Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

 Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Pa Levitiko 3:17 Aisiraeli analamulidwa kuti ‘asamadye mafuta’ pamene pa Nehemiya 8:10, anauzidwa kuti ‘adye zonona.’ Kodi malemba amenewa akutsutsana?

Mawu a Chiheberi amene anamasuliridwa kuti “mafuta” pa Levitiko 3:17 ndi osiyana ndi mawu amene anamasuliridwa kuti “zonona” pa Nehemiya 8:10. Pa Levitiko 3:17, anagwiritsa ntchito mawu akuti kelevu amene amatanthauza mafuta a nyama kapena a munthu. (Lev. 3:3; Ower. 3:22) Mavesi oyandikana ndi vesi 17, akusonyeza kuti Aisiraeli analetsedwa kudya mafuta a nyama okuta matumbo, okhala pa impso ndiponso a m’chiuno chifukwa chakuti ‘mafuta onse ndi a Yehova.’ (Lev. 3:14-16) Choncho, sankaloledwa kudya mafuta a nyama amene ankaperekedwa nsembe kwa Yehova.

Mawu akuti mashimanimu amene anamasuliridwa kuti “zonona” pa Nehemiya 8:10 sapezekanso paliponse m’Malemba a Chiheberi. Mawu a Chiheberi amenewa anachokera ku mawu akuti shameni, ndipo amatanthauza “kunenepa.” Mawu ena amene amachokera ku mawu amenewa amatanthauza kudya bwino kapena kupeza bwino. (Yerekezerani ndi Yes. 25:6) Mawu enanso ochokera ku mawu amenewa ndi shemeni ndipo amatanthauza “mafuta” monga ‘mafuta a azitona.’ (Deut. 8:8; Lev. 24:2) Choncho, mawu a pa Nehemiya 8:10, akuti “zonona” amatanthauza zakudya zimene zaphikidwa ndi mafuta ophikira ambiri kapena nyama yokhala ndi mafuta pang’ono koma osati mafuta okhaokha a nyama.

Ngakhale kuti Aisiraeli analetsedwa kudya mafuta a nyama, iwo ankaloledwa kudya zakudya zonona komanso zokoma. Zakudya zinanso zokoma, monga makeke a tirigu, zinkaphikidwa ndi mafuta osati a nyama koma opangidwa kuchokera ku mbewu monga za azitona. Choncho, kudya zonona sikukutanthauza kudya mafuta a nyama. (Lev. 2:7) Ndiponso, buku la Insight on the Scriptures limafotokoza kuti, “mawu akuti ‘zonona’ amatanthauza zinthu zokoma zophikidwa ndi mafuta opangidwa kuchokera ku mbewu.”

Komanso tikudziwa kuti Aisiraeli ankaletsedwa kudya mafuta chifukwa cha Chilamulo. Koma Akhristu amadziwa kuti iwo sali pansi pa Chilamulo ndiponso sapereka nsembe za nyama.​—Aroma 3:20; 7:4, 6; 10:4; Akol. 2:16, 17.