Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Madalitso a Yehova Alemeretsa”

“Madalitso a Yehova Alemeretsa”

 “Madalitso a Yehova Alemeretsa”

TONSEFE timafuna kudalitsidwa. Madalitso amawonjezera chimwemwe, ndi kuchititsa moyo kukhala wosangalatsa. Popeza Yehova amapereka “mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro,” madalitso enieni ndiponso okhalitsa amachokera kwa Mlengi wathu wachikondi. (Yakobo 1:17) Amapereka madalitso ambiri kwa anthu onse, ngakhale kwa amene sakum’dziŵa. Yesu ananena za Atate ake kuti: “Iye amakwezera dzuŵa lake pa oipa ndi pa abwino, namavumbitsira mvula pa olungama ndi pa osalungama.” (Mateyu 5:45) Komabe, Yehova amasamala mwapadera anthu amene amamukonda.​—Deuteronomo 28:1-14; Yobu 1:1; 42:12.

Wamasalmo analemba kuti: “Yehova . . . sadzakaniza chokoma iwo akuyenda angwiro.” (Salmo 84:11) Inde, amene akutumikira Yehova ali ndi moyo wabwino ndiponso cholinga m’moyo. Amazindikira kuti “madalitso a Yehova alemeretsa, sawonjezerapo chisoni.” Baibulo limanenanso kuti: “Iwo amene [Yehova] awadalitsa adzalandira dziko lapansi.” (Miyambo 10:22; Salmo 37:22, 29) Lidzakhalatu dalitso lalikulu limenelo!

Kodi tingatani kuti tilandire madalitso a Yehova? Tifunika kukhala ndi makhalidwe amene amam’sangalatsa. (Deuteronomo 30:16, 19, 20; Mika 6:8) Tikuona zimenezi m’zitsanzo za atumiki a Yehova atatu akale.

Yehova Amadalitsa Atumiki Ake

Nowa anali mtumiki wa Mulungu wabwino kwambiri. Pa Genesis 6:8, timaŵerenga kuti: “Nowa anapeza ufulu pamaso pa Yehova.” Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti Nowa anali womvera. Nkhaniyo imati: “Nowa anayendabe ndi Mulungu.” Nowa anatsatira mfundo zolungama zachikhalidwe za Yehova ndi kumvera malamulo ake. Panthaŵi imene dziko lapansi linadzala ndi chiwawa ndi makhalidwe oipa, Nowa ‘anachita monga mwa zonse anamlamulira iye Mulungu, momwemo anachita.’ (Genesis 6:9, 22) N’chifukwa chake Yehova anamulangiza kuti amange “chingalawa cha kupulumutsiramo iwo a m’nyumba yake.” (Ahebri 11:7) Mwa njira imeneyi, Nowa ndi banja lake anapulumuka pamene mbadwo umenewo anauwononga, ndipo mtundu wa anthu lerolino ulipo chifukwa cha iwo. Ndipo Nowa anamwalira akuyembekezera kuti adzamuukitsa ndi kukhala ndi moyo kosatha m’dziko lapansi la paradaiso. Analandiratu madalitso aakulu!

Abrahamu analinso ndi makhalidwe amene anasangalatsa Yehova. Khalidwe lake lalikulu kwambiri linali chikhulupiriro. (Ahebri 11:8-10) Abrahamu anasiya moyo wa mwanaalirenji ku Uri ndiponso kenaka ku Harana chifukwa cha kukhulupirira zimene Yehova analonjeza kuti mbewu yake idzachuluka ndipo idzadalitsa mitundu  yonse. (Genesis 12:2, 3) Ngakhale kuti anayesedwa kwa zaka zambiri, chikhulupiriro chake chinafupidwa pamene mwana wake Isake anabadwa. Kudzera mwa Isake, Abrahamu anakhala kholo la mtundu umene Mulungu anausankha, mtundu wa Israyeli, ndipo kenaka anakhala kholo la Mesiya. (Aroma 4:19-21) Ndiponso, iye ndi “kholo la onse akukhulupira,” ndipo anatchedwa “bwenzi la Mulungu.” (Aroma 4:11; Yakobo 2:23; Agalatiya 3:7, 29) Moyo wake unalitu waphindu ndipo anamudalitsadi kwambiri.

Taganizaninso za Mose, munthu wokhulupirika. Khalidwe lake lalikulu linali kuyamikira zinthu zauzimu. Mose anakana chuma cha ku Igupto ndipo “anapirira molimbika, monga ngati akuona wosaonekayo.” (Ahebri 11:27) Atakhala zaka 40 ku Midyani, anabwerera ku Igupto monga munthu wachikulire ndipo analankhula molimba mtima ndi Farao yemwe anali wolamulira wamkulu kuposa wina aliyense padziko lapansi panthaŵiyo, ndipo anamupempha kuti amasule abale ake. (Eksodo 7:1-7) Anadzionera yekha milili khumi, kugaŵikana kwa Nyanja Yofiira, ndi kuwonongedwa kwa ankhondo a Farao. Yehova anamugwiritsira ntchito kupereka Chilamulo kwa Israyeli ndiponso anakhala nkhoswe ya pangano Lake ndi mtundu watsopanowo. Mose anatsogolera mtundu wa Israyeli m’chipululu kwa zaka 40. Moyo wake unalidi ndi phindu ndipo analandira utumiki wamtengo wapatali.

Madalitso Amasiku Ano

Nkhani za anthu amene takambiranaŵa zikusonyeza kuti moyo wa anthu amene amatumikira Mulungu umakhaladi waphindu. Anthu a Yehova akamakulitsa makhalidwe monga kumvera, kukhulupirira, ndi kuyamikira zinthu zauzimu, amawadalitsa kwambiri.

Kodi akutidalitsa motani? Pamene anthu miyandamiyanda a m’Matchalitchi Achikristu akuvutika ndi njala yauzimu, ife ‘tikusonkhanira ku zokoma za Yehova.’ (Yeremiya  31:12) Kudzera mwa Yesu Kristu ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” Yehova wapereka chakudya chauzimu chochuluka chimene chikutithandiza kukhalabe mu “njirayo yakumuka nayo kumoyo.” (Mateyu 7:13, 14; 24:45; Yohane 17:3) Dalitso lina lalikulu ndilo ubale wathu wachikristu. Pamisonkhano ndiponso pa zochitika zina, kukhala pamodzi ndi olambira anzathu amene amasonyeza chikondi ndiponso amayesetsa ndi mtima wonse kuvala ‘umunthu watsopano’ kumatisangalatsa kwambiri. (Akolose 3:8-10; Salmo 133:1) Komabe, dalitso lathu lalikulu ndilo mwayi wamtengo wapatali wokhala paubale ndi Yehova Mulungu ndiponso kutsatira mapazi a Mwana wake, Kristu Yesu.​—Aroma 5:1, 8; Afilipi 3:8.

Kusinkhasinkha madalitso ameneŵa, kumatithandiza kuzindikira mmene utumiki wathu kwa Mulungu ulili wamtengo wapatali. Mwina timaganiza za fanizo la Yesu la munthu wa malonda amene anafunafuna ngale zabwino. Yesu ananena za munthuyo kuti: “Mmene anaipeza ngale imodzi ya mtengo wapatali, anapita, nagulitsa zonse anali nazo, naigula imeneyo.” (Mateyu 13:46) Ndi mmenedi timaonera ubale wathu ndi Mulungu, mwayi wamtengo wapatali wom’tumikira, ubale wathu wachikristu, chiyembekezo chathu chachikristu, ndi madalitso ena amene amabwera chifukwa cha kukhulupirira kwathu. Palibe zabwino zina zimene tingakhale nazo zoposa zimenezi.

M’bwezereni Yehova

Chifukwa chozindikira kuti Yehova amapereka mphatso iliyonse yabwino, mitima yathu imalimbikitsidwa kuyamikira madalitso amene timalandira. Kodi tingachite bwanji zimenezo? Njira imodzi ndiyo kuthandiza ena kuti nawonso apeze madalitso ngati ameneŵa. (Mateyu 28:19) M’mayiko oposa 230, Mboni za Yehova zili pakalikiliki kuchezera anansi awo ndi kuwathandiza kuti apeze madalitsoŵa. Pochita zimenezi, amagwiritsa ntchito zinthu zochepa zimene ali nazo​—nthaŵi, mphamvu, ndi chuma​—kuti athandize ena ‘kufika pozindikira choonadi.’​—1 Timoteo 2:4.

Taganizani za apainiya amene amakhala ku Glendale, California, U.S.A. Loŵeruka lililonse mmaŵa, amakalalikira ku ndende ina  kumene amayenda mtunda wa makilomita 100 kupita ndi kubwera. Ngakhale amangowalalikira akaidiwo kwa maora ochepa chabe paulendo uliwonse, iwo sagwa mphwayi. Mmodzi mwa iwo anati: “N’kopindulitsa kwambiri kutumikira m’dera lachilendo limeneli. Tikuchita zimenezi mosangalala kwambiri. Tapeza anthu achidwi ambiri moti n’kovuta kuti tilankhule ndi onse. Pakalipano tikuphunzira ndi anthu asanu, ndipo ena anayi apempha kuti tiziphunzira nawo Baibulo.”

Atumiki achikristu achangu ali osangalala kutumikira kwaulere kuti achite ntchito yopulumutsa moyo imeneyi. Amatsanzira maganizo a Yesu, yemwe anati: “Munalandira kwaulere, patsani kwaulere.” (Mateyu 10:8) Anthu miyandamiyanda padziko lonse akuchitanso chimodzimodzi. Akutumikira mopanda dyera, ndipo chifukwa cha kutumikira kwawo, namtindi wa anthu oona mtima akulabadira ndi kukhala ophunzira. M’zaka zisanu zokha zapitazo, anthu pafupifupi 1,700,000 apatulira miyoyo yawo kwa Yehova. Kuti tisamalire zosoŵa za anthu ameneŵa omwe akuchulukirachulukira, pamafunika kusindikiza mabaibulo ndi zofalitsa zothandiza kuphunzira Baibulo ndiponso kumanga Nyumba za Ufumu zatsopano ndi malo ena osonkhanira. Kodi ndalama zothandiza kuti zimenezi zipezeke zimachokera kuti? Zopereka zaufulu basi.

Anthu ambiri m’mayiko ena amavutika kuti angopezera mabanja awo zofunika zazikulu pa moyo chifukwa cha umphaŵi umene uli m’mayikowo. Malinga ndi magazini ya New Scientist, anthu okwana biliyoni imodzi amagwiritsa ntchito 70 peresenti ya ndalama zimene amapeza kugulira chakudya. Abale ndi alongo athu achikristu ambiri alinso pa umphaŵi ngati umenewo. Abale ameneŵa sangathe kupeza zinthu monga zofalitsa zachikristu kapena Nyumba ya Ufumu yabwino ngati okhulupirira anzawo sawathandiza.

Ndithudi, zimenezi sizikutanthauza kuti abale ameneŵa amangoyembekezera kuti ena aziwachitira zinthu basi. Komabe amafuna kuwathandiza. Mose, polimbikitsa Aisrayeli kuti apereke zinthu zakuthupi poyamikira madalitso a Yehova, anati: “Apereke yense monga mwa mphatso ya m’dzanja lake, monga mwa mdalitso wa Yehova Mulungu wanu anakupatsani.” (Deuteronomo 16:17) N’chifukwa chake Yesu ataona wamasiye wina akupereka “timakobiri tiŵiri” m’kachisi, anam’tamanda kwa ophunzira ake. Anachita zimene anatha. (Luka 21:2, 3) Akristunso osauka amachita zimene angathe. Ndipo zikapereŵera, zopereka za Akristu anzawo opeza bwinopo zimawathandiza.​—2 Akorinto 8:13-15.

Popereka kwa Mulungu mwa njira zimenezi, n’kofunika kukhala ndi maganizo abwino. (2 Akorinto 8:12) Paulo ananena kuti: “Yense achite monga anatsimikiza mtima, si mwa chisoni mokakamiza, pakuti Mulungu akonda wopereka mokondwerera.” (2 Akorinto 9:7) Mwa kupereka mooloŵa manja kuchokera pansi pa mtima, tonse timathandizira kuwonjezeka kwa gulu la Mulungu kumene kukuchitika ndipo zimawonjezera chimwemwe chathu.​—Machitidwe 20:35.

Kuchita nawo ntchito yolalikira ndi kupereka zaufulu ndi njira ziŵiri zimene timaperekera kwa Yehova pobwezera madalitso amene watipatsa. Ndipotu n’zolimbikitsa kudziŵa kuti Yehova akufuna kupereka madalitso ake kwa anthu ena ambiri oona mtima, amene mwina pakalipano sakum’dziŵa. (2 Petro 3:9) Ndiyetu tiyeni tipitirize kugwiritsa ntchito zinthu zimene tili nazo potumikira Mulungu kuti tipeze anthu oona mtima ndi kuwathandiza kuti akhale ndi makhalidwe ngati kumvera, chikhulupiriro, ndi kuyamikira. Mwa njira imeneyo, tidzakhala ndi chimwemwe cha kuwathandiza ‘kulaŵa ndi kuona kuti Yehova ndiye wabwino.’​—Salmo 34:8.

[Bokosi pamasamba 28, 29]

Njira Zimene Ena Amasankha Popereka Zopereka za Ntchito ya Padziko Lonse

ZOPEREKA ZA NTCHITO YA PADZIKO LONSE

Ambiri amapatula, kapena kulinganiza, ndalama zimene amaika m’mabokosi a zopereka olembedwa kuti: “Zopereka za Ntchito ya Padziko Lonse​—Mateyu 24:14.”

Mwezi uliwonse mipingo imatumiza ndalama zimenezi ku likulu la dziko lonse la Mboni za Yehova ku Brooklyn, New York, kapena ku ofesi ya nthambi yakwawo. Mungatumizenso mwachindunji ndalama zopereka modzifunira ku Accounting Office, Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, P. O. Box 30749, Lilongwe 3, Malawi, kapena ku ofesi ya nthambi ya m’dziko lanu. Mungaperekenso majuwelo kapena zinthu zina zamtengo wapatali. Tumizani pamodzi ndi kalata yachidule yofotokoza kuti zimenezo mwapereka monga mphatso yeniyeni.

MAKONZEDWE APADERA A ZOPEREKA

Ndalama zingaperekedwe pa makonzedwe apadera akuti, ngati woperekayo akuzifunanso chifukwa cha vuto linalake, adzam’bwezera zoperekazo. Kuti mudziŵe zambiri, lemberani ku Accounting Office pa adiresi imene tasonyeza pamwambapa.

KUPATSA KOLINGANIZA

Kuwonjezera pa mphatso zenizeni za ndalama ndi ndalama zoperekedwa pa makonzedwe apadera, palinso njira zina zoperekera zinthu zopititsa patsogolo utumiki wa Ufumu padziko lonse. Zimenezi zikuphatikizapo:

Inshuwalansi: Watch Tower Society ingalembetsedwe kuti ndiyo idzapatsidwe mapindu a inshuwalansi kapena penshoni.

Chuma ndi Ndalama Zoikizidwa: Chuma ndi ndalama zoikizidwa m’malonda ena zingaperekedwe kukhala za Watch Tower Society monga mphatso yeniyeni.

Malo: Malo oti atha kugulitsidwa angaperekedwe ku Watch Tower Society monga mphatso yeniyeni kapena mwa kusunga malowo amene mwiniwake angapitirizebe kukhalapo pamene ali ndi moyo. Lankhulani ndi ofesi ya nthambi ya m’dziko lanu musanakonze pangano la malo alionse.

Chuma cha Masiye: Chuma kapena ndalama zingakhale choloŵa cha Watch Tower Society kudzera m’pangano la amene adzatenga chuma cha masiye lochitidwa mwalamulo.

Ngati muli ndi chidwi ndi ena alionse mwa makonzedwe a kupatsa kolinganiza ameneŵa, lankhulani ndi a Accounting Office patelefoni kapena lemberani ku adiresi imene ili pansipa kapena ku ofesi ya Mboni za Yehova ya m’dziko lanu.

ACCOUNTING OFFICE

Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania

P. O. Box 30749,

Lilongwe 3

Telefoni: 762111