Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Munalandira Kwaulere, Patsani Kwaulere”

“Munalandira Kwaulere, Patsani Kwaulere”

“MUNALANDIRA kwaulere, patsani kwaulere.” (Mateyu 10:8) Yesu analangiza atumwi ake motero pamene anawatuma kukalalikira uthenga wabwino. Kodi atumwiwo anamvera malangizo ameneŵa? Inde, ndipo anapitiriza kutero ngakhale Yesu atachoka padziko lapansi.

Mwachitsanzo, pamene Simoni, munthu amene kale anali wamatsenga, anaona mphamvu zozizwitsa zimene mtumwi Petro ndi mtumwi Yohane anali nazo, anafuna kuwapatsa ndalama kuti am’patseko mphamvu zimenezo. Koma Petro anadzudzula Simoni pomuuza kuti: “Ndalama yako itayike nawe, chifukwa unalingirira kulandira mphatso [yaulere] ya Mulungu ndi ndalama.”​—Machitidwe 8:18-20.

Mtumwi Paulo anasonyeza mtima wofanana ndi wa Petro. Paulo akanafuna akanatha kumangokhala kuti abale ake achikristu a ku Korinto azim’pezera zonse zofunika pa moyo wake. Koma iye anagwira ntchito zolimba ndi manja ake kuti adzisamalire yekha. (Machitidwe 18:1-3) N’chifukwa chake anathadi kunena molimba mtima kuti analalikira uthenga wabwino kwa Akorinto ‘kwaulere.’​—1 Akorinto 4:12; 9:18.

N’zomvetsa chisoni kuti ambiri amene amanena kuti ndi otsatira a Kristu sanasonyeze mtima ‘wopatsa kwaulere’ ngati umenewo. Inde, ambiri a atsogoleri a chipembedzo a Matchalitchi Achikristu ‘amaphunzitsa chifukwa cha malipiro.’ (Mika 3:11) Atsogoleri ena a chipembedzo afika mpaka polemera chifukwa cha ndalama zochokera kwa nkhosa zawo. M’chaka cha 1989, mlaliki wina wa ku United States anauzidwa kuti akakhale kundende zaka 45. Chifukwa chiyani? Iye “anabera otsatira ake ndalama mamiliyoni ambiri ndipo anazigwiritsa ntchito pogulira nyumba zosiyanasiyana, magalimoto, kupita ku matchuti, ngakhale kumanga kanyumba kagalu kokhala ndi makina oziziritsa ndi kutenthetsa mpweya.”​—People’s Daily Graphic, October 7, 1989.

Ku Ghana, malinga ndi zimene inanena nyuzipepala ya Ghanaian Times ya March 31, 1990, wansembe wina wachikatolika anatenga ndalama zimene anthu anapereka m’tchalitchi n’kuziponya kumene anthuwo anakhala m’tchalitchimo. Nyuzipepalayo inati iye anatero “chifukwa chakuti, monga anthu akuluakulu, iwo anayenera kupereka ndalama zikuluzikulu.” N’zosadabwitsa kuti matchalitchi ambiri amafika mpaka polimbikitsa anthu awo kukhala adyera, kuwalimbikitsa kutchova njuga ndi kuchita zina n’zina n’cholinga choti matchalitchiwo apezepo ndalama.

Mosiyana ndi zimenezi, Mboni za Yehova zimayesetsa kutsatira chitsanzo cha Yesu ndi ophunzira ake oyambirira. Izo zilibe atsogoleri olipidwa. Wamboni aliyense ndi mtumiki amene ali ndi udindo wolalikira “uthenga . . . wabwino wa Ufumu” kwa ena. (Mateyu 24:14) Choncho, Mboni zopitirira 6,000,000 padziko lonse lapansi zikugwira ntchito yobweretsa “madzi a moyo” kwaulere kwa anthu. (Chivumbulutso 22:17) Mwa njira imeneyi, ngakhale anthu “osowa ndalama” angapindule ndi uthenga wa m’Baibulo. (Yesaya 55:1) Ngakhale kuti ndalama zoyendetsera ntchito yawo yapadziko lonse zimachokera ku zopereka zaufulu, iwo sapemphetsa ndalama. Monga atumiki oona a Mulungu, iwo ‘sachita malonda ndi mawu a Mulungu,’  koma amalankhula “moona, ngati anthu amene Mulungu anaŵatuma.”​—2 Akorinto 2:17, Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chichewa Chamakono.

Koma kodi n’chifukwa chiyani Mboni za Yehova zili zofunitsitsa kuthandiza ena pogwiritsa ntchito ndalama zawo? Kodi chimawalimbikitsa n’chiyani? Kodi kupatsa kwaulere kumatanthauza kuti iwo salandira mphoto iliyonse chifukwa cha khama lawolo?

Yankho Lotsutsa Bodza la Satana

Chimene chimalimbikitsa Akristu oona masiku ano makamaka ndi kufunitsitsa kusangalatsa Yehova, osati kudziunjikira chuma. Pochita zimenezi, amayankha bodza limene Satana Mdyerekezi ananena zaka mazana angapo zapitazo. Polankhula za munthu wolungama wotchedwa Yobu, Satana anatsutsa Yehova pofunsa kuti: “Kodi Yobu aopa Mulungu pachabe?” Satana ananena kuti Yobu anali kutumikira Mulungu kokha chifukwa chakuti Mulunguyo anali kum’tchinjiriza. Satana anati zinthu zimene Yobu anali nazo zikanangoti zithe, Yobu akanatukwana Mulungu!​—Yobu 1:7-11.

Pofuna kuthetsa nkhani imeneyo, Mulungu analola kuti Satana amuyese Yobu, ndipo anamuuza kuti: “Zonse ali nazo zikhale m’dzanja mwako.” (Yobu 1:12) Kodi n’chiyani chinachitika? Yobu anasonyeza kuti Satana ndi wabodza. Mosasamala kanthu za mavuto amene anam’gwera, Yobu anakhalabe wokhulupirika. Iye anati: “Mpaka kufa ine sinditaya ungwiro wanga.”​—Yobu 27:5, 6.

Olambira oona masiku ano amasonyeza mzimu wofanana ndi wa Yobu. Iwo satumikira Mulungu n’cholinga choti apezepo kanthu kena.

Mphatso Yaulere ya Chisomo cha Mulungu

Chifukwa china chimene chimapangitsa Akristu oona kukhala ofunitsitsa ‘kupatsa kwaulere’ n’chakuti iwowo ‘analandira kwaulere’ kuchokera kwa Mulungu. Anthu ali mu ukapolo wa uchimo ndi imfa chifukwa cha tchimo la atate athu oyambirira, Adamu. (Aroma 5:12) Mwachikondi, Yehova anakonza zoti Mwana wake adzafe imfa yansembe, chinthu chimene chinali chopweteka kwambiri kwa Mulungu. Kunena zoona, anthu sanayenerere zimenezi. Imeneyi ndi mphatso yochokera kwa Mulungu.​—Aroma 4:4; 5:8; 6:23.

N’chifukwa chake Paulo anauza Akristu odzozedwa pa Aroma 3:23, 24, kuti: “Onse anachimwa, naperewera pa ulemerero wa Mulungu; ndipo ayesedwa olungama kwaulere, ndi chisomo chake, mwa chiwombolo cha mwa Kristu Yesu.” Amene akuyembekezera kudzakhala ndi moyo kosatha padziko lapansi nawonso analandira mphatso “kwaulere.” Mphatso imeneyi imaphatikizapo mwayi wapadera woti anthu ayesedwe olungama ngati mabwenzi a Yehova.​—Yakobo 2:23; Chivumbulutso 7:14.

Nsembe ya dipo ya Kristu imatheketsanso kuti Akristu onse akhale atumiki a Mulungu. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Anandikhalitsa mtumiki wa [chinsinsi chopatulika] monga mwa mphatso [yaulere] ya chisomo cha Mulungu.” (Aefeso 3:4-7) Chifukwa chakuti anapatsidwa utumiki umenewu kudzera mwa mphatso imene sanaiyenerere ndiponso imene sakanatha kuipeza paokha, atumiki oona a Mulungu sanayembekezere kuti azilipidwanso chifukwa cholalikira za mphatso imeneyi kwa ena.

 Kodi Mphoto ya Moyo Wosatha Imalimbikitsa Mtima wa Dyera?

Kodi zimenezi zikutanthauza kuti Mulungu amafuna kuti Akristu azimutumikira popanda kuyembekezera kulandira mphoto iliyonse? Ayi, chifukwa mtumwi Paulo anauza okhulupirira anzake kuti: “Mulungu sali wosalungama kuti adzaiwala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera ku dzina lake.” (Ahebri 6:10) Ndipo Yehova si wopanda chilungamo. (Deuteronomo 32:4) M’malo mwake, Yehova ndi “wobwezera mphoto iwo akum’funa Iye.” (Ahebri 11:6) Koma kodi lonjezo la moyo wosatha m’Paradaiso sililimbikitsa mtima wadyera?​—Luka 23:43.

Chimene chimalimbikitsa Akristu oona masiku ano makamaka ndi kufunitsitsa kusangalatsa Yehova, osati kudziunjikira chuma

Ayi. Chifukwa chimodzi n’chakuti chikhumbo chokhala ndi moyo kosatha m’Paradaiso anachiyambitsa ndi Mulungu mwiniwakeyo. Ndi iyeyo amene analonjeza zimenezi kwa anthu aŵiri oyambirira. (Genesis 1:28; 2:15-17) Ndipo anakonzanso zoti ana a Adamu ndi Hava akhalebe ndi chiyembekezo chimenechi ngakhale kuti Adamu ndi Hava anataya chiyembekezo chimenechi pamene anachimwa. N’chifukwa chake Mulungu akulonjeza m’Mawu ake kuti “cholengedwa chomwe chidzamasulidwa ku ukapolo wa chivundi, ndi kuloŵa ufulu waulemerero wa ana a Mulungu.” (Aroma 8:21) Choncho, masiku ano sikulakwa kuti Akristu, monga mmene anachitira Mose kalelo, azidikirira kudzalandira mphoto. (Ahebri 11:26) Mulungu sakupereka mphoto imeneyi ngati chiphuphu. Amaipereka chifukwa chakuti iye amakondadi anthu amene amam’tumikira. (2 Atesalonika 2:16, 17) Zotsatirapo zake n’zakuti, “tikonda ife, chifukwa anayamba Iye kutikonda.”​—1 Yohane 4:19.

Cholinga Choyenera Chotumikirira Mulungu

Komabe, Akristu masiku ano ayenera kumadzipenda nthaŵi zonse kuti adziŵe cholinga chawo chotumikirira Mulungu. Pa Yohane 6:10-13, timaŵerenga kuti Yesu anadyetsa mozizwitsa khamu la anthu oposa zikwi zisanu. Izi zitachitika, anthu ena anayamba kutsatira Yesu chifukwa cha dyera basi. Yesu anawauza kuti: “Mundifuna Ine, . . . chifukwa munadya mkate, nimunakhuta.” (Yohane 6:26) Patatha zaka makumi angapo, Akristu ena odzipatulira anatumikira Mulungu koma “kosati koona.” (Afilipi 1:17) Ena amene ‘sanavomerezane nawo mawu a moyowo a Yesu Kristu’ anafika mpaka pofufuza njira zoti apeze chuma kuchokera kwa mabwenzi awo achikristu.​—1 Timoteo 6:3-5.

Masiku ano, Mkristu amene akutumikira n’cholinga chongofuna kudzakhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso akhozanso kukhala akutumikira chifukwa cha dyera. M’kupita kwa nthaŵi, zimenezi zingam’chititse kugwa mwauzimu. Chifukwa chakuti dziko la Satanali likuoneka ngati lakhalapo kwa nthaŵi yaitali kuposa mmene amaganizira, iye akhoza “kufooka” poganiza kuti mapeto akuchedwa. (Agalatiya 6:9) Mwina akhoza kukwiya kumene akaganiza za zinthu zina zakuthupi zimene anadzimana. Yesu akutikumbutsa kuti: “Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse.” (Mateyu 22:37) Zoonadi, munthu amene akutumikira Mulungu makamaka chifukwa cha chikondi saika malire pa nthaŵi yake yotumikira. Amakhala wotsimikiza kutumikira Yehova kosatha! (Mika 4:5) Sadandaula chifukwa cha zinthu zilizonse zimene anadzimana chifukwa chotumikira Mulungu. (Ahebri 13:15, 16) Chifukwa chokonda Mulungu, amaika zinthu za Mulungu poyamba m’moyo wake.​—Mateyu 6:33.

Masiku ano, olambira oona opitirira 6,000,000 ndi ‘odzipereka’ mu utumiki wa Yehova. (Salmo 110:3) Kodi inu ndinu mmodzi wa anthu ameneŵa? Ngati sindinu mmodzi wa iwo, ganizirani za zinthu zimene Mulungu akukupatsani: kumvetsetsa choonadi; (Yohane 17:3) kumasuka ku ukapolo wa ziphunzitso zonyenga zachipembedzo; (Yohane 8:32) ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo kosatha. (Chivumbulutso 21:3, 4) Mboni za Yehova zingakuthandizeni kudziŵa mmene mungalandirire zonsezi kuchokera kwa Mulungu​—kwaulere.