Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova Ndi Mulungu Woleza Mtima

Yehova Ndi Mulungu Woleza Mtima

 Yehova Ndi Mulungu Woleza Mtima

“Yehova, Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka.”​—EKSODO 34:6.

1, 2. (a) Kodi ndani amene anapindula ndi kuleza mtima kwa Yehova m’nthaŵi zakale? (b) Kodi kuleza mtima kumatanthauza chiyani?

ANTHU a m’nthaŵi ya Nowa, Aisrayeli amene anali kuyenda m’chipululu ndi Mose, Ayuda amene anali ndi moyo panthaŵi imene Yesu anali padziko lapansi​—onseŵa anakumana ndi zochitika zosiyanasiyana. Koma onse anapindula ndi khalidwe lachifundo la Yehova la kuleza mtima. Ena mwa anthu ameneŵa anapulumuka chifukwa cha khalidwe limeneli. Ndipo ifenso tingapulumuke chifukwa cha kuleza mtima kwa Yehova.

2 Kodi kuleza mtima n’chiyani? Kodi Yehova amaleza mtima panthaŵi iti, ndipo chifukwa chiyani? Kuleza mtima kumatanthauza kulolera pamene wina watilakwira kapena kutiputa dala ndiponso kusataya mtima poganiza kuti sizitheka kubwezeretsa ubale umene wawonongeka. Motero, khalidwe limeneli lili ndi cholinga. Limaganizira makamaka ubwino wa munthu amene wachititsa kuti pakhale kusagwirizana. Komabe, kuleza mtima sikutanthauza kulekerera zolakwa. Kuleza mtima kukakwaniritsa cholinga chake, kapena ngati palibe chifukwa chopitirizira kulolera zimene zachitikazo, kuleza mtima kumatha.

3. Kodi kuleza mtima kwa Yehova kuli n’cholinga chotani, ndipo kudzalekeza pati?

3 Ngakhale kuti anthu angaleze mtima, Yehova ndiye chitsanzo chachikulu cha khalidwe limeneli. Kwa zaka zambiri kuyambira pamene uchimo unasokoneza ubale wa Yehova ndi anthu amene anawalenga, Mlengi wathu waleza mtima. Ndiponso, wakonza njira yakuti anthu olapa akhale naye paubale. (2 Petro 3:9; 1 Yohane 4:10) Koma pamene kuleza mtima kwake kudzakwaniritsa cholinga chake, Mulungu adzalanga anthu amene akuchita zoipa mwadala ndipo adzawononga dongosolo loipa limene lilipoli.​—2 Petro 3:7.

N’kogwirizana ndi Makhalidwe Aakulu a Mulungu

4. (a) Kodi lingaliro la kuleza mtima amalifotokoza motani m’Malemba Achihebri? (Onaninso mawu a m’munsi.) (b) Kodi mneneri Nahumu anafotokoza kuti Yehova ndi wotani, ndipo zimenezo zikuvumbula chiyani za kuleza mtima Kwake?

4 M’Malemba Achihebri, lingaliro la kuleza mtima amalifotokoza m’mawu aŵiri a Chihebri amene tanthauzo lake lenileni ndilo “utali wa mphuno” ndipo m’Baibulo la New World Translation * mawuŵa anawamasulira kuti “kusakwiya msanga.” Mneneri Nahumu pofotokoza za kuleza mtima kwa Mulungu anati: “Yehova ndiye wolekerera mkwiyo, koma wa mphamvu yaikulu; ndi wosamasula ndithu wopalamula.” (Nahumu 1:3) Motero, kuleza mtima kwa Yehova sikutanthauza kuti alibe mphamvu ndiponso kuti kulibe malire. Mfundo yakuti Mulungu wamphamvuyonse ndi wosakwiya msanga komanso ndi wamphamvu yaikulu ikusonyeza kuti kuleza mtima kwake kuli ndi cholinga. Ali ndi mphamvu ya kulanga, koma amasiya dala kuchita zimenezo mwamsanga n’cholinga choti wolakwayo akhale ndi mpata woti asinthe. (Ezekieli 18:31, 32) Choncho, kuleza mtima kwa Yehova kumasonyeza chikondi chake ndiponso  kumasonyeza kuti amagwiritsa ntchito mphamvu zake mwanzeru.

5. Kodi kuleza mtima kwa Yehova n’kogwirizana motani ndi chilungamo chake?

5 Kuleza mtima kwa Yehova n’kogwirizananso ndi chilungamo chake. Anadzidziŵikitsa kwa Mose monga “Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza [“woleza mtima,” King James Version], ndi wa ukoma mtima wochuluka, ndi wa choonadi.” (Eksodo 34:6) Patapita zaka, Mose anaimba motamanda Yehova kuti: “Njira zake zonse ndi chiweruzo; Mulungu wokhulupirika ndi wopanda chisalungamo; iye ndiye wolungama ndi wolunjika.” (Deuteronomo 32:4) Inde, chifundo cha Yehova, kuleza mtima kwake, chilungamo chake, ndi kulunjika kwake zimakwaniritsa cholinga chimodzi mogwirizana.

Kuleza Mtima kwa Yehova Chigumula Chisanachitike

6. Kodi ndi umboni waukulu uti wa kuleza mtima umene Yehova wasonyeza kwa ana a Adamu ndi Hava?

6 Kupanduka kwa Adamu ndi Hava mu Edene kunawononga ubale wamtengo wapatali umene anali nawo ndi Mlengi wawo wachikondi, Yehova. (Genesis 3:8-13, 23, 24) Kupanduka kumeneku kunakhudza ana awo, amene analandira uchimo, kupanda ungwiro, ndi imfa. (Aroma 5:17-19) Ngakhale kuti anthu aŵiri oyambawo anachimwa mwadala, Yehova anawalola kuti abereke ana. Kenaka, anapereka mwachikondi njira yakuti ana a Adamu ndi Hava ayanjane naye. (Yohane 3:16, 36) Mtumwi Paulo anafotokoza kuti: “Mulungu atsimikiza kwa ife chikondi chake cha mwini yekha mmenemo, kuti pokhala ife chikhalire ochimwa, Kristu adatifera ife. Ndipo tsono popeza [t]inayesedwa olungama ndi mwazi wake, makamaka ndithu tidzapulumuka mkwiyo wa Mulungu mwa iyeyo. Pakuti ngati, pokhala ife adani ake, tinayanjanitsidwa ndi Mulungu mwa imfa ya Mwana wake, makamaka ndithu, popeza ife tayanjanitsidwa, tidzapulumuka ndi moyo wake.”​—Aroma 5:8-10.

7. Kodi Yehova analeza mtima motani Chigumula chisanachitike, ndipo n’chifukwa chiyani kuwononga mbadwowo kunali koyenera?

7 Kuleza mtima kwa Yehova kunaoneka m’nthaŵi ya Nowa. Zaka zoposa 100 Chigumula chisanachitike, “Mulungu anaona dziko lapansi, ndipo taonani, linavunda; pakuti anthu onse anavunditsa njira yawo pa dziko lapansi.” (Genesis 6:12) Komabe, Yehova analeza nawo mtima kwa nthaŵi yokhala ndi malire. Iye anati: “Mzimu wanga sudzakangana ndi anthu nthaŵi zonse, chifukwa iwonso ndiwo thupi lanyama: koma masiku ake adzakhala zaka zana limodzi kudza makumi aŵiri.” (Genesis 6:3) Zaka 120 zimenezo zinapereka mpata woti Nowa abeleke ana ndiponso amange chingalawa  ndi kuchenjeza anthu a m’nthaŵi yake za kubwera kwa Chigumula pamene Mulungu anamuuza kuti atero. Mtumwi Petro analemba kuti: “Kuleza mtima kwa Mulungu kunalindira, m’masiku a Nowa, pokhala m’kukonzeka chingalawa, m’menemo owerengeka, ndiwo amoyo asanu ndi atatu, anapulumutsidwa mwa madzi.” (1 Petro 3:20) Inde, amene sanali a m’banja la Nowa “sanadziŵa kanthu” pamene iye anali kulalikira. (Mateyu 24:38, 39) Koma mwa kuuza Nowa kuti amange chingalawa ndi kutumikira mwina kwa zaka makumi angapo monga “mlaliki wa chilungamo,” Yehova anapatsa anthu a m’nthaŵi ya Nowa mpata waukulu woti alape ndi kusiya zochita zawo zachiwawa ndi kuyamba kum’tumikira Iye. (2 Petro 2:5; Ahebri 11:7) Motero m’kupita kwa nthaŵi chinali chilungamo chokhachokha kuwononga mbadwo woipawo.

Kuleza Mtima Kwakukulu Kumene Anasonyeza kwa Aisrayeli

8. Kodi Yehova anasonyeza motani kuleza mtima ku mtundu wa Israyeli?

8 Yehova analeza nawo mtima Aisrayeli kwa nthaŵi yaitali kuposa zaka 120. Kwa zaka zonse zoposa 1,500 za mbiri yawo monga anthu amene Mulungu anawasankha, iwo nthaŵi zambiri anayesa kuleza mtima kwa Mulungu mpaka pamapeto. Patangopita milungu yochepa chabe kuchokera pamene anawalanditsa mozizwitsa ku Igupto, iwo anayamba kulambira mafano, kusonyeza poyera kusalemekeza Mpulumutsi wawo. (Eksodo 32:4; Salmo 106:21) M’zaka zotsatira, Aisrayeli anadandaula ndi chakudya chimene Yehova anali kuwapatsa mozizwitsa m’chipululu, anadandaula ndi ulamuliro wa Mose ndi Aroni, anatsutsana ndi Yehova, ndipo anachita dama ndi anthu akunja, ngakhalenso kulambira nawo Baala. (Numeri 11:4-6; 14:2-4; 21:5; 25:1-3; 1 Akorinto 10:6-11) Yehova akanatha kuwawononga anthu akewo ndipo chikanakhala chilungamo kuchita zimenezo, koma m’malo mwake analeza mtima.​—Numeri 14:11-21.

9. Kodi Yehova anasonyeza motani kuti ndi Mulungu woleza mtima m’nthaŵi ya Oweruza ndi m’nthaŵi imene mafumu anali kulamulira?

9 M’nthaŵi ya Oweruza, Aisrayeli anali kulambira mafano mobwerezabwereza. Akachita zimenezo, Yehova anali kuwasiya kuti adani awo awagonjetse. Koma akalapa ndi kum’pempha kuti awathandize, iye anali kuleza mtima ndi kusankha oweruza kuti awapulumutse. (Oweruza 2:17, 18) Kwa nthaŵi yaitali imene mafumu anali kulamulira, mafumu ochepa okha ndi amene analambira Yehova mosagaŵanika. Ndipo ngakhale pamene mfumu imene inali kulamulira inali yokhulupirika, anthu nthaŵi zambiri anali kuphatikiza kulambira koona ndi konyenga. Yehova akatumiza aneneri kuti akawachenjeze za kusakhulupirika kwawo, anthu nthaŵi zambiri ankakonda kumvetsera ansembe akatangale ndi aneneri onyenga m’malo momvetsera aneneri oona a Mulungu. (Yeremiya 5:31; 25:4-7) Ndipotu, Aisrayeli anali kuzunza aneneri okhulupirika a Yehova ngakhalenso kupha kumene ena mwa iwo. (2 Mbiri 24:20, 21; Machitidwe 7:51, 52) Komabe, Yehova anapitiriza kuleza mtima.​—2 Mbiri 36:15.

Kuleza Mtima kwa Yehova Sikunathe

10. Kodi ndi liti pamene kuleza mtima kwa Yehova kunafika pamapeto?

10 Komabe, zimene zinachitika zikusonyeza  kuti kuleza mtima kwa Mulungu kuli ndi malire. Mu 740 B.C.E., iye analola kuti Asuri awononge ufumu wa Israyeli wa mafuko khumi ndi kuwatengera anthuwo ku ukapolo. (2 Mafumu 17:5, 6) Ndiponso analola kuti Ababulo agonjetse ufumu wa Yuda wa mafuko aŵiri ndi kuwononga Yerusalemu ndi kachisi wake mu 607 B.C.E.​—2 Mbiri 36:16-19.

11. Kodi Yehova anasonyeza motani kuleza mtima ngakhale pamene anali kuweruza?

11 Komabe, Yehova sanaiwale kukhala woleza mtima ngakhale pamene anali kuweruza Israyeli ndi Yuda. Iye ananeneratu kudzera mwa mneneri wake Yeremiya kuti adzabwezeretsa anthu ake osankhika. Anati: “Zitapita zaka makumi asanu ndi aŵiri pa Babulo, ndidzakuyang’anirani inu, ndipo ndidzakuchitirani inu mawu anga abwino, ndi kubwezera inu kumalo kuno. Ndipo ndidzapezedwa ndi inu, . . . ndidzabwezanso undende wanu, ndipo ndidzasonkhanitsa inu kwa mitundu yonse, ndi kumalo konse kumene ndinakupitikitsirani inu.”​—Yeremiya 29:10, 14.

12. Kodi kubwerera kwa Ayuda otsalira ku dziko la kwawo kunasonyeza motani kuti Mulungu ndi amene anakutsogolera poganizira za kubwera kwa Mesiya?

12 Ayuda otsala amene anali ku ukapolo anabwereradi ku dziko lakwawo ndi kuyambanso kulambira Yehova pa kachisi amene anam’manganso mu Yerusalemu. Pokwaniritsa zolinga za Yehova, otsalira ameneŵa anali oti adzakhale ngati “mame ochokera kwa Yehova,” omwe adzatsitsimula ndi kupititsa zinthu patsogolo. Anali oti adzakhalenso olimba mtima ndi a mphamvu ngati “mkango mwa nyama zakuthengo.” (Mika 5:7, 8) Mawu omalizaŵa ayenera kuti anakwaniritsidwa m’nthaŵi ya Amakabeo. Panthaŵi imeneyo Ayuda motsogozedwa ndi banja la Amakabeo anathamangitsa adani awo m’Dziko Lolonjezedwa ndi kupatuliranso kachisi amene anawonongeka. Motero, dzikolo ndi kachisi zinasungika kuti otsalira ena okhulupirika adzalandire Mwana wa Mulungu podzaonekera ku dzikolo monga Mesiya.​—Danieli 9:25; Luka 1:13-17, 67-79; 3:15, 21, 22.

13. Kodi Yehova anapitiriza motani kuleza nawo mtima Ayuda ngakhale pamene anapha Mwana wake?

13 Ngakhale pamene Ayuda anapha Mwana wake, Yehova anapitiriza kuleza nawo mtima kwa zaka zina zitatu ndi theka. Anawapatsa mpata wokwanira woti aitanidwe kuti akhale nawo m’mbewu yauzimu ya Abrahamu. (Danieli 9:27) * Chaka cha 36 C.E chisanafike ndiponso pambuyo pake, Ayuda ena anamvera kuitana kumeneku, ndipo motero, monga mmene kenaka Paulo ananenera, ‘panapezeka otsalira monga mwa kusankha kwa chisomo.’​—Aroma 11:5.

14. (a) Kodi mwayi wokhala nawo m’mbewu yauzimu ya Abrahamu anauperekanso kwa yani mu 36 C.E.? (b) Kodi Paulo anafotokoza motani malingaliro ake a mmene Yehova amasankhira ena mwa anthu amene adzapange Israyeli wauzimu?

14 Mu 36 C.E., mwayi wamtengo wapatali wokhala nawo m’mbewu yauzimu ya Abrahamu anaupereka kwa nthaŵi yoyamba kwa anthu ena omwe sanali Ayuda kapena otembenukira ku Chiyuda. Yehova anasonyeza chisomo ndi kuleza mtima kwa onse amene anamvera. (Agalatiya 3:26-29; Aefeso 2:4-7) Paulo, poyamikira  nzeru ndi cholinga cha kuleza mtima kwachifundo kwa Yehova, kumene kumam’chititsa kupeza anthu onse amene wawaitana kudzaza Israyeli wauzimu, anafuula kuti: “Ha! kuya kwake kwa kulemera ndi kwa nzeru ndi kwa kudziŵa kwake kwa Mulungu! Osasanthulikadi maweruzo ake, ndi njira zake n’zosalondoleka!”​—Aroma 11:25, 26, 33; Agalatiya 6:15, 16.

Kuleza Mtima Chifukwa cha Dzina Lake

15. Kodi chifukwa chachikulu chimene chimachititsa Mulungu kuleza mtima n’chiti, ndipo ndi nkhani iti imene inafuna kuti papite nthaŵi yokwanira kuti aithetse?

15 N’chifukwa chiyani Yehova amaleza mtima? Chifukwa chachikulu ndicho kukweza dzina lake loyera ndi kutsimikizira kuti iye ndiye woyenera kulamulira. (1 Samueli 12:20-22) Nkhani imene Satana anadzutsa yokhudza mmene Yehova amagwiritsira ntchito ulamuliro Wake inafuna kuti papite nthaŵi yokwanira kuti aithetse mogwira mtima pamaso pa chilengedwe chonse. (Yobu 1:9-11; 42:2, 5, 6) N’chifukwa chake, pamene anthu ake anali kuzunzidwa ku Igupto, Yehova anauza Farao kuti: “Chifukwa chake ndakuimika kuti ndikuonetse mphamvu yanga, ndi kuti alalikire dzina langa pa dziko lonse lapansi.”​—Eksodo 9:16.

16. (a) Kodi kuleza mtima kwa Yehova kunathandiza motani kutenga anthu a dzina lake? (b) Kodi Yehova adzayeretsa bwanji dzina lake ndi kutsimikizira kuti Iye ndiye woyenera kulamulira?

16 Mtumwi Paulo, pofotokoza kufunika kwa kuleza mtima kwa Mulungu pokweza dzina Lake lopatulika, anagwira mawu amene Yehova ananena kwa Farao. Ndiyeno analemba kuti: “Ndipo titani ngati Mulungu, pofuna iye kuonetsa mkwiyo wake, ndi kudziŵitsa mphamvu yake, analekerera ndi chilekerero chambiri zotengera za mkwiyo zokonzekera chiwonongeko? Ndi kuti iye akadziŵitse ulemerero wake waukulu pa zotengera zachifundo, zimene iye anazikonzeratu kuulemerero, ndi ife amenenso iye anatiitana, si a mwa Ayuda okhaokha, komanso a mwa anthu amitundu? Monga atinso mwa Hoseya, Amene sanakhala anthu anga, ndidzawatcha anthu anga.” (Aroma 9:17, 22-25) Yehova anatha kutenga “anthu a dzina lake” mwa amitundu chifukwa cha kuleza mtima kwake. (Machitidwe 15:14) Motsogozedwa ndi Mtsogoleri wawo, Yesu Kristu, “opatulika” ameneŵa adzakhala mafumu  a Ufumu umene Yehova adzaugwiritsa ntchito kuyeretsa dzina Lake lalikulu ndi kutsimikizira kuti Iye ndi woyenera kulamulira.​—Danieli 2:44; 7:13, 14, 27; Chivumbulutso 4:9-11; 5:9, 10.

Kuleza Mtima kwa Yehova Kumapulumutsa

17, 18. (a) Kodi mosadziŵa tingakhale tikuimba mlandu Yehova chifukwa cha kuleza mtima kwake ngati tichita chiyani? (b) Kodi tikulimbikitsidwa kukuona motani kuleza mtima kwa Yehova?

17 Kuyambira pamene anthu anachimwa momvetsa chisoni mpaka pano, Yehova wadzionetsera kuti ndi Mulungu woleza mtima. Kuleza mtima kwake Chigumula chisanachitike kunapereka mpata woti anthu achenjezedwe ndi kukonza njira yopulumukira. Koma kuleza mtima kwake kunafika pamapeto, ndipo Chigumula chinachitika. N’chimodzimodzinso lerolino. Yehova akuleza mtima kwambiri ndipo kuleza mtima kwakeko kukutenga nthaŵi yaitali kuposa mmene ena ankayembekezera. Komabe, chimenecho si chifukwa chotayira mtima. Kuchita zimenezo kungafanane ndi kuimba mlandu Mulungu chifukwa cha kuleza mtima kwake. Paulo anafunsa kuti: “Upeputsa kodi kulemera kwa ubwino wake, ndi chilekerero ndi chipiriro chake, wosadziŵa kuti ubwino wa Mulungu ukubwezera kuti ulape?”​—Aroma 2:4.

18 Palibe amene angadziŵe kuti ndi kuleza mtima kwa Mulungu kwakukulu motani kumene tikufunikira kuti tidzapulumuke. Paulo akutilangiza ‘kugwira ntchito yake ya chipulumutso chathu ndi mantha, ndi kunthunthumira.’ (Afilipi 2:12) Mtumwi Petro analembera Akristu anzake kuti: ‘Ambuye sazengereza nalo lonjezano, monga ena achiyesa chizengerezo; komatu aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena awonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.’​—2 Petro 3:9.

19. Kodi tingapindule motani ndi kuleza mtima kwa Yehova?

19 Motero, tiyeni tikhale oleza mtima ndi mmene Yehova akuchitira zinthu. Tiyeni titsatire langizo lina la Petro lakuti ‘tiyese kulekerera kwa Ambuye wathu chipulumutso.’ Chipulumutso cha yani? Chathu ndiponso cha anthu osaŵerengeka amene akufunabe kumva ‘uthenga wabwino wa Ufumu.’ (2 Petro 3:15; Mateyu 24:14) Zimenezi zitithandize kuyamikira mmene Yehova wasonyezera kuleza mtima mwachifundo ndipo zitichititse ifenso kuleza mtima kwa ena.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 M’Chihebri, “liwu lakuti “mphuno” (ʼaph) nthaŵi zambiri amaligwiritsa ntchito mophiphiritsa kutanthauza mkwiyo. Amatero chifukwa cha kupuma kwa wefuwefu kwa munthu woti wapsa mtima kwambiri.

^ ndime 13 Onani buku lakuti Samalani Ulosi wa Danieli! lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova pa masamba 191-4. Pamenepo tinafotokoza mwatsatanetsatane ulosi umenewu.

Kodi Mungafotokoze?

• Kodi m’Baibulo “kuleza mtima” kumatanthauza chiyani?

• Kodi Yehova analeza mtima motani Chigumula chisanachitike, ukapolo wa ku Babulo utatha, ndi m’zaka za zana loyamba C.E.?

• Kodi chifukwa chachikulu chimene Yehova wasonyezera kuleza mtima n’chiti?

• Kodi tiyenera kuona motani kuleza mtima kwa Yehova?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 9]

Kuleza mtima kwa Yehova Chigumula chisanachitike kunapatsa anthu mpata wokwanira woti alape

[Chithunzi patsamba 10]

Babulo atagwa, Ayuda anapindula ndi kuleza mtima kwa Yehova

[Chithunzi patsamba 11]

M’zaka za zana loyamba, Ayuda ndi anthu omwe sanali Ayuda anapindula ndi kuleza mtima kwa Yehova

[Zithunzi patsamba 12]

Akristu lerolino amapindula ndi kuleza mtima kwa Yehova