Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mzimu wa Munthu Sufa?

Kodi Mzimu wa Munthu Sufa?

Kodi Mzimu wa Munthu Sufa?

Kodi thupi lathuli ndi la magazi ndi nyama basi kapena lili ndi chinthu chinachake chapadera? Kodi moyo wathu ndi womwewu wongokhalapo lero mawa n’kufa? Kapena kodi tili ndi chinthu chinachake chosaoneka chimene chimakhalabe ndi moyo ngakhale titafa?

ZIPEMBEDZO zosiyanasiyana padziko lonse zimaphunzitsa zinthu zosiyanasiyana zonena kuti munthu amakhala ndi moyo winanso akafa, komano zipembedzo zambiri zimagwirizana pa mfundo imodzi yakuti: Munthu amakhala ndi chinachake chimene sichifa ngakhale munthuyo atafa. Ambiri amakhulupirira kuti chinthu chimenechi ndi mzimu. Kodi inuyo mumakhulupirira zotani? Kodi mzimu n’chiyani makamaka? Kodi munthu amakhaladi ndi mzimu, ndipo kodi mzimuwo sufa ngakhale munthuyo atafa?

‘Thupi Lopanda Mzimu N’lakufa’

M’Baibulo, mawu a Chiheberi ndi Chigiriki omwe amawamasulira kuti “mzimu” kwenikweni amatanthauza “mpweya” kapena “mphepo.” Komabe mawu akuti “mzimu” sikuti amangotanthauza mpweya weniweniwu basi. Mwachitsanzo, Baibulo limati: ‘Thupi lopanda mzimu limakhala lakufa.’ (Yakobe 2:26) Motero, mzimu ndi umene umachititsa kuti thupi likhale ndi moyo.

Mphamvu yochirikiza moyo imeneyi si mpweya umene timapuma wokhawu ayi. Timamvetsa mfundo imeneyi tikaganizira mmene munthu amene watsala pang’ono kufa amakhalira, akangosiya kumene kupuma. N’zotheka kuti anthu ena amuthandize munthuyo kuyambiranso kupumako. Kodi zimenezi zimatheka bwanji? Zimatheka chifukwa choti mphamvu yochirikiza moyo imakhala ilipobe m’maselo a thupi lake. Komano mphamvu imeneyi ikangotha, n’zosatheka kumuthandiza munthuyo kuyambiranso kupuma, ngakhale mutayesetsa bwanji. Ngakhale mutayesetsa kumukupiza kapena kumupumira mpweya wochuluka motani, maselo akufawo sangathe kukhalanso ndi moyo. Motero, mzimu ndi mphamvu ya moyo imene imachititsa kuti maselo a thupi la munthu akhale amoyo ndipo munthuyo amakhalanso wamoyo. Mphamvu imeneyi imachoka kwa makolo kupita kwa ana panthawi imene anawo akuyamba kupangika m’mimba ndipo pamafunika mpweya kuti mphamvu imeneyi ipitirire kugwira ntchito.​—Yobu 34:14, 15.

Kodi munthu aliyense ali ndi mzimu winawake wongogwirizana ndi iyeyo basi? Kapena kodi mphamvu yochirikiza moyoyi n’njofanana kwa munthu aliyense? Baibulo limayankha mafunso amenewa momveka bwino. Posonyeza kuti zamoyo zonse zimakhala ndi mzimu wofanana, mfumu yanzeru Solomo inati: “Chomwe chigwera ana a anthu chigweranso nyamazo; ngakhale chowagwera n’chimodzimodzi; monga winayo angofa momwemo zinazo zifanso; inde onsewo ali ndi mpweya umodzi; . . . onse [abwereranso] kufumbi. Ndani adziwa mzimu wa ana a anthu wokwera kumwamba, ndi mzimu wa nyama wotsikira kunsi ku dziko?” (Mlaliki 3:19-21) Inde, mzimu, kapena kuti mphamvu ya moyo imene ili mwa anthu ndiponso mwa nyama ndi yofanana.

Mzimu umene umakhala m’thupi tingauyerekezere ndi mphamvu ya magetsi imene imayendetsa chipangizo chinachake. Mphamvu yosaoneka imene imayenda m’chipangizo kapena makina, ingathe kugwira ntchito zosiyanasiyana, malinga ndi chipangizocho. Mwachitsanzo, mphamvu ya magetsiyo ingathe kuyatsa magetsi ounikira kapena kuyatsa fani, kuliza wailesi, TV, kapenanso kuyatsa kompyuta. Komano siisintha kuti ikhale ngati chipangizocho. Mphamvuyo imakhalabe chimodzimodzi basi. Ndi mmenenso ulili mzimu, kapena mphamvu ya moyo. Mzimu susintha m’njira ina iliyonse kuti ukhale ngati thupi limene ulimo. Sukhala ndi umunthu ndiponso suganiza. Yangokhala mphamvu basi. Anthu ali ndi mzimu wofanana ndi wa nyama. Motero munthu akamwalira, mzimu wake sumapitirirabe kukhala ndi moyo kwina kulikonse.

Mzimu Umapita Kuti Tikafa?

Lemba la Mlaliki 12:7 limanena kuti munthu akafa: ‘Fumbi limabwerera pansi pomwe linali kale, mzimu umabwerera kwa Mulungu amene anaupereka.’ Komabe, zimenezi sizikutanthauza kuti pali mzimu umene umachoka m’thupi mwa munthu n’kuyenda mu mlengalenga kukafika kwa Mulungu. Mwachitsanzo, taganizirani zimene Yehova anauza Aisiraeli osakhulupirika kudzera mwa mneneri wake Malaki. Iye anati: “Bwererani kudza kwa ine, ndipo ine ndidzabwerera kwa inu.” (Malaki 3:7) Kuti Aisiraeli amenewo ‘abwerere’ kwa Yehova, anayenera kusiya njira zawo zoipa n’kuyambiranso kumvera malamulo a Mulungu. Tanthauzo lakuti Yehova ‘adzabwerera’ kwa Aisiraeli linali lakuti iye adzayambanso kuwayanja. Motero, pamenepa ‘kubwerera’ kwa Aisiraeli ndiponso ‘kubwerera’ kwa Yehova sikunkatanthauza kuyenda kuchoka ku malo ena kupita kwina. Mawuwa ankangotanthauza kusintha maganizo. Zimenezi zikusonyeza kuti sikuti nthawi zonse Baibulo likamati ‘kubwerera’ limatanthauza kuchoka ku malo ena kupita kwina.

N’chimodzimodzinso munthu akafa: Mawu akuti ‘mzimu umabwerera kwa Mulungu amene anaupereka’ amatanthauza kuti amene angabwezeretse mphamvu ya moyo ikachoka mwa munthu, ndi Mulungu woona yekha, amene anaipereka. Zimenezi zikutanthauza kuti chiyembekezo chilichonse choti munthu ameneyo adzakhalanso ndi moyo m’tsogolo chili m’manja mwa Mulungu.

Mwachitsanzo, taganizirani zimene uthenga wabwino wa Luka umanena pa za imfa ya Yesu Khristu. Nkhaniyo imati: “Yesu anafuula mokweza mawu nanena kuti: ‘Atate, ndikuikiza mzimu wanga m’manja mwanu.’ Atanena zimenezi anatsirizika.” (Luka 23:46) Yesu akufa, mzimu wake kapena kuti mphamvu yake ya moyo, inatuluka. Zimenezi sizikutanthauza kuti unatuluka kupita kwa Atate wake kumwamba. Kwenikweni Yesu anali m’manda, kunalibe, mpaka pamene anaukitsidwa kwa akufa tsiku lachitatu kuchokera pamene anamwalira. (Mlaliki 9:5, 10) Ngakhale ataukitsidwa, Yesu sanapite kumwamba nthawi yomweyo. M’malomwake, “anadzionetsa yekha wamoyo” kwa ophunzira ake “masiku onse 40,” ndipo pambuyo pake “ananyamulidwa m’mlengalenga.” (Machitidwe 1:3, 9) Panthawi ya imfa yake, Yesu, ‘anaikiza mzimu wake m’manja mwa Atate wake,’ ndipo sanakayikire kuti Yehova angathe kumuukitsanso.

Nangano Mzimu N’chiyani Kwenikweni?

Baibulo limanena momveka bwino kwambiri za tanthauzo la mzimu. Mwachidule mzimu ndi mphamvu ya moyo imene munthu amafunikira kuti akhale wamoyo. Pamafunika mpweya kuti mphamvu ya moyoyi ipitirire kugwira ntchito. Motero, palibe chilichonse mwa munthu chimene chimakhalabe ndi moyo munthuyo akafa.

Choncho, zoti akufa adzakhalanso ndi moyo zimadalira chiyembekezo cha kuuka kwa akufa. Baibulo limalonjeza kuti: “Musadabwe nazo zimenezi, chifukwa idzafika nthawi pamene onse ali m’manda a chikumbutso adzamva mawu ake [a Yesu] ndipo adzatuluka.” (Yohane 5:28, 29) Maziko odalirika a chiyembekezo chokhudza anthu akufa, ndiwo lonjezo losakayikitsa ngakhale pang’ono lakuti akufa adzauka, osati chiphunzitso choti munthu ali ndi mzimu umene sufa ngakhale iyeyo atafa.

M’pofunika kwambiri kudziwa molondola za kuuka kwa akufa ndiponso za mmene anthu adzapindulire nako. M’pofunikanso kudziwa Mulungu ndi Khristu. (Yohane 17:3) Mboni za Yehova za dera la kwanuko zingasangalale kwambiri kukuthandizani kuphunzira Baibulo kuti mudziwe zambiri zokhudza Mulungu, Mwana wake, ndiponso malonjezo ake. Tikukupemphani kuti muyesetse kukumana ndi Mboni za kwanuko kapena kutilembera kalata.

[Chithunzi patsamba 4]

Zonsezi zili ndi mzimu wofanana

[Mawu a Chithunzi]

Goat: CNPC​—Centro Nacional de Pesquisa de Caprinos (Sobral, CE, Brasil)