Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Musalole Kuti Kukayika Kuwononge Chikhulupiriro Chanu

Musalole Kuti Kukayika Kuwononge Chikhulupiriro Chanu

 Musalole Kuti Kukayika Kuwononge Chikhulupiriro Chanu

Tsiku lina mukuganiza kuti muli bwino. Ndiyeno tsiku lotsatira mukudwala. Mwadzidzidzi, mukupeza kuti mulibenso mphamvu. Mutu wanu ukuŵaŵa ndipo thupi lanu likupweteka. Kodi chachitika n’chiyani? Tizilombo toyambitsa matenda taloŵa ndi kufooketsa mphamvu ya thupi lanu yodziteteza ku matenda ndipo taloŵerera ziwalo zofunika kwambiri m’thupi. Ngati sitigonjetsedwa, tizilombo timeneti tingawonongeretu thanzi lanu​—mwinanso kukuphani.

NDITHUDI, ngati matenda akugwirani pamene thanzi lanu silili bwino kwenikweni, mumakhala pangozi yaikulu. Mwachitsanzo, ngati thupi lanu lafooka ndi matenda a njala, mphamvu yachitetezo ya thupi lanu “imachepa kwambiri moti ngakhale matenda osadetsa nkhaŵa akhoza kukuphani,” akutero Peter Wingate, wolemba nkhani zamankhwala.

Podziŵa zimenezi, ndani angakonde kukhala ndi njala? Mosakayika, mumayesetsa kudya bwino kuti mukhale ndi thanzi labwino. Mwinanso mukuchita zonse zomwe mungathe kuti mupewe tizilombo toyambitsa matenda. Komabe, kodi mukusamala mofananamo kuti mukhale “olama m’chikhulupiriro”? (Tito 2:2) Mwachitsanzo, kodi ndinu atcheru kuti mupewe ngozi ya kukayika kumene kumayamba pang’onopang’ono? Mtima wa munthuwe suchedwa kukayika ndipo zimenezi zimawononga chikhulupiriro ndi ubale wako ndi Yehova. Anthu ena akuoneka ngati sakudziŵa za ngozi imeneyi. Amapereka mpata woti mtima wawo uyambe kukayika podzimana okha chakudya chauzimu. Kodi mwina inu mukuchitanso zimenezo?

Kodi Kukayika N’koipa Nthaŵi Zonse?

Ndithudi, kukayika kwina si koipa. Nthaŵi zina simufunika kukhulupirira nkhani iliyonse mpaka mutatsimikiza kuti n’zoonadi. Malangizo achipembedzo akuti muzingokhulupirira zilizonse popanda kukayika ndi oopsa ndiponso achinyengo. Zoonadi, Baibulo limati chikondi “chikhulupirira zinthu zonse.” (1 Akorinto 13:7) Mkristu wachikondi amakhulupiriradi munthu amene wadalirika kwa nthaŵi yaitali. Komabe, Mawu a Mulungu amatichenjezanso kuti ‘tisakhulupirire mawu onse.’ (Miyambo 14:15) Nthaŵi zina munthu tingamukayikire chifukwa cha mbiri yake. Baibulo likuchenjeza kuti: “Pamene [wabodza] akometsa mawu ake usam’khulupirire.”​—Miyambo 26:24, 25.

Mtumwi Yohane akuchenjezanso Akristu kuti asamangokhulupirira zinthu. Akulemba kuti: “Musamakhulupirira mawu ouziridwa alionse.” Koma, “yesani mawu ouziridwawo kuona ngati achokera kwa Mulungu.” (1 Yohane 4:1, NW) “Mawu,” omwe ndi chiphunzitso kapena maganizo, angaoneke ngati akuchokera kwa Mulungu. Koma kodi  achokeradi kwa iye? Kukayika, kapena kusakhulupirira zinthu zina msanga kungakutetezeni chifukwa, monga mmene mtumwi Yohane akunenera, “onyenga ambiri adatuluka kuloŵa m’dziko lapansi.”​—2 Yohane 7.

Kukayika Kopanda Maziko

Inde, munthu afunika kufufuza ndi mtima wonse ndiponso kudzichepetsa kuti apeze zoona zake za nkhaniyo. Komabe, zimenezi zikusiyana ndi kulola kuti kukayika kopanda maziko ndi kosokoneza zinthu kuzike mizu m’maganizo ndi mumtima mwathu. Inde, kukayika kumeneku kungawononge zikhulupiriro zathu ndi ubale wathu wolimba. Kukayika kumeneku ndiko kusatsimikiza zimene umakhulupirira kapena malingaliro ndipo kumakusokoneza posankha zochita. Kodi mukukumbukira zimene Satana anachita kuti Hava akayikire Yehova? Anafunsa kuti: “Eya! kodi anatitu Mulungu, Usadye mitengo yonse ya m’mundamu?” (Genesis 3:1) Funso looneka ngati labwinobwino limeneli linam’chititsa Hava kukayika ndipo linam’sokoneza posankha zochita. Ndi mmene Satana amachitira. Mofanana ndi munthu amene amalemba makalata oneneza ena, Satana amagwiritsa ntchito mwaluso nkhani zachinyengo, zooneka ngati zoona koma zili zabodza. Momwemonso wawononga maubale osaŵerengeka abwino ndiponso odalirika pogwiritsa ntchito mwamachenjera kukayika.​—Agalatiya 5:7-9.

Wophunzira Yakobo anadziŵa kuipa kwa mtundu umenewu wa kukayika. Analemba za mwayi waukulu umene tili nawo wopempha Yehova mwaufulu kuti atithandize pamene tikumana ndi ziyeso. Yakobo akuchenjeza kuti, popemphera kwa Mulungu, ‘tipemphe ndi chikhulupiriro, wosakayika konse.’ Tikamakayika pamene tili paubale ndi Yehova ‘timafanana ndi funde la nyanja lotengeka ndi mphepo ndi kuwinduka nayo.’ Timakhala ngati “munthu wa mitima iŵiri . . . wosinkhasinka pa njira zake zonse.” (Yakobo 1:6, 8) Timakhala osatsimikiza za zikhulupiriro zathu ndipo timakhala a mitima iŵiri. Ndiyeno, monga momwe zinalili ndi Hava, timakopeka mosavuta ndi ziphunzitso ndi mafilosofi auchiwanda osiyanasiyana.

Kukhalabe ndi Thanzi Labwino Lauzimu

Komano tingatani kuti tipewe kukayika koipa kumeneku? Yankho lake n’losavuta ayi: tikanitsitse mabodza a Satana ndi kulandira mokwanira chakudya chauzimu cha Mulungu kuti tikhale “okhazikika m’chikhulupiriro.”​—1 Petro 5:8-10.

Munthu payekha afunika kudzidyetsa bwino mwauzimu. Mlembi amene tamutchula poyambapo, Peter Wingate, akufotokoza kuti: “Ngakhale pamene munthu sakugwira ntchito, thupi limafunabe chakudya kuti chithandize ntchito zina ndiponso kuti ziwalo zofunika kwambiri m’thupi zigwire ntchito. Pamafunikanso kuti maselo atsopano aloŵe m’malo maselo owonongeka.” N’chimodzimodzi ndi thanzi lathu lauzimu. Ngati sitilandira chakudya chauzimu nthaŵi ndi nthaŵi, chikhulupiriro chathu chidzazilala pang’onopang’ono ndipo kenako chidzafa monga limachitira thupi losoŵa chakudya. Yesu Kristu anatsindika mfundo imeneyi pamene anati: “Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mawu onse akutuluka m’kamwa mwa Mulungu.”​—Mateyu 4:4.

Taganizani. Kodi tinachitanji kuti chikhulupiriro chathu chilimbe titangodziŵa kumene choonadi? Mtumwi Paulo akulemba kuti: “Chikhulupiriro chidza ndi mbiri.” (Aroma 10:17) Akutanthauza kuti poyambirira tinalimbitsa chikhulupiriro ndi chidaliro chathu mwa Yehova, malonjezo ake, ndi gulu lake mwa kudya Mawu a Mulungu. Ndithudi, sitinangokhulupirira mwachimbulimbuli zonse zimene tinamva. Tinachita zimene anthu a ku Bereya anachita. ‘Tinasanthula m’malembo masiku onse, ngati zinthu zinali zotero.’ (Machitidwe 17:11) ‘Tinazindikira chimene chili chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro,’ ndipo tinatsimikiza kuti zimene tinamva zinalidi zoona. (Aroma 12:2; 1 Atesalonika 5:21) Mosakayika, kuyambira pamenepo talimbitsa chikhulupiriro chathu pamene timamvetsa bwino kuti Mawu a Mulungu ndi malonjezo ake salephera.​—Yoswa 23:14; Yesaya 55:10, 11.

Pewani Njala Yauzimu

Tsopano tiyenera kulimba kuti tikhalebe ndi chikhulupiriro ndi kupewa kukayika kumene  kungafooketse kudalira kwathu Yehova ndi gulu lake. Kuti tichite zimenezi tiyenera kupitiriza kusanthula Malemba tsiku ndi tsiku. Mtumwi Paulo akuchenjeza kuti “m’masiku otsiriza ena [amene poyamba amaoneka ngati ali ndi chikhulupiriro cholimba] adzataya chikhulupiriro, ndi kusamala mizimu yosocheretsa ndi maphunziro a ziŵanda.” (1 Timoteo 4:1) Malingaliro ndi ziphunzitso zosocheretsa zimenezi zimabala kukayika m’maganizo mwa ena ndipo zimawasiyanitsa ndi Mulungu. Tingadziteteze bwanji? Tipitirize ‘kuleredwa m’mawuwo a chikhulupiriro, ndi malangizo abwino amene tidawatsata.’​—1 Timoteo 4:6.

Komabe, n’zomvetsa chisoni kuti ambiri lerolino amasiya ‘kuleredwa m’mawuwo a chikhulupiriro’​—ngakhale kuti chakudyacho chili chaulere. Monga momwe mmodzi mwa alembi a buku la Miyambo akunenera, munthu atha kukhala ndi chakudya chauzimu chabwino ndithu, phwando lauzimu, titero kunena kwake, koma osadya ndi kupukusa chakudyacho.​—Miyambo 19:24; 26:15.

Zimenezi n’zoopsa. Mlembiyo, Wingate, akuti: “Thupi likangoyamba kugwiritsa ntchito mapuloteni akeake thanzi lake limawonongeka.” Mukasoŵa chakudya, thupi lanu limayamba kugwiritsa ntchito mafuta a m’thupi. Mafuta ameneŵa akatha, thupi limayamba kugwiritsa ntchito mapuloteni omwe ali ofunika kwambiri kuti thupi lipitirize kukula ndi kukonza minofu yowonongeka. Ziwalo zofunika kwambiri m’thupi zimasiya kugwira ntchito. Ndiyeno mwamsanga thanzi lanu limawonongekeratu.

N’zimene zinachitikira ena mwauzimu mumpingo woyambirira wachikristu. Anali kungodalira zimene anaphunzira kale. Ayenera kuti ananyalanyaza phunziro laumwini, ndipo anafooka mwauzimu. (Ahebri 5:12) Mtumwi Paulo anafotokoza kuopsa kochita zimenezi pamene analembera Akristu achihebri kuti: “Tiyenera kusamaliradi zimene tidazimvazi kuti kapena tingatengedwe ndi kusiyana nazo.” Anadziŵa kuti n’zapafupi munthu kutengeka ndi kuloŵerera m’makhalidwe oipa ‘akapanda kusamala chipulumutso chachikulu chotero.’​—Ahebri 2:1, 3.

Chofunikanso kudziŵa n’chakuti munthu amene akudwala matenda a njala saoneka wofooka kapena woonda nthaŵi zonse. N’chimodzimodzinso munthu amene akudwala matenda a njala yauzimu sangaonekere mwamsanga. Mungaoneke ngati muli ndi thanzi labwino lauzimu ngakhale kuti simudya mokwanira. Komatu zingatero kwa nthaŵi yochepa chabe. M’kupita kwa nthaŵi, mudzafooka mwauzimu, mudzayamba kukayika popanda zifukwa zenizeni, ndipo mudzalephera kumenya zolimba nkhondo ya chikhulupiriro. (Yuda 3) Mukudziŵa bwino mmene inu panokha mukudyera chakudya chauzimu ngakhale kuti ena sakudziŵa.

Motero, pitirizani kuchita phunziro laumwini. Limbanani nako kukayika mwamphamvu kwambiri. Mukamalekerera kukayika koyambitsa nkhaŵa yosatha, mungapweteke monga momwe zimakhalira mukamanyalanyaza matenda amene akuoneka ngati osadetsa nkhaŵa. (2 Akorinto 11:3) ‘Kodi tilidi m’masiku otsiriza? Kodi uyenera kukhulupirira zonse zimene Baibulo limanena? Kodi ili ndi guludi la Yehova?’ Satana angakuchititseni kukayika motero. Musanyalanyaze m’pang’ono pomwe chakudya chauzimu kuti musapereke mpata wakuti ziphunzitso zake zonyenga ziloŵe mumtima mwanu. (Akolose 2:4-7) Tsatirani uphungu umene Timoteo analandira. Khalani wophunzira wabwino wa “malembo opatulika” kuti ‘mukhalebe inu mu izi zimene munaziphunzira, ndi kutsimikizika mtima nazo.’​—2 Timoteo 3:13-15.

Mwina mungafune thandizo kuti muchite zimenezi. Mlembi amene tamugwira mawu poyambapo akupitiriza kuti: “Njala yadzaoneni  ingachititse ziwalo zopukusa chakudya kuwonongeka chifukwa chosoŵa mavitameni ndi zinthu zina zofunika kwambiri moti sizingathenso kupukusa chakudya cha nthaŵi zonse chitapezeka. Kwa nthaŵi ndithu, munthu amene ali ndi vuto limeneli afunika chakudya chosavuta kupukusa.” Pamafunika kusamala kwambiri kuti achiritse matenda amene ayamba chifukwa chosoŵa chakudya m’thupi. Mofananamo, munthu amene wanyalanyaza kotheratu phunziro la Baibulo laumwini angafunike kum’thandiza ndi kum’limbikitsa kwambiri kuti ayambenso kulakalaka chakudya chauzimu. Ngati inunso muli ndi vuto limeneli, funani thandizo ndipo landirani ndi mtima wonse thandizo lililonse lomwe angakupatseni kuti libwezeretse nyonga ndi thanzi lanu lauzimu.​—Yakobo 5:14, 15.

‘Musagwedezeke Chifukwa cha Kusakhulupirira’

Poganizira mmene Abrahamu, kholo lakalelo linalili, mwina ena angaganize kuti iye anali ndi chifukwa chokwanira chokayikira. Mwina kungaoneke kukhala koyenera kunena kuti zinali “zosayembekezeka, kuti iye akakhale kholo la mitundu yambiri ya anthu”​—ngakhale kuti Mulungu analonjeza zimenezo. Chifukwa chiyani? Eya, m’kuganiza kwaumunthu, zinaoneka ngati sizingatheke. Baibulo likuti: ‘Sanalabadira thupi lake, ndilo longa ngati lakufa ndi mimba ya Sara idaumanso.’ Komabe, sanalole m’pang’ono pomwe kuti kukayikira Mulungu ndi malonjezo ake kukhazikike m’maganizo ndi mumtima mwake. Mtumwi Paulo analemba kuti: ‘Sanafooke m’chikhulupiriro,’ ndiponso “sanagwedezeka chifukwa cha kusakhulupirira.” Abrahamu ‘anakhazikikanso mumtima kuti, chimene [Mulungu] analonjeza, anali nayonso mphamvu ya kuchichita.’ (Aroma 4:18-21) Anali paubale wolimba ndi wokhulupirika ndi Yehova kwa zaka zambiri. Sanalole konse kukayika kumene kukanafooketsa ubale umenewo.

Mungachitenso chimodzimodzi ngati ‘mugwira chitsanzo cha mawu a moyo’​—ngati mudya bwino mwauzimu. (2 Timoteo 1:13) Musaipeputse mfundo yakuti kukayika n’kwangozi. Satana akumenya nkhondo ya zida zofalitsa tizilombo topereka matenda mwauzimu, titero kunena kwake. Ngati munyalanyaza kudya chakudya chabwino chauzimu mwa kusachita phunziro la Baibulo laumwini ndi kusapezeka pamisonkhano yachikristu, mukutsegula mpata woti Satana akuukireni. Idyani mokwanira chakudya chauzimu chochuluka ndiponso cha panthaŵi yake chimene “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” akupereka. (Mateyu 24:45) Pitirizani ‘kuvomerezana nawo mawu a moyowo’ kuti mukhalebe “olama m’chikhulupiriro.” (1 Timoteo 6:3; Tito 2:2) Musalole kuti kukayika kuwononge chikhulupiriro chanu.

[Zithunzi patsamba 21]

Kodi mukudya bwino mwauzimu?