Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Phindu la Kuleza Mtima ndi Kuchita Khama

Phindu la Kuleza Mtima ndi Kuchita Khama

 Olengeza Ufumu Akusimba

Phindu la Kuleza Mtima ndi Kuchita Khama

YESU KRISTU ananeneratu kuti m’masiku otsiriza “chikondano cha anthu a unyinji chidzazilala.” Zotsatira zake n’zakuti, m’mayiko ambiri masiku ano, anthu alibe chidwi ndi uthenga wabwino wa Ufumu. Ndipo ena amaipidwa ndi chipembedzo.​—Mateyu 24:12, 14.

Ngakhale zili choncho, chifukwa cha chikhulupiriro ndiponso kuleza mtima, ofalitsa Ufumu akugonjetsa zovuta zimenezi, monga mmene nkhani yotsatirayi yochokera ku dziko la Czech Republic ikusonyezera.

Mboni ziŵiri zinalankhula ndi mkazi pakhomo pali potseka. Patapita nthaŵi, mkaziyu anatsegula chitseko pang’ono, n’kutulutsa dzanja kuti atenge magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! amene Mboni zija zimagaŵira. Kenaka mkaziyo ananena kuti “zikomo kwambiri,” ndipo anatseka chitseko. “Kodi tidzabwerenso?” Mbonizo zinafunsana. Mmodzi wa Mbonizo, amene ndi mpainiya, kapena kuti mtumiki wa nthaŵi zonse, anaganiza zodzapitanso, koma atapitako zinachitikanso chimodzimodzi, ndipo zimenezi zinachitika kwa chaka chathunthu.

Ataganiza zoti asinthe njira imene amalankhulilana ndi mkaziyo, mpainiyayo anapemphera kwa Yehova kuti amuthandize. Atapitanso kuti akamugaŵire magazini, anafunsa mkaziyo mafunso aubwenzi: “Muli bwanji? Kodi munasangalala kuŵerenga magazini aja?” Poyamba, mkaziyo sanayankhe, koma atapitanso maulendo ena angapo, anayamba kumasuka. Nthaŵi ina anatsegula chitseko, koma anangocheza mwachidule.

Poona kuti mkaziyu sankafuna kucheza naye pachitsekopo, mpainiyayo anaganiza zomulembera kalata kuti am’fotokozere cholinga chimene amabwerera komanso kum’pempha kuti azichita naye phunziro la Baibulo lapanyumba. Pomalizira pake, atapirira ndi kuchita khama kwa chaka ndi theka, mpainiyayo anayambitsa phunziro la Baibulo ndi mwininyumbayo. Anadabwa komanso analimbikitsidwa pamene mkaziyu anamuuza kuti: “Ndakhala ndikukhulupirira Mulungu kuyambira nthaŵi imene munayamba kundibweretsera magazini.”

Zoonadi, phindu la kuleza mtima ndi kuchita khama mu ntchito yolalikira Ufumu ndi kupanga ophunzira n’lakuti mumapeza chimwemwe.​—Mateyu 28:19, 20.