Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Msonkhano wa Pachaka pa October 6, 2001

Msonkhano wa Pachaka pa October 6, 2001

 Msonkhano wa Pachaka pa October 6, 2001

MSONKHANO WA PACHAKA wa mamembala a Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania udzachitika pa October 6, 2001, pa Nyumba ya Msonkhano ya Mboni za Yehova, pa 2932 Kennedy Boulevard, Jersey City, ku New Jersey. Msonkhano woyamba udzakhala wa mamembala okhaokha pa 9:15 a.m., ndipo msonkhano wa pachaka wa onse udzatsatira pa 10:00 a.m.

Mamembala a bungweli adziŵitse Ofesi ya Mlembi tsopano lino ngati maadiresi awo olandirira makalata anasintha m’chaka chapitachi. Akatero ndiye kuti m’July adzalandira makalata owadziŵitsa anthaŵi zonse ndi mapepala ochitira voti.

Mamembalawo abweze mapepala ochitira voti omwe adzawatumizire pamodzi ndi mapepala owadziŵitsa za msonkhano wa pachakawu ku Ofesi ya Mlembi wa Sosaite pasanafike pa August 1. Membala aliyense alembe ndi kutumiza pepala lake lochitira voti mofulumira, ndipo afotokoze ngati adzapezeka pamsonkhanowu kapena ayi. Atsindike mfundo imeneyi papepala lililonse lochitira voti chifukwa n’limene lidzagwiritsidwa ntchito kudziŵa amene adzapezekapo.

Pulogalamu yonse, limodzi ndi msonkhano wa kayendetsedwe ka ntchito ndi malipoti, zidzatha pa 1:00 p.m. kapena kupitirira pang’ono pamenepo. Sipadzakhala pulogalamu yamasana. Chifukwa cha kuchepa kwa malo, okhala ndi matikiti okha ndi amene adzawalola kuloŵa. Sadzalunzanitsa patelefoni msonkhano wa pachakawu ku nyumba zina zosonkhanira.