Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Moyo Waulemerero Potumikira Yehova

Moyo Waulemerero Potumikira Yehova

Mbiri ya Moyo wanga

Moyo Waulemerero Potumikira Yehova

YOSIMBIDWA NDI RUSSELL KURZEN

Ndinabadwa pa September 22, 1907, patatsala zaka zisanu ndi ziŵiri kuti tiloŵe m’nyengo yapadera yomwe inayamba ndi kuulika kwa nkhondo yoyamba yapadziko lonse. Banja lathu linali la mwanaalirenji pankhani yofunika kwambiri. Ndikuganiza kuti muvomerezana nane mukamva mbiri yathu mwachidule.

AGOGO aakazi a Kurzen anayamba kufunafuna choonadi ponena za Mulungu, akali kamtsikana. Asanakwanitse zaka 13, iwo anapita ku matchalitchi angapo a m’tauni yakwawo, yochititsa kaso kwambiri ya Spiez ku Switzerland. Mu 1887, patapita zaka zingapo kuchokera pamene iwo anakwatiwa, banja la a Kurzen linatsagana ndi gulu la anthu osamukira ku United States.

Banjali linakhazikika ku Ohio, komwe mu 1900, Agogo akaziwo anapeza chuma chomwe ankasakasaka. Anachipeza m’buku la Chijeremani la Charles Taze Russell lakuti The Time Is at Hand. Iwo anazindikira mofulumira kuti zomwe anaŵerenga m’bukulo zinali ndi mfundo za choonadi cha m’Baibulo. Ngakhale kuti Agogoŵa ankaŵerenga Chingelezi movutikira, iwo analembetsa kuti azilandira magazini a Chingelezi a Nsanja ya Olonda. Motero anaphunzira zambiri zokhudza choonadi cha m’Baibulo ndiponso anaphunzira Chingelezi panthaŵi imodzimodziyo. Agogo aamuna analibe chidwi ndi zinthu zauzimu monga ankachitira akazi awo.

Mwa ana 11 a Agogo a Kurzen, ana aamuna aŵiri, John ndi Adolph, ndiwo anayamikira chuma chauzimu chomwe agogo aakaziwo anapeza. A John ndiwo anali atate wanga, ndipo anabatizidwa mu 1904 ku St. Louis, Missouri, pamsonkhano wa Ophunzira Baibulo, dzina la Mboni za Yehova panthaŵiyo. Chifukwa choti Ophunzira Baibulo ambiri sanali opata kwenikweni, msonkhanowo anauika pa masiku ofanana ndi masiku a Chionetsero cha Zamalonda Chapadziko Lonse chomwe chinachitikira ku St. Louis pofuna kupezerapo mwayi pa mitengo yotsika ya sitima chifukwa cha chionetserocho. Kenako, mu 1907, Ang’ono awo a bambo anga, a Adolph, anabatizidwa pa msonkhano wa ku Niagara Falls ku New York. Bambo anga ndi ang’ono awowo analalikira mwachangu zinthu zomwe anaphunzira m’Baibulo, ndipo m’kupita kwa nthaŵi, onseŵa anakhala atumiki a nthaŵi zonse (omwe tsopano amatchedwa apainiya).

Chotero, pomwe ndinkabadwa mu 1907, banja lathu linali lolemera kale mwauzimu. (Miyambo 10:22) Ndinali khanda lenileni mu 1908 pamene makolo anga, a John ndi a Ida, anapita nane ku msonkhano wakuti “Kupita Patsogolo ku Chilakiko” wa ku Put-in-Bay ku Ohio. Joseph F. Rutherford, yemwe panthaŵiyo anali mtumiki woyendayenda ndiye anali tcheyamani wa msonkhanowo. Milungu ingapo msonkhanowu usanachitike, iye anali ku tauni ya Dalton ku Ohio, komwe anakacheza ku nyumba kwathu ndi kukamba nkhani kwa Ophunzira Baibulo a m’tauniyi.

N’zoona kuti sindikumbukira zimenezi, koma ndimakumbukira msonkhano wa m’tauni ya Mountain Lake Park ku Maryland, mu 1911. Kumsonkhanowo, ine ndi mlongo wanga wamng’ono, Esther, tinakumana ndi Charles Taze Russell, yemwe ankayang’anira ntchito yolalikira ya padziko lonse ya Ophunzira Baibulo.

Pa June 28, 1914, tsiku lomwe dziko lonse linaloŵa m’nkhondo chifukwa cha kuphedwa kwa Archduke Ferdinand ndi mkazi wake ku Sarajevo, ine ndi banja lathu tinali nawo pamsonkhano womwe unachitika mwabata mu mzinda wa Columbus ku Ohio. Kuchokera nthaŵiyo mpaka pano, ndakhala ndi mwayi wochita nawo misonkhano yambiri ya anthu a Yehova. Misonkhano ina inali ya anthu 100 okha kapena kuposerapo pang’ono. Ndipo ina inali ya khwimbi la anthu, yochitikira mu ena mwa masitediyamu akuluakulu a dziko lapansi.

Nyumba Yathu Inali Pamalo Ofunika Kwambiri

Kuchokera mu 1908 mpaka 1918, kunyumba kwathu ku Dalton, tauni yomwe inali pakati pa mizinda ya Pittsburgh ku Pennsylvania, ndi Cleveland ku Ohio, n’komwe ankachitira misonkhano yampingo waung’ono wa Ophunzira Baibulo. Nyumba yathuyo inakhala monga malo ocherezerako okamba nkhani ambiri oyendayenda. Ankamangirira akavalo ndi ngolo zawo kuseli kwa balani yathu ndi kufotokozera anthu osonkhana panyumbapo zinthu zomwe zawachitikira ndiponso zinthu zauzimu zamtengo wapatali. Inkakhalatu nthaŵi yolimbikitsa kwambiri!

Atate ankagwira ntchito yauphunzitsi, koma mtima wawo unali pa ntchito yophunzitsa, yaikulu kwambiri pa zonse, ya utumiki wachikristu. Anaonetsetsa kuti aphunzitsa banja lawo ponena za Yehova, ndipo madzulo alionse tinkapempherera pamodzi monga banja. M’ngululu ya 1919, Atate anagulitsa kavalo ndi ngolo yathu ndipo anagula galimoto yamtundu wa 1914 Ford ndi ndalama zokwana madola 175, kuti athe kulalikira anthu ambiri. Mu 1919 ndi mu 1922, banja lathu linayenda pa galimotoyi kupita ku Cedar Point, Ohio, ku misonkhano yosaiŵalika ya Ophunzira Baibulo.

Banja lathu lonse​—ine; Amayi; Atate; Esther; ndi mng’ono wanga, John​—linkachita nawo ulaliki. Ndikukumbukira nthaŵi yoyamba pamene mwininyumba anandifunsa funso la m’Baibulo. Ndinali ndi zaka zisanu ndi ziŵiri. Mwamunayo anandifunsa kuti, “Mwana iŵe, Armagedo n’chiyani?” Atate atandithandizako pang’ono, ndinatha kum’patsa yankho la m’Baibulo.

Kuyamba Utumiki Wanthaŵi Zonse

Mu 1931 banja lathu linakhala nawo pamsonkhano wa mu mzinda wa Columbus ku Ohio, komwe tinasangalala kwambiri kulandira dzina latsopano lakuti Mboni za Yehova. John anasangalala kwambiri moti anaganiza zoti iye ndi ine tiyambe ntchito ya upainiya. * Tinayambadi, ndipo nawonso Amayi, Atate ndi Esther anatero. Tinalitu ndi chuma chapadera kwambiri​—banja logwirizana pa ntchito yokoma yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu! Sinditopa kuthokoza Yehova chifukwa cha dalitso limeneli. Ngakhale kuti tinali osangalala kwambiri, zinthu zina zambiri zosangalatsa zinali kutiyembekezera.

Mu February wa 1934, ndinayamba kutumikira ku likulu la dziko lonse la Mboni za Yehova (lotchedwa Beteli) ku Brooklyn mu mzinda wa New York. John nayenso anabwera patatha milungu ingapo. Tinkakhala m’chipinda chimodzi mpaka mu 1953, pamene anakwatira mkazi wake wapamtima, Jessie.

Ine ndi John titapita ku Beteli, makolo athu anavomera kuchita upainiya m’madera osiyanasiyana a United States ndipo Esther ndi mwamuna wake, George Read, ankapita nawo. Makolo athu anachitabe upainiya mpaka pamene anamaliza moyo wawo wapadziko lapansi mu 1963. Esther ndi mwamuna wake ali ndi banja labwino, ndipo ndili ndi mbumba yomwe ndimaikonda kwambiri.

Ntchito ndi Mayanjano a pa Beteli

John anagwiritsa ntchito luso lake ndipo anathandizana ndi atumiki ena a pa Beteli, pa ntchito monga kupanga magalamafoni oyenda nawo. Mboni za Yehova zikwizikwi zinkagwiritsa ntchito magalamafoni ameneŵa polalikira ku khomo ndi khomo. John anathandizanso kulemba mapulani ndi kupanga makina okutira ndi kuika zizindikiro pa magazini omwe amatumizidwa kwa olembetsa kuti azilandira magazini.

Utumiki wanga wa pa Beteli ndinayambira komangira mabuku. Panthaŵiyo, mu fakitale munkagwira ntchito anyamata ena omwe mpaka pano akutumikirabe pa Beteli mokhulupirika. Ena mwa ameneŵa ndi Carey Barber ndi Robert Hatzfeld. Ena mwa anyamatawo, omwe ndimawakumbukira bwino, koma anamwalira, ndi monga Nathan Knorr, Karl Klein, Lyman Swingle, Klaus Jensen, Grant Suiter, George Gangas, Orin Hibbard, John Sioras, Robert Payne, Charles Fekel, Benno Burczyk, ndi John Perry. Ankagwira ntchitoyo chaka ndi chaka mosaŵiringula kapena kuyembekezera “kukwezedwa paudindo.” Komabe, ambiri mwa Akristu okhulupirika, odzozedwa ndi mzimu ameneŵa, analandira maudindo akuluakulu pamene gulu limakula. Ena mpaka anatumikira m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova.

Ndinapeza phunziro lofunika kwambiri chifukwa chogwira ntchito ndi abale odzipereka ndi mtima wonse ameneŵa. Ogwira ntchito yolembedwa amalandira malipiro a ndalama chifukwa cha zomwe achita. Mphoto yawo ndi imeneyo. Kutumikira pa Beteli kumadzetsa madalitso auzimu ochuluka kwambiri, ndipo ndi amuna ndi akazi auzimu okha omwe amazindikira ndi kusangalala kulandira mphoto yoteroyo.​—1 Akorinto 2:6-16.

Nathan Knorr, yemwe anabwera pa Beteli ali ndi zaka 18, mu 1923, anali woyang’anira ntchito ya m’fakitale mu ma 1930. Ankabwera m’fakitalemo tsiku ndi tsiku ndi kulonjera wogwira ntchito aliyense. Kusonyeza chidwi ndi anthu koteroko kunkatisangalatsa kwambiri anthu ongobwera kumene pabetelife. Mu 1936 tinalandira makina atsopano osindikizira mabuku kuchokera ku Germany, ndipo ena mwa abale achinyamata anali ndi ntchito yaikulu yolumikiza makinaŵa. Choncho, kwa nthaŵi yoposa mwezi umodzi, Mbale Knorr ankavala ovololo n’kumathandizana nawo mpaka pamene makinawo anayamba kugwira ntchito.

Mbale Knorr anali munthu wakhama pantchito moti ambirife sitinkafanana naye. Koma ankadziŵanso kupumula. Ngakhale pambuyo poti walandira udindo woyang’anira ntchito yolalikira ya pa dziko lonse ya Mboni za Yehova mu January 1942, nthaŵi zina ankaseŵera mpira wa baseball limodzi ndi banja la Beteli ndiponso limodzi ndi ophunzira a sukulu yaumishonale ya Gileadi, kusukuluyi pafupi ndi South Lansing ku New York.

Mu April 1950, banja la Beteli linasamukira ku chigawo chatsopano cha nsanjika khumi cha nyumba yathu yogonamo ya ku 124 Columbia Heights, Brooklyn ku New York. Chipinda chodyeramo chatsopano chinali chachikulu moti tonse tinkadyera pamodzi. M’kati mwa zaka zitatu zomwe nyumbayi inali kumangidwa, sitinkatha kukhala ndi pulogalamu ya kulambira kwa m’maŵa. Inalitu nthaŵi yosangalatsa kwambiri pamene pulogalamuyo inayambiranso! Mbale Knorr anandisankha kuti ndizikhala naye pa tebulo la tcheyamani n’cholinga choti ndizimukumbutsa mayina a anthu obwera kumene pa banja lathuli. Ndinkakhala pa mpando umenewo pa nthaŵi ya kulambira kwa m’maŵa ndi chakudya cha m’maŵa kwa zaka 50. Kenako, pa August 4, 2000, chipindacho chinatsekedwa ndipo anandipatsa malo mu chipinda chimodzi mwa zipinda zodyeramo zokonzedwanso pa hotela yakale ya Towers Hotel.

Kwa kanthaŵi kochepa mu ma 1950, ndinagwirapo ntchito m’fakitale. Ndinkagwira ntchito yosindikiza mabuku pogwiritsa ntchito njira yamakedzana yosindikizira ndi makina achikale a Linotype. Sindinaikonde ntchitoyi, koma William Peterson, yemwe ankayang’anira makinawo, anali munthu wabwino kwambiri moti ndinasangalalabe kugwira ntchito m’fakitalemo. Kenako, mu 1960, panafunika antchito odzifunira oti apente nyumba yogonamo yatsopano pa 107 Columbia Heights. Ndinasangalala kuthandiza nawo pokonza nyumba zatsopanozi kuti banja lathu la Beteli lomwe limakulabe lizikhalamo.

Patapita nthaŵi pang’ono, chimalizire kupenta nyumba ya 107 Columbia Heights, ndinaona ngati maloto atandipatsa ntchito yolandira alendo pa Beteli. Zaka 40 zapitazi zomwe ndatumikira monga wolandira alendo zakhala zaka zosangalatsa kwambiri kuposa nthaŵi ina iliyonse yomwe ndakhala pa Beteli. Kaya anali anthu odzacheza kapena mamembala atsopano a banja la Beteli amene ankabwera pa Beteli, kunali kosangalatsa kuona zipatso za mgwirizano wathu pofuna kuwonjezera anthu mu Ufumu wa Mulungu.

Ophunzira Akhama a Baibulo

Banja lathu la Beteli ndi lolemera mwauzimu chifukwa choti anthu ake amakonda Baibulo. Nditangobwera kumene pa Beteli, ndinafunsa Emma Hamilton, amene ankagwira ntchito yoona ngati Chingelezi chalembedwa molondola, kuti anaŵerenga kangati Baibulo lonse. Iye anayankha kuti: “Maulendo 35, kenako ndinasiya kuŵerengera.” Anton Koerber, Mkristu winanso wodalirika amene ankatumikira pa Beteli panthaŵi yofanana ndi ya Emma, ankakonda kunena kuti: “Osatalikirana ndi Baibulo.”

Mbale Russell atamwalira mu 1916, Joseph F. Rutherford anatenga udindo woyendetsa gulu wa Mbale Russell. Rutherford anali wolankhula mwamphamvu, ndiponso wodziŵa kulankhula pamaso pa anthu. Popeza anali woimira anthu pa milandu, iye analimbana ndi bwalo lamilandu la Supreme Court ku United States pamilandu ya Mboni za Yehova. Rutherford atamwalira mu 1942, Mbale Knorr anamuloŵa m’malo, ndipo anayesetsa kukulitsa luso lake lolankhula pamaso pa anthu. Chifukwa choti ndinkakhala m’chipinda choyandikana ndi chake, nthaŵi zambiri ndinkamumva akuyesezera mobwerezabwereza kukamba nkhani zake. M’kupita kwa nthaŵi, chifukwa cha khama loterolo, anakhala munthu wodziŵa kulankhula bwino pamaso pa anthu.

Mu February 1942, Mbale Knorr anathandiza kukhazikitsa dongosolo lothandiza abale tonse a pa Beteli kukulitsa luso lathu lophunzitsa ndi kulankhula. Sukuluyi inalimbikitsa kufufuza nkhani za m’Baibulo ndi kulankhula pamaso pa anthu. Poyamba, aliyense wa ife ankapemphedwa kulankhula nkhani zazifupi za anthu a m’Baibulo. Nkhani yanga yoyambirira inali yonena za Mose. Mu 1943, m’mipingo ya Mboni za Yehova munayambika sukulu yofanana ndi imeneyi ndipo ikuchitikabe mpaka pano. Mpaka lerolino, pa Beteli amalimbikitsabe kuti munthu alidziŵe bwino Baibulo ndiponso kuti akulitse luso lophunzitsa mogwira mtima.

Kalasi yoyamba ya sukulu yaumishonale ya Gileadi inayamba mu February 1943. Tsopano, kalasi ya 111 ya sukuluyi yangomaliza kumene maphunziro ake. Kwa zaka zoposa 58 kuchokera pamene inatsegulidwa, sukuluyi yaphunzitsa anthu oposa 7,000 kuti atumikire monga amishonale padziko lonse. Chochititsa chidwi n’chakuti, potsegulira sukuluyi mu 1943, padziko lonse lapansi panali Mboni za Yehova zongopitirira pang’ono 100,000. Tsopano pali anthu oposa 6,000,000 omwe akulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu!

Kuyamikira Choloŵa Changa Chauzimu

Patangotsala pang’ono kuti Gileadi ikhazikitsidwe, anthu atatu a ku Beteli anatipatsa ntchito yochezera mipingo ya mu United States. Tinkatha tsiku limodzi, masiku angapo, ngakhalenso mlungu, kulimbikitsa mipingoyo mwauzimu. Ankatitcha kuti otumikira abale, dzina lomwe kenako analisintha n’kukhala mtumiki wa dera, kapena woyang’anira dera. Patapita nthaŵi pang’ono, atatsegula Sukulu ya Gileadi, anandipempha kuti ndibwerere kukaphunzitsa nawo maphunziro ena. Ndinali mlangizi wanthaŵi zonse m’kalasi yachiŵiri mpaka yachisanu, ndiponso ndinagwirizira malo a mlangizi wina wanthaŵi zonse ndi kuphunzitsa m’kalasi ya 14. Kukhala pansi ndi ophunzira, n’kupenda nawo pamodzi zochitika zoyambirira m’mbiri yamakono ya gulu la Yehova​—zambiri mwa zomwe zinachitikazo ndinkafotokoza kuchokera pa zomwe zinandichitikira​—kunandipangitsa kuyamikira kwambiri choloŵa changa chapadera chauzimu.

Mwayi winanso wapadera womwe ndakhala nawo m’zaka zimenezi ndiwo kukhala nawo pamisonkhano ya mayiko ya anthu a Yehova. Mu 1963, ndinazungulira pa dziko lonse limodzi ndi nthumwi zina zoposa 500 kupita ku misonkhano ya “Uthenga Wabwino Wosatha.” Misonkhano ina yosaiŵalika yomwe ndinapezekapo ndi imene inachitikira m’mizinda ya Warsaw ku Poland, mu 1989; Berlin ku Germany, mu 1990; ndi Moscow ku Russia, mu 1993. Pamsonkhano uliwonse, ndinali ndi mwayi wokumana ndi ena mwa abale ndi alongo athu okondedwa omwe kwa zaka zambiri anapirira chizunzo mu ulamuliro wa Nazi, ulamuliro Wachikomyunizimu, kapena maulamuliro onse aŵiriŵa. Zimenezi zinalitu zolimbikitsa chikhulupiriro changa kwabasi!

Moyo wanga potumikira Yehova wakhaladi waulemerero! Madalitso auzimu saatha. Ndipo mosiyana ndi chuma chakuthupi, tikawoloŵa manja pogaŵira zinthu zamtengo wapatali zimenezi, chuma chathu chimawonjezeka. Nthaŵi zina ndimamva ena akunena kuti amalakalaka akanapanda kuleredwa monga a Mboni za Yehova. Ati amaganiza kuti akanayamikira kwambiri choonadi cha Baibulo ngati akanayamba akhalapo kunja kwa gulu la Mulungu.

Nthaŵi zonse, zimandipweteka kumva achinyamata akunena zimenezi chifukwa choti akamanena zimenezi, iwo amakhala akunena kuti n’kwabwino kuleredwa osadziŵa njira za Yehova. Komano, taganizani za makhalidwe onse oipa ndiponso malingaliro onse olakwika omwe anthu amafunikira kusiya akapeza choonadi cha Baibulo atakula kale. Nthaŵi zonse ndimayamikira kwambiri chifukwa choti makolo anga analera ana awo atatu m’chilungamo. John anatumikirabe Yehova mokhulupirika mpaka pa imfa yake mu July 1980, ndipo Esther adakali Mboni yokhulupirika mpaka pano.

Ndimasangalala kwambiri ndikamakumbukira ubwenzi wabwino womwe ndakhala nawo ndi abale ndi alongo okhulupirika. Tsopano ndakhala pa Beteli zaka zosangalatsa kwambiri zoposa 67. Ngakhale kuti sindinakwatirepo, ndili ndi ana auzimu, komanso ndili ndi zidzukulu zauzimu zambirimbiri. Ndipo ndimasangalala ndikalingalira za anthu onse atsopano a m’banja lathu lauzimu, lapadziko lonse, omwe sindinakumanepo nawo pakali pano, aliyense wa ameneŵa ndi wamtengo wapatali. Alidi oona mawu akuti: “Madalitso a Yehova alemeretsa”!​—Miyambo 10:22.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 16 Ndinabatizidwa pa March 8, 1932. Chotero ndinabatizidwa ataganiza kale zoti ndichite upainiya.

[Chithunzi patsamba 20]

Kuyambira kudzanja lamanzere kupita ku lamanja: atate ali ndi mchimwene wanga, John, pamiyendo, Esther, ine ndi amayi

[Zithunzi patsamba 23]

Kuphunzitsa kalasi ya Gileadi mu 1945

Pamwamba kudzanja lamanja: Alangizi a Sukulu ya Gileadi, Eduardo Keller, Fred Franz, ine, ndi Albert Schroeder

[Chithunzi patsamba 24]

Kulingalira za moyo wanga waulemerero potumikira Yehova