Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Tetezani Chikumbumtima Chanu

Tetezani Chikumbumtima Chanu

 Tetezani Chikumbumtima Chanu

UKANGOGANIZA zokwera ndege imene kompyuta yake ili ndi malangizo olakwika, umachita mantha. Tsono tinene kuti munthu wina wasokoneza malangizo a kaulukidwe ka ndegeyo kapena kuwalakwitsa dala malangizowo. Eya, ndi mmenenso zilili mophiphiritsa. Winawake akuyesetsa dala kuchita zomwezo ndi chikumbumtima chanu. Akufunitsitsa atawononga mtsogoleri wanuyu amene amakuthandizani pa makhalidwe abwino. Chimene akufuna n’chakuti inuyo mukaombane ndi Mulungu!​—Yobu 2:2-5; Yohane 8:44.

Kodi m’maliwongo wofuna kuwononga anzakeyu ndani? Baibulo limati ndi ‘njoka yokalambayo, iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse.’ (Chivumbulutso 12:9) Anayamba ntchito yakeyo m’munda wa Edene pamene, mwa kugwiritsa ntchito maganizo onyengerera, anakopa Hava kuti aiŵale chabwino chimene anali kuchidziŵa ndi kupandukira Mulungu. (Genesis 3:1-6, 16-19) Chiyambireni pamenepo, Satana walimbikitsa kukhazikitsa magulu achinyengo okhaokha osonkhezera anthu onse kukhala adani a Mulungu. Mwa magulu ameneŵa, lamlandu kwambiri ndi chipembedzo chonyenga.​—2 Akorinto 11:14, 15.

Chipembedzo Chonyenga Chimawononga Chikumbumtima

Baibulo ku Chivumbulutso limasonyeza kuti chipembedzo chonyenga ndi mkazi wophiphiritsa wachigololo dzina lake Babulo Wamkulu. Zimene amaphunzitsa zasokoneza chikumbumtima cha anthu ambiri ndipo zawalimbikitsa kudana ndi amene zikhulupiriro zawo n’zosiyana ndi zake ngakhale kuwachita chiwawa kumene. Ndipotu, malinga ndi Chivumbulutso, chipembedzo chonyenga chili ndi mlandu waukulu kwa Mulungu​—mlandu wa kukhetsa magazi a “onse amene anaphedwa padziko,” kuphatikizapo olambira Mulunguyo.​—Chivumbulutso 17:1-6; 18:3, 24.

Yesu anachenjeza ophunzira ake za mmene chipembedzo chonyenga chidzasokonezera miyezo ya makhalidwe ya ena. Iye anati: “Ikudza nthaŵi imene yense wakupha inu adzayesa kuti atumikira Mulungu.” Anthu achiwawa ngati amenewo ndi akhungu bwanji pankhani ya makhalidwe abwino! Yesu anati: ‘Sanadziŵa Atate, kapena Ine.’ (Yohane 16:2, 3) Yesu atangonena mawu ameneŵa, sipanapite nthaŵi anamupha. Amene analimbikitsa zimenezi ndi atsogoleri ena a chipembedzo amene chikumbumtima chawo chinagwirizana ndi umbanda wawo. (Yohane 11:47-50) Powasiyanitsa otsatira ake enieni ndi anthuwo, Yesu anati otsatira akewo amadziŵika ndi kukondana kwawo wina ndi mnzake. Ndipo chikondi chawochi ndi chachikulu zedi, pakuti chimafika ndi kwa adani awo omwe.​—Mateyu 5:44-48; Yohane 13:35.

Njira ina imene chipembedzo chonyenga chawonongera chikumbumtima cha ambiri ndiyo  kupanda kwake khalidwe kapena kulimbikitsa kwake makhalidwe ofala amtundu uliwonse. Mtumwi Paulo anati polosera zimenezi: “Idzafika nthaŵi imene sadzalola chiphunzitso cholamitsa; komatu poyabwa m’khutu adzadziunjikitsa aphunzitsi monga mwa zilakolako za iwo okha.”​—2 Timoteo 4:3.

Masiku ano, atsogoleri a chipembedzo amakanda anthu m’khutu mwawo moyabwa mwa kuwauza kuti kugonana musanakwatirane kungakhale kovomerezeka kwa Mulungu. Ena amalolera akazi okhaokha kapena amuna okhaokha kugonana. Ndipo ngakhale abusa ena amachita zomwezo. Nkhani ina m’nyuzipepala ya ku Britain ya The Times inati “abusa ogonana amuna okhaokha khumi ndi atatu odziŵika bwino” anawasankha kukhala m’Sinodi Yaikulu ya Church of England. Atsogoleri a tchalitchi akamanyanyala miyezo ya makhalidwe abwino imene ili m’Baibulo koma matchalitchi awo osawachita chilichonse, kodi nkhosa zawo zidzatsata ziti? N’chifukwa chake anthu ambiri ali osokonezekeratu.

Zimakhalatu zosangalatsa kutsogozedwa ndi mfundo za choonadi za makhalidwe abwino ndi zauzimu zimene Baibulo limaphunzitsa. (Salmo 43:3; Yohane 17:17) Mwachitsanzo, Baibulo limaphunzitsa kuti adama ndi achigololo “sadzaloŵa Ufumu wa Mulungu.” (1 Akorinto 6:9, 10) Limatiuza kuti amuna ndi akazi amene amasandutsa ‘machitidwe awo a chibadwidwe akhale machitidwe osalingana ndi chibadwidwe amachita chamanyazi’ pamaso pa Mulungu. (Aroma 1:26, 27, 32.) Mfundo za choonadi za makhalidwe abwino zimenezi sizopeka anthu opanda ungwiro ayi; ndi miyezo youziridwa ya Mulungu, imene iyeyo sanaithetse ayi. (Agalatiya 1:8; 2 Timoteo 3:16) Koma Satana alinso ndi njira zina zowonongera chikumbumtima.

Muzisankha Zosangalatsa

Inde, kusonkhezera wina kuchita choipa si nkhani yabwino ayi koma kum’chititsa kuti azilakalaka choipa ndi nkhani yoopsa. Izi ndi zimene akufuna Satana “mkulu wa dziko lapansi.” Kuti aike maganizo ake opotoka mu mtima wa opusa kapena osadziŵa​—makamaka achinyamata amene savuta kuwasokoneza​—amagwiritsa ntchito zinthu ngati mabuku oipa, mafilimu, nyimbo, maseŵera a pakompyuta, ndi zithunzi zolaula za pa Intaneti.​—Yohane 14:30; Aefeso 2:2.

“Achinyamata [ku United States] amaonera ziwawa pafupifupi 10 000 pachaka,” linatero lipoti lina m’magazini ya Pediatrics, “ndipo mapulogalamu a ana ndiwo achiwawa koposa.” Lipotilo linatinso “pachaka, achinyamata amamvera mawu, miyambi ndi njerengo zachiwerewere pafupifupi 15 000.” Ndiponso linati mapulogalamu amene ambiri amakonda kuonera “amasonyeza nkhani 8 pa ola limodzi za anthu akugonana, ndipo zimenezi zikuposa zomwe zinkachitika m’chaka cha 1976 kuŵirikiza kanayi.” N’zosadabwitsanso kuti malinga ndi lipotili, anapeza kuti “mawu otukwana nawonso akuwonjezeka kwambiri.” Anthu amaonera zimenezi ngakhale kuti Baibulo ndi maumboni ambiri a sayansi akutichenjeza kuti zimasintha anthu kukhala oipa. Chotero, ngati mukufuna kukondweretsa Mulungu ndi  kupindula, labadirani Miyambo 4:23. Lembali limati: “Tchinjiriza mtima wako koposa zonse uzisunga; pakuti magwero a moyo atulukamo.”​—Yesaya 48:17.

Nyimbo zambiri zotchuka zimawononganso chikumbumtima. Woimba wina amene nyimbo zake ndi zotchuka ndipo zili patsogolo m’mayiko ambiri a kumadzulo “amayesetsa kuchita zowanyansa anthu,” linachenjeza motero lipoti lina m’nyuzipepala ya The Sunday Mail ya ku Australia. Nkhaniyo inati “nyimbo zake zimalimbikitsa mankhwala osokoneza bongo, kugonana ndi wachibale komanso kugwirira” ndipo inati “amaimba za kupha mkazi wake ndi kutaya mtembo wake m’nyanja.” Mawu ena a nyimbo zakezo n’ngonyansa zedi moti sitingawatchulenso muno. Chodabwitsa n’chakuti iyeyo analandira mphoto yapamwamba chifukwa cha nyimbo zake. Kodi mungakonde kufesa maganizo oipa ngati amene tatchulaŵa mu mtima mwanu ngakhale amamveka okoma chifukwa chophatikizidwa m’nyimbo? Tikukhulupirira kuti simungakonde, chifukwa onse ochita zimenezo amaipitsa chikumbumtima chawo ndipo amapereka mpata woti pomaliza pake akhale ndi “mtima woipa,” ndiponso adani a Mulungu.​—Ahebri 3:12; Mateyu 12:33-35.

Chotero sankhani zosangalatsa mwanzeru. Baibulo limatilimbikitsa kuti: “Zinthu zilizonse zoona, zilizonse zolemekezeka, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zokongola, zilizonse zimveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china, zilingirireni izi.”​—Afilipi 4:8.

Mayanjano Amakhudza Chikumbumtima Chanu

Pamene Neil ndi Franz anali ana, anali ndi mayanjano abwino ndi Akristu enieni. * Koma m’kupita kwa nthaŵi, anatero Neil, “ndinayamba kuyanjana ndi mabwenzi oipa.” Mapeto ake anachita zaupandu, anaponyedwa m’ndende ndipo akunong’oneza bondo. N’zimene zinachitikiranso Franz. Iye anadandaula kuti: “Ndinkaganiza kuti nditha kuyanjana ndi achinyamata a kudziko ndipo sangandisinthe. Koma malinga ndi zimene Agalatiya 6:7 amanena, ‘Mulungu sanyozeka; pakuti chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta.’ Zinthu zitandivuta m’pamene ndinadziŵa kuti wolakwa ndine osati Yehova ayi. Moyo wanga wonse ndidzakhala m’ndende chifukwa cha mlandu umene ndinachita.”

Sikuti anthu ngati Neil ndi Franz amayamba zaupandu kamodzi n’kamodzi ayi; poyamba sangaganize n’komwe kuchita zimenezo. Amayamba kuloŵerera pang’onopang’ono, ndipo amayamba ndi mayanjano oipa. (1 Akorinto 15:33) Akatero angayambe mankhwala osokoneza bongo kapena kumwa moŵa mwauchidakwa. Ena anenapo zoti chikumbumtima ndiyo “mbali ya munthu imene imasungunuka m’moŵa” ndipo zimenezi n’zoona. Zikangotero, basi munthu amakhala woti akhoza kuchita zaupandu kapena chiwerewere mosavuta.

Nanga n’kuwayambiranji mavutowo? Musatero, koma yanjanani ndi anthu anzeru amene  amakondadi Mulungu. Iwo adzakuthandizani kulimbikitsa chikumbumtima chanu kuti chizikutsogolerani bwino, ndipo mudzapeŵa zovuta zambiri. (Miyambo 13:20) Ngakhale Neil ndi Franz akali m’ndende, iwo tsopano amaona chikumbumtima chawo kukhala mphatso yochokera kwa Mulungu; chofunika kuchiphunzitsa bwino komanso kuchisamala. Ndiponso akulimbikira kuti amange ubale wolimba ndi Yehova, Mulungu wawo. Khalani anzeru, ndipo mutengerepo phunziro pa zolakwa zawo.​—Miyambo 22:3.

Chisamaleni Chikumbumtima Chanu

Tikamakulitsa kukonda kwathu Mulungu ndi kum’khulupirira komanso kumuopa moyenera, timasonyeza kuti tikufuna kuchisamala chikumbumtima chathu. (Miyambo 8:13; 1 Yohane 5:3) Baibulo limasonyeza kuti ngati chikumbumtima chilibe zinthu zimenezi, chimakhala chosalimba pankhani ya makhalidwe. Mwachitsanzo, Salmo 14:1 limanena za anthu amene mu mtima mwawo amati: “Kulibe Mulungu.” Kodi kupanda kwawo chikhulupiriro koteroko kumakhudza bwanji khalidwe lawo? Vesiyo ikupitiriza kuti: “Achita zovunda, achita ntchito zonyansa.”

Anthu opanda chikhulupiriro mwa Mulungu alibenso chiyembekezo cholimba chakuti zinthu zidzakhala bwino kutsogolo. Choncho, amangokhala ndi moyo wofuna zalero zokha, ndipo amaloŵerera m’zilakolako zawo za thupi. Maganizo awo n’ngakuti: “Tidye timwe pakuti maŵa timwalira.” (1 Akorinto 15:32) Koma amene mtima wawo uli pa mphoto ya moyo wosatha sakopeka ndi zosangalatsa za dzikoli zakanthaŵi chabe. Chikumbumtima chawo chophunzitsidwa bwino, monga kompyuta yolondola youlutsira ndege, chimawathandiza kukhalabe panjira yokhulupirika ndi yomvera Mulungu.​—Afilipi 3:8.

Kuti chikumbumtima chanu chikhalebe cholimba ndi cholondola, chifunikira kutsogozedwa ndi Mawu a Mulungu nthaŵi zonse. Baibulo limatiuza kuti utsogoleri ngati umenewo ulipo pamene limanena mophiphiritsa kuti: “Makutu ako adzamva mawu kumbuyo kwa iwe akuti, Njira ndi iyi, yendani inu m’menemo: potembenukira inu kulamanja, ndi potembenukira kulamanzere.” (Yesaya 30:21) Ndiye muzipatula nthaŵi yoŵerenga Baibulo tsiku lililonse. Zimenezi zidzakuthandizani ndi kukulimbikitsani pamene mukuyesetsa kuchita chabwino kapena mukakhala ndi nkhaŵa yaikulu. Dziŵani kuti ngati mum’khulupirira Yehova ndi mtima wonse, azikutsogolerani pankhani ya makhalidwe ndi ya uzimu. Inde, tengerani chitsanzo wamasalmo yemwe analemba kuti: “Ndaika Yehova patsogolo panga nthaŵi zonse: popeza ali pa dzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka.”​—Salmo 16:8; 55:22.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 16 Tasintha mayina.

[Zithunzi patsamba 5]

Chipembedzo chonyenga, chimene Baibulo limati ndi “Mkazi Wachigololo,” chili ndi mlandu wophetsa chikumbumtima cha anthu ambiri

[Mawu a Chithunzi]

Wansembe akudalitsa asirikali: Chithunzithunzi cha U.S. Army

[Zithunzi patsamba 6]

Kuonera chiwawa ndi chiwerewere kumawononga chikumbumtima chanu

[Chithunzi patsamba 7]

Chikumbumtima chanu chikamatsogozedwa ndi Mawu a Mulungu nthaŵi zonse chidzakhala chotetezeka