Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kupeza Njira Yothetseratu Umphaŵi

Kupeza Njira Yothetseratu Umphaŵi

 Kupeza Njira Yothetseratu Umphaŵi

NGAKHALE kuti padziko lonse lapansi akunena zosalimbikitsa pa nkhani ya umphaŵi, anthu ena akukhulupirira kuti pali zinthu zina zimene anthu angachite polimbana ndi umphaŵi. Mwachitsanzo, mutu wa nkhani mu nyuzipepala yotchedwa Manila Bulletin unanena zimene lipoti la Asian Development Bank linafotokoza zoti “mayiko a ku Asia akhoza kuthetseratu njala m’zaka 25.” Bankili linanena kuti, kutukuka kwa zachuma ndi kumene kungachotse anthu pa umphaŵi.

Mabungwe ena ndiponso maboma akhazikitsa mfundo zambirimbiri ndi njira zosiyanasiyana pofuna kuthetsa vutoli. Zina mwa njirazi ndi izi: thumba la boma lothandiza anthu osauka, maphunziro abwino, kukhululukira ngongole zimene mayiko otukuka kumene ali nazo ku mayiko olemera, kuchotsa mfundo zokhwima zogulitsira katundu kunja kuti mayiko osauka azigulitsa katundu wawo mosavutika, ndi kumanga nyumba zotsika mtengo za anthu osauka.

M’chaka cha 2000, pamsonkhano wa United Nations General Assembly anakhazikitsa zolinga zoti azikwaniritse podzafika chaka cha 2015. Zolingazo zinaphatikizapo kuthetseratu umphaŵi wosasimbika ndi njala komanso kusiyana kwakukulu pa ndalama zimene anthu amapeza m’mayiko. Ngakhale kuti zolinga zimenezi zingakhale zabwino, anthu ambiri akukayikira ngati zingatheke m’dziko lopanda mgwirizanoli.

Mfundo Zothandiza Polimbana ndi Umphaŵi

Popeza n’zokayikitsa kuti zinthu zikhoza kusinthadi padziko lonse lapansi, kodi munthu  angachipeze kuti chithandizo? Monga tanenera kale, kulipo kumene kungapezeke nzeru zimene zingathandize anthu masiku ano. Kodi zingapezeke kuti? M’Mawu a Mulungu, Baibulo.

Kodi n’chiyani chimasiyanitsa Baibulo ndi zinthu zina zonse zimene anthu angapezeko nzeru? N’lochokera kwa Mlengi wathu amenenso ndi wolamulira wamkulu. M’mawu ake mumapezeka nzeru zapamwamba, mfundo zothandiza zimene zimagwira ntchito kwa anthu onse, padziko lonse, ndiponso nthaŵi zonse. Ngati mfundo zimenezi zitatsatiridwa, zingathandize anthu osauka kukhala ndi moyo wosangalala ngakhale panopo. Tiyeni tione zitsanzo zingapo.

Muziona Ndalama Moyenera. Baibulo limati: “Nzeru ichinjiriza monga ndalama zichinjiriza; koma kudziŵa kupambana, chifukwa nzeru isunga moyo wa eni ake.” (Mlaliki 7:12) Kodi lembali likutanthauzanji? Ndalama si yankho la zonse. N’zoonadi kuti ndalama n’zothandiza. Zimatithandiza kugula zinthu zina zimene timafuna, koma zili m’polekezera. Pali zinthu zofunika kwambiri zimene simungagule ndi ndalama. Kudziŵa mfundo imeneyi kungatithandize kuona chuma moyenera, n’kupeŵa nkhaŵa zimene anthu amene amafuna kukhala ndi ndalama zambiri amakhala nazo. Ndalama sizingagule moyo, koma kuchita zinthu mwanzeru kungateteze moyo tsopano ndiponso kungatsegule mwayi wokhala ndi moyo wosatha.

Musamafune Zimene Simungakwanitse. Zinthu zimene timakhumba n’zosiyana ndi zinthu zimene zimafunikadi pamoyo wathu. Tiyenera choyamba kusamala zinthu zofunika pamoyo wathu. Tikhoza kukhulupirira kuti tikufunika kukhala ndi chinthu chinachake, pamene kwenikweni si chinthu chofunikadi pa moyo. Munthu wanzeru amagwiritsa ntchito ndalama zimene amapeza pa zinthu zazikulu zofunikadi pamoyo​—chakudya, zovala, pogona ndi zina zotero. Kenako, asanagule kena kalikonse, amaona ngati ndalama zotsalazo zingakwane kugula zinthu zina. M’chitsanzo chimodzi cha Yesu, analimbikitsa kuti munthu aziyamba “wakhala pansi, naŵerengera mtengo wake, aone ngati ali nazo zakuimaliza.”​—Luka 14:28.

Ku Philippines, Eufrosina, yemwe akulera yekha ana ake atatu popanda bambo awo, wakhala akukumana ndi mavuto opeza zinthu zofunika pamoyo ndipo amagwiritsa ntchito ndalama mosinira kuchokera panthaŵi imene mwamuna wake anam’siya zaka zambiri zapitazo. Mwa kuchita zimenezi, iye waphunzitsa anawo kudziŵa zinthu zofunikadi kugula. Mwachitsanzo, anawo angaone chinthu chimene achikonda. M’malo mongoyankha kuti ayi, amakhala nawo pansi n’kuwauza kuti: “Chabwino, mutha kugula zimenezo ngati mukufuna, koma musankhepo. Tili ndi ndalama zoti tigule chinthu chimodzi. Tigule chinthu chimene mwachikondachi, kapena tigule nyama yochepa kapena ndiwo zamasamba zoti tikadyere mpunga kwa mlungu wathunthu. Ndiye musankha chiti? Tanenani.” Nthaŵi zambiri, anawo amaona mwamsanga mfundo yake ndipo amavomereza kuti akhale ndi chakudya m’malo mwa chinthucho.

Muzikhutira. Mfundo ina ya m’Baibulo imati: “Pokhala nazo zakudya ndi zofunda, zimenezi zitikwanire.” (1 Timoteo 6:8) Ndalama payokha sibweretsa chisangalalo. Anthu ambiri olemera si osangalala, koma anthu ambiri osauka ndi osangalala. Anthu osauka aphunzira kukhala okhutira ndi zinthu zochepa zofunikadi pamoyo. Yesu ananenapo zokhala ndi ‘diso lakumodzi’ limene limakhala lolunjika pa zinthu zofunika kwambiri. (Mateyu 6:22) Mfundoyi imathandiza munthu kukhala wokhutira. Anthu ambiri osauka ndi okhutira chifukwa chakuti ndi mabwenzi  a Mulungu ndipo ali ndi mtendere m’mabanja mwawo, zinthu zimene sangazigule ndi ndalama.

Zimenezi ndi zitsanzo zochepa chabe za mfundo zothandiza za m’Baibulo zimene zingathandize anthu osauka kuti apirire mavuto awo. Koma pali zinanso. Mwachitsanzo, peŵani makhalidwe oipa monga kusuta fodya ndi kutchova njuga, zimene zimaononga ndalama. Dziŵani zinthu zofunika kwambiri pamoyo, makamaka zinthu zauzimu. Kumene ntchito ndi yosoŵa, yesani kugwira ntchito yodzilemba nokha yochita zinthu zimene ena amazifuna. (Miyambo 22:29; 23:21; Afilipi 1:9-11) Baibulo limalimbikitsa kugwiritsa ntchito “nzeru yeniyeni ndi kulingalira” chifukwa “udzatengapo moyo.”​—Miyambo 3:21, 22.

Ngakhale kuti mfundo zopezeka m’Baibulo zingathandizeko anthu amene akulimbana ndi umphaŵi, mafunso okhudza zam’tsogolo alipobe. Kodi anthu osauka adzangokhalabe osauka mpaka kalekale? Kodi kusiyana kwa anthu olemera kwambiri ndi osauka kwambiri kudzatha? Tiyeni tione njira yothetsera vutoli imene anthu ambiri sakuidziŵa.

Baibulo Limatipatsa Chiyembekezo

Anthu ambiri amavomereza kuti Baibulo ndi buku labwino. Komabe, nthaŵi zambiri anthuŵa sazindikira kuti limafotokoza mwachindunji za kusintha kwakukulu kumene kuchitike posachedwapa.

Mulungu akufuna kuchitapo kanthu kuti athetse mavuto a anthu, kuphatikizapo umphaŵi. Mulungu akufuna kuchotsa maboma a anthu chifukwa chakuti sangathe kapenanso sakufuna kuthetsa mavutoŵa. Kodi adzachita motani zimenezi? Baibulo limafotokoza momveka bwino pa Danieli 2:44 kuti: “Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu woti sudzaonongeka ku nthaŵi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse. Nudzakhala chikhalire.”

Atachotsa “maufumu,” kapena kuti maboma ameneŵa, Wolamulira amene Mulungu anam’sankha adzachitapo kanthu. Wolamulira ameneyu si munthu ngati ifeyo koma ndi munthu wamphamvu wakumwamba wofanana ndi Mulungu, ndipo ali ndi mphamvu zotha kusintha zinthu kwambiri​—kusintha kofunika kumene kungathetse kusiyana komwe kulipo pakati pa olemera ndi osauka. Mulungu wasankha Mwana wake kuti achite zimenezi. (Machitidwe 17:31) Lemba la Salmo 72:12-14 limafotokoza zimene Wolamulira ameneyu adzachite, kuti: “Adzapulumutsa waumphaŵi wofuulayo; ndi wozunzika amene alibe mthandizi. Adzachitira nsoni wosauka ndi waumphaŵi, nadzapulumutsa moyo wa aumphaŵi. Adzaombola moyo wawo ku chinyengo ndi chiwawa; ndipo mwazi wawo udzakhala wamtengo pamaso pake.” Limeneli ndi lonjezo labwino kwambiri! Anthu adzapeza mpumulo! Wolamulira wosankhidwa ndi Mulungu adzachita zimenezi kuti athandize anthu osauka ndi aumphaŵi.

Mavuto ambiri amene amabwera chifukwa cha umphaŵi adzathetsedwa pa nthaŵi imeneyo. Vesi 16 la Salmo 72 limati: “M’dzikomo  mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pa mapiri.” Sikudzakhalanso njala chifukwa chosoŵa chakudya, ndalama, kapena chifukwa cha kusagaŵa bwino chakudya.

Mavuto ena adzathetsedwanso. Mwachitsanzo, masiku ano anthu ambiri padziko lapansili alibe nyumba yawoyawo. Komatu, Mulungu akulonjeza kuti: “Iwo adzamanga nyumba ndi kukhalamo; ndipo iwo adzawoka minda yamphesa, ndi kudya zipatso zake. Iwo sadzamanga, ndi wina kukhalamo; iwo sadzawoka, ndi wina kudya; pakuti monga masiku a mtengo adzakhala masiku a anthu anga; ndi osankhidwa anga adzasangalala nthaŵi zambiri ndi ntchito za manja awo.” (Yesaya 65:21, 22) Aliyense adzakhala ndi nyumba yake ndiponso adzasangalala ndi ntchito yake. Chotero, Mulungu akulonjeza zothetseratu umphaŵi. Sipadzakhalanso kusiyana pakati pa anthu olemera ndi osauka, ndipo anthu sadzachitanso kuvutikira kuti apeze zofunika pamoyo.

Anthu ena akangomva kumene malonjezo a Baibulo ameneŵa, amaganiza kuti n’zosatheka. Komabe, kufufuza mosamalitsa m’Baibulo kumasonyeza kuti zonse zimene Mulungu analonjeza m’mbuyomu zinachitikadi. (Yesaya 55:11) Choncho, nkhani siyakuti kaya zimenezi zidzachitikadi. Koma, funso limene muyenera kudzifunsa n’lakuti, Kodi ndiyenera kuchita chiyani kuti ndidzapindule zimenezi zikadzachitika?

Kodi Mudzakhalako?

Chifukwa chakuti boma limenelo ndi la Mulungu, tiyenera kukhala anthu amene Mulungu adzawavomereza kukhala nzika mu ulamuliro umenewo. Iye sanatisiye mu mdima osatiuza mmene tingayenerere ufumuwo. Malangizo ake ali m’Baibulo.

Wolamulira wosankhidwa, Mwana wa Mulungu, ndi wolungama. (Yesaya 11:3-5) Chotero, amene adzalandira moyo mu boma limeneli adzayenera kukhalanso anthu olungama. Miyambo 2:21, 22 amati: “Oongoka mtima adzakhala m’dziko, angwiro nadzatsalamo. Koma oipa adzalikhidwa m’dziko, achiwembu adzazulidwamo.”

Kodi pali njira ina iliyonse imene ingatithandize kukwanitsa kuchita zinthu zofunika zimenezi? Inde, ilipo. Mwa kuphunzira Baibulo ndi kugwiritsa ntchito malangizo ake, mukhoza kudzasangalala ndi moyo umenewu. (Yohane 17:3) Mboni za Yehova n’zokonzeka kukuthandizani kuti muphunzire. Tikukupemphani kuti mugwiritse ntchito mwayi umenewu kuti mudzakhale nawo m’dziko limene simudzakhala umphaŵi ndi kusoŵa chilungamo.

[Chithunzi patsamba 5]

Eufrosina: “Kugwiritsa ntchito ndalama mosinira kumathandiza banja langa kukhala ndi zinthu zofunika pamoyo”

[Zithunzi patsamba 6]

Ndalama singagule zinthu monga ubwenzi ndi Mulungu ndi mtendere m’banja