Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi N’kuphunziriranji Baibulo?

Kodi N’kuphunziriranji Baibulo?

 Kodi N’kuphunziriranji Baibulo?

BILL anali mnyamata wojintcha, wophunzira ndiponso wopeza bwino. Komabe, sanali wokhutira. Moyo wake unalibe cholinga ndipo zimenezi zinali kum’vutitsa maganizo kwambiri. Pofuna kupeza cholinga m’moyo, anafufuza zipembedzo zosiyanasiyana koma sizinam’khutiritse. Mu 1991 anakumana ndi wa Mboni za Yehova, yemwe anam’patsa buku lofotokoza zomwe Baibulo limanena pankhani ya cholinga cha moyo. Anapangana zophunzira Baibulo kuti Bill amvetse nkhaniyi komanso nkhani zina.

Pokumbukira Bill anati: “Tinachitadi phunziro lathu loyamba ndipo popeza kuti kaŵirikaŵiri tinkaŵerenga Baibulo, ndinazindikira kuti n’zimene ndakhala ndikufuna. Mayankho a m’Baibulo anali osangalatsa kwabasi. Titamaliza phunzirolo, ndinakwera galimoto yanga kupita ku mapiri. Kumeneko, ndinatuluka m’galimoto langalo, ndikuyamba kufuula chifukwa cha chimwemwe chodzaza tsaya. Zinalitu zosangalatsa kwabasi kuti tsopano ndinali kuzindikira mayankho a mafunso anga.”

 N’zoona kuti si aliyense wopeza choonadi cha m’Baibulo amene amachita kufuula ndi chisangalalo. Ngakhale zili choncho, kuzindikira mayankho a mafunso ofunika kwambiri m’moyo kumakhala kosangalatsa zedi kwa anthu ambiri. Amamva monga momwe anamvera munthu wa m’fanizo la Yesu yemwe anapeza chuma chobisika m’munda. Yesu anati: “M’kuchikonda kwake achoka, nagulitsa zonse ali nazo, nagula munda umenewu.”​—Mateyu 13:44.

Chinsinsi cha Moyo Watanthauzo

Bill anadzifunsa kuti, Kodi cholinga cha moyo n’chiyani? Afilosofi, amaphunziro apamwamba a zaumulungu ndiponso asayansi ayesetsa kufuna kupeza yankho la funso limeneli kwa zaka masauzande ambiri. Anthu alemba mabuku osaŵerengeka pofuna kuyankha funsoli. Koma zonsezi zalephera ndipo ambiri angonena kuti funsoli silingayankhidwe. Komabe yankho lilipo. Ngakhale kuti n’lozama, sikuti n’lovuta kulimvetsa ayi. Baibulo limafotokoza yankho limenelo. Chinsinsi cha moyo wachimwemwe ndiponso watanthauzo ndicho: Kukhala ndi unansi woyenera ndi Yehova, Mlengi ndi Atate wathu wakumwamba. Kodi unansi umenewu timaupeza motani?

Pali mbali ziŵiri pankhani ya kuyandikira kwa Mulungu zomwe zimaoneka ngati zotsutsana. Amene amayandikira kwa Mulungu amamuopa ndiponso kumukonda. Tiyeni tione malemba aŵiri omwe akuvomereza mfundoyi. Kalekale, Mfumu yanzeru Solomo inachita kafukufuku wosamalitsa wokhudza anthu ndipo inalemba zomwe inapeza m’buku la m’Baibulo la Mlaliki. Posimba mwachidule zomwe anapezazo, Solomo analemba kuti: ‘Mawu atha, zonse zamveka zatha; opa Mulungu, musunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi.’ (Mlaliki 12:13) Patapita zaka mazana ambiri, atam’funsa lomwe linali lamulo lalikulu kuposa onse m’Chilamulo chomwe Mose analandira, Yesu anayankha kuti: ‘Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse.’ (Mateyu 22:37) Kodi kwa inuyo zikumveka zodabwitsa kuti tiyenera kuopa Mulungu ndiponso kumukonda? Tiyeni tione kufunika koopa ndi kukonda Mulungu komanso mmene zimenezi zimagwirira ntchito limodzi popanga unansi wabwino ndi Mulungu.

Zimene Kuopa Mulungu Kumatanthauza

Kuopa Mulungu mwaulemu n’kofunika kwambiri ngati tikufuna kumulambira movomerezeka. Baibulo limati: “Kumuopa Yehova ndiko chiyambi cha nzeru.” (Salmo 111:10) Mtumwi Paulo analemba kuti: “Tikhale nacho chisomo, chimene tikatumikire nacho Mulungu mom’kondweretsa, ndi kum’chitira ulemu ndi mantha.” (Ahebri 12:28) Nayenso mngelo amene mtumwi Yohane anamuona m’mlengalenga m’masomphenya, anayamba kulengeza uthenga wabwino ndi mawu akuti: “Opani Mulungu, m’patseni ulemerero.”​—Chivumbulutso 14:6, 7.

Kuopa Mulungu kumeneku komwe n’kofunika kwambiri si kuopa monthunthumira ayi. Tingaope monthunthumira ngati titaopsezedwa ndi wachifwamba woopsa. Koma kuopa Mulungu ndiko kupereka ulemu waukulu kwa Mlengi. Kumaphatikizaponso kuopa kusam’kondweretsa Mulungu chifukwa chakuti ndiye Woweruza Wamkulu ndiponso Wamphamvuyonse amene ali ndi mphamvu komanso ulamuliro wolanga osamvera.

Mantha ndi Chikondi N’zogwirizana

Komabe, Yehova safuna kuti anthu amutumikire chifukwa chakuti akuchita naye mantha ayi. Yehova ali Mulungu wachikondi kwabasi moti mtumwi Yohane analemba kuti: “Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yohane 4:8) Yehova Mulungu wakhala akuchita mwachikondi kwambiri ndi anthu ndipo amafuna kuti nawonso am’konde. Koma kodi zimenezi zikugwirizana bwanji ndi  kuopa Mulungu? Ziŵirizi n’zogwirizana kwambiri. Wamasalmo analemba kuti: ‘Unansi ndi Yehova uli kwa iwo akumuopa Iye.’​—Salmo 25:14, NW.

Talingalirani ulemu ndi mantha amene mwana amakhala nawo kwa atate ake amphamvu ndi anzeru. Panthaŵi imodzimodziyo, mwana woteroyo amasangalala ndi chikondi cha bambo ake. Mwanayo amakhulupirira bambo akewo ndipo amadalira malangizo awo, podziŵa kuti mosakayika malangizowo adzam’pindulitsa. Chimodzimodzinso ifeyo, ngati timakonda ndi kuopa Yehova, tidzamvera malangizo ake ndipo tidzapindula. Tamverani zomwe Yehova ananena zokhudza Aisrayeli. Iye anati: “Akadakhala nawo mtima wotere wakundiopa ine, ndi kusunga malamulo anga masiku onse, kuti chiwakomere iwo ndi ana awo nthaŵi zonse!”​—Deuteronomo 5:29.

Inde, kuopa Mulungu si ukapolo koma ufulu ndipo sikubweretsa chisoni koma chimwemwe. Yesaya analosera za Yesu kuti: “adzakondwera nako kumuopa Yehova.” (Yesaya 11:3) Ndipo wamasalmo analemba kuti: “Wodala munthu wakuopa Yehova, wakukondwera kwambiri ndi malamulo ake.”​—Salmo 112:1.

N’zodziŵikiratu kuti sitingamuope kapena kum’konda Mulungu ngati sitikum’dziŵa. N’chifukwa chake kuphunzira Baibulo kuli kofunika. Kuphunzira koteroko kudzatithandiza kumvetsa umunthu wa Mulungu ndi kuzindikira kuti n’kwanzeru kutsatira malangizo ake. Pamene tikum’yandikirabe Mulungu, tikuyesetsa kuchita chifuniro chake ndiponso tikusonkhezereka kusunga malamulo ake podziŵa kuti adzatipindulitsa.​—1 Yohane 5:3.

N’zosangalatsa kudziŵa kuti wina ali pa njira yoyenera m’moyo. Ndi mmene zilili kwa Bill yemwe tam’tchula poyamba uja. Posachedwapa, iye anati: “Kwa zaka zisanu ndi zinayi chiphunzirireni Baibulo koyamba, unansi wanga ndi Yehova wakula kwambiri. Chisangalalo chomwe ndinali nacho poyamba chakula kufika pa moyo wachimwemwe chenicheni. Nthaŵi zonse ndimaona moyo kukhala wabwino. Ndimagwira ntchito yatanthauzo tsiku lililonse osati kuvutika ndi kufunafuna zosangalatsa. Yehova ndi munthu weniweni kwa ine tsopano, ndipo ndikudziŵa kuti ali ndi chidwi chenicheni ndi moyo wanga.”

M’nkhani yotsatira, tidzafotokoza kwambiri za mmene kudziŵa Yehova kumabweretsera chimwemwe ndi mapindu kwa anthu amene amakugwiritsa ntchito m’miyoyo yawo.

[Mawu Otsindika patsamba 5]

Kumuyandikira Mulungu kumatanthauza kumukonda ndiponso kumuopa

[Chithunzi patsamba 6]

Yesu anakondwera ndi kuopa Yehova