Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Dziŵani Mmene Mungachitire Zinthu Moganizira Ena

Dziŵani Mmene Mungachitire Zinthu Moganizira Ena

Dziŵani Mmene Mungachitire Zinthu Moganizira Ena

PEGGY anaona mwana wake wamwamuna akulankhula mawu opweteka kwa mng’ono wake. Iye anam’funsa kuti: “Kodi ukuganiza kuti imeneyo inali njira yabwino kwambiri yolankhulira ndi mbale wako? Taonatu tsopano mmene mbale wako wakwiyira.” Kodi n’chifukwa chiyani ananena zimenezi? Amafuna kuphunzitsa mwana wakeyo mmene angamachitire zinthu moganizira ena.

Mtumwi Paulo analimbikitsa Timoteo, bwenzi lake lachinyamata, kuti akhale “waulere pa onse [kapena kuti, “woganizira ena”].” Mwakutero, Timoteo akanapeŵa kukhumudwitsa ena. (2 Timoteo 2:24) Kodi kuchita zinthu moganizira ena n’kutani? Kodi ndi zinthu ziti zimene mungaongolere pa nkhani imeneyi? Ndipo kodi mungathandize bwanji ena kuti aphunzire kuchita zimenezi?

Kodi Kuchita Zinthu Moganizira Ena N’kutani?

Kuganizira ena kumatanthauza kuzindikira ngati zinthu sizili bwino n’kutha kulankhula kapena kuchita zinthu zothandiza mogwirizana ndi mmene zinthuzo zilili. Munthu woganizira ena amazindikira mmene ena akumvera ndipo amatha kudziŵa mmene mawu ake kapena zimene angachite zingawakhudzire enawo. Koma kuchita zimenezi sikuti kumangofunika luso basi, kumafunikanso kukhala wofunitsitsa kupeŵa kukhumudwitsa ena.

Mu nkhani ya m’Baibulo ya Gehazi, mtumiki wa Elisa, timapezamo chitsanzo cha munthu wosaganizira ena pochita zinthu. Mkazi wa ku Sunemu amene mwana wake wamwamuna anali atangofa kumene m’manja mwake anabwera kwa Elisa kuti adzalimbikitsidwe. Atafunsidwa ngati anthu onse anali bwino, iye anayankha kuti: “Ali bwino.” Ndipo mkaziyo atafika pafupi ndi mneneriyo, “Gehazi anayandikira kuti am’kankhe.” Koma Elisa anati: “Um’leke, pakuti mtima wake ulikumuwawa.”​—2 Mafumu 4:17-20, 25-27.

Kodi n’chifukwa chiyani Gehazi anachita zinthu mopupuluma ndi mosaganizira ena chotero? N’zoona kuti mkaziyo sanafotokoze mmene anali kumvera atafunsidwa. Koma anthu ambiri saulula mmene akumvera kwa munthu wina aliyenseyo. Ngakhale zili choncho, mosakayikira mkaziyo anasonyeza mmene anali kumvera mwa njira ina yake. Zikuoneka kuti Elisa anazindikira zimenezi, koma Gehazi sanazindikire, kapena mwina anazindikira koma mwadala sanafune kuchitapo kanthu kalikonse. Zimenezi zikusonyeza bwino chifukwa chofala chimene chimachititsa anthu kuchita zinthu mosaganizira ena. Ngati munthu akungoganiza za kufunika kwa ntchito yake, n’zosavuta kuti asaone mavuto kapena zosoŵa za anthu amene akuchita nawo zinthu. Amakhala ngati dalaivala wa basi amene amafunitsitsa kuti akafike kumene akupitako panthaŵi yake moti saima kuti atenge anthu mu msewu.

Kuti tisakhale munthu wochita zinthu mosaganizira ena ngati Gehazi, tiyenera kuwakomera mtima anthu, chifukwa sitikudziŵa mmene akumvera. Tiyenera kukhala maso kuti tithe kuona zizindikiro zimene zimasonyeza mmene munthu akumvera, ndiyeno tikaona zimenezi tizilankhula mawu olimbikitsa kapena kuchita zinthu mokoma mtima. Kodi ndi zinthu ziti zimene mungaongolere pa nkhani imeneyi?

Kuzindikira Mmene Ena Akumvera

Yesu anali katswiri pa nkhani yozindikira mmene anthu ena akumvera, n’kudziŵa njira yabwino kwambiri yowakomera mtima. Panthaŵi ina akudya m’nyumba ya Simoni, Mfarisi, mkazi amene amadziŵika m’mudzimo kuti anali “wochimwa” anafika pafupi naye. Mkaziyu, mofanana ndi wa ku Sunemu uja, sananenenso chilichonse, koma zimene anachita zinasonyeza mmene amamvera. Mkaziyo “anatenga nsupa ya alabastero ya mafuta onunkhira bwino, naimirira kumbuyo, pa mapazi a [Yesu], nalira, nayamba kukhathamiza mapazi ake ndi misozi, nawapukuta ndi tsitsi la mutu wake, nampsompsonetsa mapazi ake, nawadzoza ndi mafuta onunkhira bwino.” Yesu anazindikira tanthauzo la zonse zimene mkaziyo anachita. Ndipo ngakhale Simoni sananene chilichonse, Yesu anazindikira kuti mumtima mwake amanena kuti: “Akadakhala mneneri uyu akadazindikira ali yani, ndi wotani mkaziyo wom’khudza Iye, chifukwa ali wochimwa.”​—Luka 7:37-39.

Tangoganizirani mmene zinthu zikanaipira ngati Yesu akanakankhira mkaziyo kumbali, kapena ngati akanauza Simoni kuti: “Iwe ndiwe mbuli eti? Sungaone kuti mkazi ameneyu walapa?” M’malo mwake, Yesu mwanzeru anafotokozera Simoni fanizo la mwamuna amene anakhululukira munthu wina ngongole yaikulu ndiponso munthu wina amene anali naye ngongole yaing’ono. “Ndani wa iwo adzaposa kum’konda?” anafunsa Yesu. Choncho, m’malo mooneka ngati waipidwa ndi Simoni, Yesu anatha kumuyamikira chifukwa cha yankho lolondola limene anapereka. Ndiyeno mokoma mtima anam’thandiza Simoni kuona zizindikiro zambiri zimene mkaziyo anachita zosonyeza mmene anali kumvera komanso zosonyeza kulapa. Yesu kenaka anatembenukira kwa mkaziyo n’kumusonyeza mokoma mtima kuti akudziŵa mmene akumvera. Anamuuza kuti machimo ake akhululukidwa, ndipo kenaka anati: “Chikhulupiriro chako chakupulumutsa iwe; muka ndi mtendere.” Ndithudi mawu abwino amenewo ayenera kuti anamulimbikitsa n’kumupatsa mphamvu zoti akapitirize kuchita zabwino. (Luka 7:40-50) Yesu anatha kuchita zinthu moganizira ena chifukwa chakuti ankayang’anitsitsa kuti aone mmene anthu akumvera ndipo akadziŵa zimenezi ankachita zinthu mwachifundo.

Mofanana ndi mmene Yesu anathandizira Simoni, nafenso tikhoza kuphunzira n’kuthandizanso ena kuti azitha kuzindikira mmene munthu akumvera pongoona mmene akuonekera. Atumiki odziŵa bwino kulalikira nthaŵi zina angathe kuphunzitsa luso limeneli kwa anthu atsopano mu utumiki wachikristu. Akamaliza kulankhula ndi munthu polalikira uthenga wabwino, akhoza kukambirana za zizindikiro zimene anaziona zosonyeza mmene munthuyo amamvera. Kodi munthuyo amachita manyazi, amakayikira, ananyansidwa, kapena anali wotanganidwa? Kodi njira yabwino kwambiri yothandizira munthuyo ingakhale yotani? Akulu angathandizenso abale ndi alongo amene achita zinthu mosaganizirana ndipo akwiyitsana. Thandizani aliyense kumvetsa mmene mnzakeyo akumvera. Kodi akumva kuti wam’chitira chipongwe, sanamuganizire, kapena sanamumvetsetse? Kodi kukoma mtima kungamuthandize bwanji munthuyo kuti amvenso bwino?

Makolo angachite bwino ngati ataphunzitsa ana awo kumamva chisoni munthu wina akamavutika, chifukwa zimenezi n’zimene zingawathandize kuchita zinthu moganizira ena. Mwana wamwamuna wa Peggy, uja tinamutchula poyamba uja, anaona kuti nkhope ya mng’ono wake yasintha, wachita msunamo, ndipo akuoneka kuti akufuna kulira. Iye anazindikira kuti mbale wakeyo akumva kupweteka mumtima. Mogwirizana ndi zimene mayi ake amafuna, iye anadandaula ndi zimene anachitazo ndipo anaganiza zosintha khalidwe lake. Ana aamuna a Peggy aŵiri onsewo anagwiritsa ntchito bwino zimene anaphunzira ali ana, ndipo patapita zaka anadzakhala odziŵa bwino kupanga ophunzira ndiponso abusa abwino mu mpingo wachikristu.

Sonyezani Kuti Mukumvetsa

Kuchita zinthu moganizira ena kumafunika makamaka ngati muli ndi dandaulo ndi munthu wina. N’zosavuta kuti mum’chotsere ulemu munthu winayo. Nthaŵi zonse ndi bwino kuyamba ndi kumuyamikira pa zinthu zinazake zimene wachita. M’malo momunena, yesetsani kuthetsa vutolo. Fotokozani mmene zimene wachitazo zakukhudzirani, ndipo muuzeni chinthu chenicheni chimene mukufuna kuti asinthe. Kenaka khalani okonzeka kumvetsera. Mwina simunamumvetse mnzanuyo.

Anthu amafuna aone kuti mukumvetsa mfundo yawo ngakhale simukugwirizana nayo. Yesu analankhula mozindikira, mosonyeza kuti anali kumvetsa chifukwa chimene Marita anali kudera nkhaŵa. Iye anati: “Marita, Marita, uda nkhaŵa nuvutika ndi zinthu zambiri.” (Luka 10:41) Mofananamo, ngati munthu akulankhula za vuto linalake, m’malo momuuza zimene mukuganiza kuti zingathandize musanamvetsetse nkhaniyo, njira yanzeru yosonyeza kuti mwamvetsa nkhaniyo ndiyo kulifotokozanso vutolo kapena dandaulo lakelo m’mawu anu. Imeneyi ndi njira yabwino yosonyeza kuti mukumvetsa.

Dziŵani Zinthu Zosafunika Kunena

Pamene Mfumukazi Estere anafuna kupempha mwamuna wake kuti alepheretse chiwembu cha Hamani chofuna kupha Ayuda, iye mwanzeru anakonza zinthu m’njira yoti akamupempha mwamuna wakeyo asavute. Atatero m’pamene anaiyamba nkhani yovutayo. Koma tingaphunzireponso kanthu poona zinthu zimene sananene. Iye mwanzeru sanatchulepo mbali imene mwamuna wake anachita nawo pokonza chiwembu choipacho.​—Estere 5:1-8; 7:1, 2; 8:5.

Mofananamo, tikapita kukayendera mwamuna wosakhulupirira wa mlongo wachikristu, ndi bwino kuyamba ndi kum’funsa mwanzeru za zinthu zimene amakonda, m’malo mongofikira kum’sonyeza Baibulo. Ku Nyumba ya Ufumu kukabwera mlendo atavala zovala zosagwirizana ndi malowo kapena kukabwera munthu amene wakhala akujomba ku misonkhano kwa nthaŵi yaitali, ndi bwino kumulandira ndi manja aŵiri m’malo motchula zovala zakezo kapena kusapezeka kwake pa misonkhano kwa nthaŵi yaitali. Ndipo mukaona kuti munthu watsopano wachidwi ali ndi malingaliro olakwika, ndi bwino kupeŵa kumuongolera nthaŵi yomweyo. (Yohane 16:12) Kuchita zinthu moganizira ena kumaphatikizapo kukhala wokoma mtima mwa kudziŵa ndi kupeŵa zinthu zosafunika kunena.

Mawu Amene Amathandiza

Kudziŵa mmene mungachitire zinthu moganizira ena kudzakuthandizani kumvana kwambiri ndi ena, ngakhale pamene munthu wina sanakumvetseni bwino ndipo wakukwiyirani kwambiri. Mwachitsanzo, pamene amuna a Efraimu ‘anatsutsana kolimba’ ndi Gideoni, iye mwanzeru powayankha anafotokoza momveka bwino zimene zinachitikadi ndiponso anavomereza moona mtima zinthu zimene amuna a Efraimu anali atakwanitsa kuchita. Zimenezi zinasonyeza kuganizira ena chifukwa Gideoni anazindikira chifukwa chake anthuwo anali atapsa mtima, ndipo kudzichepetsa kwake kunawapangitsa kumvanso bwino.​—Oweruza 8:1-3; Miyambo 16:24.

Nthaŵi zonse muziyamba mwaganiza mmene ena amvere akamva zimene mukufuna kunenazo. Mukamayesetsa kuchita zinthu moganizira ena mudzakhala ndi chimwemwe chimene lemba la Miyambo 15:23 likufotokoza. Ilo limati: “Munthu akondwera ndi mayankhidwe a m’kamwa mwake; ndi mawu a pa nthaŵi yake kodi sali abwino?”

[Chithunzi patsamba 31]

Makolo angaphunzitse ana awo kuti azimvera ena chifundo

[Chithunzi patsamba 31]

Akristu odziŵa bwino kulalikira angaphunzitse atsopano kuti aziganizira ena