulapa moona mtima. Kunena zoona umphumphu wathu ndi chinthu chamtengo wapatali. Tiyeni tonsefe tikhale ngati Davide n’kunena motsimikiza kuti: “Koma ine, ndidzayenda m’ungwiro [“umphumphu,” NW] wanga.”​—Sal. 26:11.

[Mawu a M’munsi]

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi mungatani kuti mukhale munthu wosunga umphumphu?

• Kodi mungachite bwanji kuti mupitirize kusunga umphumphu?

• Kodi munthu angatani kuti ayambirenso kusunga umphumphu?

[Mafunso]

[Bokosi patsamba 8]

‘ANACHITA ZINTHU ZABWINO KWAMBIRI’

Mawu amenewa ananena ndi mayi wina amene anali ndi pakati pa miyezi isanu. Ananena izi ataona kuti munthu wina wosam’dziwa anasonyeza kukoma mtima ndiponso kusunga umphumpu. Mayiyu anali mu kantini ina ya khofi. Patapita nthawi ndithu atachoka mu kantiniyo, anazindikira kuti waiwala chikwama chake. M’chikwamamo munali ndalama zokwana madola 2,000 ndipo ndalama zimenezi zinali zochuluka kuposa zimene ankayenda nazo nthawi zonse. Pambuyo pake anauza mtolankhani wa nyuzipepala ina kuti: “Ndinadandaula kwambiri.” Koma mayi wina wachitsikana anatola chikwamacho ndipo anayamba kufufuza mwiniwake. Atalephera kumupeza anakapereka ndalamazo ku polisi, ndipo apolisi anamupeza mayi wapakati uja. Mwini wa chikwamacho anayamikira mayi wachitsikanayo ndipo anati, “Anachita zinthu zabwino kwambiri.” N’chifukwa chiyani iye anayesetsa kuti abweze ndalamazo? Nyuzipepalayo inanena kuti, iye ndi wa Mboni za Yehova ndipo “anasonyeza kukhulupirika chifukwa cha zimene amaphunzira ku chipembedzo chake.”

[Chithunzi patsamba 9]

Achinyamata angasunge umphumphu poyesedwa

[Chithunzi patsamba 10]

Panthawi ina Davide analephera kusunga umphumphu, koma anayambiranso