Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Chikhulupiriro Chingasinthe Moyo Wanu

Chikhulupiriro Chingasinthe Moyo Wanu

Chikhulupiriro Chingasinthe Moyo Wanu

“NDITHUDI n’kotheka kukhala ndi makhalidwe abwino popanda kukhulupirira Mulungu.” Ananena choncho motsindika mayi wina wokhulupirira kuti Mulungu n’ngwosadziŵika. Iye ananena kuti polera ana ake ankawaphunzitsa makhalidwe abwino kwambiri, ndipo mmalo mwake nawonso, analera ana awo mofanana, koma onsewatu anatero popanda kukhulupirira Mulungu.

Kodi ndiye kuti kukhulupirira Mulungu n’kosafunika? Mwina munthuyu ankaganiza choncho. Ndipotu n’zoonadi kuti si kuti aliyense amene sakhulupirira Mulungu ndi munthu woipa. Mtumwi Paulo ananenapo za “anthu a mitundu” osadziŵa Mulungu koma amene “amachita mwa okha za lamulo.” (Aroma 2:14) Anthu onse, ngakhalenso okhulupirira kuti Mulungu n’ngwosadziŵika, anabadwa ndi chikumbumtima. Anthu ambiri amayesa kutsatira chikumbumtima chawo ngakhale kuti sakhulupirira Mulungu amene anawapatsa mphamvu imeneyi yosiyanitsira chabwino ndi choipa.

Komabe chikhulupiriro cholimba mwa Mulungu, chozikidwa m’Baibulo, chili ndi mphamvu zambiri zochititsa anthu zinthu zabwino kuposa zimene chikumbumtima chili nazo pachokha. Chikhulupiriro chozikidwa pa Mawu a Mulungu, Baibulo, chimaphunzitsa chikumbumtima, ndipo chimapangitsa kuti chikhale chokonzeka kusiyanitsa chabwino ku choipa. (Ahebri 5:14) Ndiponsotu, chikhulupiriro chimalimbikitsa anthu kuti akhalebe ndi miyezo yapamwamba ngakhale pamene ali pa mavuto aakulu. Mwachitsanzo, m’zaka za zana la 20, mayiko ambiri anayamba kulamulidwa ndi zipani zakuba, zimene zinachititsa kuti anthu ooneka kuti ndi amakhalidwe abwino achite nkhanza zoopsa. Komabe, anthu okhala ndi chikhulupiriro chenicheni mwa Mulungu anakana kusiya kutsata malangizo a makhalidwe abwino, ngakhale pamene moyo wawo unali kuopsezedwa. Kuphatikizanso apo, chikhulupiriro chozikidwa m’Baibulo chingathe kusintha anthu. Chingathe kupulumutsa miyoyo yooneka ngati yotayika ndipo chingathandize anthu kupeŵa kulakwitsa kwakukulu. Taonani zitsanzo zingapo chabe.

Chikhulupiriro Chingasinthe Moyo Wabanja

“Chifukwa cha chikhulupiriro chako wakwanitsa kuchita zosatheka.” Anatero woweruza wa ku England pamene anali kunena chigamulo chake pa nkhani ya kumangidwa kwa ana a John ndi Tania. Pamene John ndi Tania anadziŵika kwa akuluakulu a boma anali osakwatirana ndipo moyo wawo unali wovuta. John anali ndi vuto la kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo komanso chizoloŵezi chomatchova njuga, ndiye anayamba umbanda kuti azipeza ndalama zochitira mikhalidwe yake yoipayi. Iye ananyalanyaza ana ake ngakhalenso mayi wawo. Nanga kodi ndi “chozizwitsa” chotani chimene chinachitika?

Tsiku lina John anamva mwana wa mchimwene wake akulankhula za Paradaiso. Izi zinam’chititsa chidwi ndipo anakafunsa makolo ake a mnyamatayu. Makoloŵa ndi a Mboni za Yehova, ndipo anam’thandiza John kuphunzira zimenezi kuchokera m’Baibulo. Mwapang’onopang’ono John ndi Tania anayamba kukhala ndi chikhulupiriro chozikidwa m’Baibulo chimene chinasintha moyo wawo. Anakalembetsa ukwati wawo monga mwa lamulo ndipo anasiya makhalidwe awo oipa. Akuluakulu a boma amene anali kuyendera nyumba yawo anapezako chinthu chimene m’mbuyomo sichikadatheka ngakhale pang’ono; anapeza banjalo lili losangalala ndiponso lili m’nyumba yosamalidwa bwino, malo oyeneradi kulereramo ana. Woweruzayo ananena zoona kuti “chozizwitsa” chimenechi chachitika chifukwa cha chikhulupiriro chatsopano chimene John ndi Tania anapeza.

Makilomita zikwizikwi kuchokera ku England, kunali mkazi wapabanja ku Near East amene anangotsala pang’ono kuloŵa nawo m’chiŵerengero chosautsa zedi. Iye anali kukonzekera zokhala mmodzi wa anthu mamiliyoni amene chaka chilichonse mabanja awo amatha mwa kusudzulana. Anali ndi mwana, koma kungoti mwamuna wake anali wamkulu kwambiri kuposa iyeyo. Ndipo pa chifukwa ichi, abale ake anali kumulimbikitsa kuti amusudzule, motero anali atayamba kutero. Komabe, iye anali kuphunzira Baibulo ndi wa Mboni za Yehova. Pamene wa Mboniyu anamva za nkhaniyi, anamulongosolera zimene Baibulo limanena pa nkhani ya Banja. Mwachitsanzo, zakuti banja ndi mphatso yochokera kwa Mulungu ndipo kuti si chinthu choyenera kuchitaya mosaganizira bwino. (Mateyu 19:4-6, 9) Chamumtima, mkaziyo anaganiza motere: ‘N’zodabwitsa kuti mayi uyu, amene sindim’dziŵa, akuyesa kupulumutsa banja lathu pamene achinansi anga ndi amene akufuna kulithetsa.’ Chikhulupiriro chake chatsopano chinam’thandiza kusunga banja lake.

Chiŵerengero chosautsa chokhudza moyo wa banja ndicho cha kuchotsa mimba. Lipoti la bungwe la United Nations linanena kuti makanda osabadwa osachepera 45 miliyoni amaphedwa chifukwa cha kuchotsa dala mimba. Chochitika chilichonse choterechi ndi tsoka lalikulu. Kuphunzira Baibulo kunathandiza mayi wina ku Phillipines kupeŵa kukulitsa nawo chiŵerengerochi.

Mayiyu anayenderedwa ndi a Mboni za Yehova, ndipo analandira bulosha la phunziro la Baibulo lotchedwa Kodi Mulungu Amafunanji Kwa Ife?, * ndiponso anayamba kuphunzira Baibulo. Patatha miyezi ina iye analongosola chifukwa chake anatero. Panthaŵi yoyamba imene a Mboniwo anamuyendera, mayiyu anali ndi pakati koma iye pamodzi ndi mwamuna wake anagwirizana zakuti achotse mimbayo. Komabe, chithunzi cha mwana wosabadwa chimene chili patsamba 24 la buloshali chinam’khudza mtima mayiyu. Ndipo mawu ozikidwa m’Baibulo olongosola kuti moyo n’ngopatulika chifukwa ‘chitsime cha moyo chili ndi Mulungu’, anam’chititsa iye kuti asaphe mwana wake. (Salmo 36:9) Tsopano iye ndi mayi wokhala ndi chimwana chokongola ndiponso chathanzi.

Chikhulupiriro Chimathandiza Anthu Onyozedwa

Ku Ethiopia, anthu aŵiri osavala bwino anapita ku msonkhano wochitidwa ndi Mboni za Yehova kuti akalambire. Pamapeto pa msonkhanowo, Wamboni wina anawapatsa moni ndi kuwauza dzina lake mwansangala. Anthuwo anam’pempha kuti awapatseko kangachepe. Wamboniyo sanawapatse ndalama ayi, koma anawapatsa chinthu chofunika kuposa ndalama. Iye anawalimbikitsa powauza kuti akulitse chikhulupiriro mwa Mulungu, chimene chili cha “mtengo wake woposa wa golidi.” (1 Petro 1:7) Mmodziyo anamvera ndipo anayamba kuphunzira Baibulo. Zimenezi zinam’pangitsa kusintha moyo wake. Atayamba kukula m’chikhulupiriro, anasiya kusuta, kumwa moŵa mwauchidakwa, chimasomaso, ndi kugwiritsa ntchito khat (mankhwala osokoneza bongo ovuta kusiya). Anaphunzira kudzithandiza yekha mmalo mopemphapempha ndipo tsopano amakhala moyo wopanda zautchisi ndiponso wopindulitsa.

Ku Italy, munthu wazaka 47 anapatsidwa chilango choti akhale m’ndende kwa zaka khumi ndipo anaikidwa m’chipatala chandende chochiritsa nthenda za maganizo. Wamboni za Yehova wina amene amaloledwa kuloŵa m’ndende kuti athandize anthu mwauzimu anaphunzira naye Baibulo. Munthuyu anapita patsogolo mwamsanga. Chikhulupiriro chinasintha moyo wake kwambiri mwakuti tsopano akaidi anzake amapita kwa iyeyo kuti akawalangize mmene angathetsere mavuto awo. Chikhulupiriro chake chozikidwa m’Baibulo chachititsa kuti apatsidwe ulemu, kuopedwa, ndiponso kukhulupiridwa ndi akuluakulu a pandendepo.

M’zaka zimene tikukhalazi nyuzipepala zakhala zikusimba za nkhondo zapachiweniweni mu Africa. Nkhani zoopsa kwambiri ndizo zosimba za anyamata ang’onoang’ono amene amaphunzitsidwa kukhala asilikali. Ana ameneŵa amapatsidwa mankhwala osokoneza bongo, amazunzidwa, ndiponso amakakamizidwa kuchita zinthu zoopsa kwambiri kwa achibale awo n’cholinga chakuti atsimikizire kuti ali okhulupirika kugulu lokha limene akulimenyera nkhondo. Kodi chikhulupiriro chozikidwa m’Baibulo n’champhamvu zokwanira kusintha miyoyo ya ana otereŵa? Chinali chokwanira m’zochitika zina ziŵiri.

Ku Liberia, Alex anali mnyamata wa kuguwa m’Tchalitchi cha Chikatolika. Koma atafika zaka 13, analoŵa nawo m’gulu lina lankhondo ndipo anasanduka msilikali wamng’ono wotchuka. Anayamba ufiti kuti asamachite mantha kunkhondo. Alex anaona anzake ambiri akuphedwa koma iye anali kupulumuka. Mu 1997 anapezana ndi a Mboni za Yehova ndipo anaona kuti sanali kumunyoza. Mmalo mwake, iwo anam’thandiza pomuphunzitsa zimene Baibulo limanena pa nkhani ya chiwawa. Alex anachokamo m’gulu lankhondo lija. Chikhulupiriro chake chitayamba kukula, iye anatsatira lamulo la Baibulo lakuti: “Apatuke pachoipa, nachite chabwino; afunefune mtendere ndi kuulondola.”​—1 Petro 3:11.

Panthaŵi yomweyi, mwana wina wotchedwa Samson amene poyamba anali msilikali, anatulukira m’mudzi umene Alex akukhala pakali pano. Iye anali mnyamata wa kwaya koma mu 1993 anasanduka msilikali, n’kuyamba kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, kukhulupirira mizimu, ndiponso chimasomaso. Mu 1997 anam’tulitsa pansi zida. Ndiye pamene Samson anali pa ulendo wopita ku Monrovia kuti akaloŵe kagulu kapadera ka zachitetezo anakumana ndi mnzake amene anamusintha maganizo pomuuza kuti ayambe kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, ndipo chotsatira chake chinali chakuti anakhala ndi chikhulupiriro chozikidwa m’Baibulo. Zimenezi zinam’limbitsa mtima kotero kuti anasiya khalidwe lake lokonda nkhondo. Alex ndi Samson yemwe, pakali pano akukhala moyo wamtendere ndiponso wamakhalidwe abwino. Kodi pali chinthu china chilichonse chimene chikadasintha moyo wa anthu amene akhala akuvutitsidwa chonchi kupatulako chikhulupiriro chozikidwa m’Baibulo?

Chikhulupiriro Choyenera

Zitsanzo zimenezi n’zochepa chabe, palinso zambiri zimene tingathe kuzitchula kusonyeza mphamvu ya chikhulupiriro chenicheni chozikidwa m’Baibulo. N’zoona kuti si kuti aliyense amene amangoti amakhulupirira Mulungu ndiye kuti ali ndi miyezo yapamwamba ya m’Baibulo. N’zoona kuti anthu ena osakhulupirira Mulungu angakhale abwinopo kuposa anthu ena odzitcha Akristu. Ichi n’chifukwa chakuti chikhulupiriro chozikidwa m’Baibulo si ndicho kungonena kuti mumakhulupirira Mulungu.

Mtumwi Paulo anati chikhulupiriro ndicho “chikhazikitso cha zinthu zoyembekezeka, chiyesero cha zinthu zosapenyeka.” (Ahebri 11:1) Motero, chikhulupiriro chimaphatikizapo chiyembekezo chachikulu chozikidwa pa umboni wotsimikizirika bwino wokhudza zinthu zosaoneka. Kwenikweni chimaphatikizapo kusakayikira ngakhale pang’ono kuti Mulungu aliko, kuti amatiganizira, ndiponso kuti adzadalitsa onse amene amachita chifuniro chake. Mtumwiyu ananenanso kuti: “Iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphoto iwo akum’funa Iye.”​—Ahebri 11:6.

Chinali chikhulupiriro choterechi chimene chinasintha moyo wa John, Tania, ndiponso anthu ena otchulidwa m’nkhani ino. Chinapangitsa kuti akhale ndi chidaliro pa Mawu a Mulungu, Baibulo, kaamba ka chitsogozo pamene akusankha chochita. Chinawathandiza kuchita zinthu modzimana kwa kanthaŵi kuti asatenge njira yosavuta koma ili yoipa. Ngakhale kuti nkhanizi n’zosiyanasiyana, izo zinayamba mofanana. Wamboni za Yehova wina anaphunzira Baibulo ndi anthu ameneŵa, ndipo anayamba kuona kuti mawu amene Baibulo limanena akuti: “Mawu a Mulungu ali amoyo ndipo amapatsa mphamvu,” n’ngoona. (Ahebri 4:12, NW) Mphamvu ya Mawu a Mulungu inathandiza aliyense wa anthu ameneŵa kukhala ndi chikhulupiriro champhamvu chimene chinasintha moyo wawo kukhala wabwinopo.

Mboni za Yehova zikugwira ntchito m’mayiko 230 ndiponso m’zilumba za m’nyanja. Akukupatsani mwayi wa kuphunzira Baibulo. N’chifukwa chiyani akutero? Chifukwa chakuti ali otsimikiza kuti chikhulupiriro chozikidwa m’Baibulo chingasinthe kwambiri ngakhalenso moyo wanu womwe.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 10 Lofalitsidwa ndi Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania.

[Zithunzi patsamba 3]

Chikhulupiriro chozikidwa m’Baibulo chimasintha miyoyo kukhala yabwinopo

[Mawu a Chithunzi patsamba 2]

Title card of Biblia nieświeska by Szymon Budny, 1572