Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Thandizo Lofunika Kuti Mumvetse Baibulo

Thandizo Lofunika Kuti Mumvetse Baibulo

Thandizo Lofunika Kuti Mumvetse Baibulo

BAIBULO ndi buku lapadera kwambiri. Olemba ake amati anauziridwa ndi Mulungu ndipo nkhani zake zimachitiradi umboni wakuti zimenezo n’zoona. (2 Timoteo 3:16) Mwa zina, Baibulo limasonyeza komwe tinachokera, cholinga cha moyo ndiponso zomwe zidzachitika m’tsogolo. Ndithudi, limeneli ndi buku lofunikadi kuliphunzira!

Mwinamwake mwayesapo kale kuŵerenga Baibulo koma mwaona kuti n’lovuta kulimvetsa. Mwina simukudziŵa mmene mungapezere mayankho a mafunso anu. Ngati ndi choncho, simuli nokha ayi. Munthu wina amene anakhalako m’zaka za zana loyamba nayenso anali ndi vuto lomweli. Iye anakwera galeta lake paulendo wochokera ku Yerusalemu kupita ku dziko lakwawo ku Ethiopia. Mdindo wa ku Ethiopia ameneyo anali kuŵerenga mokweza buku la ulosi la m’Baibulo la Yesaya, lomwe linali litatha zaka zoposa mazana asanu ndi aŵiri chilembedwereni.

Mwadzidzidzi, munthu wina anathamangira galetalo ndipo anam’lonjera. Munthuyo anali Filipo, wophunzira wa Yesu, ndipo anafunsa Mwaitiopiyayo kuti: “Kodi muzindikira chimene muŵerenga?” Mwaitiopiyayo anayankha kuti: “Ndingathe bwanji, popanda munthu wonditsogolera ine?” Kenako anapempha Filipo kuti akwere pa galetalo. Filipo anafotokoza lemba lomwe munthuyo anali kuŵerenga komanso ‘analalikira kwa iye za Yesu.’​—Machitidwe 8:30-35.

Monga momwe Filipo kalelo anathandizira Mwaitiopiya kumvetsa Mawu a Mulungu, Mboni za Yehova nazonso zikuthandiza anthu kumvetsa Baibulo lerolino. Izo zidzakondwa kukuthandizani inunso. Nthaŵi zambiri, ndi bwino kuphunzira Baibulo mwadongosolo, kuyambira ndi ziphunzitso zoyambirira za m’Malemba. (Ahebri 6:1) Pamene mukupita patsogolo, mudzatha kumvetsa zomwe mtumwi Paulo anazitcha kuti: “chakudya chotafuna,” kutanthauza choonadi chakuya. (Ahebri 5:14) Ngakhale kuti mukuphunzira Baibulo, mabuku ena othandiza pophunzira Baibulo, angakuthandizeni kupeza ndi kumvetsa ndime zina m’Baibulo pankhani zosiyanasiyana.

Nthaŵi zambiri, mutha kukonza zoti muziphunzira panthaŵi ndi malo omwe mukufuna. Ena amaphunzira ngakhale pa telefoni. Phunziroli silikhala la m’kalasi ayi. Mmalo mwake, limakhala la inu mwini malinga ndi mmene mulili, komwe munakulira ndiponso maphunziro anu. Simulipira phunziro la Baibulo lotereli ayi. (Mateyu 10:8) Sipakhala mayeso ndipo simudzakhala opanikizika. Mafunso anu adzayankhidwa ndipo mudzaphunzira mmene mungam’fikire pafupi Mulungu. Komabe, kodi n’kuphunziriranji Baibulo? Onani zina mwa zifukwa zotsimikiza kuti kuphunzira Baibulo kungawonjezere chimwemwe m’moyo wanu.